Achinyamata, Muzisankha Zochita Mwanzeru
‘Inu anyamata ndi inunso anamwali, tamandani dzina la Yehova.’—SAL. 148:12, 13.
1. Kodi achinyamata ambiri ali ndi mwayi wochita zinthu ziti?
TIKUKHALA m’nthawi yapadera kwambiri. Kuposa kale lonse, anthu mamiliyoni ambiri ochokera m’mitundu yonse akubwera m’gulu la Yehova. (Chiv. 7:9, 10) Achinyamata ambiri akusangalala pothandiza ena kumvetsa mfundo za m’Baibulo. (Chiv. 22:17) Ena akuchititsa maphunziro a Baibulo ndipo akuthandiza anthu kukhala ndi makhalidwe abwino. Achinyamata ena akulalikira uthenga wabwino kwa anthu olankhula chinenero china. (Sal. 110:3; Yes. 52:7) Kodi mungatani kuti muchite zambiri pa ntchito yosangalatsa imene anthu a Yehova akugwira?
2. Kodi chitsanzo cha Timoteyo chikusonyeza bwanji kuti Yehova ndi wofunitsitsa kupatsa achinyamata maudindo m’gulu lake? (Onani chithunzi pamwambapa.)
2 Ngati ndinu wachinyamata, panopa mungachite zinthu zimene zingakuthandizeni kudzakhala ndi mwayi wotumikira Mulungu m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, zikuoneka kuti Timoteyo wa ku Lusitara anasankha zinthu mwanzeru. Izi zinamuthandiza kuti akhale mmishonale pamene anali ndi zaka pafupifupi 20 kapena kuposerapo pang’ono. (Mac. 16:1-3) Zikuoneka kuti patangopita miyezi yochepa, Paulo anamutumanso ku Tesalonika kuti akalimbikitse abale. Paulo anachita zimenezi chifukwa chakuti anachoka ku Tesalonika mofulumira kwambiri pothawa ziwawa atangokhazikitsa kumene mpingo. (Mac. 17:5-15; 1 Ates. 3:1, 2, 6) Timoteyo ayenera kuti anasangalala kwambiri atapatsidwa udindo umenewu.
CHINTHU CHOFUNIKA KWAMBIRI CHIMENE MUNGASANKHE
3. Kodi chinthu chofunika kwambiri chimene mungasankhe ndi chiti ndipo mungasankhe liti?
3 Pamene muli wachinyamata muyenera kusankha zochita pa nkhani zikuluzikulu. Koma kusankha kutumikira Yehova n’kofunika kwambiri kuposa chinthu china chilichonse. Kodi ndi liti pamene mungasankhe zimenezi? Yehova anati: “Kumbukira Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako.” (Mlal. 12:1) Munthu angasonyeze kuti ‘akukumbukira’ Yehova akamamutumikira ndi mtima wonse. (Deut. 10:12) Kusankha kutumikira Mulungu ndi mtima wonse ndi kofunika kwambiri chifukwa kudzakhudza moyo wanu wonse.—Sal. 71:5.
4. Kodi ndi nkhani zazikulu ziti zomwe zidzakhudze zimene mungachite potumikira Mulungu?
4 N’zoona kuti kusankha kutumikira Yehova si chinthu chokhacho chimene chidzakhudze tsogolo lanu. Palinso nkhani zina zofunika zimene muyenera kusankha. Mudzafunika kusankha kukhala pa banja kapena ayi, amene mudzakwatirane naye ndiponso mmene mudzapezere zofunika pa moyo. Nkhanizi ndi zofunikanso koma choyamba, mungachite bwino kusankha ngati mukufuna kutumikira Yehova ndi mtima wonse kapena ayi. (Deut. 30:19, 20) Tikutero chifukwa chakuti nkhani zonsezi ndi zogwirizana. Zimene mudzasankhe pa nkhani ya banja ndiponso ntchito zidzakhudza zimene mungachite potumikira Mulungu. (Yerekezerani ndi Luka 14:16-20.) Kusankha kutumikira Mulungu ndi mtima wonse kudzakhudzanso zimene mudzasankhe pa nkhani ya banja ndiponso ntchito. Choncho, choyamba muyenera kusankha zochita pa nkhani zazikulu kwambiri.—Afil. 1:10.
