MBIRI YA MOYO WANGA
Ndinalola Kuti Yehova Azinditsogolera pa Moyo Wanga
NDILI wachinyamata, ndinasankha kuti ndizigwira ntchito imene inkandisangalatsa. Koma Yehova anandipempha kuti ndisankhe zosiyana ndi zimenezi ndipo zinali ngati akundiuza kuti, “Ndidzakupatsa nzeru ndi kukulangiza njira yoti uyendemo.” (Sal. 32:8) Kulola Yehova kuti azinditsogolera pa moyo wanga, kwathandiza kuti ndikhale ndi mwayi wochita zinthu zambiri zosangalatsa pomutumikira komanso kupeza madalitso monga kukatumikira ku Africa kwa zaka 52.
KUCHOKA KU ENGLAND KUPITA KU MALAWI
Ndinabadwa mu 1935 ku Darlaston, mbali ya dera lina ku England lomwe limatchedwa Black Country. Derali limadziwika ndi dzinali chifukwa cha utsi wakuda womwe umachoka m’mafakitale ambiri omwe ali m’derali. Ndili ndi zaka pafupifupi 4, makolo anga anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Ndili ndi zaka zapakati pa 14 ndi 15 ndinatsimikizira kuti zimene makolo anga anaphunzira ndi choonadi ndipo ndinabatizidwa mu 1952 ndili ndi zaka 16.
Pa nthawiyo ndinayamba ntchito pakampani ina yaikulu yopanga zipangizo zogwirira ntchito komanso zitsulo za galimoto. Kenako ndinayamba kuphunzira ntchito ya usekilitale pakampaniyi ndipo ndinkaikonda kwambiri ntchitoyi.
Ndinkafunika kusankha zochita mwanzeru pamene woyang’anira woyendayenda anandipempha kuti ndizichititsa Phunziro la Buku la Mpingo mumpingo wakwathu wa Willenhall. Koma zinali zovuta kuti ndisankhe zochita pa nkhaniyi chifukwa pa nthawiyo ndinkasonkhana ndi mipingo iwiri. Mkati mwa mlungu, ndinkasonkhana ndi mpingo wa pafupi ndi kumene ndinkagwira ntchito ku Bromsgrove, womwe unali pa mtunda wamakilomita 32 kuchokera kumene ndinkakhala. Ndipo kumapeto kwa mlungu ndikabwerera kunyumba kwa makolo anga, ndinkasonkhana ndi mpingo wa ku Willenhall.
Chifukwa choti ndinkafuna kuthandiza gulu la Yehova, ndinavomera zimene woyang’anira woyendayenda uja anandipempha ngakhale kuti zimenezi zinachititsa kuti ndisiye ntchito imene ndinkaikonda ija. Kulola kuti Yehova azinditsogolera, kwandithandiza kuti ndikhale ndi moyo wosangalala kwambiri ndipo sindimanong’oneza bondo.
Pamene ndinkasonkhana ndi mpingo wa Bromsgrove, ndinakumana ndi mlongo wina wokongola komanso wokonda kutumikira Yehova dzina lake Anne ndipo tinakwatirana mu 1957. Tinkasangalala kuchitira limodzi upainiya wokhazikika, upainiya wapadera, utumiki woyendayenda komanso utumiki wa pa Beteli. Anne wakhala akundithandiza kukhala wosangalala pa moyo wanga wonse.
Mu 1966, tinasangalala titalowa nawo kalasi nambala 42 ya Sukulu ya Giliyadi. Tinatumizidwa ku Malawi, dziko limene limatchedwanso kuti warm heart of Africa chifukwa anthu ake amadziwika kuti ndi okoma mtima komanso amakonda kulandira alendo. Koma sitinkadziwa kuti sitikhalitsa m’dzikolo.
KUTUMIKIRA PA NTHAWI YOVUTA KU MALAWI
Tinafika ku Malawi pa 1 February, 1967. Titaphunzira chinenero cha m’dzikolo kwa mwezi umodzi, tinayamba utumiki woyang’anira chigawo. Tinkayendera galimoto ina yotchedwa Jeep, yomwe anthu ankaganiza kuti ikhoza kuyenda pena paliponse ngakhalenso kuwoloka mitsinje. Koma zimenezi si zinali zoona chifukwa galimotoyi inkangowoloka madzi osazama kwambiri. Nthawi zina tinkakhala m’nyumba za udzu, zomwe zinkafunika kuikidwa pulasitiki kudenga m’nyengo ya mvula. Tinayamba movutikira utumiki wathu waumishonale komabe tinkaukonda.
