NKHANI YOPHUNZIRA 2
“Sandulikani mwa Kusintha Maganizo Anu”
“Sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.”—AROMA 12:2.
NYIMBO NA. 88 Ndidziwitseni Njira Zanu
ZIMENE TIPHUNZIREa
1-2. Kodi tiyenera kupitiriza kuchita chiyani pambuyo pobatizidwa? Fotokozani.
KODI mumakonza kangati m’nyumba mwanu? N’kutheka kuti pa nthawi yoyamba pamene munkasamukiramo, munakonza bwino paliponse. Koma kodi n’chiyani chingachitike pambuyo pake ngati mutasiya kukonzamo? Monga mukudziwira, mungadenso mwamsanga ndi fumbi. Kuti m’nyumbamo muzikhalebe mwaukhondo, mumafunika kukonzamo pafupipafupi.
2 Pamafunikanso khama lofanana ndi limeneli pa zimene timaganiza komanso khalidwe lathu. N’zoona kuti tisanabatizidwe, tinayesetsa kusintha moyo wathu kuti “tidziyeretse ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi kapena mzimu.” (2 Akor. 7:1) Komabe panopa tifunika kutsatira malangizo a mtumwi Paulo akuti tipitirize ‘kukhala atsopano.’ (Aef. 4:23) N’chifukwa chiyani tiyenera kupitirizabe kuchita khama? Chifukwa kaganizidwe ndi zochita za anthu a m’dzikoli zingatidetse mofulumira. Kuti zimenezi zisatichitikire komanso kuti tipitirize kukhala ovomerezeka pamaso pa Yehova, nthawi zonse tiyenera kumafufuza zimene timaganiza, khalidwe lathu komanso zimene timalakalaka.
PITIRIZANI “KUSINTHA MAGANIZO ANU”
3. Kodi “kusintha maganizo anu” kumatanthauza chiyani? (Aroma 12:2)
3 Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tisinthe maganizo athu? (Werengani Aroma 12:2.) Mawu a Chigiriki omwe anamasuliridwa kuti “kusintha maganizo anu” angamasuliridwenso kuti “kukonzanso maganizo anu.” Choncho, zimenezi sizikutanthauza kuti tizingochita ntchito zabwino zochepa chabe. M’malomwake, tiyenera kumafufuza umunthu wathu wamkati komanso kumasintha pamene pakufunikira kutero, n’cholinga choti zochita zathu zizigwirizana kwambiri ndi mfundo za Yehova. Tiyenera kuchita zimenezi, osati kamodzi kokha koma nthawi zonse.
4. Kodi tingatani kuti tipewe kutengera maganizo ndi zochita za anthu a m’dzikoli?
4 Tikadzakhala angwiro, nthawi zonse tizidzachita zinthu zosangalatsa Yehova. Koma panopa tiyenera kuchita khama kuti tizichita zomusangalatsa. Taonani kugwirizana komwe kulipo pakati pa kusintha maganizo ndi kuzindikira chifuniro cha Mulungu, monga mmene Paulo analembera pa Aroma 12:2. M’malo mongotengera zochita ndi kaganizidwe ka anthu a m’dzikoli, choyamba tiyenera kudzifufuza ngati zolinga zathu komanso zimene timasankha zimatsogoleredwa ndi maganizo a Mulungu osati a dzikoli.
5. Kodi tingatani kuti tizifufuza maganizo athu pa nkhani ya kuyandikira kwa tsiku la Yehova? (Onani chithunzi.)
5 Taganizirani izi: Yehova amafuna kuti ‘tizikumbukira nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku lake.’ (2 Pet. 3:12) Dzifunseni kuti: ‘Kodi zochita zanga zimasonyeza kuti ndikuzindikira kuti dziko loipali liwonongedwa posachedwapa? Kodi zimene ndimasankha pa nkhani ya maphunziro komanso ntchito zimasonyeza kuti ndimaona kutumikira Yehova kukhala kofunika kwambiri pa moyo wanga? Kodi ndimakhulupirira kuti Yehova adzandipatsa zofunikira ineyo ndi banja langa kapena nthawi zonse ndimadera nkhawa za zinthu zakuthupi?’ Taganizirani mmene Yehova amasangalalira akationa tikuyesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi chifuniro chake.—Mat. 6:25-27, 33; Afil. 4:12, 13.
