Tiziganizira Kwambiri Chikondi cha Yehova
“Ndidzasinkhasinkha za ntchito zanu zonse.”—SAL. 77:12.
1, 2. (a) N’chiyani chimakutsimikizirani kuti Yehova amakonda anthu ake? (b) Kodi anthufe tinalengedwa ndi mtima wofuna chiyani?
N’CHIYANI chimakutsimikizirani kuti Yehova amakonda anthu ake? Tisanayankhe funsoli, tiyeni tione zitsanzo zitatu. Chitsanzo choyamba ndi cha mlongo wina dzina lake Taylene. Akhristu anzake ankamulimbikitsa kuti azidziwa malire a zinthu zimene angakwanitse. Iye anati: “Anzanga ankandilangiza pafupipafupi ndipo umenewu ndi umboni wakuti Yehova amandikonda kwambiri.” Chitsanzo chachiwiri ndi cha mlongo wina dzina lake Brigitte. Mwamuna wake anamwalira n’kumusiya ali ndi ana awiri. Iye anati: “Kulera ana m’dziko la Satanali n’kovuta kwambiri makamaka ngati ukuwalera wekha. Koma ndaona umboni woti Yehova amandikonda kwambiri. Wandithandiza pa nthawi imene ndinkalira komanso kupwetekedwa mtima ndipo sanalole kuti ndikumane ndi mavuto amene sindingathe kuwapirira.” (1 Akor. 10:13) Chitsanzo chachitatu ndi cha mlongo wina dzina lake Sandra. Mlongoyu amadwala matenda oti sangachire ndipo tsiku lina pa msonkhano wachigawo anathandizidwa kwambiri ndi mkazi wa m’bale wina wodziwika. Mwamuna wa Sandra anati: “Mlongoyu sitinkadziwana naye koma tinasangalala kwambiri kuona kuti akutisonyeza chikondi. Zinthu zimene abale ndi alongo athu amachita potithandiza, ngakhale zitakhala zochepa, zimasonyeza kuti Yehova amatikonda.”
2 Anthufe tinalengedwa ndi mtima wofuna kukonda ena komanso kukondedwa. Koma nthawi zina tikhoza kukhumudwa chifukwa cha mavuto azachuma, matenda kapena mavuto ena pamene tikutumikira Mulungu. Mavuto amenewa angatichititse kumva ngati Yehova satikonda. Maganizo amenewa akabwera tiyenera kukumbukira kuti iye amationa kuti ndife amtengo wapatali ndipo ‘wagwira dzanja lathu lamanja’ kuti atithandize. Ngati tikhalabe okhulupirika, iye sadzatiiwala.—Yes. 41:13; 49:15.
3. N’chiyani chingatithandize kukhulupirira kuti Yehova amatikonda?
3 Anthu amene tawatchula m’ndime yoyambayi anakumana ndi mavuto koma anaona kuti Yehova ankawathandiza. Nafenso tikhoza kutsimikizira kuti Yehova ali kumbali yathu. (Sal. 118:6, 7) M’nkhaniyi tikambirana zinthu 4 zimene zimasonyeza kuti Yehova amatikonda. Zinthu zake ndi (1) zimene analenga, (2) Mawu ake, (3) pemphero ndiponso (4) dipo. Kuganizira kwambiri zinthu zabwino zimene Yehova wachita kungatithandize kuyamikira kwambiri chikondi chake.—Werengani Salimo 77:11, 12.
