NKHANI YOPHUNZIRA 19
Okonda Chilungamo Palibe Chowakhumudwitsa
“Okonda chilamulo chanu amapeza mtendere wochuluka, ndipo palibe chowakhumudwitsa.”—SAL. 119:165.
NYIMBO NA. 122 Khalani Olimba Komanso Osasunthika.
ZIMENE TIPHUNZIREa
1-2. (a) Fotokozani zimene wolemba mabuku wina ananena. (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
MASIKU ano anthu ambiri amanena kuti amakhulupirira Yesu koma satsatira zimene iye anaphunzitsa. (2 Tim. 4:3, 4) Ndipotu wolemba mabuku wina ananena kuti: “Pakanakhala kuti masiku ano pali munthu amene angalankhule ngati mmene Yesu ankalankhulira . . . , kodi tikanamukana ngati mmene anthu ena anachitira zaka 2,000 zapitazo? . . . Yankho lodziwikiratu ndi lakuti: Inde, ndi zimene tikanachita.”
2 Yesu ali padzikoli, anthu ambiri anamumva akuphunzitsa ndiponso anamuona akuchita zozizwitsa koma anakana kumukhulupirira. Chifukwa chiyani? Munkhani yapita ija, tinakambirana zifukwa 4 zimene zinapangitsa anthu kuti akane Yesu. Tsopano tiyeni tikambirane zifukwa zinanso 4. Tikamakambirana zimenezi, tionanso chifukwa chake anthu masiku ano amakana kumvetsera zimene otsatira a Yesu amaphunzitsa komanso zimene zingatithandize kuti tisakhumudwe n’kusiya kutumikira Yehova.
(1) YESU ANALIBE TSANKHO
3. Kodi Yesu ankachita chiyani, chomwe chinachititsa kuti ena akhumudwe naye?
3 Pamene anali padzikoli, Yesu ankachita zinthu ndi aliyense. Mwachitsanzo, iye ankadya ndi anthu olemera komanso audindo koma nthawi zambiri ankachitanso zinthu ndi osauka ndiponso oponderezedwa. Kuwonjezera apo, ankachitiranso chifundo anthu omwe ambiri ankawaona ngati “ochimwa.” Koma anthu ena odziona ngati olungama anakhumudwa ndi zimene Yesu ankachitazi. Iwo anafunsa ophunzira ake kuti: “N’chifukwa chiyani inu mumadya ndi kumwa limodzi ndi okhometsa msonkho ndi anthu ochimwa?” Poyankha, Yesu anawauza kuti: “Anthu athanzi safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna. Ine sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa kuti alape.”—Luka 5:29-32.
4. Mogwirizana ndi ulosi wa Yesaya, kodi Ayuda ankayenera kuyembekezera chiyani chokhudza Mesiya?
4 Kodi Malemba amati chiyani? Kudakali zaka zambiri kuti Mesiya abwere, mneneri Yesaya ananeneratu kuti anthu adzamukana. Ulosiwo unanena kuti: “Iye ananyozedwa ndipo anthu anali kumupewa. . . . Ife tinali kuyang’ana kumbali kuti tisaone nkhope yake. Ananyozedwa ndipo tinamuona ngati wopanda pake.” (Yes. 53:3) Popeza Mesiya anali woti “anthu” azidzamupewa, Ayuda a m’nthawi ya Yesu ankayenera kuyembekezera kuti iye azikanidwa.
5. Kodi anthu ambiri amawaona bwanji otsatira a Yesu masiku ano?
5 Kodi vuto limeneli liliponso masiku ano? Inde. Atsogoleri achipembedzo ambiri amasangalala kulandira m’mipingo mwawo anthu omwe ndi otchuka, olemera komanso amene amaonedwa ngati anzeru m’dzikoli. Iwo amalola anthuwa kukhala m’zipembedzo zawo ngakhale kuti makhalidwe komanso zochita zawo n’zosemphana ndi zimene Mulungu amafuna. Anthu m’dzikoli amaona kuti atumiki a Yehova omwe amatsatira mfundo zake zamakhalidwe abwino ndi osafunika, choncho atsogoleri achipembedzo amanyoza atumiki a Yehovawo. Mogwirizana ndi zimene mtumwi Paulo ananena, Mulungu anasankha anthu amene amaonedwa ngati ‘achabechabe.’ (1 Akor. 1:26-29) Komabe, Yehova amaona kuti atumiki ake onse okhulupirika ndi amtengo wapatali.
