Usodzi Panyanja ya Galileya
KODI moyo wa msodzi unali wotani panyanja ya Galileya m’nthawi ya Yesu? Yankho la funso limeneli limatithandiza kumvetsa nkhani zambiri za m’Mauthenga Abwino, monga imene tangomaliza kukambiranayi.
Nyanja imeneyi ndi yaikulu pafupifupi makilomita 21 m’litali ndipo m’lifupi ndi ya makilomita pafupifupi 12. Asodzi akhala akupha nsomba zambiri m’nyanja imeneyi kwanthawi yaitali. Zikuoneka kuti malo a ku Yerusalemu otchedwa “chipata chansomba” anali msika wa nsomba. (Nehemiya 3:3) Nsomba zina zimene zinkagulitsidwa kumsika umenewu zinali zochokera m’nyanja ya Galileya.
Mtumwi Petulo anali wochokera m’tauni ya Betsaida yomwe inali mphepete mwa nyanja ya Galileya. Mwina dzina la tauniyi limatanthauza “Nyumba ya Msodzi.” Tauni ina imene inali mphepete mwa nyanjayi ndi Magadani, kapena kuti Magadala, kumene Yesu anapita ndi ophunzira ake nthawi ina atayenda panyanja. (Mateyo 15:39) Malinga ndi zimene wolemba mabuku wina ananena, dzina lachigiriki la tauniyi lingamasuliridwe kuti “Mudzi Wokonzera Nsomba.” Tauniyi inali ndi mafakitale akuluakulu okonzera nsomba. Ndipo anthu ankati akapha nsomba m’deralo, ankapita nazo kumeneku kukaziumitsa, kuzithira mchere kapenanso kuziviika m’madzi enaake kuti apange msuzi umene ankausunga m’mitsuko. Akakonza nsombazo, ankazitumiza m’madera ena a ku Isiraeli kapena kunja.
Choncho ku Galileya m’nthawi ya Yesu, bizinesi yopha, kukonza ndi kugulitsa nsomba inali ya ndalama zambiri. Anthu angaganize kuti bizinesi imeneyi inkathandiza anthu ambiri m’derali kupeza ndalama. Koma si mmene zinalili. Katswiri wina wamaphunziro ananena kuti, “anthu sankasodza ‘mwachisawawa’ monga mmene anthu owerenga Chipangano Chatsopano masiku ano angaganizire.” Katswiriyu ananenanso kuti: “Boma ndi limene linkayang’anira ntchitoyi ndipo amene ankapindula nayo kwambiri ndi anthu otchuka basi.”
Panthawiyi, Herode Antipa anali wolamulira kapena kuti mfumu ya chigawo cha Galileya ndipo anachita kusankhidwa ndi ufumu wa Roma. Choncho, iye ndi amene ankayang’anira misewu, madoko ndiponso zinthu zachilengedwe za m’dera lake monga migodi ndi nkhalango. Ankayang’aniranso ntchito zaulimi ndi zausodzi. Herode ankapeza ndalama zambiri chifukwa cha zinthu zimenezi. Sitikudziwa kwenikweni njira imene ankatsatira potolera ndalama za msonkho ku Galileya panthawi ya Yesu. Komabe, zikuoneka kuti njira imene Herode ankatsatira, ndi yofanana ndi njira imene ankatsatira atsogoleri achigiriki kapena achiroma m’madera ena. Ndalama zambiri zimene ankapeza pantchito zosiyanasiyana za m’derali ndiponso pazinthu zachilengedwe, zinkapita kwa anthu olemera m’malo mopita kwa anthu osauka amene amagwira ntchitozo.
Msonkho Unali Wokwera
M’nthawi ya Yesu, madera abwino a ku Galileya anali akubanja lachifumu ndipo anagawidwa m’magawo akuluakulu. Herode Antipa ankapereka magawo amenewa ngati mphatso kwa akuluakulu a boma lake ndiponso anthu ena. Anthu wamba ndi amene ankapereka ndalama zoti Herode Antipa azilipirira zinthu zimene amafunika pamoyo wake wofuna zinthu zambiri, kumangira zinthu zikuluzikulu, kuyendetsera boma lake ndiponso kupereka mphatso kwa anzake kapena kumizinda ina. Anthu amanena kuti misonkhoyi inali yokwera ndipo ankapondereza kwambiri anthu wamba.
