Kodi Mwalowa mu Mpumulo wa Mulungu?
“Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu.”—AHEB. 4:12.
1. Kodi tingalowe bwanji mu mpumulo wa Mulungu masiku ano, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi n’zovuta nthawi zina?
M’NKHANI yapitayi tinaphunzira kuti tingalowe mu mpumulo wa Mulungu ngati timamumvera ndiponso kuchita zinthu mogwirizana ndi zolinga zake. Koma nthawi zina kuchita zimenezi n’kovuta. Mwachitsanzo, tikamva kuti Yehova amadana ndi zinthu zina zimene timakonda, zimativuta kumvera nthawi yomweyo. Zimenezi zikutanthauza kuti tifunika kuphunzira kukhala ‘okonzeka kumvera.’ (Yak. 3:17) M’nkhani ino tikambirana zinthu zingapo zimene zingachititse kuti tivutike kumvera Mulungu ndiponso kuchita zinthu mogwirizana ndi cholinga chake.
2, 3. Kodi tiyenera kupitiriza kuchita chiyani kuti tikhalebe amtengo wapatali kwa Yehova?
2 Kodi inuyo mumatani mukapatsidwa malangizo ochokera m’Baibulo? Malemba amatiuza kuti Mulungu akufuna kubweretsa m’gulu lake “zinthu zamtengo wapatali zochokera ku mitundu yonse ya anthu.” (Hag. 2:7) Tisanaphunzire choonadi, ambirife tinali kuchita zinthu zimene Yehova sankasangalala nazo. Koma chifukwa chokonda Mulungu ndi Mwana wake wokondedwa, tinasintha mmene timaganizira ndiponso mmene timachitira zinthu pa moyo wathu kuti tisangalatse Mulungu. Tinapempha Yehova kuti atithandize ndiponso tinachita khama kusintha kuti tiyenerere kubatizidwa. Patapita nthawi, tsiku losangalatsa linafika pamene tinabatizidwa.—Werengani Akolose 1:9, 10.
3 Komabe, nkhondo yolimbana ndi kupanda ungwiro sinathe pamene tinabatizidwa. Nkhondoyi ipitirirabe mpaka pamene kupanda ungwiro kudzatha. Yehova watilonjeza kuti atithandiza ngati tipitiriza kuyesetsa kuchita zinthu zomusangalatsa.
Ngati Tikufunika Kusintha Zinthu Zina pa Moyo Wathu
4. Kodi tingalandire malangizo ochokera m’Baibulo m’njira zitatu ziti?
4 Kuti tisinthe zinthu zina pa moyo wathu, tiyenera kudziwa zimene n’zofunika kusintha. Nkhani yogwira mtima imene m’bale wina wakamba ku Nyumba ya Ufumu kapena imene taiwerenga m’magazini athu ingatithandize kuzindikira vuto lina limene tili nalo. Koma ngati sitinaone kuti tili ndi vuto pamene vutolo linatchulidwa m’nkhani inayake, Yehova angagwiritse ntchito Mkhristu mnzathu kutiuza za vuto lathulo.—Werengani Agalatiya 6:1.
5. Tchulani zinthu zina zosayenera zimene tingachite tikapatsidwa malangizo, ndipo n’chifukwa chiyani abusa achikhristu ayenera kuyesetsabe kutithandiza?
