Kodi Akulu Ndi Atumiki Othandiza Angaphunzire Chiyani Kwa Timoteyo?
CHAKA chatha, abale ambiri anavomerezedwa kukhala akulu ndi atumiki othandiza m’gulu lathu padziko lonse. Ngati ndinu mmodzi mwa anthu amene anavomerezedwa, muyenera kuti mumasangalala kwambiri ndi utumiki wanu watsopanowu.
Koma mwina nthawi zina simulephera kukhala ndi nkhawa. Mwachitsanzo, m’bale wina dzina lake Jason ananena kuti: “Nditangovomerezedwa ndinali ndi nkhawa kwambiri poganizira za udindo wanga.” Umu ndi mmenenso anamvera Mose ndi Yeremiya atapatsidwa utumiki wina ndi Yehova. (Eks. 4:10; Yer. 1:6) Ngati nanunso mumamva choncho, kodi mungachepetse bwanji nkhawa n’kumapita patsogolo? Chitsanzo cha Timoteyo chikhoza kukuthandizani pa nkhaniyi.—Mac. 16:1-3.
MUZITSANZIRA TIMOTEYO
Timoteyo ayenera kuti anali asanakwanitse zaka 20 kapena atangokwanitsa kumene pamene mtumwi Paulo anamupempha kuti aziyenda naye. Popeza anali wamng’ono, ayenera kuti ankadzikayikira ndipo ankaona kuti sangachite bwino udindo wake. (1 Tim. 4:11, 12; 2 Tim. 1:1, 2, 7) Koma patapita zaka 10, Paulo anauza mpingo wa ku Filipi kuti: “Ine, mwa Ambuye Yesu ndikuyembekeza kutumiza Timoteyo kwa inu posachedwapa . . . Pakuti ndilibe wina wamtima ngati iye, amene angasamaledi za inu moona mtima.”—Afil. 2:19, 20.
N’chiyani chinathandiza Timoteyo kuti akhale mkulu wabwino? Tiyeni tikambirane zinthu 6 zimene zinamuthandiza zomwe zingatithandizenso ifeyo.
1. Ankakonda anthu komanso kuwaganizira. Paulo anauza abale a ku Filipi kuti Timoteyo “angasamaledi za inu moona mtima.” (Afil. 2:20) Apa zikuonekeratu kuti Timoteyo ankakonda anthu ndipo ankawaganizira. Ankafunitsitsa kuti zinthu ziziwayendera bwino mwauzimu ndipo ankadzipereka ndi mtima wonse kuti awathandize.
Tiyenera kupewa kukhala ngati dalaivala wa basi amene amaganizira kwambiri zokafika pa nthawi yake osaganizira zoti kaya anthu akwera kapena ayi. M’bale William amene wakhala mkulu kwa zaka zoposa 20 anapereka malangizo kwa amene angolandira kumene udindo kuti: “Muzikonda abale. Muziganizira kwambiri zimene akufunikira osati mmene zinthu zikuyendera mumpingo.”
2. Ankaika zinthu zauzimu pamalo oyamba. Posiyanitsa maganizo a Timoteyo ndi a anthu ena, Paulo anati: “Ena onse akungofuna za iwo eni, osati za Khristu Yesu.” (Afil. 2:21) Paulo analemba kalatayi ali ku Roma ndipo anazindikira kuti abale akumeneko ankangoganizira zawo zokha. Mwina tingati sankadzipereka ndi mtima wonse pa nkhani zokhudza kulambira. Koma umu si mmene Timoteyo analili. Mwayi wotumikira Yehova ukapezeka, iye ankakhala ndi maganizo amene Yesaya anali nawo oti: “Ine ndilipo! Nditumizeni.”—Yes. 6:8.
Kodi inuyo mungatani kuti zinthu zina zimene mumafunika kuchita zisasokoneze zinthu zokhudza kulambira? Choyamba, muyenera kuika zinthu zofunika kwambiri pamalo oyamba. Paja mtumwi Paulo anapereka malangizo akuti: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.” (Afil. 1:10) Mwachidule tingati muziika patsogolo zofuna za Mulungu. Chachiwiri, muyenera kukhala moyo wosalira zambiri. Pewani zinthu zimene zingakuthereni nthawi komanso mphamvu. Paja Paulo analangiza Timoteyo kuti: “Thawa zilakolako zaunyamata, koma tsatira chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, ndi mtendere.”—2 Tim. 2:22.