Mu April, ndinazindikira kuti posakhalitsa tikumana ndi mavuto kuchokera ku boma. Ndinamva zimene pulezidenti wa ku Malawi, Dr. Hastings Banda analankhula pa wailesi. Iye ananena kuti a Mboni za Yehova sankapereka misonkho komanso ankasokoneza pa nkhani za ndale. Komatu zonsezi zinali zabodza. Tinkadziwa kuti nkhani yaikulu inali yoti sitinkalowerera ndale, makamaka kukana kwathu kugula khadi la chipani.
Pofika mu September, tinawerenga munyuzipepala kuti pulezidenti akuti abale athu akuyambitsa mavuto kwina kulikonse. Pamsonkhano wina wandale iye analankhula kuti boma ligamula mwamsanga kuti ntchito ya Mboni za Yehova iletsedwe. Ntchito yathu inaletsedwadi pa 20 October, 1967. Pasanapite nthawi yaitali, apolisi komanso akuluakulu oona za anthu olowa ndi otuluka m’dziko, anabwera kudzatseka ofesi ya nthambi komanso kudzalamula amishonale kuti achoke m’dzikoli.
Titakhala m’ndende masiku atatu tinatumizidwa ku Mauritius dziko lomwe linkalamuliridwa ndi Britain. Komabe akuluakulu a boma sanatilole kuti tikhale kumeneko monga amishonale. Choncho tinatumizidwa kukatumikira ku Rhodesia (panopa ndi Zimbabwe). Titafika, mmodzi wa akuluakulu oona za olowa ndi otuluka m’dzikolo, yemwe anali waukali, anatikaniza kukhala m’dzikolo ponena kuti: “Akuthamangitsani ku Malawi. Sanakuloleninso kukhala ku Mauritius, ndiye mwaona kuti kunoko ndiye kophweka eti?” Anne anayamba kulira. Zinkaoneka kuti aliyense sankatifuna. Pa nthawiyi ndinaganiza zongobwerera kwathu ku England. Pamapeto pake, akuluakulu oona za anthu olowa ndi otuluka m’dziko, anatilola kuti tikagone ku ofesi ya nthambi, koma tsiku lotsatira tikaonekere ku likulu lawo. Tinatopa kwambiri, komabe tinapitiriza kusiya zonse m’manja mwa Yehova. Tsiku lotsatira masana, mosayembekezereka tinapatsidwa chilolezo chokhala m’dzikolo monga alendo. Sindingaiwale mmene ndinamvera pa tsikuli. Ndinatsimikiza kuti Yehova ndi amene ankatitsogolera.
NDINAPATSIDWA UTUMIKI WATSOPANO WOTUMIKIRA ABALE A KU MALAWI NDILI KU ZIMBABWE
Ndili ku ofesi ya nthambi ya ku Zimbabwe, ndinkatumikira m’Dipatimenti ya Utumiki ndipo ndinkathandiza abale a ku Malawi ndi ku Mozambique. Abale a ku Malawi ankazunzidwa kwambiri. Ntchito yanga inkaphatikizapo kumasulira malipoti ochokera kwa oyang’anira madera a ku Malawi. Tsiku lina madzulo ndikumalizitsa lipoti lina, ndinalira kwambiri nditawerenga za nkhanza zimene abale ndi alongo ankakumana nazo.a Koma ndinalimbikitsidwanso chifukwa cha kukhulupirika ndi kupirira kwawo.—2 Akor. 6:4, 5.
Tinkachita zonse zomwe tingathe pothandiza abale omwe anatsala ku Malawi komanso amene anathawira ku Mozambique kuti azipeza mabuku athu. Gulu lomasulira Chichewa, chilankhulo chomwe chimalankhulidwa kwambiri ku Malawi, linasamukira kufamu ya m’bale wina ku Zimbabwe. Mokoma mtima m’baleyo anawamangira malo okhala komanso ofesi. Kumeneko iwo anapitiriza ntchito yawo yofunika, yomasulira mabuku othandiza pophunzira Baibulo.
Tinakonza zoti chaka chilichonse oyang’anira madera a ku Malawi azidzachita nawo msonkhano wachigawo wa Chichewa ku Zimbabwe. Pamsonkhanowu, iwo ankapatsidwa ma autilaini a nkhani a msonkhano wachigawo. Ndipo akamabwerera ku Malawi, iwo ankayesetsa mmene angathere kugawa ma autilainiwo kwa abale. Chaka china atabwera ku Zimbabwe, tinakwanitsa kukonza Sukulu ya Utumiki wa Ufumu n’cholinga chofuna kulimbikitsa oyang’anira madera olimba mtimawa.