5 N’zovuta kulandira malangizo ochokera kwa munthu wina wopanda ungwiro ngakhale kuti munthuyo wawapereka mwachikondi. Koma malinga ndi Agalatiya 6:1, Yehova amalamula anthu oyenerera mwauzimu kuti ‘ayese’ kutithandiza “ndi mzimu wofatsa.” Tikalandira ndiponso kutsatira malangizo amene atipatsa, tidzakhala amtengo wapatali kwambiri kwa Mulungu. N’zochititsa chidwi kuti popemphera sitivutika kuvomereza kuti ndife opanda ungwiro. Koma munthu akatiuza za vuto linalake limene tili nalo, timafuna kupereka zifukwa, kunena kuti si vuto lalikulu, kukayikira cholinga cha munthuyo kapena kunena kuti sanatilankhule bwino. (2 Maf. 5:11) Ngati talandira malangizo ena, tikhozanso kupsa mtima n’kunena zinthu zimene pambuyo pake tingamve nazo chisoni ndiponso zimene zingakhale zokhumudwitsa kwa amene akutipatsa malangizoyo. Mwachitsanzo, sitingasangalale kumva malangizo okhudza zimene munthu wa m’banja mwathu wachita, mmene timavalira kapena mmene timadzisamalirira. Sitingasangalalenso kumva malangizo okhudza zosangalatsa zimene timakonda koma zimene Yehova amadana nazo. Komabe nthawi zambiri mtima ukakhala m’malo, timavomereza kuti malangizowo anali oyenerera.
6. Kodi mawu a Mulungu amasonyeza bwanji “zimene munthu akuganiza komanso zolinga za mtima wake”?
6 Lemba la Aheberi 4:12, limene lili kumayambiriro kwa nkhani ino, limatikumbutsa kuti mawu a Mulungu “ndi amphamvu.” N’zoona kuti mawu a Mulungu ali ndi mphamvu zothandiza anthu kusintha moyo wawo. Amatithandiza kusintha zinthu tisanabatizidwe ndiponso titabatizidwa. M’lemba lomweli, Paulo anauzanso Aheberi kuti mawu a Mulungu “amalasa munthu mumtima mpaka kulekanitsa moyo ndi mzimu, komanso mfundo za mafupa ndi mafuta a m’mafupa. Mawu a Mulungu amathanso kuzindikira zimene munthu akuganiza komanso zolinga za mtima wake.” Izi zikutanthauza kuti zimene timachita tikadziwa bwino cholinga cha Mulungu chokhudza ifeyo, zimasonyeza zimene zili mumtima mwathu. Mawu oti “moyo” m’lembali akunena zimene anthu ena amaona mwa ife. Pamene mawu oti “mzimu” akunena za mmene tilili kwenikweni mkati mwathu. Koma kodi nthawi zina pamakhala kusiyana pakati pa zimene anthu amaona mwa ife ndi mmene tilili kwenikweni mkati mwathu? (Werengani Mateyu 23:27, 28.) Taganizirani zimene inuyo mungachite mukakumana ndi zinthu zotsatirazi.
Tipitirizebe Kuyendera Limodzi ndi Gulu la Yehova
7, 8. (a) Kodi n’kutheka kuti Akhristu ena achiheberi anapitiriza kutsatira zinthu zina m’Chilamulo cha Mose pa chifukwa chiti? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti zimenezo zinali zosemphana ndi cholinga cha Yehova?
7 Ambirife timadziwa bwino mawu a pa lemba la Miyambo 4:18 akuti: “Njira ya olungama ili ngati kuwala kwamphamvu kumene kumamka kuwonjezereka mpaka tsiku litakhazikika.” Izi zikutanthauza kuti mwapang’onopang’ono timatha kumvetsa bwino kwambiri zolinga za Mulungu ndiponso kuchita zimene zimamusangalatsa.
8 Malinga ndi zimene tinakambirana m’nkhani yapita ija, Yesu atafa Akhristu ambiri achiyuda sanafune kusiya kutsatira Chilamulo cha Mose. (Mac. 21:20) Ngakhale kuti Paulo anafotokoza mogwira mtima kuti Akhristu sayenera kutsatira Chilamulo, anthu ena anakana mawu ake ouziridwawa. (Akol. 2:13-15) Mwina iwo anaganiza kuti angapewe kuzunzidwa akamapitiriza kutsatira zinthu zina za m’Chilamulo. Koma Paulo analembera Akhristu achiheberi n’kuwauza mosapita m’mbali kuti sangalowe mu mpumulo wa Mulungu ngati sakuchita zinthu mogwirizana ndi cholinga Chake.a (Aheb. 4:1, 2, 6; werengani Aheberi 4:11.) Kuti Yehova asangalale ndi Akhristuwo, iwo anayenera kuzindikira kuti Yehova tsopano akufuna kuti anthu ake azimulambira m’njira ina.
9. Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru akasintha mmene timamvera mfundo zina za m’Malemba, kodi tiyenera kuchita chiyani?
9 Masiku ano, kapolo wokhulupirika ndi wanzeru wasintha mmene timamvera mfundo zina za m’Baibulo. Izi ziyenera kutilimbikitsa kukhulupirira kwambiri kapoloyu. Abale oimira “kapolo” ameneyu akaona kuti tiyenera kusintha mmene timamvera mfundo ina ya choonadi, sazengereza kusintha. Chofunika kwambiri kwa abalewo ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi cholinga cha Mulungu osati kudziteteza kuti anthu asamawatsutse ngati asintha mmene timamvera mfundo zina. Nanga inuyo mumachita chiyani ngati kapolo wokhulupirika ndi wanzeru wasintha mmene timamvera mfundo zina za m’Malemba?—Werengani Luka 5:39.
10, 11. Kodi abale ena anatani atauzidwa kuti ayambe kugwiritsa ntchito njira zina zolalikirira ndipo tikuphunzira chiyani pa zimenezi?
10 Tiyeni tikambirane chitsanzo china. Zaka pafupifupi 100 zapitazo Ophunzira Baibulo ena amene anali aluso pokamba nkhani, ankaganiza kuti kukamba nkhani inali njira yabwino yolalikirira. Iwo ankakonda kulankhula pamaso pa anthu ambiri. Ena a iwo ankasangalala anthu akamayamikira nkhani zawo. Koma kenako zinadziwika kuti Yehova akufuna kuti anthu ake azilalikira m’njira zosiyanasiyana kuphatikizapo kupita kunyumba ndi nyumba. Abale ena amene anali odziwa kukamba bwino nkhani anakana zimenezi. Ankaoneka ngati anthu odzipereka kwambiri kwa Yehova koma zimene anachita pa nthawiyi zinasonyeza kuti sanali auzimu. Yehova sanawadalitse ndipo iwo anasiya gulu lake.—Mat. 10:1-6; Mac. 5:42; 20:20.
11 Izi sizikutanthauza kuti kulalikira kunyumba ndi nyumba kunali kophweka kwa anthu amene anapitiriza kumvera gulu la Yehova. Poyamba, anthu ambiri anavutika kugwira ntchito imeneyi koma anamvera. Patapita nthawi, iwo anasiya kuchita mantha ndipo Yehova anawadalitsa. Kodi inuyo mumatani akakuuzani kuti muchite ulaliki winawake umene simunayesepo ndipo mukuona kuti ndi wovuta? Kodi mumalolera n’kuyesa?
Munthu Amene Timamukonda Akasiya Yehova
12, 13. (a) N’chifukwa chiyani Yehova amanena kuti munthu wosalapa azichotsedwa mu mpingo? (b) Kodi makolo ena achikhristu amakumana ndi vuto lotani ndipo n’chifukwa chiyani limakhala lopweteka kwambiri?
12 Tonsefe timadziwa mfundo yakuti ngati tikufuna kusangalatsa Mulungu tiyenera kukhala aukhondo, a khalidwe labwino ndiponso oyera mwauzimu. (Werengani Tito 2:14.) Koma nthawi zina zingakhale zovuta kumvera Mulungu pa nkhani ngati zimenezi. Tiyerekeze kuti banja lina lachikhristu limene ndi lokhulupirika lili ndi mwana mmodzi yekha ndipo iye wasiya choonadi. M’malo mosankha kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndiponso ndi makolo ake oopa Mulungu, iye wasankha kuchita “zinthu zosangalatsa koma zosakhalitsa zauchimo.” Choncho wachotsedwa mu mpingo.—Aheb. 11:25.