3. Ankatumikira mwakhama. Paulo anakumbutsa Akhristu a ku Filipi kuti: “Mukudziwa kudalirika kumene [Timoteyo] anaonetsa, kuti monga mwana ndi bambo ake, watumikira monga kapolo limodzi ndi ine kupititsa patsogolo uthenga wabwino.” (Afil. 2:22) Mawu amenewa akusonyeza kuti Timoteyo sanali waulesi. Iye ankagwira ntchito mwakhama limodzi ndi Paulo ndipo izi zinachititsa kuti azigwirizana kwambiri.
Masiku ano, m’gulu la Yehova muli ntchito zambirimbiri. Ntchito zake zimakhala zosangalatsa ndipo zimathandiza kuti muzigwirizana kwambiri ndi abale ndi alongo. Choncho muziyesetsa kuti muzikhala ndi “zochita zambiri nthawi zonse mu ntchito ya Ambuye.”—1 Akor. 15:58.
4. Ankatsatira zimene waphunzira. Paulo anauza Timoteyo kuti: “Iwe wayesetsa kutsatira chiphunzitso changa, moyo wanga, cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, ndi kupirira kwanga.” (2 Tim. 3:10) Timoteyo ankayesetsa kutsatira zimene ankaphunzira ndipo izi zinamuthandiza kuti ayenerere maudindo ena akuluakulu.—1 Akor. 4:17.
Kodi inuyo muli ndi m’bale kapena mlongo amene mumatengera chitsanzo chake? Ngati mulibe yesetsani kuti mupeze mmodzi. M’bale Tom amene wakhala mkulu kwa zaka zambiri ananena kuti: “Mkulu wina wodziwa zambiri ankandithandiza ndipo ndinaphunzira zambiri. Ndinkakonda kumufunsa malangizo ndipo ndinkatsatira zimene wandiuza. Izi zinandithandiza kuti ndisiye kudzikayikira.”
5. Ankapitiriza kudziphunzitsa. Paulo anauza Timoteyo kuti: “Ukhale ndi chizolowezi chochita zinthu zokuthandiza kuti ukhalebe wodzipereka kwa Mulungu.” (1 Tim. 4:7) Katswiri wa masewero othamanga amakhala ndi kochi wake koma nayenso payekha amafunika kudziphunzitsa. Ndiyeno Paulo anauza Timoteyo kuti: “Pitiriza kukhala wodzipereka powerenga pamaso pa anthu, powadandaulira, ndi powaphunzitsa. . . . Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama. Dzipereke pa zinthu zimenezi kuti anthu onse aone kuti ukupita patsogolo.”—1 Tim. 4:13-15.
Nanunso muyenera kupitiriza kudziphunzitsa. Musalole kuti moyo wanu wauzimu ungokhala pamodzimodzi kapena kumangoyendera njira zakale zochitira zinthu mumpingo. Muyeneranso kupewa mtima wodzidalira n’kumaganiza kuti mukhoza kuthana ndi vuto lililonse popanda kufufuza njira yothandiza. Choncho yesetsani kutsanzira Timoteyo amene anatsatira malangizo akuti: “Nthawi zonse uzisamala ndi zimene umachita komanso zimene umaphunzitsa.”—1 Tim. 4:16.
6. Ankadalira mzimu wa Yehova. Paulo ataganizira utumiki wa Timoteyo anamulangiza kuti: “Chuma chapadera chimene anachiika m’manja mwakochi, uchisunge mothandizidwa ndi mzimu woyera umene uli mwa ife.” (2 Tim. 1:14) Timoteyo anayenera kudalira mzimu woyera wa Mulungu kuti ateteze utumiki wake.
M’bale Donald amene wakhalanso mkulu kwa zaka zambiri ananena kuti: “Akulu ndi atumiki othandiza ayenera kuona kuti ubwenzi wawo ndi Mulungu ndi wofunika kwambiri. Akamatero ‘mphamvu zawo zidzapitiriza kuwonjezeka.’ Akamapempha Yehova kuti awapatse mzimu woyera komanso kuyesetsa kukhala ndi makhalidwe amene mzimuwo umatulutsa amathandiza kwambiri abale ndi alongo.”—Sal. 84:7; 1 Pet. 4:11.
MUZIONA KUTI UTUMIKI WANU NDI WAMTENGO WAPATALI
Zimasangalatsa kwambiri kuona anthu amene angopatsidwa kumene udindo akupita patsogolo. Jason amene tamutchula kumayambiriro uja anati: “Pa nthawi yonse imene ndakhala mkulu ndaphunzira zambiri ndipo ndasiya kudzikayikira. Panopa ndimasangalala kwambiri ndi utumiki wanga ndipo ndimaona kuti ndi wamtengo wapatali.”
Kodi nanunso mudzayesetsa kuti muzipita patsogolo mwauzimu? Yesetsani kutsanzira Timoteyo. Mukatero mudzathandiza kwambiri anthu a Yehova.