6. Kodi tiyenera kupitirizabe kuchita chiyani?
6 Nthawi ndi nthawi, tiyenera kumafufuza zimene timaganiza kenako n’kumasintha pamene pakufunikira kutero. Paulo anauza Akhristu a ku Korinto kuti: “Pitirizani kudziyesa kuti muone ngati mukadali olimba m’chikhulupiriro. Pitirizani kudziyesa kuti mudziwe kuti ndinu munthu wotani.” (2 Akor. 13:5) Kukhala “olimba m’chikhulupiriro,” kumaphatikizapo zambiri osati kumangopezeka pamisonkhano kapena kugwira nawo ntchito yolalikira nthawi zonse. Kumaphatikizaponso maganizo, zolakalaka ndi zolinga zathu. Choncho tiyenera kupitiriza kusintha maganizo athu powerenga Mawu a Mulungu kuti tiziphunzira mmene amaganizira, kenako n’kumachita zomwe tingathe kuti zochita zathu zizigwirizana ndi chifuniro cha Yehova.—1 Akor. 2:14-16.
‘VALANI UMUNTHU WATSOPANO’
7. Mogwirizana ndi Aefeso 4:31, 32, n’chiyaninso chomwe tiyenera kuchita, nanga n’chifukwa chiyani kuchita zimenezi kungakhale kovuta?
7 Werengani Aefeso 4:31, 32. Kuwonjezera pa kusintha mmene timaganizira, tiyeneranso “kuvala umunthu watsopano.” (Aef. 4:24) Zimenezitu zimafunika kuchita khama. Mwa zina, tiyenera kuyesetsa kuti tisiye makhalidwe oipa monga kuwawidwa mtima kwa njiru, kupsa mtima komanso mkwiyo. N’chifukwa chiyani kuchita zimenezi kungakhale kovuta? Chifukwa makhalidwe ena oipa amakhala kuti anazika mizu. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti anthu ena ‘amakonda kukwiya’ komanso ‘amakonda kupsa mtima.’ (Miy. 29:22) Kusintha makhalidwe oipa omwe tinazolowera kumafuna kupitirizabe kuchita khama ngakhale pambuyo pobatizidwa, monga mmene tionere mu chitsanzo chotsatirachi.
8-9. Kodi chitsanzo cha Stephen chikusonyeza bwanji kufunika kopitirizabe kuvula umunthu wakale?
8 M’bale wina dzina lake Stephen, ankavutika kulamulira mkwiyo wake. Iye anati: “Nthawi zina zinkandivutabe kuugwira mtima ngakhale pambuyo pobatizidwa. Mwachitsanzo, tsiku lina ndikulalikira kunyumba ndi nyumba, mbava inaba wailesi m’galimoto mwanga ndipo ndinaithamangitsa. Nditatsala pang’ono kuigwira, inaponyera pansi wailesiyo n’kupitiriza kuthawa. Nditafotokozera anzanga amene ndinkalalikira nawo kuti ndalanditsa wailesi yomwe inabedwa, mkulu wa mumpingo mwathu anandifunsa kuti, ‘Stephen, mbavayo ukanaigwira ukanaitani?’ Funso limeneli linandipangitsa kuti ndiganize mofatsa komanso kuti ndiziyesetsa kumachita zinthu mwamtendere.”b
9 Monga mmene chitsanzo cha Stephen chikusonyezera, mosayembekezereka tingapezeke kuti tachitanso khalidwe linalake loipa lomwe timaganiza kuti tinalisiya. Ngati zimenezi zitakuchitikirani, musamataye mtima kapenanso kumaganiza kuti mwalephera. Ngakhale mtumwi Paulo anavomereza kuti: “Pamene ndikufuna kuchita chinthu chabwino, choipa chimakhala chili ndi ine.” (Aroma 7:21-23) Popeza kuti Akhristu onse si angwiro, amafunika kulimbana ndi makhalidwe oipa, omwe nthawi ndi nthawi amabwera ngati mmene zimakhalira ndi fumbi m’nyumba. Timafunika kuchita khama kuti tikhalebe oyera. Kodi tingachite bwanji zimenezi?
10. Kodi tingatani kuti tisiye makhalidwe oipa? (1 Yohane 5:14, 15)
10 Muzipemphera kwa Yehova za khalidwe loipa lomwe mukulimbana nalo ndipo muzikhulupirira kuti akuyankhani komanso kukuthandizani. (Werengani 1 Yohane 5:14, 15.) Ngakhale kuti Yehova sangachotse khalidwelo mozizwitsa, adzakupatsani mphamvu kuti mulisiye. (1 Pet. 5:10) Muzichita mogwirizana ndi mapemphero anu poyesetsa kusachita zinthu zomwe zingakupangitseni kuyambiranso kusonyeza umunthu wakale. Mwachitsanzo, muzisamala kuti musamaonere mafilimu, mapulogalamu a pa TV kapena kuwerenga nkhani zomwe zimachititsa makhalidwe omwe mukufuna kusiya kuoneka ngati abwinobwino. Komanso musamangokhalira kuganizira zinthu zoipa.—Afil. 4:8; Akol. 3:2.