KODI MUCHITA CHIYANI MUDAKALI WACHINYAMATA?
5, 6. Fotokozani zinthu zosangalatsa zimene ena akumana nazo chifukwa choti ali achinyamata anasankha zinthu mwanzeru. (Onaninso nkhani yakuti “Zimene Ndinasankha Ndili Mwana” patsamba 32.)
5 Choyamba, sankhani kutumikira Mulungu ndipo ganizirani zimene iye akufuna kuti muzichita. Kenako mungasankhe kuti mudzamutumikira bwanji. M’bale wina wa ku Japan analemba kuti: “Pamene ndinali ndi zaka 14, ndinapita kukalalikira limodzi ndi mkulu wina wa mumpingo wathu. Mkuluyo anaona kuti sindikusangalala ndi utumikiwo ndipo anandiuza mokoma mtima kuti: ‘Pita kunyumba Yuichiro, ndipo ukakhale pansi n’kuganizira mofatsa zimene Yehova wakuchitira.’ Ndinachitadi zimenezo, ndipo ndinapitiriza kuganizira ndi kupempherera nkhaniyi kwa masiku angapo. Pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kusintha mmene ndinkaonera zinthu moti ndinayamba kutumikira Yehova mosangalala. Ndinkakonda kuwerenga nkhani zokhudza amishonale ndipo ndinayamba kuganizira zochita zambiri potumikira Mulungu.”
6 Yuichiro ananenanso kuti: “Ndinaganiza zoyamba kuchita zinthu zimene zidzandithandize kukatumikira Yehova kudziko lina m’tsogolo. Mwachitsanzo, ndinaganiza zophunzira Chingelezi. Nditamaliza sukulu ndinayamba ntchito yophunzitsa Chingelezi imene inkandipatsa mpata wochitanso upainiya. Nditakwanitsa zaka 20 ndinayamba kuphunzira Chimongoliya ndipo ndinapita kukagulu ka abale ndi alongo olankhula Chimongoliya. Patapita zaka ziwiri, mu 2007, ndinapita m’dziko la Mongolia. Nditapita kolalikira limodzi ndi apainiya ena kumeneko ndinaona kuti anthu ambiri ankafunitsitsa kuphunzira Mawu a Mulungu. Choncho ndinaganiza zosamukira kumeneko kuti ndikathandize pa ntchitoyi. Ndiyeno ndinabwerera ku Japan kuti ndikakonzekere zosamuka. Panopa ndakhala ndikuchita upainiya ku Mongolia kuyambira mu April 2008. Ndimakumana ndi mavuto ena, koma anthu akumvetsera uthenga wabwino ndipo ndili ndi mwayi wowathandiza kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. Ndikuona kuti ndinasankha zinthu mwanzeru kwambiri pa moyo wanga.”
7. Kodi ndi zinthu ziti zimene aliyense ayenera kusankha yekha, ndipo Mose anatipatsa chitsanzo chotani?
7 Wa Mboni za Yehova aliyense ayenera kusankha yekha zimene adzachite potumikira Mulungu. (Yos. 24:15) Sitingakuuzeni zoti mukhale pabanja kapena ayi, ndipo sitingakusankhireni munthu woti mukwatirane naye kapena ntchito yoti muzigwira. Kodi mudzasankha ntchito imene sidzatenga nthawi yaitali kuiphunzira? Ena mwa achinyamatanu mukukhala kumudzi kumene anthu ambiri ndi osauka, pamene ena a inu mukukhala m’mizinda imene anthu ambiri ndi opeza bwino. Komanso mumasiyana khalidwe, luso, zimene mwachita pa moyo, zimene mumakonda ndiponso kulimba kwa chikhulupiriro chanu. Nawonso achinyamata achiheberi ku Iguputo anali osiyana kwambiri ndi Mose. Iye ali mwana anali ndi mwayi wokhala m’nyumba ya mfumu, pamene Aheberi ena anali akapolo. (Eks. 1:13, 14; Mac. 7:21, 22) Mofanana ndi inuyo, iwonso ankakhala m’nthawi yapadera. (Eks. 19:4-6) Aliyense ankayenera kusankha zimene adzachite pa moyo wake. Ndipo Mose anasankha zinthu mwanzeru.—Werengani Aheberi 11:24-27.
