NKHANI YOPHUNZIRA 48
Mukhoza Kukhalabe Olimba Mtima pa Nthawi Yovuta
“‘Limbani mtima, . . . pakuti ine ndili ndi inu,’ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.”—HAG. 2:4.
NYIMBO NA. 118 “Tiwonjezereni Chikhulupiriro”
ZIMENE TIPHUNZIREa
1-2. (a) Kodi zochitika za masiku ano zikufanana bwanji ndi za m’nthawi ya Ayuda omwe anabwerera ku Yerusalemu? (b) Kodi Ayuda ankakumana ndi mavuto ati? (Onani bokosi lakuti “M’nthawi ya Hagai, Zekariya ndi Ezara.”)
KODI nthawi zina mumada nkhawa mukaganizira zam’tsogolo? Mwina ntchito yanu yatha ndipo mukudera nkhawa kuti muzipezera bwanji banja lanu zinthu zofunika pa moyo. Mwinanso mumaona kuti banja lanu ndi losatetezeka chifukwa cha mavuto a zandale, kuzunzidwa kapenanso kutsutsidwa pa ntchito yolalikira. Kodi mukukumana ndi ena mwa mavuto amenewa? Ngati ndi choncho, kukambirana mmene Yehova anathandizira Aisiraeli atakumana ndi mavuto ngati omwewa kungakuthandizeni.
2 Ayuda omwe anali atakhala ku Babulo kwa zaka zambiri, ankafunika kukhala ndi chikhulupiriro kuti asiye moyo wabwino n’kupita kudziko limene ambiri mwa iwo sankalidziwa bwinobwino. Atafika kumeneko, sipanatenge nthawi yaitali kuti ayambe kukumana ndi mavuto a zachuma, a zandale komanso kutsutsidwa. Choncho ambiri zinawavuta kuika maganizo pa ntchito yomanganso kachisi wa Yehova. Ndiye cha m’ma 520 B.C.E., Yehova anatumiza aneneri awiri, Hagai ndi Zekariya, kuti akawalimbikitse. (Hag. 1:1; Zek. 1:1) Munkhaniyi tiona kuti aneneriwa analimbikitsadi anthuwa. Komabe patapita zaka pafupifupi 50, Ayudawo anafookanso. Ezara, yemwe anali katswiri wokopera Chilamulo, anabwera ku Yerusalemu kuchokera ku Babulo kuti adzalimbikitse anthu a Mulunguwo kuti aziika patsogolo zinthu zokhudza kulambira koona.—Ezara 7:1, 6.
3. Kodi tikambirana mafunso ati? (Miyambo 22:19)
3 Maulosi a Hagai ndi Zekariya anathandiza anthu a Mulungu kalelo kuti apitirize kukhulupirira Yehova pamene ankatsutsidwa. Maulosiwa angatithandizenso ifeyo masiku ano kuti tipitirize kukhulupirira kuti Yehova angatithandize pamene tikukumana ndi mavuto. (Werengani Miyambo 22:19.) Munkhaniyi tikambirana uthenga umene Mulungu anapereka kudzera mwa Hagai ndi Zekariya komanso chitsanzo cha Ezara, ndipo tiyankha mafunso awa: Kodi Ayuda omwe anabwerera anamva bwanji atakumana ndi mavuto? N’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kuchita zimene Mulungu amafuna pa nthawi imene tikukumana ndi mavuto? Nanga tingatani kuti tizikhulupirira Yehova tikakumana ndi mavuto?
KODI AYUDA ANAMVA BWANJI ATAKUMANA NDI MAVUTO?
4-5. N’chiyani chinachititsa Ayuda kuti asiye kugwira mwakhama ntchito yomanga kachisi?
4 Ayuda atabwerera ku Yerusalemu anali ndi ntchito yambiri yoti agwire. Mwamsanga, iwo anamanga guwa la nsembe komanso maziko a kachisi. (Ezara 3:1-3, 10) Koma posakhalitsa khama lawo linachepa. Kuwonjezera pa kumanga kachisi, iwo ankafunikanso kumanga nyumba zawo, kulima minda komanso kupezera mabanja awo chakudya. (Ezara 2:68, 70) Iwo ankatsutsidwanso ndi adani awo omwe anakonza chiwembu choletsa ntchito yomanganso kachisi.—Ezara 4:1-5.