Herode analinso ndi ulamuliro waukulu panyanja ya Galileya. Choncho, iye ndi amene ankayang’anira ntchito yosodza panyanjayi ndipo nthawi zina ankapatsa udindo woyang’anira ntchitoyi kwa anthu ena. M’madera amene iye ankayang’anira, anthu olemera ankapereka ndalama zambiri kuboma kuti apatsidwe chilolezo choti ndalama za misonkho zomwe azitolera kwa asodzi zizikhala zawo. Anthu amenewa ndi amene anali ndi mphamvu zolola asodzi kupha nsomba panyanjayo. Ena amati Mateyo ankagwira ntchito kwa anthu amenewa “yopereka chilolezo chopha nsomba” m’deralo. Iwo amatero chifukwa chakuti ofesi yake yotolera msonkho inali ku Kaperenao, womwe unali mzinda wa m’mphepete mwa nyanja ya Galileya, wofunika kwambiri pantchito ya usodzi.a
Umboni wa zaka za m’ma 100 B.C.E. umasonyeza kuti nthawi zambiri anthu a ku Palestina popereka msonkho, ankapereka zinthu zina m’malo mwa ndalama. Choncho, asodzi akuluakulu ankapereka nsomba pakati pa 25 ndi 40, pa nsomba 100 zilizonse n’cholinga chakuti aziloledwa kupha nsomba m’nyanjayi. Zikalata zakale zimasonyeza kuti m’madera ena omwe ankalamuliridwa ndi Aroma, boma ndi limene linkayang’anira ntchito yosodza pogwiritsa ntchito anthu amene analembedwa ntchito yoyang’anira. Ku Pisidiya, kunali asilikali amene ankaletsa anthu kupha nsomba popanda chilolezo ndipo iwo ankaonetsetsa kuti asodzi akapha nsomba, agulitse kwa anthu ovomerezeka ndi boma basi. Ndipo anthuwo ankapereka msonkho ndiponso ankagwira ntchito yawo moyang’aniridwa ndi boma.
Munthu wina ananena kuti malamulo ndiponso misonkho yonseyi ikusonyeza kuti “mfumu kapena anthu amene mfumuyo inawapatsa udindo wotolera misonkho, ndi amene ankapindula kwambiri, osati asodzi.” Ndalama zimene anthu ena ogwira ntchito zosiyanasiyana ankapeza zinalinso zochepa chifukwa ankapereka misonkho yokwera kwambiri. Palibe munthu amene amasangalala ndi kupereka msonkho. Komabe, Mauthenga Abwino amasonyeza kuti anthu ambiri ankadana ndi otolera misonkho pachifukwa chinanso. Iwo ankalemera chifukwa anali osaona mtima, adyera ndiponso chifukwa choti ankakakamiza anthu wamba kupereka ndalama zambiri.—Luka 3:13; 19:2, 8.
Asodzi Otchulidwa M’Mauthenga Abwino
Mauthenga abwino amasonyeza kuti Simoni Petulo ankagwira ntchito yausodzi ndi anthu ena. Anthu amene anamuthandiza kukoka ukonde atapha nsomba mozizwitsa anali ‘anzake amene anali m’ngalawa ina.’ (Luka 5:3-7) Akatswiri a maphunziro amanena kuti “asodzi ankakhala ‘m’magulu’ . . . kuti apeze chilolezo chopha nsomba.” Ziyenera kuti ndi mmene ana a Zebedayo, Petulo, Andireya ndi anzawo ena anapezera chilolezo chawo.
Malemba sanena ngati asodzi a ku Galileya amenewa anali ndi ngalawa ndiponso zipangizo zawozawo zophera nsomba. Anthu ena amakhulupirira kuti anali nazo. Ndipotu, Baibulo limanena kuti Yesu anakwera ngalawa “ya Simoni.” (Luka 5:3) Komabe, pankhani imeneyi ena amanena kuti, “n’zotheka kuti ngalawazi zinali zimene magulu a asodzi ankabwereka kwa anthu amene ankapereka chilolezo chakuti anthu azipha nsomba.” Kaya zimenezi n’zoona kapena ayi, Malemba amangonena kuti Yakobe ndi Yohane anali kukonza maukonde awo. Asodzi ayenera kuti ankagulitsa nsomba zawo motchipa, ndipo nthawi zina, ankalemba aganyu kuti awagulitsire.
Choncho, asodzi a ku Galileya a m’nthawi ya Yesu ankachita zambiri kuposa zimene tingaganizire. Bizinesi yawo inali mbali ya ntchito yaikulu ya zachuma m’deralo. Kudziwa zimenezi kumatithandiza kumvetsa bwino nkhani za m’Mauthenga Abwino ndiponso mawu a Yesu onena za asodzi komanso ntchito yawo yopha nsomba. Nkhaniyi ikutithandizanso kwambiri kumvetsa chikhulupiriro cha Petulo, Andireya, Yakobe ndi Yohane. Iwo ankadalira kwambiri ntchito yopha nsomba. Kaya anthuwa anali ndi chuma chochuluka bwanji pamene Yesu ankawaitana, iwo anasiya nthawi yomweyo ntchito imene inkawathandiza kupeza zinthu zofunika pamoyo wawo. Anachita zimenezi kuti akhale“asodzi a anthu.”—Mateyo 4:19.
[Mawu a M’munsi]
a Zikuoneka kuti mtumwi Petulo anasamukira ku Kaperenao kuchoka ku Betsaida kuti azikagwira ntchito yopha nsomba ndi mchimwene wake Andireya komanso ana a Zebedayo. Yesu anakhalanso ku Kaperenao kwa kanthawi ndithu.—Mateyo 4:13-16.
[Mapu patsamba 25]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Nyanja ya Hula
Betsaida
Kaperenao
Magadani
Nyanja ya Galileya
Yerusalemu
Nyanja Yakufa
[Mawu a Chithunzi]
Todd Bolen/Bible Places.com
[Mawu a Chithunzi patsamba 26]
Todd Bolen/Bible Places.com