Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Yesu anauza anthu kuti: “Khalani angwiro, monga mmene Atate wanu wakumwamba alili wangwiro.” Kodi zingatheke bwanji kuti anthu masiku ano akhale “angwiro”?—Mat. 5:48.
Kuti tiyankhe funso limeneli, choyamba tiyenera kumvetsa tanthauzo la mawu akuti “ungwiro” m’Baibulo. Nthawi zina pamene Malemba amafotokoza zinthu kukhala “zangwiro” satanthauza kuti zinthuzo zilibe vuto lililonse. Koma Yehova ndiye wangwiro, kutanthauza kuti salakwitsa chilichonse. Anthu ndiponso zinthu sizingakhale zangwiro kwenikweni. Mawu a m’Baibulo achiheberi komanso achigiriki amene anamasuliridwa kuti “ungwiro” amatanthauza “kukwanira,” “kukhwima” ndiponso “kusalakwika” mogwirizana ndi mfundo zokhazikitsidwa mwa lamulo. Nthawi zambiri tikamagwiritsa ntchito mawuwa sikuti amanena za zinthu zimene zilibe cholakwa chilichonse. Mwachitsanzo, ena akamafotokoza za munthu amene sakudwala ndipo ali ndi mphamvu amati munthuyo ndi wangwiro.
Adamu ndi Hava analengedwa angwiro. Iwo anali ndi makhalidwe abwino, ubwenzi wabwino ndi Yehova ndiponso thanzi labwino kwambiri. Iwo anali angwiro mogwirizana ndi mfundo zimene Mlengi wawo anakhazikitsa. Chifukwa cha kusamvera, iwo anakhala operewera pa mfundo zimenezi ndipo sanakhalenso angwiro limodzi ndi mbadwa zawo zonse. Choncho kudzera mwa Adamu, uchimo, kupanda ungwiro ndiponso imfa zinafalikira kwa anthu onse.—Aroma 5:12.
Malinga ndi zimene Yesu ananena pa Ulaliki wa Paphiri, ngakhale anthu ochimwa akhoza kukhala angwiro pa mlingo winawake. Pa ulaliki umenewu iye anafotokoza mfundo zimene zingathandize anthu kukhala angwiro posonyeza chikondi. Chikondi chake ndi chofanana ndi chimene Mulungu amasonyeza anthu. Yesu anati: “Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani, kuti musonyeze kuti ndinudi ana a Atate wanu wakumwamba. Chifukwa iye amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsira mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.” (Mat. 5:44, 45) Ophunzira a Yesu akamasonyeza chikondi choterechi amakhala akutsatira chitsanzo changwiro cha Mulungu.
Masiku ano, a Mboni za Yehova padziko lonse amayesetsa kwambiri kusonyeza anthu chikondi chimenechi. Iwo amafunitsitsa kuthandiza anthu osiyanasiyana kudziwa choonadi cha m’Baibulo mosaganizira za chikhalidwe, mtundu kapena chipembedzo cha anthuwo. Panopa a Mboni akuchititsa maphunziro a Baibulo oposa 7,000,000 m’mayiko 236.
Yesu anafunsa kuti: “Mukamakonda anthu okhawo amene amakukondani, kodi mudzalandira mphoto yotani? Kodi okhometsa msonkho sachitanso zimenezo? Ngati mupatsa moni abale anu okha, kodi n’chiyani chachilendo chimene mukuchita? Kodi anthu a mitundu ina nawonso sachita zomwezo?” (Mat. 5:46, 47) Akhristu oona sakondera anthu ena chifukwa cha maphunziro kapena mtundu wawo. Iwo sakonda anthu okhawo amene angawabwezere zabwino. M’malomwake iwo amathandiza anthu osauka, odwala, achinyamata ndi achikulire omwe. Akamatero, Akhristu amatsanzira chikondi cha Yehova ndipo amakhala angwiro pa mlingo winawake.
Kodi zidzatheka kukhala angwiro ngati mmene Adamu analili poyamba? Inde. Chifukwa chokhulupirira nsembe ya dipo imene Yesu anapereka, anthu omvera adzakhala angwiro mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu. Pa nthawi imeneyi, ‘Mwana wa Mulungu adzawononga ntchito za Mdyerekezi.’—1 Yoh. 3:8.