5 Ayudawo ankavutikanso chifukwa cha mavuto a zachuma komanso zandale. Dziko lawo linkalamuliridwa ndi ufumu wa Perisiya. Koresi yemwe anali mfumu ya Perisiya atafa mu 530 B.C.E., Kambisesi yemwe analowa m’malo mwake anayamba nkhondo yofuna kugonjetsa Aiguputo. Popita ku Iguputoko, asilikali ake ayenera kuti ankalamula Aisiraeli kuti awapatse chakudya, madzi komanso pokhala, zomwe zinangowonjezera mavuto awo. Dariyo Woyamba, yemwe analowa m’malo mwa Kambisesi, atangoyamba kulamulira panali mavuto ambiri a zandale komanso anthu oukira. Mosakayikira mavuto amenewa ayenera kuti anachititsa Ayudawo kuti azida nkhawa kuti azipeza bwanji zinthu zofunika pa moyo. Chifukwa cha zimenezi, Ayuda ena ankaona kuti imeneyi siinali nthawi yabwino kuyamba kumanganso kachisi wa Yehova.—Hag. 1:2.
6. Mogwirizana ndi Zekariya 4:6, 7, kodi ndi mavuto ena ati omwe Ayuda ankakumana nawo, nanga Zekariya anawalimbikitsa bwanji?
6 Werengani Zekariya 4:6, 7. Kuwonjezera pa mavuto a zachuma komanso zandale, Ayuda ankazunzidwanso. Mu 522 B.C.E., adani awo anakwanitsa kuletsa ntchito yomanganso kachisi. Koma Zekariya anawatsimikizira kuti Yehova adzagwiritsa ntchito mzimu wake wamphamvu powathandiza kuti apitirizebe ntchito yawo ngakhale kuti panali mavuto. Mu 520 B.C.E., Mfumu Dariyo analamula kuti kachisiyo apitirize kumangidwa ndipo anapereka ndalama komanso anthu oti athandize pa ntchitoyo.—Ezara 6:1, 6-10.
7. Kodi Ayuda amene anabwerera ku Yerusalemu anapeza madalitso ati atayamba kuika zimene Mulungu amafuna pamalo oyamba?
7 Kudzera mwa Hagai ndi Zekariya, Yehova analonjeza anthu akewo kuti adzawathandiza ngati ataika ntchito yomanga kachisi pamalo oyamba. (Hagai 1:8, 13, 14; Zekariya 1:3, 16) Atalimbikitsidwa ndi aneneriwo, Ayudawo anayambiranso kumanga kachisi mu 520 B.C.E. ndipo anamaliza pasanathe zaka 5. Popeza kuti Ayudawo ankaika zimene Mulungu ankafuna pamalo oyamba ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto, iye anawathandiza kuti akhale naye pa ubwenzi komanso kuwapatsa zimene ankafunikira. Zotsatira zake n’zakuti iwo anayamba kulambira Yehova mosangalala.—Ezara 6:14-16, 22.
MUZIIKA PAMALO OYAMBA ZIMENE MULUNGU AMAFUNA
8. Kodi mawu a pa Hagai 2:4, angatithandize bwanji kuti tiziika maganizo athu pa zimene Mulungu amafuna? (Onaninso mawu a m’munsi.)
8 Pamene chisautso chachikulu chikuyandikira, n’zofunika kwambiri kuti tizimvera lamulo lakuti tizilalikira. (Maliko 13:10) Koma tikhoza kuvutika kuti tiziika maganizo athu onse pa ntchito yolalikira ngati anthu akutitsutsa kapena ngati tikukumana ndi mavuto a zachuma. Ndiye kodi n’chiyani chingatithandize kuti tiziika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba? Tisamakayikire kuti “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba”b ali kumbali yathu. Iye adzatithandiza tikapitiriza kuika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba. Choncho palibe chifukwa choti tizichitira mantha.—Werengani Hagai 2:4.