8. Kodi achinyamata amene akuganizira zimene adzachite pa moyo wawo angapeze kuti thandizo?
8 Yehova angakuthandizeni kusankha zinthu mwanzeru mudakali wachinyamata. Iye amatipatsa mfundo zimene zingathandize munthu aliyense. (Sal. 32:8) Nawonso makolo anu, ngati ndi a Mboni, komanso akulu mumpingo angakuthandizeni kuzindikira mmene mungagwiritsire ntchito mfundozi pa moyo wanu. (Miy. 1:8, 9) Tiyeni tikambirane mfundo zitatu za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni kusankha zochita mwanzeru kuti zinthu zidzakuyendereni bwino m’tsogolo.
MFUNDO ZITATU ZA M’BAIBULO ZOMWE ZINGAKUTHANDIZENI
9. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova amatilemekeza potipatsa ufulu wosankha zochita? (b) Kodi ‘kufunafuna Ufumu choyamba’ kumapatsa munthu mwayi uti?
9 Mufunefune Ufumu wa Mulungu choyamba ndi chilungamo chake. (Werengani Mateyu 6:19-21, 24-26, 31-34.) Yehova amatilemekeza potipatsa ufulu wosankha tokha zochita. Sikuti iye amanena kuti achinyamata azigwiritsa ntchito nthawi yawo yonse polalikira za Ufumu. Koma Yesu anatiuza mfundo yothandiza yakuti tizifunafuna Ufumu choyamba. Mukhoza kusankha nokha zimene mungachite potsatira mfundo imeneyi. Zimenezi zingakupatseni mwayi wosonyeza mmene mumakondera Mulungu ndiponso anthu anzanu komanso mmene mumayamikirira chiyembekezo chanu cha moyo wosatha. Muyenera kuganizira mofatsa musanasankhe zochita pa nkhani ya banja kapena ntchito. Mungadzifunse kuti, Kodi zimene ndikufuna kusankha zidzandichititsa kuganizira kwambiri za chuma kapena zidzandithandiza kuika patsogolo Ufumu wa Mulungu ndi chilungamo chake?
10. (a) N’chiyani chinathandiza Yesu kukhala wosangalala? (b) Kodi muyenera kusankha bwanji zochita kuti inunso mukhale wosangalala?
10 Muzisangalala kutumikira ena. (Werengani Machitidwe 20:20, 21, 24, 35.) Yesu anatikomera mtima potiphunzitsa mfundo yofunika imeneyi. Iye anali munthu wosangalala chifukwa chakuti ankachita zofuna za Atate wake m’malo mochita zofuna zake. Yesu ankasangalala kuona anthu ofatsa akumvetsera mwachidwi uthenga wabwino. (Luka 10:21; Yoh. 4:34) Mwina inunso mwaona nokha kuti kuthandiza anthu ena n’kosangalatsa. Mukamagwiritsa ntchito mfundo zimene Yesu anaphunzitsa posankha zochita pa nkhani zikuluzikulu, mudzakhala wosangalala komanso mudzasangalatsa Yehova.—Miy. 27:11.
11. (a) N’chifukwa chiyani Baruki anasiya kukhala wosangalala? (b) Kodi Yehova anapatsa Baruki malangizo ati?
11 Timakhala osangalala kwambiri tikamatumikira Yehova. (Miy. 16:20) Zikuoneka kuti Baruki, yemwe anali mlembi wa Yeremiya, anaiwala mfundo imeneyi. Pa nthawi ina, kutumikira Yehova sikunkamusangalatsanso. Ndiyeno Yehova anamuuza kuti: “Iwe, ukufunafunabe zinthu zazikulu. Leka kuzifunafuna. Anthu onse ndikuwagwetsera tsoka ndipo iwe ndidzakupatsa moyo wako monga chofunkha chako kulikonse kumene ungapite.” (Yer. 45:3, 5) Kodi mukuona kuti n’chiyani chimene chikanathandiza Baruki kukhala wosangalala? Kodi ndi kufunafuna zinthu zazikulu kapena kutumikira Mulungu mokhulupirika n’kupulumuka pamene Yerusalemu akuwonongedwa?—Yak. 1:12.
