Mumzinda wa Harana Munkachitika Zinthu Zambiri
ANTHU amene amawerenga Malemba akangomva dzina lakuti Harana, nthawi yomweyo amakumbukira Abulahamu mtumiki wokhulupirika. Ali pa ulendo wawo wochokera ku Uri kupita ku Kanani, Abulahamu, mkazi wake Sara, bambo ake a Tera ndiponso mwana wa mphwake Loti, anakhala ku Harana. Kumeneku Abulahamu anapeza katundu wambiri. Bambo ake atamwalira, iye anapitiriza ulendo wake wopita kudziko limene Yehova Mulungu anamulonjeza. (Gen. 11:31, 32; 12:4, 5; Mac. 7:2-4) Patapita nthawi, Abulahamu anauza mtumiki wake wamkulu kuti apite ku Harana kapena dera lapafupi ndi mzindawu kuti akapezere mwana wake Isake, mkazi. Yakobo mdzukulu wa Abulahamu anakhalaponso kumeneku kwa zaka zambiri.—Gen. 24:1-4, 10; 27:42-45; 28:1, 2, 10.
Pamene Mfumu Sanakeribu ya Asuri inaopseza Mfumu Hezekiya ya Yuda, inatchula Harana kuti unali umodzi mwa “mitundu” imene inagonjetsedwa ndi mafumu a Asuri. Apa mawu akuti “Harana” sakutanthauza mzinda wokhawo ayi, koma akuphatikizaponso madera ena ozungulira mzindawu. (2 Maf. 19:11, 12) Ulosi wa Ezekieli umasonyeza kuti Harana unali umodzi mwa mizinda imene inkachita malonda ndi Turo, ndipo uwu ndi umboni wakuti mzinda wa Harana unali wofunika kwambiri pa nkhani ya malonda.—Ezek. 27:1, 2, 23.
Panopa mzinda wa Harana ndi tauni yaing’ono yomwe ili pafupi ndi mzinda wa Şanlıurfa womwe uli cha kum’mawa kwa dziko la Turkey. Koma kalelo mumzinda wa Harana munkachitika zinthu zambiri. Mzindawu ndi umodzi mwa mizinda yakale yochepa chabe imene imadziwikabe ndi dzina lake la m’Baibulo. Mu m’chinenero cha Asuri dzinali linkalembedwa kuti Harranu ndipo limatanthauza “Msewu” kapena “Msewu wa Amalonda.” Zimenezi zikusonyeza kuti mzinda wa Harana unali pa mphambano ya misewu imene amalonda ochokera m’mizinda ina ikuluikulu ankadutsa. Zolemba zakale zimene zinafukulidwa ku Harana, zimasonyeza kuti amayi a Mfumu Nabonidasi wa ku Babulo anali mkulu wa ansembe wamkazi pa kachisi wa Sin, yemwe anali mulungu wa mwezi wa ku Harana. Anthu ena amanena kuti Nabonidasi ndi amene anamanganso kachisi ameneyu. Kuchokera nthawi imeneyo, pakhala maufumu osiyanasiyana koma mzinda wa Harana udakalipobe.
Masiku ano mzinda wa Harana ndi wosiyana kwambiri ndi mmene unalili kale. Mzinda wakale wa Harana unali wotukuka kwambiri ndiponso wofunika makamaka m’nyengo zina. Koma masiku ano ku Harana kwangokhala nyumba za madenga ozungulira. M’mbali mwa mzindawu muli mabwinja a zinthu zakale. M’dziko lapansi latsopano limene Mulungu walonjeza, anthu amene anakhalapo ku Harana monga Abulahamu, Sara ndiponso Loti adzaukitsidwa. N’zoonekeratu kuti iwo adzatiuza zambiri zokhudza mzinda wa Harana mmene munkachitika zinthu zambiri.
[Chithunzi patsamba 20]
Mabwinja a ku Harana
[Chithunzi patsamba 20]
Nyumba za madenga ozungulira
[Chithunzi patsamba 20]
Mmene mzinda wa Harana umaonekera masiku ano