9-10. Kodi mawu a Yesu a pa Mateyu 6:33, anathandiza bwanji banja lina?
9 Taganizirani zimene zinachitikira banja la Oleg ndi Irina,c omwe akuchita upainiya. Atasamuka kuti akathandize kumpingo wina, ntchito inawathera chifukwa cha mavuto a zachuma omwe anali m’dziko lawo. Ngakhale kuti iwo sanali pa ntchito pafupifupi kwa chaka, ankaona kuti Yehova akuwathandiza ndipo nthawi zina abale ndi alongo ankawapatsa zimene ankafunikira. Kodi n’chiyani chinawathandiza kupirira? Oleg yemwe poyamba ankada nkhawa ananena kuti: “Kutanganidwa ndi ntchito yolalikira kunatithandiza kuti tiziika maganizo athu pa zinthu zofunika kwambiri pa moyo.” Iwo ankachita khama mu utumiki uku akufufuza ntchito.
10 Tsiku lina akuchokera mu utumiki anamva kuti mnzawo wina anayenda mtunda wa makilomita 160 kudzawapatsa zikwama ziwiri zodzaza ndi zinthu zosiyanasiyana zomwe anawagulira. Oleg anati: “Tsiku limeneli tinaona umboni wakuti Yehova komanso abale ndi alongo amatiganizira. Tinatsimikizira kuti Yehova sasiya atumiki ake ngakhale zitaoneka kuti alibe mtengo wogwira.”—Mat. 6:33.
11. Kodi zinthu zidzatiyendera bwanji tikamaika maganizo athu pa zimene Mulungu amafuna?
11 Yehova amafuna kuti tiziika maganizo athu onse pa ntchito yolalikira, yomwe ndi yopulumutsa moyo. Mogwirizana ndi zomwe taona mundime 7, Hagai analimbikitsa anthu a Mulungu kuti ayambirenso ntchito yomanga kachisi ngati kuti akuyala kumene maziko. Ndipo Yehova anawalonjeza kuti akatero ‘adzawadalitsa.’ (Hag. 2:18, 19) Ifenso Yehova adzatidalitsa tikamaika pamalo oyamba ntchito imene watipatsa.
KODI TINGATANI KUTI TIZIDALIRA KWAMBIRI YEHOVA?
12. N’chifukwa chiyani Ezara ndi Ayuda omwe anachoka ku ukapolo ankafunika kukhala ndi chikhulupiriro cholimba?
12 Mu 468 B.C.E., Ezara anayenda ndi gulu lachiwiri la Ayuda pochokera ku Babulo kupita ku Yerusalemu. Kuti ayende ulendowu, Ezara ndi Ayudawo ankafunika kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Iwo akanadutsa m’misewu yoopsa, atanyamula golide ndi siliva wochuluka yemwe anaperekedwa kuti akathandize pa ntchito yomanga kachisi. Izi zikanachititsa kuti anthu achiwembu awaukire. (Ezara 7:12-16; 8:31) Kuwonjezera pamenepo, iwo anazindikira kuti ku Yerusalemu sikunalinso kotetezeka. Mumzindawo munalibe anthu ambiri ndipo mpanda ndi mageti ake zinkafunika kukonzedwa. Kodi tingaphunzire chiyani kwa Ezara pa nkhani yokhulupirira kwambiri Yehova?
13. Kodi Ezara anatani kuti azikhulupirira kwambiri Yehova? (Onaninso mawu a m’munsi.)
13 Ezara anali ataona Yehova akuthandiza anthu ake pa nthawi yamavuto. Mu 484 B.C.E., Ezara ayenera kuti ankakhala ku Babulo pamene Mfumu Ahasiwero inalamula kuti Ayuda onse mu ufumu wa Perisiya aphedwe. (Esitere 3:7, 13-15) Pa nthawiyo moyo wa Ezara unali pangozi. Zitatero, Ayuda “m’zigawo zonse” anayamba kulira komanso kusala kudya popempha Yehova kuti awatsogolere. (Esitere 4:3) Kodi mukuganiza kuti Ezara ndi Ayuda anzake anamva bwanji zinthu zitasintha n’kuwaipira anthu omwe anakonza chiwembucho? (Esitere 9:1, 2) Zimene Iye anaona pa nthawiyo zinamuthandiza kukonzekera mavuto omwe anakumana nawo m’tsogolo, ndipo ziyenera kuti zinamuthandiza kukhulupirira kwambiri kuti Yehova amateteza anthu ake.d