11. Kodi tingachite zinthu ziti kuti tipitirize kuvala umunthu watsopano?
11 Ngakhale kuti munavula umunthu wakale, n’zofunikanso kuti muvale watsopano. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Muzikhala ndi cholinga choti muzitsanzira Yehova pamene mukuphunzira zokhudza makhalidwe ake. (Aef. 5:1, 2) Mwachitsanzo, mukamawerenga nkhani ya m’Baibulo yomwe imasonyeza kuti Yehova amakhululuka, muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndimakhululukira ena?’ Mukamawerenga nkhani yosonyeza kuti Yehova amachitira chifundo anthu omwe akukumana ndi mavuto, muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ndimachitira chifundo Akhristu anzanga omwe akuvutika ndipo ndimasonyeza zimenezi mwa zochita zanga?’ Pitirizani kusintha maganizo anu pamene mukuvala umunthu watsopano ndipo muzidzilezera mtima mukamachita zimenezi.
12. Kodi Stephen anaona bwanji kuti Baibulo lili ndi mphamvu zotha kusintha munthu?
12 Stephen yemwe tamutchula kale uja, anaona kuti pang’ono ndi pang’ono anayamba kukwanitsa kuvala umunthu watsopano. Iye anati: “Kuyambira nthawi imene ndinabatizidwa, ndimakumanabe ndi zinthu zina zimene zingandipangitse kuti ndisaugwire mtima. Anthu akandiputa ndimangochokapo kuopera kuti ndingachite zachiwawa. Mkazi wanga komanso anthu ena ambiri amandiyamikira chifukwa choti ndimayesetsa kuugwira mtima. Moti ndekhanso sindimvetsa mmene ndinasinthira. Ndimaona kuti sindinasinthe chifukwa cha nzeru zanga koma chifukwa chakuti Baibulo lili ndi mphamvu zotha kusintha munthu.”
PITIRIZANI KULIMBANA NDI ZILAKOLAKO ZOIPA
13. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizilakalaka zinthu zoyenera? (Agalatiya 5:16)
13 Werengani Agalatiya 5:16. Pofuna kutithandiza kuti tizichita zoyenera, Yehova mowolowa manja amatipatsa mzimu wake woyera. Tikamaphunzira Mawu a Mulungu, mzimu woyera umagwira bwino ntchito pa moyo wathu. Timalandiranso mzimu woyera tikapezeka pamisonkhano. Pamisonkhanoyi timacheza ndi abale ndi alongo omwe mofanana ndi ifeyo, akuyesetsa kuti azichita zoyenera ndipo zimenezi ndi zolimbikitsa. (Aheb. 10:24, 25; 13:7) Tikamapemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima komanso kumuchonderera kuti atithandize kusiya khalidwe linalake, iye adzatipatsa mzimu wake woyera kuti tipitirize kulimbana ndi khalidwelo. Ngakhale kuti izi sizingachititse kuti tisiye kulakalaka zinthu zoipa, komabe zingatithandize kuti tisachite zoipazo. Monga mmene lemba la Agalatiya 5:16 limanenera, anthu amene amayenda mwa mzimu, ‘sangatsatire chilakolako cha thupi.’
14. N’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kumalakalaka zinthu zoyenera?
14 Tikayamba kuchita zinthu zokhudza kulambira nthawi zonse, tiziyesetsa kuti tisasiye kuzichita ndipo tizipitiriza kulakalaka zinthu zabwino. Chifukwa chiyani? Chifukwa tili ndi mdani yemwe amativutitsa nthawi zonse. Mdani ameneyu ndi mtima wofuna kuchita zoipa. Ngakhale pambuyo pobatizidwa, tingazindikire kuti tikumakopeka ndi zinthu zoipa monga juga, kuledzera kapena kuonera zolaula. (Aef. 5:3, 4) M’bale wina wachinyamata anavomereza kuti: “Chinthu chimodzi chomwe chakhala chikundivutitsa kwambiri ndi mtima wolakalaka amuna anzanga. Ndinkaona ngati zimenezi zingochitika kwa kanthawi koma nthawi zina ndimavutikabe ndi chilakolako chimenechi.” Kodi mungatani ngati inunso mumavutika kwambiri ndi chilakolako choipa?