TIZIGANIZIRA ZIMENE YEHOVA ANALENGA
4. Kodi tikamaganizira zimene Yehova analenga, timazindikira chiyani?
4 Zinthu zimene Mulungu analenga zimasonyeza kuti ndi wachikondi. (Aroma 1:20) Iye analenga dziko ndiponso zinthu za padziko n’cholinga choti tizikhalabe ndi moyo bwinobwino. Mwachitsanzo, anatipatsa zinthu zosiyanasiyana zimene tingadye. Anatilenganso m’njira yoti tizimva kukoma kwa chakudyacho. (Mlal. 9:7) Izi zikusonyeza kuti Yehova amafuna kuti moyo wathu ukhale wosangalatsa. Mlongo wina wa ku Canada dzina lake Catherine amakonda kwambiri kuona chilengedwe, makamaka kuyambira mwezi wa March mpaka May. Iye anati: “Pa nthawiyi, kumakhala maluwa okongola komanso mbalame zimabwerera kuchokera kumene zinapita pa nyengo yozizira. Ndimasangalala kuona timbalame tinatake timene timabwera kudzadya chakudya chimene ndimasiya penapake. N’zoonekeratu kuti Yehova amatikonda chifukwa analenga zinthu zambiri zokongola.” Atate wathu wachikondi amasangalala kwambiri ndi zimene analenga ndipo amafuna kuti ifenso tizisangalala nazo.—Mac. 14:16, 17.
5. Kodi Yehova anasonyeza bwanji chikondi polenga anthu?
5 Yehova anatilenganso kuti tizigwira ntchito zosiyanasiyana zimene zingatithandize kukhala osangalala. (Mlal. 2:24) Cholinga chake chinali chakuti anthu adzaze dziko lapansi, aliyang’anire komanso ayang’anire zamoyo zonse zapadzikoli. (Gen. 1:26-28) Iye anasonyezanso chikondi kwambiri potilenga m’njira yoti tizitha kumutsanzira.—Aef. 5:1.
TIZIYAMIKIRA MAWU A MULUNGU
6. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira kwambiri Mawu a Mulungu?
6 Mulungu anasonyezanso kuti amatikonda kwambiri potipatsa Mawu ake. Baibulo limafotokoza zinthu zambiri zokhudza Yehova ndiponso mmene amachitira zinthu ndi anthu. Mwachitsanzo, Malemba amasonyeza zimene iye ankachita ndi Aisiraeli omwe ankamuchimwira mobwerezabwereza. Lemba la Salimo 78:38 limati: “Anawamvera chifundo. Anali kukhululukira machimo awo ndipo sanali kuwawononga. Nthawi zambiri anali kubweza mkwiyo wake, ndipo sanali kuwasonyeza ukali wake wonse.” Kuganizira mawu a mulembali kungatithandize kuona kuti Yehova amatikonda. Choncho musakayikire kuti Yehova amakukondani kwambiri.—Werengani 1 Petulo 5:6, 7.
7. N’chifukwa chiyani tiyenera kuona kuti Baibulo ndi lamtengo wapatali?
7 Kuti makolo ndi ana azikhulupirirana ndiponso kukondana, ayenera kulankhulana momasuka komanso mwachikondi. N’chimodzimodzi ndi Atate wathu wakumwamba. Ngakhale kuti sitiona Mulungu ndiponso kumva mawu ake, iye amagwiritsa ntchito Baibulo kuti azilankhula nafe. Choncho tiziona kuti Baibulo ndi lamtengo wapatali ndipo tiziliwerenga. (Yes. 30:20, 21) Yehova amafunitsitsa kutitsogolera ndiponso kutiteteza. Iye amafunanso kuti timudziwe komanso kumukhulupirira.—Werengani Salimo 19:7-11; Miyambo 1:33.
8, 9. Kodi Yehova akufuna kuti tidziwe chiyani? Fotokozani chitsanzo cha m’Baibulo pa nkhaniyi.
8 Yehova amafuna kuti tidziwe kuti amatikonda ndiponso samangoyang’ana zimene talakwitsa. Iye amafufuza zinthu zabwino mumtima mwathu. (2 Mbiri 16:9) Mwachitsanzo, anachita zimenezi ndi Mfumu Yehosafati ya ku Yuda. Pa nthawi ina, Yehosafati anagwirizana ndi Mfumu Ahabu ya ku Isiraeli kuti akalande Ramoti-giliyadi kwa Asiriya. Aneneri onyenga 400 ananamiza Ahabu kuti akapambana nkhondoyo. Koma mneneri wa Yehova dzina lake Mikaya ananena kuti akagonjetsedwa. Ahabu anaphedwa pa nkhondoyo ndipo Yehosafati anapulumukira mkamwa mwa mbuzi. Yehosafati atabwerera ku Yerusalemu anadzudzulidwa chifukwa chogwirizana ndi mfumu yoipayo. Ngakhale zinali choncho, Yehu mwana wa Haneni anauza Yehosafati kuti: “Pali zinthu zabwino zimene zapezeka mwa inu.”—2 Mbiri 18:4, 5, 18-22, 33, 34; 19:1-3.
