‘Aliyense Apereke Chopereka kwa Yehova’
KODI munthu wina akakuchitirani zabwino mumachita chiyani pofuna kuyamikira? Tiyeni tione zimene akuluakulu a asilikali a Isiraeli anachita poyamikira atapambana pa nkhondo yomenyana ndi Amidiyani. Nkhondoyi inamenyedwa Aisiraeli atachimwa chifukwa cholambira Baala wa ku Peori. Mulungu anathandiza anthu ake kuti apambane ndipo zinthu zimene analanda anazipereka kwa asilikali 12,000 ndiponso kwa Aisiraeli ena onse. Malinga ndi malangizo amene Yehova anawapatsa, asilikaliwo anapereka zina mwa zinthu zimene analandirazo kwa ansembe. Aisiraeli ena onse anaperekanso zina mwa zinthu zimene analandira kwa anzawo a fuko la Levi ndipo zinthu zimenezi zinali zochuluka mofanana ndi zimene asilikali anapereka kwa ansembe.—Num. 31:1-5, 25-30.
Koma akuluakulu a asilikali ankafuna kuchitanso zinthu zina. Iwo anauza Mose kuti: “Atumiki anufe tawerenga amuna onse ankhondo amene tikuwayang’anira, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene akusowapo.” Iwo anaganiza zoti apereke kwa Yehova golide ndi zinthu zina zokongoletsera. Zinthu zokongoletsera zimene anapereka zinali zolemera makilogalamu 190.—Num. 31:49-54.
Masiku anonso anthu ambiri ali ndi mtima wofuna kuyamikira Yehova chifukwa cha zinthu zabwino zimene wawachitira. Ndipotu si atumiki a Mulungu okha amene ali ndi mtima woyamikira. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi dalaivala wa basi amene anatenga anthu popita ndiponso pobwera ku msonkhano wa mayiko ku Bologna m’dziko la Italy mu 2009. Chifukwa chakuti ankayendetsa basi mosamala ndipo anali wofatsa, anthu amene anakwera basiyo anaganiza zomulembera kalata yoyamikira komanso kumupatsa ndalama ndi buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Koma dalaivalayo anati: “Ndayamikira kwambiri kalatayi ndi buku lomwe mwandipatsa. Koma tengani ndalamazi. Ndikufuna kuti ndalama zimenezi zithandize pa ntchito yanu. Ngakhale kuti sindine wa Mboni za Yehova, ndikufuna kupereka ndalama zimenezi chifukwa ndaona kuti mumachita zinthu chifukwa cha chikondi.”
Njira imodzi imene mungasonyezere kuyamikira zimene Yehova wakuchitirani ndi mwa kupereka zopereka zothandiza pa ntchito ya padziko lonse ya Mboni za Yehova. (Mat. 24:24) Bokosi limene lili m’munsimu likusonyeza njira zimene ena amaperekera.