6. Kodi tingatsanzire bwanji maganizo a Yesu, omwe afotokozedwa pa Mateyu 11:25, 26?
6 Kodi tingatani kuti tisakhumudwe n’kusiya kutumikira Yehova? (Werengani Mateyu 11:25, 26.) Musamaone anthu a Mulungu ngati mmene dzikoli limawaonera. Muzikumbukira kuti Yehova amagwiritsa ntchito anthu odzichepetsa okha kuti achite chifuniro chake. (Sal. 138:6) Ndiponso muziganizira zinthu zimene Yehova wakwanitsa kuchita pogwiritsa ntchito anthu amene dziko siliwaona kuti ndi anzeru kapena ophunzira.
(2) YESU ANATSUTSA MFUNDO ZABODZA
7. N’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti Afarisi anali achinyengo, nanga iwo anatani atamva zimenezi?
7 Yesu ankadzudzula molimba mtima zochita zachinyengo za atsogoleri achipembedzo. Mwachitsanzo, iye anadzudzula chinyengo cha Afarisi omwe ankaona kuti kusamba m’manja n’kofunika kwambiri kuposa kusamalira makolo awo. (Mat. 15:1-11) N’kutheka kuti ophunzira ake anadabwa ndi zimene iye ananena. Choncho, iwo anamufunsa kuti: “Kodi mukudziwa kuti Afarisi akhumudwa ndi zimene mwanena zija?” Yesu anawayankha kuti: “Mbewu iliyonse imene sinabzalidwe ndi Atate wanga wakumwamba idzazulidwa. Alekeni amenewo. Iwo ndi atsogoleri akhungu. Chotero ngati munthu wakhungu akutsogolera wakhungu mnzake, onse awiri adzagwera m’dzenje.” (Mat. 15:12-14) Ngakhale kuti zomwe Yesu ananena zinakwiyitsa atsogoleri achipembedzo, zimenezi sizinamulepheretse kulankhula choonadi.
8. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti Mulungu savomereza zonse zimene zipembedzo zimaphunzitsa?
8 Yesu anadzudzulanso zinthu zachinyengo zimene atsogoleri achipembedzo ankaphunzitsa. Iye sananene kuti Mulungu amavomereza zonse zimene zipembedzo zimaphunzitsa. M’malomwake, iye ananena kuti anthu ambiri adzayenda pamsewu waukulu ndi wotakasuka wopita kuchiwonongeko, pomwe ochepa adzayenda pamsewu wopanikiza wopita kumoyo. (Mat. 7:13, 14) Yesu ananena momveka bwino kuti ena adzaoneka ngati akutumikira Mulungu. Iye anachenjeza kuti: “Chenjerani ndi aneneri onyenga amene amabwera kwa inu atavala ngati nkhosa, koma mkati mwawo ali mimbulu yolusa. Mudzawazindikira ndi zipatso zawo.”—Mat. 7:15-20.
9. Kodi Yesu anadzudzula zinthu zina ziti zimene atsogoleri achipembedzo ankaphunzitsa?
9 Kodi Malemba amati chiyani? Ulosi wa m’Baibulo unaneneratu kuti Mesiya adzakhala wodzipereka kwambiri panyumba ya Yehova. (Sal. 69:9; Yoh. 2:14-17) Kudzipereka kumeneku ndi komwe kunachititsa kuti Yesu adzudzule zachinyengo zimene atsogoleri achipembedzo ankachita komanso zinthu zabodza zomwe ankaphunzitsa. Mwachitsanzo, Yesu ankaphunzitsa kuti akufa ali mtulo koma Afarisi ankakhulupirira kuti mzimu wa munthu suufa. (Yoh. 11:11) Yesu anaukitsa Lazaro koma Asaduki sankakhulupirira kuti akufa adzauka. (Yoh. 11:43, 44; Mac. 23:8) Yesu ankaphunzitsa kuti anthu amachita kusankha okha kuti azitumikira Mulungu koma Afarisi ankaphunzitsa kuti Mulungu kapena mphamvu inayake yosaoneka ndi zimene zimachititsa zonse zomwe zimachitika pa moyo wathu.—Mat. 11:28.
