NKHANI YOPHUNZIRA 42
Odala Ndi Anthu Okhulupirika Kwa Yehova
“Odala ndi anthu osalakwitsa kanthu . . . , anthu amene akutsatira chilamulo cha Yehova.”—SAL. 119:1.
NYIMBO NA. 124 Tizikhulupirika Nthawi Zonse
ZIMENE TIPHUNZIREa
1-2. (a) Kodi maboma ena achita zotani polimbana ndi anthu a Yehova, nanga anthu a Yehovawo amatani? (b) N’chifukwa chiyani tingakhalebe osangalala ngakhale pamene tikuzunzidwa? (Fotokozani chithunzi chapachikuto.)
PANOPA ntchito yathu ndi yoletsedwa m’mayiko oposa 30 padziko lonse. M’mayiko ena mwa amenewa, olamulira anaika m’ndende abale ndi alongo athu. Kodi iwo analakwa chiyani? Palibe, Yehova samaona kuti iwo analakwitsa chilichonse. Zimene iwo amachita ndi kuwerenga ndi kuphunzira Baibulo, kuuza ena zimene amakhulupirira komanso kusonkhana ndi Akhristu anzawo. Iwo amakananso kulowerera ndale. Ngakhale kuti atumiki okhulupirika a Mulunguwa amatsutsidwa chonchi, iwo amapitirizabe kukhala okhulupirika zomwe zimasonyeza kuti iwo ndi odziperekab kwambiri kwa Yehova. Kuchita zimenezi kumawathandiza kukhala osangalala.
2 N’kutheka kuti mwaonapo zithunzi za ena mwa a Mboni olimba mtimawa ndipo mumaona kuti nkhope zawo ndi zosangalala. Iwo amasangalala chifukwa amadziwa kuti Yehova akusangalala nawo chifukwa chokhalabe okhulupirika kwa iye. (1 Mbiri 29:17a) Yesu anati: “Odala ndi anthu amene akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo, . . . Kondwerani, dumphani ndi chimwemwe, chifukwa mphoto yanu ndi yaikulu.”—Mat. 5:10-12.
CHITSANZO CHOMWE TINGATENGERE
3. Mogwirizana ndi zimene zili pa Machitidwe 4:19, 20, kodi atumwi anatani pamene ankazunzidwa, nanga n’chifukwa chiyani anachita zimenezo?
3 Zomwe abale ndi alongo athu akukumana nazo ndi zimenenso atumwi anapirira pomwe ankazunzidwa chifukwa cholalikira za Yesu. Mobwerezabwereza oweruza a khoti lalikulu la Ayuda ‘anawalamula kuti asiye kulankhula m’dzina la Yesu.’ (Mac. 4:18; 5:27, 28, 40) Ndiye kodi atumwiwo anatani? (Werengani Machitidwe 4:19, 20.) Iwo ankadziwa kuti yemwe ‘anawalamula kuti alalikire kwa anthu ndi kupereka umboni wokwanira’ wonena za Khristu ali ndi udindo waukulu kuposa oweruzawo. (Mac. 10:42) Choncho polankhula m’malo mwa atumwiwo, Petulo ndi Yohane molimba mtima ananena kuti apitiriza kumvera Mulungu osati oweruzawo ndipo sasiya kulankhula zokhudza Yesu. Apa zinali ngati iwo akufunsa oweruzawo kuti, ‘Kodi mukuganiza kuti anthu akuyenera kumvera inu kuposa Mulungu?’
4. Monga mmene lemba la Machitidwe 5:27-29 likusonyezera, kodi atumwi anapereka chitsanzo chotani kwa Akhristu onse oona, nanga tingawatsanzire bwanji?
