Misonkhano ya Utumiki ya June
Mlungu Woyambira June 7
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Mbiri Yateokalase.
Mph. 15: “Tikuphunzitsidwa ndi Yehova.” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosapitirira imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pemphani omvetsera kusimba mapindu ena amene apeza mu Sukulu ya Utumiki Wateokalase, Sukulu ya Utumiki Waupainiya, Sukulu ya Utumiki wa Ufumu, ndi zina zotero. Gogomezerani mmene zimenezi zathandizira anthu a Yehova kukhala ogwira mtima kwambiri mu utumiki.
Mph. 20: “Gwiritsani Ntchito Nthaŵi Yanu Moyenera.” Kukambirana kwa wopangitsa Phunziro la Buku la Mpingo ndi wofalitsa wozoloŵera mmodzi kapena aŵiri asimbe mmene agwiritsira ntchito nthaŵi yawo bwino kuti atengemo mbali mokwanira mu utumiki wakumunda. Afotokoze kufunika kwa ndandanda yotsatirika ndipo agogomezere kufunika kokhala nayo. Anene mmene amapeŵera zinthu zotayitsa nthaŵi monga kuyamba mochedwa, kusakonzekera bwino, kapena kucheza kwambiri mkati mwa utumiki. Mukumalingalira za mikhalidwe ya kumaloko, perekani malingaliro othandiza a mmene angagwiritsire ntchito nthaŵi moyenera.
Nyimbo Na. 48 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 14
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 20: “Kodi Mungathandize?” Nkhani yokambirana ndi omvetsera yokambidwa ndi mkulu. Phatikizanipo malingaliro othandizira mabanja a kholo limodzi opezeka mu Galamukani! ya October 8, 1995, masamba 8-9. Pemphani ena kusimba kuyamikira kwawo chithandizo chachikondi chimene analandira kuchokera kwa ena mumpingo.
Nyimbo Na. 53 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 21
Mph. 7: Zilengezo za pampingo. Ngati mpingo uli ndi mabuku a Achichepere Akufunsa kapena Youth mu sitoko, sonyezani mmene angagwiritsidwire ntchito mogwira mtima mu utumiki pamene tikukhulupirira kupeza achinyamata ambiri panyumba.
Mph. 20: “Samalirani Kapesedwe ndi Kavalidwe Kanu.” Kupenda nkhaniyi mwa mafunso ndi mayankho. Wochititsa akhale mkulu. Onani mmene chidziŵitsochi chingagwiritsidwire ntchito kumaloko.
Mph. 18: “Kodi Mumaona Maonekedwe Akunja Okha?” Nkhani yokambirana ndi omvetsera. Gogomezerani zifukwa zimene sitiyenera kufulumiza kuweruza anthu amene timakumana nawo. Pendani mwachidule phunziro limene Yehova anaphunzitsa Yona, amene molakwa anaweruza omwe anawaona ngati osayenera. (Onani Nsanja ya Olonda ya August 15, 1997, masamba 21-2, ndime 17-19.) Pemphani omvetsera kusimba za anthu osiyanasiyana amene akhala akukumana nawo m’gawo, anene zimene zimawathandiza kuwaona bwino anthuwa ndi kusiya chiweruzo m’manja mwa Yehova.
Nyimbo Na. 77 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 28
Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani onse kupereka malipoti a utumiki wakumunda a June. Pendani mabuku ogaŵira mu July. Sonyezani mabolosha amene mpingo uli nawo ambiri, ndipo perekani mfundo imodzi kapena ziŵiri zimene tinganene paulaliki wathu. Phatikizanipo chitsanzo chokonzekeredwa bwino cha ulaliki.
Mph. 13: Chifukwa Chiyani Yehova Amalola Chizunzo pa Anthu Ake? Nkhani yokambidwa ndi mkulu, yochokera mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 1998, masamba 10,11, ndime 6-10, pamutu wakuti “Chikhulupiriro Chiyesedwa—Chifukwa Chiyani?” Monga mmene Yesu ananeneratu, ‘timadedwa ndi anthu onse.’ (Mat. 24:9) Tingakumane ndi chitsutso mu utumiki, pocheza ndi anansi achikunja, kapena pokhala pamodzi ndi anthu amene sali Mboni kuntchito kapena kusukulu. Mlankhuli afotokoze mwanjira yabwino chifukwa chake Yehova amalola chizunzo kapena chitsutso chimenechi ndi mmene kupirira kwathu pomalizira pake kudzabweretsere madalitso.
Mph. 20: “Mwayi Umene Sunapezekeponso.” Nkhani yokambirana ndi omvetsera. Ikambidwe ndi mkulu, akambe mosangalatsa, amvetsere mayankho kuchokera kwa omvetsera ochuluka.
Nyimbo Na. 75 ndi pemphero lomaliza.