10. N’chifukwa chiyani anthu ambiri amakana kumvetsera zimene timaphunzitsa?
10 Kodi vuto limeneli liliponso masiku ano? Inde. Anthu ambiri amakana kumvetsera uthenga wathu chifukwa timagwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo pothandiza ena kudziwa zinthu zabodza zomwe zipembedzo zimaphunzitsa. Atsogoleri achipembedzo amaphunzitsa anthu awo kuti Mulungu amalanga anthu oipa kumoto. Iwo amaphunzitsa zimenezi pofuna kuti anthu asamachite zoipa. Monga atumiki a Yehova omwe amalambira Mulungu yemwe ndi wachikondi, timathandiza anthu kudziwa kuti zimenezi ndi zabodza. Atsogoleriwo amaphunzitsanso kuti mzimu wa munthu suufa. Zimenezi zikanakhala zoona, sipakanafunikanso kuti anthu adzaukitsidwe. Choncho timathandiza anthu kudziwa kuti izi si zomwe Baibulo limaphunzitsa. Komanso, mosiyana ndi zipembedzo zambiri zomwe zimaphunzitsa kuti Mulungu kapena mphamvu inayake yosaoneka ndi zimene zimachititsa zonse zomwe zimachitika pa moyo wathu, timaphunzitsa kuti aliyense ali ndi ufulu wosankha kutumikira Mulungu kapena ayi. Ndiye kodi atsogoleri achipembedzo amatani chifukwa cha zimene timachitazi? Nthawi zambiri, iwo amakwiya.
11. Mogwirizana ndi mawu a Yesu a pa Yohane 8:45-47, kodi Mulungu amafuna kuti anthu ake azichita chiyani?
11 Kodi tingatani kuti tisakhumudwe n’kusiya kutumikira Yehova? Ngati timakonda choonadi, tiyenera kukhulupirira komanso kumvera zimene Mulungu amanena. (Werengani Yohane 8:45-47.) Mosiyana ndi Satana Mdyerekezi, ndife okhazikika m’choonadi. Timachita zinthu mogwirizana ndi zimene timakhulupirira. (Yoh. 8:44) Mulungu amafuna kuti anthu ake ‘azinyansidwa ndi choipa’ ndipo ‘azigwiritsitsa chabwino,’ ngati mmene Yesu anachitira.—Aroma 12:9; Aheb. 1:9.
(3) YESU ANAZUNZIDWA
12. Kodi mmene Yesu anafera, zinachititsa bwanji kuti Ayuda ambiri amukane?
12 Kodi chifukwa china chomwe chinachititsa Ayuda kukana Yesu chinali chiyani? Paulo anati: “Ife timalalikira za Khristu amene anapachikidwa. Kwa Ayuda, chimenechi ndi chinthu chokhumudwitsa.” (1 Akor. 1:23) Kodi mmene Yesu anafera, zinachititsa bwanji kuti Ayuda ambiri amukane? Kwa iwo, kuphedwa kwa Yesu pamtengo wozunzikirapo kunachititsa kuti azimuona ngati wachifwamba komanso wochimwa, osati Mesiya.—Deut. 21:22, 23.
13. Kodi Ayuda amene anakana Yesu analephera kuzindikira chiyani?
13 Ayuda omwe anakana Yesu analephera kuzindikira kuti iye anali wosalakwa, anaimbidwa milandu yabodza komanso anachitiridwa zinthu zopanda chilungamo. Anthu amene ankaweruza mlandu wa Yesu, anapotoza chilungamo. Oweruza a Khoti Lalikulu la Ayuda anakumana mofulumira ndipo poweruza mlanduwo sankatsatira malamulo. (Luka 22:54; Yoh. 18:24) M’malo momvetsera mlanduwo komanso maumboni ake mosakondera, iwo ankafunafuna “umboni wonama kuti amunamizire mlandu Yesu ndi kumupha.” Izi zitakanika, mkulu wa ansembe anayesetsa kuchititsa Yesu kuti alankhule zinthu zimene akanamukola nazo mawu n’cholinga choti apezeke wolakwa. Zimenezinso zinali zosemphana ndi malamulo oweruzira mlandu. (Mat. 26:59; Maliko 14:55-64) Komanso Yesu ataukitsidwa, oweruza opanda chilungamowa anapereka ndalama zasiliva zambiri kwa asilikali a Chiroma, omwe ankalondera manda ake kuti afalitse nkhani yabodza yokhudza zimene zinachitika kuti thupi la Yesu lisapezeke m’mandamo.—Mat. 28:11-15.