13 Makolo ake akumva chisoni kwambiri. Pa nkhani ya munthu wochotsedwa, iwo amadziwa kuti Baibulo limati: “Muleke kuyanjana ndi aliyense wotchedwa m’bale, amene ndi wadama, kapena waumbombo, kapena wopembedza mafano, wolalata, chidakwa, kapena wolanda, ngakhale kudya naye munthu wotereyu ayi.” (1 Akor. 5:11, 13) Iwo amadziwanso kuti palembali mawu akuti “aliyense” akuphatikizapo wachibale amene sakukhala naye pakhomo. Koma mwana wawoyo amamukonda kwambiri. Chifukwa cha zimenezi, iwo angaganize kuti: ‘Sitingathandize mwana wathu kuti abwerere kwa Yehova tikasiya kucheza naye. Ndi bwino kuti tizicheza nayebe.’b
14, 15. Kodi makolo ayenera kukumbukira chiyani akamasankha zochita ngati mwana wawo wachotsedwa?
14 Timamvera chisoni kwambiri makolo oterewa. Mwana wawo anachita kusankha yekha kuti achite zoipa m’malo mosankha kukhalabe pa ubwenzi wabwino ndi makolo ake ndiponso Akhristu anzake. Koma palibe zimene makolowo akanachita. M’pake kuti iwo akumva chisoni kwambiri.
15 Kodi n’chiyani chimene makolowo adzachita? Kodi adzamvera malangizo omveka bwino a Yehova? N’zoona kuti pangakhale zinthu zina zokhudza banja lawo zimene ayenera kukambirana ndi mwana wawoyo mwa apa ndi apo. Koma kodi angaganize kuti pali zifukwa zambirimbiri zowachititsa kulankhula naye? Posankha zochita pa nkhaniyi iwo ayenera kukumbukira mmene zosankha zawo zingakhudzire Yehova. Yehova ali ndi cholinga ponena kuti munthu wosalapa azichotsedwa. Cholinga chake n’chakuti gulu lake likhale loyera ndiponso kuti, ngati n’kotheka, zimenezi zithandize wochimwayo kusintha maganizo ake. Kodi makolo achikhristu angachite bwanji zinthu mogwirizana ndi cholinga chimenechi?
16, 17. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Aroni?
16 Aroni, yemwe anali mkulu wake wa Mose, anakumananso ndi vuto chifukwa cha ana ake aamuna awiri. Taganizirani mmene Aroni anamvera chisoni pamene Yehova anawononga Nadabu ndi Abihu chifukwa chopereka kwa Yehova zofukiza pamoto wosaloledwa. N’zoona kuti izi zinachititsa kuti asachezenso ndi makolo awo. Koma nkhani sinathere pomwepa. Yehova analangiza Aroni ndi ana ake okhulupirika kuti asalire maliro awo. Iye anawauza kuti: “Musalekerere tsitsi lanu osalisamala, ndipo musang’ambe zovala zanu [polira] kuti mungafe ndiponso kuti Mulungu angakwiyire khamu lonseli.” (Lev. 10:1-6) Kodi tikuphunzira chiyani pamenepa? Tiyenera kukonda kwambiri Yehova kuposa achibale athu osakhulupirika.
17 Masiku ano, Yehova sapheratu anthu amene amaphwanya malamulo ake. Chifukwa cha chikondi, iye amawapatsa mwayi woti alape. Kodi Yehova angamve bwanji ngati makolo a mwana wosalapa samvera malangizo ake n’kumapitiriza kucheza ndi mwana wawo wochotsedwa?
18, 19. Kodi Akhristu amene amatsatira malangizo a Yehova okhudza achibale awo ochotsedwa amapeza madalitso otani?
18 Anthu ambiri amene anachotsedwa amavomereza kuti zimene anzawo ndiponso achibale awo anachita posiya kucheza nawo zinawathandiza kuti abwerere m’gulu la Yehova. Pamene ankavomereza kuti mtsikana wina abwezeretsedwe, akulu analemba kuti, “Chinthu china chimene chinathandiza kuti mtsikanayo asinthe chinali chakuti mchimwene wake anatsatira malangizo okhudza anthu ochotsedwa.” Mtsikanayo ananena kuti, “Mchimwene wanga anali wokhulupirika potsatira malangizo a m’Malemba ndipo izi zinandithandiza kuti ndibwerere.”