4 Atumwi anapereka chitsanzo chabwino chimene Akhristu onse oona akutsatirabe mpaka pano chomwe ndi “kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.” (Werengani Machitidwe 5:27-29.) Atamenyedwa chifukwa chokhalabe okhulupirika, atumwiwo anachoka pamaso pakhoti lalikulu la Ayudawo “ali osangalala chifukwa chakuti Mulungu anawaona kuti ndi oyenera kuchitiridwa chipongwe chifukwa cha dzina la Yesu” ndipo anapitiriza kulalikira.—Mac. 5:40-42.
5. Kodi ndi mafunso ati ofunika kupeza mayankho ake?
5 Chitsanzo cha atumwiwa chimachititsa kuti tikhalebe ndi mafunso ena. Mwachitsanzo, kodi zikanatheka bwanji kuti iwo azimvera Mulungu osati anthu, pa nthawi yofananayo n’kumamvera lamulo la m’Malemba lakuti, “aliyense azimvera olamulira akuluakulu?” (Aroma 13:1) Kodi tingatani kuti “tizimvera maboma ndiponso olamulira,” monga mmene mtumwi Paulo ananenera, koma n’kukhalabe okhulupirika kwa Mulungu monga Wolamulira wathu wamkulu?—Tito 3:1.
“OLAMULIRA AKULUAKULU”
6. (a) Kodi “olamulira akuluakulu” otchulidwa pa Aroma 13:1 ndi ndani, nanga tiyenera kumachita nawo bwanji zinthu? (b) Kodi ndi mfundo yoona iti imene imakhudza olamulira onse?
6 Werengani Aroma 13:1. Pavesili mawu akuti “olamulira akuluakulu” akunena za anthu omwe amalamulira maboma. Akhristu amayenera kumvera olamulira amenewa. Iwo amathandiza kuti m’dziko musakhale chisokonezo, amaonetsetsa kuti anthu akutsatira malamulo komanso nthawi zina amateteza anthu a Yehova. (Chiv. 12:16) Choncho timalamulidwa kuti tizipereka misonkho, tiziwaopa komanso tiziwapatsa ulemu umene amafuna. (Aroma 13:7) Komabe olamulirawa ali ndi mphamvu chifukwa chakuti Yehova wawalola kuti akhale nazo. Yesu anamveketsa bwino mfundo imeneyi pamene ankafunsidwa mafunso ndi bwanamkubwa wa Chiroma, Pontiyo Pilato. Pamene Pilato ananena kuti ali ndi mphamvu zotha kumumasula kapena kumupereka kuti aphedwe, Yesu anamuuza kuti: “Simukanakhala ndi mphamvu iliyonse pa ine mukanapanda kupatsidwa kuchokera kumwamba.” (Yoh. 19:11) Monga mmene zinalili ndi Pilato, mphamvu za olamulira komanso andale onse masiku ano zili ndi malire.
7. Kodi ndi pa zochitika ziti zimene sitikuyenera kumvera olamulira, nanga olamulirawa ayenera kudziwa chiyani?
7 Akhristu amamvera maboma ngati malamulo awo sakutsutsana ndi malamulo a Mulungu. Koma sitingamvere anthu ngati akutipempha kuchita zinthu zimene Mulungu amadana nazo kapena ngati akutiletsa kuchita zimene Mulungu amafuna. Mwachitsanzo, iwo angamafune kuti achinyamata azilowa usilikali n’kumamenya nawo nkhondo.c Kapenanso angaletse Baibulo ndi mabuku athu ofotokoza Baibulo komanso kutiletsa kulalikira ndi kuchita misonkhano. Olamulira akamagwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika, monga ngati kuzunza otsatira a Khristu, adzayankha kwa Mulungu chifukwa Yehova akuona.—Mlal. 5:8.
8. Kodi pali kusiyana kotani pa mawu akuti “akuluakulu” ndi mawu akuti “wamkulukulu,” nanga kudziwa zimenezi n’kothandiza bwanji?