Mu February 1975, ndinapita kukayendera abale ndi alongo a ku Malawi omwe anathawira kumakampu a ku Mozambique. Iwo ankatsatira malangizo atsopano a gulu la Yehova kuphatikizapo okhudza kukhala ndi bungwe la akulu. Akulu atsopanowa anakonza zoti pakhale zochita zambiri zokhudza kulambira monga kukamba nkhani za onse, kukambirana lemba la tsiku ndi Nsanja ya Olonda ngakhalenso kuchita misonkhano ikuluikulu. Zinthu pakampupo zinkachitika ngati pamsonkhano wachigawo ndipo panali madipatimenti monga yoyeretsa, kugawa chakudya komanso chitetezo. Abale okhulupirikawa anachita zambiri mothandizidwa ndi Yehova ndipo zimenezi zinandilimbikitsa kwambiri.
Chakumapeto kwa zaka za m’ma 1970, ofesi ya nthambi ku Zambia inayamba kuyang’anira ntchito za ku Malawi. Komabe ndinkaganizira kwambiri abale a ku Malawi komanso kuwapempherera, monganso mmene ambiri ankachitira. Popeza ndinali m’Komiti ya Nthambi ku Zimbabwe, nthawi zambiri ndinkakumana ndi oimira likulu lathu limodzi ndi abale a ku Malawi, South Africa ndi Zambia. Nthawi zonse tikamakambirana funso linkakhala lakuti, “Kodi tingachite zotani kuti tithandize abale a ku Malawi?”
M’kupita kwa nthawi, abale anasiya kuzunzidwa kwambiri. A Mboni omwe anathawa m’dzikoli anayamba kubwerera ku Malawi pomwe ena omwe anatsala anayamba kupeza mpumulo ku nkhanza zomwe ankachitiridwa. Mayiko oyandikana nawo anayamba kuvomereza a Mboni kuti azilalikira komanso kuchita misonkhano. Nalonso dziko la Mozambique linachita zimenezi m’chaka cha 1991. Koma tinkafunsa kuti, ‘Kodi a Mboni za Yehova adzamasulidwa liti ku Malawi?’
KUBWERERA KU MALAWI
Zinthu pa nkhani ya ndale zinayamba kusintha ku Malawi ndipo mu 1993, boma linasiya kuletsa ntchito ya Mboni za Yehova. Pasanapite nthawi yaitali ndinkacheza ndi mmishonale wina yemwe anandifunsa kuti, “Kodi mubwereranso ku Malawi?” Pa nthawiyi ndinali ndi zaka 59 ndiye ndinamuyankha kuti, “Ayi ndakula kwambiri.” Koma tsiku lomwelo tinalandira uthenga wochokera ku Bungwe Lolamulira wotiuza kuti tibwerere ku Malawi.
Tinkakonda kutumikira ku Zimbabwe choncho zinali zovuta kwa ife kuti tichoke. Tinali titakhazikika komanso titapeza anzathu abwino kwambiri. Mokoma mtima, Bungwe Lolamulira linatiuza kuti tinali ndi ufulu wosankha kupita ku Malawi kapena kukhalabe ku Zimbabwe komweko. Choncho tikanatha kusankha kuchita zomwe tinkafuna. Koma ndinakumbukira zimene Abulahamu ndi Sara anachita atakalamba pochoka kwawo n’kusiya moyo wabwino umene ankakhala chifukwa chofuna kumvera malangizo a Yehova.—Gen. 12:1-5.
Tinaganiza zotsatira malangizo a gulu la Yehova, n’kubwerera ku Malawi pa 1 February 1995, patatha zaka 28 kuchokera pamene tinafika m’dzikoli koyamba. Panakhazikitsidwa Komiti ya Nthambi yomwe munali ine ndi abale ena awiri. Ndipo mwamsanga tinayamba kukhazikitsanso ntchito ya Mboni za Yehova.
YEHOVA NDI AMENE AMAKULITSA
N’zosangalatsa kuona Yehova akukulitsa ntchito yathu m’Malawi. Chiwerengero cha ofalitsa chinawonjezeka kwambiri kuchoka pa pafupifupi 30,000 mu 1993 kufika pa ofalitsa oposa 42,000 mu 1998.b Bungwe Lolamulira linavomereza kuti pamangidwe ofesi ya nthambi yatsopano kuti izisamalira ofalitsa omwe ankawonjezerekawa. Tinagula malo okwana maekala 30 ku Lilongwe ndipo ndinasankhidwa kuti ndikhale m’komiti yoyang’anira zomangamanga.
