Apainiya Athandiza Ena
1 Yesu anati: “Dzinthu dzichuluka, koma antchito achepa; potero pemphani Mwini dzinthu, kuti akankhe antchito kukututa kwake.” Popeza kuti otuta a m’zaka za zana loyamba anali ochepa ndipo anali ndi ndime yaikulu yoti afole, Yesu akanatha kuwatumiza mmodzimmodzi kuti afikire anthu ochuluka ndi uthenga wabwino. M’malomwake, ‘anawatuma iwo aŵiriaŵiri.’ (Luka 10:1, 2) Nchifukwa ninji aŵiriaŵiri?
2 Ophunzira amenewo anali atsopano ndiponso osazoloŵera. Akanatha kuphunzitsana ndi kulimbikitsana mwakugwirira ntchito pamodzi. Monga mmene Solomo ananenera, “aŵiri aposa mmodzi.” (Mlal. 4:9, 10) Ngakhale pambuyo pakutsanuliridwa kwa mzimu woyera pa Pentekoste mu 33 C.E., Paulo, Barnaba, ndi ena anali kutsagana ndi okhulupirira anzawo mu utumiki. (Mac. 15:35) Unalidi mwayi waukulu kwa ena kuphunzitsidwa mwachindunji ndi amuna odziŵa oterowo!
3 Programu Yabwino ya Maphunziro: Mofanana ndi mpingo unzake wa m’zaka za zana loyamba, mpingo wachikristu wamakono ndi gulu lolalikira. Umatipatsanso maphunziro. Chikhumbo chathu chachikulu, aliyense payekha, chiyenera kukhala kulalikira mbiri yabwino mogwira mtima kwambiri. Chithandizo chilipo kuti ofalitsa ochuluka athe kukhala ogwira mtima kwambiri.
4 Pa Sukulu Yautumiki Waufumu yomwe inachitika posachedwapa, Sosaite inalengeza za programu yakuti apainiya azithandiza ena mu utumiki wakumunda. Kodi zimenezi nzofunika? Inde. Ofalitsa oposa miliyoni imodzi abatizidwa m’zaka zitatu zapitazi, ndipo ochuluka a ameneŵa akufunika kuphunzitsidwa kuti akhale ogwira mtima kwambiri m’ntchito yolalikira. Kodi ndani amene angagwiritsiridwe ntchito kukwaniritsa chosoŵa chimenechi?
5 Apainiya anthaŵi zonse angathandize. Gulu la Yehova limawapatsa uphungu ndi maphunziro ochuluka. Apainiya amalandira malangizo ogwirizana ndi zosoŵa zawo m’Sukulu Yautumiki Waupainiya ya milungu iŵiri. Amapindulanso ndi misonkhano yomwe amakhala nayo ndi woyang’anira dera ndi woyang’anira chigawo, ndiponso chitsogozo cha akulu. Ngakhale kuti si apainiya onse amene ali ndi chidziŵitso monga mmene Paulo ndi Barnaba analili, iwo apatsidwa maphunziro abwino kwambiri, amene amasangalala kuwauzako ena.
6 Kodi Ndani Adzapindula? Kodi ndi ofalitsa achatsopano kapena amene angobatizidwa kumene okha amene akulowetsedwa m’programuyi? Kutalitali! Pali achinyamata ndi achikulire amene azindikira choonadi kwa zaka zingapo koma ndi oti angayamikire kuthandizidwa m’mbali zina za utumiki. Ena amagaŵira mabuku bwino kwambiri koma amavutika kuti apange maulendo obwereza kapena kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Ena savutika kuyambitsa maphunziro a Baibulo koma amaona kuti ophunzira awo sapita patsogolo. Kodi nchiyani chimene chimawabwezera m’mbuyo? Apainiya ozoloŵera angapemphedwe kuti athandize m’mbali zimenezi. Apainiya ena amadzutsa chidwi, kuyambitsa maphunziro a Baibulo, ndi kutsogoza ophunzira achatsopano ku gulu mogwira mtima. Chidziŵitso chawo chidzathandizadi m’programu yatsopano imeneyi.
7 Kodi mumaona kuti ndandanda yanu sikulolani kuti muzipezeka pa kukumana kwa utumiki wakumunda kumene kumachitika mokhazikika mumpingo wanu monga mmene mumafunira? Mpainiya angakhale wokhoza kugwira nanu ntchito panthaŵi zina pamene ofalitsa ena palibe.
8 Kugwirizana Nkofunika: Kaŵiri pachaka, akulu azipanga makonzedwe kuti ofalitsa amene akufuna kuthandizidwa aloŵe mu programu ya Apainiya Athandiza Ena. Ngati muvomera kuti mulandire chithandizo chimenecho, gwirizanani ndi mpainiya amene wauzidwa kuti akuthandizeniyo, pangani ndandanda yautumiki yoyenerera ndi kumaitsatira. Sungani mapangano anu onse. Pamene mukugwirira ntchito limodzi, onetsetsani njira zogwira mtima zolalikirira uthenga wabwino. Onani chifukwa chake mafikidwe ena ali ogwira mtima. Ganizirani za malingaliro amene mpainiyayo angapereke kuti muwongolere ulaliki wanu. Pamene mugwiritsira ntchito zimene mukuphunzira, kupita kwanu patsogolo mu utumiki kudzaonekera, kwa inu ndiponso kwa ena. (Onani 1 Timoteo 4:15.) Gwirani ntchito limodzi mwakaŵirikaŵiri monga mmene mungathere, mukumachitira limodzi mbali zonse za utumiki, kuphatikizapo umboni wamwamwayi, koma muzisumika maganizo kwambiri pa mbali imene mukufunikira chithandizo.
9 Woyang’anira utumiki amafuna kudziŵa mmene mukupitira patsogolo. Nthaŵi ndi nthaŵi adzakambirana ndi wochititsa Phunziro la Buku la Mpingo kuti aone mmene mukupindulira ndi programuyo. Nayenso woyang’anira dera adzakuthandizani pamene akuchezera mpingo wanu.
10 Yehova akufuna kuti anthu ake aphunzitsidwe ndi ‘kukonzekeretsedwa kuchita ntchito iliyonse yabwino.’ (2 Tim. 3:17) Onani programu ya Apainiya Athandiza Ena ngati makonzedwe abwino othandizira amene akufuna kupititsa patsogolo luso lawo la kulalikira uthenga. Ngati muli ndi mwayi wakuchita nawo programuyi, teroni moyamikira, modzichepetsa ndi mwachimwemwe.