8 Mawu akuti “akuluakulu” amatanthauza “anthu apamwamba” kapena amene ali ndi “udindo waukulu.” Koma sizimatanthauza kuti anthuwa ndi “apamwamba kwambiri” kapenanso kuti ali ndi “udindo waukulu kwambiri,” chifukwa zimenezi ndi zomwe mawu akuti “wamkulukulu” amatanthauza. Ngakhale kuti maboma amatchulidwa kuti “olamulira akuluakulu”, pali wolamulira wina waudindo waukulu kwambiri yemwe amatchedwa wamkulukulu. Maulendo 4 m’Baibulo, Yehova Mulungu amatchedwa kuti “Wamkulukulu.”—Dan. 7:18, 22, 25, 27.
“WAMKULUKULU”
9. Kodi mneneri Danieli anaona chiyani m’masomphenya?
9 Mneneri Danieli anaona masomphenya omwe amasonyeza bwino kuti Yehova ndi wamkulu kwambiri kuposa olamulira onse. Choyamba Danieli anaona zilombo zazikulu 4, zomwe zikuimira maulamuliro omwe anali amphamvu padziko lonse monga Babulo, Mediya ndi Perisiya, Girisi, Roma komanso ulamuliro wa Britain ndi America, womwe ukulamulira panopa. (Dan. 7:1-3, 17) Kenako Danieli anaona Yehova Mulungu atakhala pampando wachifumu mu khoti lake kumwamba. (Dan. 7:9, 10) Zimene mneneri wokhulupirikayu anaona pambuyo pake, ziyenera kukhala chenjezo kwa olamulira masiku ano.
10. Mogwirizana ndi Danieli 7:13, 14, 27, kodi Yehova anapereka kwa ndani ulamuliro wa dziko lapansi, nanga zimenezi zikutiuza chiyani ponena za iye?
10 Werengani Danieli 7:13, 14, 27. Mulungu anatenga mphamvu zonse ndi ulamuliro womwe maboma anali nawo n’kuzipereka kwa oyenerera komanso amphamvu kwambiri. Ndiye kodi anazipereka kwa ndani? Anazipereka kwa “wina wooneka ngati mwana wa munthu,” Yesu Khristu komanso “oyera a Wamkulukulu,” omwe ndi a 144, 000 amene adzalamulire “mpaka kalekale.” (Dan. 7:18.) N’zoonekeratu kuti Yehova ndiye “Wamkulukulu” chifukwa iye yekha ndi amene ali ndi mphamvu zochita zimenezi.
11. Kodi Danieli analembanso chiyani posonyeza kuti Yehova ndi wamkulu kwambiri kuposa olamulira onse?
11 Zimene Danieli anaona m’masomphenya zikugwirizana kwambiri ndi zimene anali atanena kale. Danieli ananena kuti: “Mulungu wakumwamba amachotsa mafumu ndi kuika mafumu.” Iye analembanso kuti “Wam’mwambamwamba ndiye Wolamulira wa maufumu a anthu, . . iye akafuna kupereka ulamuliro kwa munthu aliyense, amamupatsa.” (Dan. 2:19-21; 4:17) Kodi pali nthawi zimene Yehova anachotsa kapena kuika olamulira? Inde.
