Madalitso a Kugwira Ntchito ndi Ena
1 Kodi muganiza kuti pali madalitso omwe amadza mwa kugwira ntchito ndi ena mu utumiki? Yesu anatero. Ngakhale kuti zotuta zinali zochuluka ndipo antchito oŵerengeka, iye anatumiza ophunzira 70 m’munda “aŵiriaŵiri.” Onsewo anali ndi nthaŵi yopindulitsa chotani nanga akumalalikira ku “mudzi uliwonse, ndi malo alionse kumene ati afikeko mwini”!—Luka 10:1, 17; Mat. 9:37.
2 Kugwira ntchito ndi ena kumatsitsimula. Enafe tili amanyazi ndipo kumatikhalira kovuta kufikira anthu osawadziŵa. Kukhala ndi wina kungatipatse chidaliro cha kulankhula Mawu a Mulungu molimba mtima. Pamene tili ndi wina, kungakhale kosavuta kuchita ntchitoyo mwa njira imene taphunzitsidwa. (Miy. 27:17) Munthu wanzeru anati: “Aŵiri aposa mmodzi.”—Mlal. 4:9.
3 Nkwabwino kugwira ntchito ndi ofalitsa ndi apainiya osiyanasiyana. Anzake a mu utumiki a mtumwi Paulo anaphatikizapo Barnaba, Sila, Timoteo, ndi Yohane Marko, ndipo iwo anapeza madalitso ochuluka polalikira pamodzi. Zingakhalenso motero lerolino. Kodi munagwirapo ntchito pamodzi ndi wina yemwe wakhala m’choonadi kwa nthaŵi yaitali? Mutaona luso lake popereka umboni, muyenera kuti munatengapo malingaliro abwino omwe akuthandizani kuwongokera. Kodi munatsaganapo ndi ofalitsa achatsopano? Pamenepo mwinamwake munakhoza kuwagaŵira zina za zimene mwaphunzira kwakuti mwina munawathandiza kukhala ogwira mtima kwambiri ndi kupeza chisangalalo chokulirapo mu utumiki wawo.
4 Kodi pakali pano mukuchititsa phunziro la Baibulo? Ngati ndi tero, bwanji osaitanira mmodzi wa akulu kapena woyang’anira dera kutsagana nanu? Kumakhala kopindulitsa kwa ophunzira Baibulo athu kuzoloŵerana ndi oyang’anira. Ngati mukuwopa kuchititsa phunziro pamaso pa mkulu, mwinamwake iye angakhale wofunitsitsa kulichititsa pamene inu mukupenyerera. Pambuyo pake, khalani womasuka kumfunsa malingaliro a mmene mungathandizire wophunzira wanu kupita patsogolo mofulumira.
5 Khalani wolimbikitsa pamene mugwira ntchito ndi ena. Perekani ndemanga zabwino ponena za gawo. Musadyere ena miseche kapena kuŵiringula ponena za makonzedwe a mpingo. Sumikani maganizo anu pa utumiki ndi pa madalitso ochokera kwa Yehova. Ngati mutero, onse aŵirinu mudzabwerera kunyumba muli wotsitsimulidwa mwauzimu.
6 Mikhalidwe yanu ingakuchititse kukhala kovuta kwa inu kugwira ntchito nthaŵi zonse ndi abale ndi alongo ena. Komabe, ngati kuli kotheka, bwanji osalinganiza kupatula nthaŵi yoti mudzagwire ntchito ndi wofalitsa wina? Nonse aŵirinu mudzapeza madalitso!—Aroma 1:11, 12.