14. Kodi mlongo wina anaphunzirapo chiyani ataona mmene Yehova anamuthandizira pa nthawi ya mavuto?
14 Yehova akatithandiza pa nthawi ya mavuto timayamba kumudalira kwambiri. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Anastasia yemwe amakhala ku Eastern Europe. Iye anasiya ntchito yomwe ankagwira kuti isamuchititse kulowerera ndale. Anastasia anati: “Ndinali ndisanakhalepo wopanda ndalama pa moyo wanga wonse. Ndinasiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova ndipo ndinaona akundisamalira mwachikondi. Ndikadzakhalanso kuti si ndili pa ntchito sindidzaopa chilichonse. Ngati Atate wanga wakumwamba akundisamalira panopa, adzandisamaliranso m’tsogolo.”
15. Kodi n’chiyani chinathandiza Ezara kuti azikhulupirirabe Yehova? (Ezara 7:27, 28.)
15 Ezara anaona Yehova akumusamalira pa moyo wake. Kuganizira nthawi zimene Yehova anamuthandizapo pa moyo wake kunathandiza Ezara kuti azimukhulupirira kwambiri. Iye ananena kuti “dzanja la Yehova Mulungu wanga linkandithandiza.” (Werengani Ezara 7:27, 28.) Ezara ananena mawu amenewa maulendo 6 m’buku lomwe limadziwika ndi dzina lake.—Ezara 7:6, 9; 8:18, 22, 31.
16. Kodi ndi pa nthawi ziti pomwe tingaone Yehova akutithandiza pa moyo wathu? (Onaninso chithunzi.)
16 Yehova akhoza kutithandiza tikakumana ndi mavuto. Mwachitsanzo, tikamapempha abwana athu kuti tikapezeke kumsonkhano wachigawo kapena tikamawapempha nthawi yoti tizikapezeka pamisonkhano yampingo, timam’patsa Yehova mpata woti atithandize ndipo tikhoza kudabwa ndi mmene zinthu zingayendere. Zikatero timayambanso kudalira kwambiri Yehova.
17. Kodi Ezara anasonyeza bwanji kuti anali wodzichepetsa atakumana ndi mavuto? (Onani chithunzi chapachikuto.)
17 Ezara anali wodzichepetsa ndipo ankapempha Yehova kuti amuthandize. Nthawi iliyonse yomwe wapanikizika kwambiri chifukwa cha maudindo ake, iye ankapemphera kwa Yehova modzichepetsa. (Ezara 8:21-23; 9:3-5) Chifukwa cha zimenezi anthu ena ankakhala ofunitsitsa kumuthandiza komanso kutsanzira chikhulupiriro chake. (Ezara 10:1-4) Tikaona kuti tikudera nkhawa za mmene tingapezere zinthu zofunika pa moyo kapena mmene tingatetezere banja lathu, tizipemphera kwa Yehova ndipo tisamakayikire kuti atiyankha.
18. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova?
18 Tikakhala odzichepetsa n’kumalola kuti Yehova komanso Akhristu anzathu atithandize, tidzayamba kudalira kwambiri Mulungu. Erika, yemwe ali ndi ana atatu anapitirizabe kudalira Yehova ngakhale pamene anakumana ndi mavuto aakulu. Pa kanthawi kochepa, iye anapita padera komanso mwamuna wake anamwalira. Pofotokoza zomwe zinamuchitikirazi, iye anati: “Munthu sungadziwiretu mmene Yehova angakuthandizire, chifukwa iye amakuthandiza m’njira imene sumaiyembekezera. Ndazindikira kuti iye anayankha ambiri mwa mapemphero anga kudzera m’mawu omwe anzanga ankandiuza komanso zimene ankandichitira. Ndikamafotokozera anzanga mmene ndikumvera zimakhala zosavuta kuti andithandize.”