14. Kodi Malemba ananeneratu chiyani zokhudza imfa ya Mesiya?
14 Kodi Malemba amati chiyani? Ngakhale kuti Ayuda ambiri m’nthawi ya Yesu sankayembekezera kuti Mesiya adzafunika kuti afe, taonani zimene Malemba ananeneratu zokhudza iye, kuti: “Anakhuthula moyo wake mu imfa ndipo anaonedwa monga mmodzi wa ochimwa. Iye ananyamula tchimo la anthu ambiri ndipo analowererapo kuti athandize olakwa.” (Yes. 53:12) Choncho kuphedwa kwa Yesu monga munthu wochimwa, sichinali chifukwa chomveka choti Ayudawo amukanire.
15. Kodi ndi milandu yotani imene a Mboni za Yehova akhala akuimbidwa yomwe yachititsa kuti anthu ena azikana uthenga wawo?
15 Kodi vuto limeneli liliponso masiku ano? N’zosachita kufunsa. Mofanana ndi Yesu yemwe anaimbidwa mlandu wabodza komanso kugamulidwa kuti ndi wolakwa, a Mboni za Yehova masiku ano amakumananso ndi mavuto amenewa. Tiyeni tione zitsanzo zingapo. M’zaka za m’ma 1930 ndi m’ma 1940, makhoti ambiri ku America ankaweruza milandu yokhudza ufulu wathu wolambira Mulungu. Oweruza ena ankaonekeratu kuti ankaweruza mokondera n’cholinga choti tisapambane pa milanduyo. Ku Quebec, m’dziko la Canada, tchalitchi ndi boma zinkachita zinthu mogwirizana potsutsa ntchito yathu. Ofalitsa ambiri anamangidwa chifukwa chongouza anthu ena zokhudza Ufumu wa Mulungu. M’nthawi ya ulamuliro wankhanza wa Nazi ku Germany, abale ambiri achinyamata anaphedwa. Ndipo m’zaka zaposachedwapa, abale ambiri ku Russia akhala akuimbidwa milandu komanso kumangidwa chifukwa chouza ena mfundo za m’Baibulo, zimene boma likumati ndi “zoopsa.” Ngakhalenso Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika la m’chinenero cha Chirasha, linaletsedwa ndipo linaikidwa m’gulu la “zinthu zoopsa” chifukwa lili ndi dzina la Mulungu loti Yehova.
16. Mogwirizana ndi 1 Yohane 4:1, n’chifukwa chiyani sitiyenera kusocheretsedwa ndi nkhani zabodza zokhudza anthu a Yehova?
16 kodi tingatani kuti tisakhumudwe n’kusiya kutumikira Yehova? Muzifufuza kuti mudziwe zoona zenizeni. Pa ulaliki wake wa paphiri, Yesu anachenjeza anthu amene ankamumvetsera kuti anthu ena adzawanamizira “zoipa zilizonse.” (Mat. 5:11) Mabodza amenewa amachokera kwa Satana. Iye amagwiritsa ntchito otsutsa kuti azifalitsa mabodza okhudza anthu amene amakonda choonadi. (Chiv. 12:9, 10) Sitiyenera kumvetsera zinthu zabodza zimene adani athu amanena. Ndipo tisamalole kuti zinthu zabodzazi zitichititse mantha kapenanso kufooketsa chikhulupiriro chathu.—Werengani 1 Yohane 4:1.
(4) YESU ANAPEREKEDWA KOMANSO ANAKANIDWA
17. Kodi zomwe zinachitika Yesu atangotsala pang’ono kuphedwa zikanachititsa bwanji ena kuti amukane?
17 Atangotsala pang’ono kuphedwa, Yesu anaperekedwa ndi mmodzi wa atumwi ake 12. Mtumwi wake wina anamukana katatu ndipo usiku woti aphedwa mawa lake, atumwi ena onse anamuthawa. (Mat. 26:14-16, 47, 56, 75) Koma Yesu sanadabwe ndi zimenezi. Ndipotu anali ataneneratu kuti izi ndi zomwe zidzachitike. (Yoh. 6:64; 13:21, 26, 38; 16:32) Poona zimene zinachitikazi, anthu ena akanakhumudwa n’kuyamba kuganiza kuti, ‘Ngati umu ndi mmene atumwi a Yesu achitira, sindingakonde kukhala m’gulu lawo.’