12. Kodi Ramiro anasankha chiyani chimene chinamuthandiza kukhala wosangalala?
12 M’bale wina dzina lake Ramiro anaona kuti kutumikira ena n’kosangalatsa kwambiri. Iye anati: “Ndimachokera m’banja losauka limene limakhala kumudzi wina kumapiri a Andes. Choncho unali mwayi waukulu pamene mkulu wanga ananena kuti andilipirira kuti ndipite kuyunivesite. Koma ndinali nditangobatizidwa kumene ndipo mpainiya wina anali atandipempha kuti ndikalalikire naye kukatauni kena. Ndinapita kukatauni kameneka ndipo ndinaphunzira kumeta tsitsi. Kenako ndinatsegula malo anga ometera tsitsi kuti ndizipeza kangachepe. Pamene tinkapempha anthu kuti tiziphunzira nawo Baibulo, ambiri ankavomera ndiponso kuyamikira. Patapita nthawi, ndinayamba kusonkhana ndi mpingo wa chinenero cha kumeneko umene unali utangokhazikitsidwa kumene. Panopa ndakhala ndikuchita upainiya kwa zaka 10. Palibe ntchito ina imene ingandisangalatse kuposa kuthandiza anthu kumva uthenga wabwino m’chinenero chawo.”
13. N’chifukwa chiyani ndi bwino kutumikira Yehova mwakhama mudakali wachinyamata?
13 Sangalalani potumikira Yehova mudakali wachinyamata. (Werengani Mlaliki 12:1.) Musaganize kuti muyenera kupeza kaye ntchito yabwino kuti mudzatumikire Yehova m’tsogolo. Mungachite bwino kuyamba kutumikira Yehova mwakhama mudakali wachinyamata. Achinyamata ambiri alibe udindo wosamalira banja ndipo ali ndi thanzi labwino komanso mphamvu zambiri. Choncho akhoza kuchita zambiri potumikira Mulungu. Kodi inuyo mukufuna kuchita chiyani potumikira Yehova mudakali wachinyamata? Mwina muli ndi cholinga chokhala mpainiya. Kapena mukufuna kulalikira m’gawo la anthu olankhula chinenero china. Mwinanso mukuona kuti mungachite zambiri mumpingo wanu womwewo. Koma kaya mukufuna kuchita chiyani potumikira Mulungu, mufunikabe kukhala ndi njira yopezera zofunika pa moyo. Kodi mudzasankha ntchito yotani? Nanga mudzayenera kuiphunzira kwa nthawi yaitali bwanji?
MFUNDO ZA M’BAIBULO ZINGAKUTHANDIZENI KUSANKHA ZOCHITA MWANZERU
14. Pamene mukuganizira zimene mudzachite m’tsogolo, kodi muyenera kusamala ndi chiyani?
14 Mfundo zitatu za m’Baibulo zimene takambiranazi zingakuthandizeni kusankha bwino ntchito. Aphunzitsi anu ayenera kuti akudziwa ntchito zimene zimapezeka mosavuta kwanuko. Mwina pangakhale ofesi ina ya boma imene ingakuuzeni zimene mungaphunzire kuti musamavutike kupeza ntchito kwanuko kapena kumene mukufuna kukatumikira. N’zoona kuti zimene anthu ngati amenewo angakuuzeni zingakhale zothandiza, komabe muyenera kusamala. Anthu amene sakonda Yehova angakuchititseni kuti muzikonda zinthu zam’dzikoli. (1 Yoh. 2:15-17) Mukaona zimene zikuchitika m’dzikoli, n’zosavuta kuti mtima wanu ukunyengeni.—Werengani Miyambo 14:15; Yer. 17:9.