19 Ndiyeno kodi tiyenera kuchita chiyani? Tiyenera kumvera Yehova pa zinthu zonse. Koma popeza ndife opanda ungwiro, nthawi zina tingavutike kuchita zimenezi. Tiyenera kukhulupirira ndi mtima wonse kuti zimene Yehova amatiuza, nthawi zonse zimakhala zothandiza.
“Mawu a Mulungu Ndi Amoyo”
20. Kodi tingamve lemba la Aheberi 4:12 m’njira ziwiri ziti? (Onani mawu a m’munsi.)
20 Pamene Paulo ankalemba kuti “mawu a Mulungu ndi amoyo,” kwenikweni sanali kunena za Baibulo, lomwe ndi Mawu ouziridwa a Mulungu.c Mavesi ena m’chaputalachi amasonyeza kuti ankanena za malonjezo a Mulungu. Paulo ankatanthauza kuti Mulungu saiwala lonjezo lake. Yehova ananena zimenezi kudzera mwa mneneri Yesaya pamene anati: “Mawu otuluka pakamwa panga . . . sadzabwerera kwa ine popanda kukwaniritsa cholinga chake, koma . . . adzakwaniritsadi zimene ndinawatumizira.” (Yes. 55:11) Choncho tiyenera kukhala oleza mtima ngati tikuona kuti Mulungu sakukwaniritsa malonjezo ake pa nthawi imene ifeyo timafuna. Yehova “akugwirabe ntchito” kuti akwaniritse bwinobwino cholinga chake.—Yoh. 5:17.
21. Kodi lemba la Aheberi 4:12 lingalimbikitse bwanji Akhristu achikulire okhulupirika a “khamu lalikulu”?
21 Akhristu achikulire a “khamu lalikulu” amene ndi okhulupirika atumikira Yehova kwa zaka zambiri. (Chiv. 7:9) Ambiri sankaganiza kuti adzakalamba dziko loipali lilipobe. Ngakhale zili choncho, iwo akuyesetsabe kutumikira Yehova. (Sal. 92:14) Iwo amadziwa kuti mawu a Mulungu ndi amoyo ndipo malonjezo a Yehova adzakwaniritsidwa. Mulungu amaona kuti cholinga chake n’chofunika kwambiri choncho amasangalala akamaona kuti ifenso timaona kuti cholinga chakechi n’chofunika. Palibe chimene chingalepheretse Yehova kukwaniritsa cholinga chake pa tsiku lake la 7 lomwe ndi la mpumulo. Iye amadziwanso kuti, monga gulu, anthu ake azichita zinthu mogwirizana ndi cholinga chakechi. Kodi inuyo mwalowa mu mpumulo wa Mulungu?
[Mawu a M’munsi]
a Atsogoleri ambiri achiyuda ankatsatira kwambiri Chilamulo cha Mose koma pamene Mesiya anabwera, iwo sanamuzindikire. Iwo sanali kuchita zinthu mogwirizana ndi cholinga cha Mulungu.
b Onani buku lakuti “Khalanibe M’chikondi cha Mulungu,” tsamba 207 mpaka 209.
c Masiku ano, Mulungu amatilankhula kudzera m’Mawu ake Baibulo, lomwe lili ndi mphamvu zotithandiza kusintha moyo wathu. Choncho tingati mawu a Paulo a pa Aheberi 4:12 amanenanso za Baibulo.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tilowe mu mpumulo wa Mulungu?
• Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa cholinga cha Mulungu ndi kukhala wofunitsitsa kusintha tikalandira malangizo a m’Malemba?
• Kodi kumvera Yehova kumakhala kovuta pa zinthu ziti, koma n’chifukwa chiyani kumverabe kuli kofunika kwambiri?
• Kodi tingamve lemba la Aheberi 4:12 m’njira ziwiri ziti?
[Chithunzi patsamba 31]
Makolo akumva chisoni kwambiri