12. Perekani chitsanzo chosonyeza mmene kale Yehova anachotsera mafumu m’mipando yawo. (Onani chithunzi.)
12 Yehova wakhala akusonyeza kuti iye ndi wamkulu kwambiri kuposa “olamulira akuluakulu.” Taganizirani zitsanzo zitatu izi. Farao wa ku Iguputo ankagwiritsa ntchito yaukapolo anthu a Yehova ndipo mobwerezabwereza anakana kuwamasula. Koma Mulungu anawamasula ndipo anamiza Farao m’Nyanja Yofiira. (Eks. 14:26-28; Sal. 136:15) Mfumu Belisazara wa ku Babulo anakonza phwando ndipo ‘anadzikweza pamaso pa Ambuye wakumwamba’ komanso ‘anatamanda milungu wamba yasiliva ndi yagolide’ m’malo motamanda Yehova. (Dan. 5:22, 23) Koma Mulungu anatsitsa munthu wodzikwezayu. Iye anaphedwa “usiku womwewo” ndipo ufumu wake unaperekedwa kwa Amedi ndi Aperisiya. (Dan. 5:28, 30, 31) Mfumu Herode Agiripa I wa ku Palesitina anapha mtumwi Yakobo ndipo kenako anaika m’ndende mtumwi Petulo n’cholinga choti amuphenso. Koma Yehova anamulepheretsa kukwaniritsa zolinga zakezi. “Mngelo wa Yehova anamukantha,” ndipo anafa.—Mac. 12:1-5, 21-23.
13. Perekani chitsanzo cha mmene Yehova anagonjetsera olamulira omwe anachita mgwirizano.
13 Yehova anasonyezanso kuti ndi wamkulu kwambiri kuposa olamulira omwe anachita mgwirizano. Iye anamenyera nkhondo Aisiraeli ndipo anawathandiza kuti awononge mgwirizano wa mafumu 31 a Chikanani komanso kuti agonjetse mbali yaikulu ya Dziko Lolonjezedwa. (Yos. 11:4-6, 20; 12:1, 7, 24) Yehova anagonjetsanso Mfumu Benihadadi limodzi ndi olamulira ena 32 a Asiriya omwe ankamenyana ndi Aisiraeli.—1 Maf. 20:1, 26-29.
14-15. (a) Kodi Mfumu Nebukadinezara ndi Dariyo ananena zotani zokhudza ulamuliro wa Yehova? (b) Kodi wolemba masalimo ananena chiyani zokhudza Yehova ndi anthu ake?
14 Mobwerezabwereza Yehova wakhala akusonyeza kuti iye ndi Wamkulukulu. Mfumu Nebukadinezara wa ku Babulo atadzikweza chifukwa chokhala ndi ‘mphamvu komanso ulemerero waukulu,’ m’malo movomereza kuti Yehova ndi woyenera kutamandidwa, Mulungu anamuchititsa misala. Atachira, Nebukadinezara ‘anatamanda Wam’mwambamwamba’ ndipo anavomereza kuti “ulamuliro wa [Yehova] udzakhalapo mpaka kalekale.” Anawonjezeranso kuti: “Palibe aliyense amene angaletse dzanja lake.” (Dan. 4:30, 33-35) Pambuyo poti Danieli wakumana ndi mayesero komanso kuti Yehova wamupulumutsa m’dzenje la mikango, Mfumu Dariyo inalamula kuti: “Anthu azinjenjemera ndi kuchita mantha pamaso pa Mulungu wa Danieli. Pakuti iye ndi Mulungu wamoyo, amene adzakhalapo mpaka kalekale ndipo ufumu wake sudzawonongeka komanso ulamuliro wake udzakhalapo kwamuyaya.”—Dan. 6:7-10, 19-22, 26, 27.
15 Wolemba masalimo anati: “Yehova wasokoneza zolinga za anthu a mitundu ina. Walepheretsa maganizo a mitundu ya anthu.” Anawonjezera kuti : “Wodala ndi mtundu umene Mulungu wawo ndi Yehova, anthu amene iye wawasankha kukhala cholowa chake.” (Sal. 33:10, 12) Tilitu ndi zifukwa zabwino kwambiri zotichititsa kukhalabe okhulupirika kwa Yehova.