18. Kodi zimene zinachitika Yesu atangotsala pang’ono kuphedwa zinakwaniritsa maulosi ati?
18 Kodi Malemba amati chiyani? Zaka zambiri Yesu asanabwere padzikoli, Yehova ananeneratu m’Mawu ake kuti Mesiya adzaperekedwa ndi ndalama 30 zasiliva. (Zek. 11:12, 13) Ananeneratunso kuti yemwe adzapereke Yesu adzakhala mmodzi wa anzake apamtima. (Sal. 41:9) Mneneri Zekariya analembanso kuti: “Ipha m’busa ndipo nkhosa zake zibalalike.” (Zek. 13:7) Choncho m’malo mokhumudwa ndi zimenezi, chikhulupiriro cha anthu oona mtima chikanalimba poona kuti maulosi amenewa akwaniritsidwa pa Yesu.
19. Kodi anthu oona mtima amazindikira chiyani?
19 Kodi vuto limeneli liliponso masiku ano? Inde. M’nthawi yathu ino, a Mboni ena odziwika bwino asiya choonadi n’kukhala a mpatuko ndipo amayesetsa kupatutsa ena kuti awatsatire. Iwo akhala akufalitsa malipoti oipa, nkhani zosocheretsa komanso mabodza okhudza Mboni za Yehova kudzera m’manyuzipepala, pa wailesi, pa TV komanso pa intaneti. Koma anthu oona mtima sasocheretsedwa ndi zimenezi. M’malomwake, iwo amazindikira kuti Baibulo linaneneratu kuti zinthu zimenezi zidzachitika.—Mat. 24:24; 2 Pet. 2:18-22.
20. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisasocheretsedwe ndi anthu amene asiya choonadi? (2 Timoteyo 4:4, 5)
20 Kodi tingatani kuti tisakhumudwe n’kusiya kutumikira Yehova? Tiyenera kulimbitsa chikhulupiriro chathu pophunzira Mawu a Mulungu nthawi zonse, kupemphera pafupipafupi komanso kudzipereka pa ntchito imene Yehova anatipatsa kuti tizigwira. (Werengani 2 Timoteyo 4:4, 5.) Tikakhala ndi chikhulupiriro, sitingasokonezedwe tikamva malipoti oipa. (Yes. 28:16) Popeza timakonda Yehova, Mawu ake komanso abale athu, sitingakhumudwe n’kusiya kumutumikira chifukwa choti ena asiya choonadi.
21. Ngakhale kuti anthu ambiri masiku ano amakana uthenga wathu, kodi cholimbikitsa n’chiyani?
21 Mu nthawi ya Yesu, anthu ambiri anakhumudwa ndipo anakana kumutsatira. Komabe, anthu enanso ambiri anamukhulupirira. Amenewa akuphatikizapo woweruza wa Khoti Lalikulu la Ayuda komanso “ansembe ambirimbiri.” (Mac. 6:7; Mat. 27:57-60; Maliko 15:43) Masiku anonso, anthu mamiliyoni ambiri amakhulupirira Yesu. Chifukwa chiyani? Chifukwa iwo amadziwa komanso amakonda choonadi chopezeka m’Malemba. Mawu a Mulungu amanena kuti: “Okonda chilamulo chanu amapeza mtendere wochuluka, ndipo palibe chowakhumudwitsa.”—Sal. 119:165.
NYIMBO NA. 124 Tizikhulupirika Nthawi Zonse
a Munkhani yapitayi, tinakambirana zifukwa 4 zimene zinachititsa anthu ena m’mbuyomu kukana Yesu komanso zomwe zimachititsa anthu kukana kumvetsera otsatira ake masiku ano. Munkhaniyi tikambirana zifukwa zinanso 4. Tionanso chifukwa chake anthu oona mtima amene amakonda Yehova, salola kuti chilichonse chiwakhumudwitse n’kusiya kumutumikira.
b MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Yesu akudya limodzi ndi Mateyu komanso okhometsa misonkho.
c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Yesu akuthamangitsa ogulitsa malonda m’kachisi.
d MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Yesu amunyamulitsa mtengo wake wozunzikirapo
e MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Yudasi akupereka Yesu pomupsompsona.