9 Kumayambiriro kwa ulamuliro wake, Yehosafati analamula akalonga, Alevi ndiponso ansembe kuti azikaphunzitsa Chilamulo cha Yehova m’mizinda yonse ya Yuda. Zimenezi zinathandiza kwambiri moti anthu a m’mayiko ozungulira Yuda anayamba kuopa Yehova. (2 Mbiri 17:3-10) N’zoona kuti Yehosafati anachita zinthu zosayenera koma Yehova anakumbukirabe zabwino zimene anachita. Nafenso nthawi zina timachita zinthu zosayenera. Koma nkhani ya Yehosafatiyi ikutitsimikizira kuti Yehova adzapitirizabe kutikonda tikamayesetsa ndi mtima wonse kuchita zinthu zomusangalatsa.
TIZIYAMIKIRA MWAYI WA PEMPHERO
10, 11. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti pemphero ndi mphatso yapadera yochokera kwa Yehova? (b) Kodi Mulungu angayankhe bwanji mapemphero athu? (Onani chithunzi patsamba 9.)
10 Bambo wachikondi amamvetsera ana ake akamalankhula. Iye amafuna kudziwa nkhawa zawo ndiponso zimene akuvutika nazo mumtima. Nayenso Atate wathu wakumwamba Yehova amamvetsera tikamapemphera kwa iye.
11 Tili ndi mwayi wopemphera kwa Yehova nthawi iliyonse. Iye ndi Mnzathu ndipo nthawi zonse amafuna kumvetsera mapemphero athu. Mlongo Taylene amene tamutchula poyamba uja anati: “Tikhoza kumuuza chilichonse.” Tikamauza Mulungu zimene zili mumtima mwathu, iye akhoza kutiyankha pogwiritsa ntchito Baibulo, magazini athu kapena Akhristu anzathu. Yehova amamvetsera tikamamuuza mavuto athu ndipo amatimvetsa. Izi zili choncho ngakhale pamene palibe munthu amene akumvetsa mavuto athuwo. Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amatikonda kwambiri.
12. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira mapemphero amene analembedwa m’Baibulo? Perekani chitsanzo.
12 Tingaphunzire zambiri pa mapemphero amene analembedwa m’Baibulo. Choncho nthawi zina tingachite bwino kukambirana mapempherowa pa Kulambira kwa Pabanja. Kuganizira zimene atumiki akale ananena pouza Yehova za mumtima mwawo, kungathandize kuti mapemphero athu akhale abwino. Mwachitsanzo, mungakambirane zimene Yona ananena pochonderera Yehova ali m’mimba mwa chinsomba. (Yona 1:17; 2:1-10) Kapena mungakambiranenso pemphero lochokera pansi pa mtima limene Solomo anapereka potsegulira kachisi. (1 Maf. 8:22-53) Mungaganizirenso zinthu zothandiza zimene Yesu ananena m’pemphero lachitsanzo. (Mat. 6:9-13) Koma chofunika kwambiri n’chakuti “zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.” Izi zidzakuthandizani kuyamikira kwambiri chikondi cha Yehova.—Afil. 4:6, 7.
TIZIYAMIKIRA DIPO
13. Kodi dipo limathandiza kuti anthu akhale ndi mwayi uti?
13 Yehova anasonyeza chikondi chosaneneka potumiza Yesu kuti akhale dipo n’cholinga choti “tipeze moyo kudzera mwa iye.” (1 Yoh. 4:9) Pofotokoza za mphatso imeneyi, mtumwi Paulo analemba kuti: “Khristu anafera anthu osapembedza Mulungu pa nthawi yoikidwiratu. Pakuti n’chapatali kuti munthu wina afere munthu wolungama. Zoonadi, mwina wina angalimbe mtima kufera munthu wabwino. Koma Mulungu akuonetsa chikondi chake kwa ife, moti pamene tinali ochimwa, Khristu anatifera.” (Aroma 5:6-8) Zimene Yesu anachitazi zinathandiza kuti anthu akhale ndi mwayi wogwirizana ndi Mulungu.