NKHONDO YOMALIZA
16. Kodi sitikayikira chiyani ponena za “chisautso chachikulu,” nanga n’chifukwa chiyani? (Onani chithunzi.)
16 Tawerenga zimene Yehova wakhala akuchita m’mbuyomu. Ndiye tiyembekezere zotani m’tsogolomu? Sitikukayikira kuti Yehova adzapulumutsa atumiki ake okhulupirika pa nthawi ya “chisautso chachikulu.” (Mat. 24:21; Dan. 12:1) Iye adzachita zimenezi pamene mgwirizano wa mayiko wotchedwa Gogi wa ku Magogi udzaukire atumiki a Yehova okhulupirika padziko lonse. Ngakhale mgwirizanowo utadzaphatikizapo mayiko onse 193, omwe ali m’bungwe la United Nations, iwo sadzatha kulimbana ndi Wamkulukulu ndi gulu lake lakumwamba. Yehova akulonjeza kuti: “Ndidzadzilemekeza, kudziyeretsa ndi kuchititsa kuti mitundu yambiri ya anthu indidziwe, ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”—Ezek. 38:14-16, 23; Sal. 46:10.
17. Kodi Baibulo limati n’chiyani chidzachitikire mafumu a dziko lapansi komanso anthu amene amakhalabe okhulupirika kwa Yehova?
17 Kuukira kwa Gogi kudzayambitsa nkhondo ya Aramagedo, pomwe Yehova adzawononge “mafumu a dziko lonse lapansi.” (Chiv. 16:14, 16; 19:19-21) Mosiyana ndi zimenezi, “owongoka mtima ndi amene adzakhale m’dziko lapansi, ndipo opanda cholakwa ndi amene adzatsalemo.”—Miy. 2:21.
TIYENERA KUKHALABE OKHULUPIRIKA
18. Kodi Akhristu ambiri oona akhala akufunitsitsa kuchita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani? (Danieli 3:28)
18 Kwa zaka zambiri Akhristu akhala akulolera kuvutika komanso kuika moyo wawo pangozi chifukwa chokonda Yehova monga Wolamulira wawo wamkulu. Iwo ndi okhulupirika ngati Aheberi atatu omwe anapulumutsidwa mung’anjo yoyaka moto chifukwa chokhala okhulupirika kwa Wolamulira Wamkulukulu.—Werengani Danieli 3:28.
19. Kodi Yehova adzaweruza anthu ake potengera chiyani, nanga ifeyo tiyenera kuchita chiyani?
19 Posonyeza kufunika kokhalabe wokhulupirika kwa Mulungu, wolemba masalimo Davide anati: “Yehova adzapereka chigamulo ku mitundu ya anthu. Ndiweruzeni inu Yehova, mogwirizana ndi chilungamo changa, komanso mogwirizana ndi mtima wanga wosagawanika.” (Sal. 7:8.) Iye analembanso kuti: “Mtima wanga wosagawanika ndiponso wowongoka unditeteze.” (Sal. 25:21.) Chinthu chofunika kwambiri ndi kupitirizabe kukhala okhulupirika kwa Yehova kaya tikumane ndi zotani pa moyo wathu. Tikatero, tidzamva ngati mmene anamvera wolemba masalimo yemwe analemba kuti: “Odala ndi anthu osalakwitsa kanthu, . . . anthu amene akutsatira chilamulo cha Yehova.”—Sal. 119:1.
NYIMBO NA. 122 Khalani Olimba Komanso Osasunthika
a Baibulo limalimbikitsa Akhristu kuti azimvera olamulira akuluakulu omwe ndi maboma a m’dzikoli. Koma maboma ena amachita kuonetseratu kuti amatsutsa Yehova ndi atumiki ake. Ndiye kodi tingatani kuti tizimvera olamulirawa koma n’kumakhalabe okhulupirika kwa Yehova?
b TANTHAUZO LA MAWU ENA: Kukhalabe okhulupirika kwa Yehova kumatanthauza kukhalabe okhulupirika kwa iye ndi ulamuliro wake ngakhale pamene tikuyesedwa.
c Onani nkhani yakuti, “N’chifukwa Chiyani Masiku Ano Sitimenya Nkhondo Ngati Mmene Ankachitira Aisiraeli?” yomwe ili m’magaziniyi.