15. N’chifukwa chiyani n’zolimbikitsa kudziwa kuti ‘anthu enanso’ amavutika ndi zilakolako zoipa? (Onani chithunzi.)
15 Ngati mukulimbana ndi chilakolako chinachake choipa chomwe ndi champhamvu, muzikumbukira kuti zimenezi sizikuchitikira inu nokha. Baibulo limati: “Palibe mayesero amene mwakumana nawo osiyana ndi amene amagwera anthu ena.” (1 Akor. 10:13a) Baibulo lina linamasulira vesili kuti: “Palibe mayesero amene mwakumana nawo omwe ndi achilendo.” Mawuwa ankapita kwa Akhristu a ku Korinto, amuna ndi akazi omwe. Ena mwa iwo poyamba anali achigololo, ogonana ndi amuna kapena akazi anzawo ndiponso zidakwa. (1 Akor. 6:9-11) Kodi mukuganiza kuti pambuyo pobatizidwa, iwo sankavutikanso ndi zilakolako zoipa? Ayi, ndithu. N’zoona kuti anali odzozedwa koma sanali angwiro. N’zosakayikitsa kuti nthawi ndi nthawi ankalimbanabe ndi zilakolako zoipazi. Izitu ziyenera kutilimbikitsa chifukwa zikusonyeza kuti chilakolako choipa chilichonse chimene mukulimbana nacho, winawake anakwanitsa kuchigonjetsa. Choncho mungathe kukhalabe “olimba m’chikhulupiriro . . . podziwa kuti anzanunso m’gulu lonse la abale . . . akukumana ndi masautso ngati omwewo.”—1 Pet. 5:9.
16. Kodi ndi msampha uti umene tiyenera kupewa, nanga n’chifukwa chiyani?
16 Muzipewa msampha woganiza kuti palibe amene angamvetse vuto linalake lomwe mukulimbana nalo. Maganizo amenewa angakuchititseni kutaya mtima n’kumaona kuti simungathenso kulimbana ndi zilakolako zoipa. Koma Baibulo limapereka malangizo akuti: “Mulungu ndi wokhulupirika ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapirire, koma pamene mukukumana ndi mayeserowo iye adzapereka njira yopulumukira kuti muthe kuwapirira.” (1 Akor. 10:13b) Choncho ngakhale kuti timalimbana ndi chilakolako chinachake choipa, tingathe kupirira. Mothandizidwa ndi Yehova, tingathe kupewa kutsatira chilakolakocho.
17. Ngakhale kuti sitingapeweretu kulakalaka zinthu zoipa, kodi tingapewe kuchita chiyani?
17 Nthawi zonse muzikumbukira kuti: Popeza si inu angwiro, simungapeweretu kulakalaka zoipa. Koma mukayamba kulakalaka zinthu zoipa, muzichotsa mwamsanga maganizo amenewo ngati mmene Yosefe anachitira zinthu mofulumira pothawa mkazi wa Potifara. (Gen. 39:12) Simuyenera kuchita zoipa zomwe mukulakalakazo.
PITIRIZANI KUCHITA KHAMA
18-19. Kodi ndi mafunso ati omwe tiyenera kudzifunsa pamene tikuyesetsa kusintha maganizo athu?
18 Timafunika kuchita khama kuti tipitirize kusintha maganizo athu kuti azigwirizana ndi chifuniro cha Yehova. Nthawi zonse muzidzifunsa kuti: ‘Kodi ndimachita zinthu zosonyeza kuti ndikuzindikira nthawi yapadera yomwe tikukhalamoyi? Kodi ndikupita patsogolo pa nkhani yovala umunthu watsopano? Kodi ndimalola kuti mzimu wa Yehova uzinditsogolera pa moyo wanga kuti ndizipewa kuchita zoipa zomwe ndimalakalaka?’
19 Mukamadzifufuza, musamayembekezere kuti muzichita zinthu ngati munthu wangwiro koma muziona mmene mukupitira patsogolo. Ngati pali zina zimene mukuona kuti mufunika kukonza, musamataye mtima. M’malomwake, muzitsatira mfundo ya pa Afilipi 3:16, yakuti: “Tiyeni tipitirize kupita patsogolo mwa kuyenda moyenera m’njira yomweyo.” Mukamachita zimenezi, mungakhale otsimikiza kuti Yehova adzakudalitsani pamene mukuyesetsa kusintha maganizo anu.
NYIMBO NA. 36 Timateteza Mtima Wathu
a Mtumwi Paulo analangiza Akhristu anzake kuti asamaganize kapena kuchita zinthu potengera nzeru za nthawi ino. Malangizo amenewatu ndi othandizanso kwa ife masiku ano. Sitiyenera kulola kuti zochitika za m’dzikoli zizikhudza kaganizidwe ndi zochita zathu ngakhale pang’ono. Kuti izi zitheke, tiyenera kupitiriza kusintha kaganizidwe kathu ngati tazindikira kuti sikakugwirizana ndi zimene Mulungu amafuna. Munkhaniyi, tikambirana mmene tingachitire zimenezi.
b Onani nkhani yakuti “Moyo Wanga Unkangoipiraipirabe,” mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 2015.
c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale wachinyamata akuganizira zimene ayenera kusankha pakati pochita maphunziro apamwamba kapena utumiki wa nthawi zonse.