14, 15. Kodi dipo limapereka mwayi uti kwa (a) Akhristu odzozedwa? (b) anthu amene akuyembekezera kudzakhala padzikoli?
14 Yehova wasonyezanso anthu ena chikondi m’njira yapadera. (Yoh. 1:12, 13; 3:5-7) Anthuwo adzozedwa ndi mzimu woyera kuti akhale “ana a Mulungu.” (Aroma 8:15, 16) Paulo ananena kuti odzozedwawa ‘anawakweza ndi kuwakhazika pamodzi m’malo akumwamba mogwirizana ndi Khristu Yesu.’ (Aef. 2:6) Popeza kuti odzozedwa ena sanapite kumwamba, n’chifukwa chiyani Paulo ananena zimenezi? Ananena chifukwa chakuti Yehova wawalonjeza kuti adzalandira moyo wosatha kumwamba.—Aef. 1:13, 14; Akol. 1:5.
15 Koma anthu ena onse amene amakhulupirira dipo amakhala anzake a Yehova. Iwo ali ndi mwayi wodzakhalanso ana a Mulungu n’kulandira moyo wosatha m’Paradaiso padzikoli. Choncho dipo limasonyeza kuti Yehova amakonda kwambiri anthu. (Yoh. 3:16) Ngati tikuyembekezera kudzakhala padzikoli, tiyenera kupitiriza kutumikira Mulungu mokhulupirika. Tisamakayikirenso kuti moyo umene adzatipatse m’dziko latsopano udzakhala wosangalatsa kwambiri. Zonse tanenazi zikusonyeza kuti dipo ndi umboni waukulu kwambiri wakuti Mulungu amatikonda.
TIZISONYEZA KUTI TIMAKONDA YEHOVA
16. Kodi kuganizira zimene Yehova watichitira kungatithandize bwanji?
16 Yehova wachita zinthu zambirimbiri zosonyeza kuti amatikonda moti sitingathe kuziwerenga. Davide anaimba kuti: “Kwa ine maganizo anu ndi ofunika kwambiri, inu Mulungu, ndipo ndi ochuluka zedi. Nditati ndiyese kuwawerenga, angakhale ochuluka kwambiri kuposa mchenga.” (Sal. 139:17, 18) Tiyeni tiziganizira zimene Mulungu watichitira kuti ifenso tizimukonda kwambiri. Tiyeni tiziyesetsanso kuchita zonse zimene tingathe pomutumikira.
17, 18. Tchulani zinthu zina zimene tingachite posonyeza kuti timakonda Mulungu.
17 Tingasonyeze m’njira zambiri kuti timakonda Yehova. Mwachitsanzo, timasonyeza kuti timakonda Mulungu ndiponso anzathu tikamachita khama pa ntchito yolalikira. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Timasonyezanso kuti timakonda kwambiri Yehova tikamakhala okhulupirika poyesedwa. (Werengani Salimo 84:11; Yakobo 1:2-5.) Tikakumana ndi mavuto aakulu, tisakayikire kuti Mulungu amadziwa mmene tikumvera ndipo adzatithandiza. Tikutero chifukwa chakuti iye amaona kuti ndife amtengo wapatali.—Sal. 56:8.
18 Timaganizira zimene Mulungu analenga ndiponso zochita zake chifukwa chomukonda kwambiri. Timasonyezanso kuti timakonda Mulungu ndiponso kuyamikira Mawu ake tikamaphunzira Baibulo mwakhama. Timapempheranso kwa Mulungu pafupipafupi chifukwa chomukonda. Kuganizira nsembe ya dipo imene Mulungu anapereka chifukwa cha machimo athu kumatithandizanso kumukonda kwambiri. (1 Yoh. 2:1, 2) Izi ndi zinthu zochepa chabe zimene Yehova watichitira zomwe zimatichititsa kumukonda kwambiri.