M’bale Guy Pierce wa m’Bungwe Lolamulira ndi amene anakamba nkhani yopereka ofesi ya nthambiyi mu May 2001. A Mboni oposa 2,000 a m’dzikoli anaitanidwa kumwambowu ndipo ambiri mwa iwo anali oti anabatizidwa zaka zoposa 40 m’mbuyomo. Abale ndi alongo okhulupirikawa, anapirira kuzunzidwa pa nthawi imene ntchito yathu inali yoletsedwa. Iwo anali osauka koma anali ndi chikhulupiriro komanso anali pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Yehova. Pa nthawiyi, iwo anasangalala kuona malo pa ofesi ya nthambi yatsopanoyi. Kulikonse komwe ankapita akamaona malo, ankaimba nyimbo za Ufumu molandizana mawu zomwe zinachititsa kuti mwambowo ukhale wosaiwalika komanso wosangalatsa kwa ine. Umenewu unali umboni wosatsutsika wakuti Yehova amadalitsa anthu omwe amapirira mayesero mokhulupirika.
Ntchito yomanga ofesi ya nthambi itatha, ndinkasangalala kupatsidwa mwayi wopereka kwa Yehova Nyumba za Ufumu. Mipingo ya ku Malawi inapeza mwayi wokhala ndi malo olambirira kudzera mupulogalamu yomanga Nyumba za Ufumu m’mayiko omwe abale sangakwanitse. Kale mipingo ina inkasonkhana m’zisakasa zomangidwa ndi mitengo ya bulugamu. Ankafolera ndi udzu komanso kumanga mabenchi ataliatali adothi okhalira. Tsopano abale amagwira ntchito mwakhama poumba njerwa n’kuziwotcha ndipo amamangira malo okongola ochitira misonkhano. Koma iwo amakondabe mabenchi chifukwa pabenchi pamatha kukhala anthu ambiri.
Ndinkasangalalanso kuona Yehova akuthandiza anthu kukhala olimba mwauzimu. Ndinkachita chidwi kwambiri makamaka ndi achinyamata a ku Africa omwe mofunitsitsa ankadzipereka pa utumiki wawo ndipo ankapindula ndi maphunziro amene gulu la Yehova limapereka. Zimenezi zinkachititsa kuti azipatsidwa maudindo ambiri pa Beteli komanso kumipingo. Mipingo inkalimbikitsidwa ndi oyang’anira madera omwe anali atangoikidwa kumene ndipo ambiri mwa iwo anali okwatira. Mabanjawa anasankha kumachita zambiri potumikira Yehova podzimana kuti asakhale ndi ana ngakhale kuti chikhalidwe ndi makolo awo ankawakakamiza.
NDIMAKHUTIRA NDI ZIMENE NDINASANKHA
Pambuyo potumikira ku Africa kwa zaka 52, ndinayamba kukumana ndi mavuto okhudza thanzi langa. Bungwe Lolamulira linavomereza zimene Komiti ya Nthambi inasankha zoti ndibwerere n’kumakatumikira ku Britain. Tinakhumudwa chifukwa chosiya utumiki womwe tinkaukonda komabe banja la Beteli la ku Britain likutisamalira bwino kwambiri m’zaka zathu zaukalamba.
Ndimakhulupirira kuti ndinasankha bwino kwambiri kulola kuti Yehova azinditsogolera pa moyo wanga. Ndikanadalira nzeru zanga n’kupitiriza ntchito yomwe ndinkagwira, moyo wanga sukanakhala mmene ulilimu. Yehova nthawi zonse ankadziwa zimene ndinkafunikira kuti ‘awongole njira zanga.’ (Miy. 3:5, 6) Monga wachinyamata, ndinkasangalala kuphunzira zambiri zokhudza ntchito yomwe ndinkagwira pakampani yaikulu ija. Koma gulu la Yehova linandipatsa ntchito yabwino kwambiri yomwe ndimakhutira nayo. Kwa ine, kutumikira Yehova kwandithandiza ndipo kupitirizabe kundithandiza kukhala ndi moyo wabwino kwambiri.
a Mbiri ya Mboni za Yehova ku Malawi inafalitsidwa mu Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la Chingelezi la 1999 tsamba 148 mpaka 223 komanso kabuku kakuti Mboni za Yehova m’Malawi.
b Panopa ku Malawi kuli ofalitsa oposa 100,000.