15, 16. Kodi ndi ndani amene angakupatseni malangizo othandiza okhudza ntchito?
15 Mutadziwa bwino ntchito zimene mungathe kuphunzira, mungafunike malangizo abwino. (Miy. 1:5) Kodi ndi ndani amene angakuthandizeni kusankha ntchito yabwino pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo? Ndi anthu amene amakonda Yehova, amene amakukondani, kukudziwani bwino komanso amene akudziwa mmene zinthu zilili pa moyo wanu. Iwo angakuthandizeni kudziwa zimene mungakwanitse kuchita komanso chifukwa chake mukufuna kuchita zinazake. Mwina zimene angakuuzeni zingakuthandizeni kuonanso bwino zolinga zanu. Ndipotu ngati makolo anu amakonda Yehova ndiye kuti muli ndi mwayi waukulu. Komanso akulu mumpingo wanu amadziwa zambiri ndipo angakupatseni malangizo abwino. Kuwonjezera pamenepo, mungalankhule ndi apainiya komanso oyang’anira oyendayenda. Mwina mungawafunse kuti, N’chifukwa chiyani munasankha kuchita utumiki wa nthawi zonse? Kodi munayamba bwanji upainiya, nanga mumapeza bwanji zofunika pa moyo wanu? N’chiyani chimakusangalatsani pochita utumiki umenewu?—Miy. 15:22.
16 Amene akukudziwani bwino angakupatseni malangizo othandiza. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mukufuna kusiya sukulu n’kuyamba upainiya makamaka chifukwa chakuti mukuona kuti sukulu ndi yovuta. Munthu amene amakukondani angazindikire zolinga zanu ndipo angakuthandizeni kuona kuti mukamapita kusukulu mungaphunzire kukhala wakhama pochita zinthu. Kukhala wakhama n’kofunika kwambiri kuti muzichita zambiri potumikira Yehova.—Sal. 141:5; Miy. 6:6-10.
17. Kodi tiyenera kupewa kusankha zinthu ziti?
17 N’zoona kuti Mkhristu aliyense amakumana ndi zinthu zimene zingasokoneze ubwenzi wake ndi Yehova. (1 Akor. 15:33; Akol. 2:8) Koma mitundu ina ya ntchito ingabweretse mavuto ambiri amene angawononge ubwenzi wathu ndi Mulungu. Kodi mukudziwa anthu ena m’dera lanu amene “chikhulupiriro chawo chasweka ngati ngalawa” atasankha ntchito inayake? (1 Tim. 1:19) Mungachite bwino kupewa kusankha zinthu zimene zingawononge ubwenzi wanu ndi Mulungu.—Miy. 22:3.
TUMIKIRANI MULUNGU MOSANGALALA MUDAKALI WACHINYAMATA
18, 19. Ngati panopa munthu alibe mtima wofunitsitsa kutumikira Yehova, kodi angachite chiyani?
18 Ngati muli ndi mtima wofunitsitsa kutumikira Yehova, muli ndi mwayi wochita zambiri pomutumikira mudakali wachinyamata. Muzisankha zochita mwanzeru n’cholinga choti muzitumikira Yehova mosangalala m’nthawi yapaderayi.—Sal. 148:12, 13.
19 Koma kodi mungachite chiyani ngati panopa mulibe mtima wofunitsitsa kutumikira Yehova? Musataye mtima, koma pitirizani kuyesetsa kulimbitsa chikhulupiriro chanu. Mtumwi Paulo atafotokoza kuti ankayesetsa kwambiri kuti azichita zinthu zimene Mulungu angadalitse, analemba kuti: “Ngati muli ndi maganizo osiyana ndi amenewa m’mbali ina iliyonse, Mulungu adzakuululirani maganizo oyenerawo. Komabe, mulimonse mmene tapitira patsogolo, tiyeni tipitirize kupita patsogolo mwa kuyenda moyenera m’njira yomweyo.” (Afil. 3:15, 16) Pitirizani kuganizira za chikondi cha Mulungu ndiponso malangizo ake anzeru. Kuposa wina aliyense, Yehova angakuthandizeni kusankha zochita mwanzeru mudakali wachinyamata.