PITRIZANI KUDALIRA YEHOVA MPAKA MAPETO
19-20. Kodi tikuphunzirapo chiyani kwa Ayuda omwe sanabwerere ku Yerusalemu?
19 Tingaphunzirenso mfundo yofunika kwa Ayuda omwe sanabwerere ku Yerusalemu. Ena sakanatha kuchita zambiri chifukwa cha ukalamba, matenda aakulu kapenanso udindo wosamalira banja. Ngakhale zinali choncho, iwo anapereka ndi mtima wonse zinthu zothandizira Ayuda omwe anabwererawo. (Ezara 1:5, 6) Zikuoneka kuti patapita zaka 19, kuchokera pamene gulu loyamba linabwerera ku Yerusalemu, Ayuda omwe anatsala ku Babulo ankapitirizabe kutumiza mphatso zoti zikathandize anzawo ku Yerusalemuko.—Zek. 6:10.
20 Ngakhale kuti sitingathe kuchita zambiri potumikira Mulungu tisamakayikire kuti iye amayamikira zimene timakwanitsa kuchita kuti timusangalatse. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? M’nthawi ya Zekariya, Yehova anauza mneneriyu kuti apange chisoti chachifumu pogwiritsa ntchito golide ndi siliva yemwe Ayuda omwe anatsala ku Babulo anatumiza. (Zek. 6:11) “Chisoti chachifumucho” chinali choti ‘chizidzawakumbutsa’ za zinthu zimene anapereka mowolowa manja. (Zek. 6:14, mawu a m’munsi.) Tingakhale otsimikiza kuti Yehova sadzaiwala zimene timachita mwakhama pomutumikira ngakhale pamene tikukumana ndi mavuto.—Aheb. 6:10.
21. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizikhalabe olimba mtima tikaganizira zam’tsogolo?
21 N’zosachita kufunsa kuti tipitiriza kukumana ndi mavuto m’masiku otsirizawa ndipo mwina zinthu ziziipiraipira. (2 Tim. 3:1, 13) Koma sitiyenera kuda nkhawa kwambiri. Kumbukirani zimene Yehova anauza anthu ake m’masiku a Hagai. Iye anati: “Ine ndili ndi inu . . . musachite mantha.” (Hag. 2:4, 5) Ifenso tisamakayikire kuti Yehova adzakhala nafe tikamachita zimene amafuna. Tikamatsatira zimene taphunzira m’maulosi a Hagai ndi Zekariya komanso pa chitsanzo cha Ezara, sitidzasiya kukhulupirira Yehova ngakhale titakumana ndi mavuto otani m’tsogolo.
NYIMBO NA. 122 Khalani Olimba Komanso Osasunthika
a Nkhaniyi yakonzedwa kuti itithandize kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova ngakhale pamene tikukumana ndi mavuto a zachuma, a zandale kapenanso tikamatsutsidwa pa ntchito yolalikira.
b Mawu akuti “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba” amapezeka maulendo 14 m’buku la Hagai. Zimenezi zinkakumbutsa Ayuda komanso zimatikumbutsa ifeyo kuti Yehova ali ndi mphamvu zopanda malire komanso amatsogolera magulu ankhondo a angelo kumwamba.—Sal. 103:20, 21.
c Mayina ena asinthidwa.
d Ezara anali katswiri wokopera Chilamulo ndipo anayamba kukhulupirira kwambiri maulosi a Yehova asanapite ku Yerusalemu.—2 Mbiri 36:22, 23; Ezara 7:6, 9, 10; Yer. 29:14.
e MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale akupempha abwana ake kuti akapezeke pamsonkhano wachigawo, koma akumukaniza. Pokonzekera kuti akakumanenso ndi abwana ake, iye akupempha Yehova kuti amuthandize komanso kumutsogolera. Akusonyeza abwana akewo kapepala koitanira kumsonkhano komanso kuwafotokozera ubwino wophunzira Baibulo. Abwanawo akuchita chidwi ndipo akusintha maganizo.