MBIRI YA MOYO WANGA
Moyo Wabwino Kwambiri Potumikira Yehova
MU 1951, ndinafika ku Rouyn, yomwe ndi tauni yaing’ono mumzinda wa Quebec ku Canada. Ndinafika pakhomo lomwe linali pa adiresi imene ndinapatsidwa. Marcel Filteau,a mmishonale yemwe analowa Sukulu ya Giliyadi ndi amene anabwera kudzatsegula. Iye anali ndi zaka 23 ndipo anali wamtali, pomwe ine ndinali ndi zaka 16 komanso wamfupi. Ndinamuonetsa kalata yosonyeza kuti ndine mpainiya. Atawerenga anandiyang’ana n’kundifunsa kuti, “Koma amayi ako akudziwa kuti uli kuno?”
NDINALEREDWA M’BANJA LOMWE AMAYI NDI AMENE ANALI A MBONI
Ndinabadwa mu 1934 ndipo makolo anga anachokera ku Switzerland. Iwo anakhazikika m’tauni ina ya migodi yotchedwa Timmins ku Ontario ku Canada. Cha m’ma 1939, mayi anga anayamba kuwerenga magazini a Nsanja ya Olonda komanso kupezeka pamisonkhano ya Mboni za Yehova. Akamapita kumisonkhano, ankanditenga limodzi ndi azibale anga 6. Pasanapite nthawi, iwo anakhala a Mboni za Yehova.
Bambo anga sanasangalale ndi zimenezi, koma amayi ankakonda choonadi ndipo anatsimikiza kuti akhalabe okhulupirika kwa Yehova. Iwo anachita zimenezi cha m’ma 1940 ngakhale kuti pa nthawiyo ntchito ya Mboni za Yehova inali yoletsedwa ku Canada. Iwo nthawi zonse ankalemekeza bambo komanso kuchita nawo zinthu mokoma mtima ngakhale pamene bambo ankawalankhula mwaukali ndiponso mowanyoza. Chitsanzo chawo chabwino chinathandiza ineyo ndi azibale anga kuti tiphunzire choonadi. N’zosangalatsa kuti patapita nthawi, bambo anasintha ndipo anayamba kuchita nafe zinthu mokoma mtima.
NDINAYAMBA UTUMIKI WA NTHAWI ZONSE
Mu 1950, ndinakapezeka nawo pamsonkhano wakuti Kuwonjezeka kwa Teokrase, womwe unachitikira ku New York. Ndinayamba kufuna kuchita zambiri potumikira Yehova nditakumana ndi abale ndi alongo ochokera m’mayiko osiyanasiyana komanso nditamvetsera zosangalatsa zimene abale ndi alongo omwe analowa Sukulu ya Giliyadi anafotokoza pamsonkhanowo. Ndinkafunitsitsa kwambiri nditayamba utumiki wa nthawi zonse ndiye nditangofika kunyumba, ndinafunsira upainiya wokhazikika. Ofesi ya nthambi ya ku Canada inandiyankha kuti ndiyenera kubatizidwa kaye. Choncho, ndinabatizidwa pa 1 October 1950. Patatha mwezi umodzi, ndinakhala mpainiya wokhazikika ndipo dera loyamba lomwe ndinatumizidwa ndi ku Kapuskasing. Tauni imeneyi inali kutali kwambiri ndi komwe ndinkakhala pa nthawiyo.
Mu 1951, ofesi ya nthambi inapempha a Mboni omwe ankalankhula Chifulenchi kuti aone ngati angasamukire kudera lina la ku Quebec, komwe kumalankhulidwa chinenerochi. Kumeneko kunkafunika ofalitsa ambiri. Popeza kuti ndinkadziwa Chifulenchi ndi Chingelezi, ndinavomera kupita ndipo ndinatumizidwa ku Rouyn. Sindinkadziwana ndi aliyense kumeneko. Popita ndinangopatsidwa adiresi monga ndatchulira kumayambiriro kuja. Koma zonse zinayenda bwino. Marcel anakhala mnzanga wapamtima ndipo tinasangalala kutumikira limodzi ku Quebec kwa zaka 4, kenako ndinakhala mpainiya wapadera.
SUKULU YA GILIYADI KOMANSO ZOMWE NDINKAYEMBEKEZERA
Ndili ku Quebec, ndinasangalala kulandira kalata yondidziwitsa kuti ndikalowe nawo kalasi nambala 26 ya Sukulu ya Giliyadi, yomwe inachitikira ku South Lansing ku New York. Tinamaliza maphunziro pa 12 February 1956 ndipo ndinatumizidwa ku West Africa, m’dziko lomwe panopa limatchedwa Ghana.b Koma ndisanapite, ndinkafunika kubwerera ku Canada kuti ndikapeze zikalata za ulendowu ndipo ndinkaona ngati ndikayembekezera kwa milungu yochepa.
Ndinayembekezera zikalatazi ku Toronto kwa miyezi 7. Pa nthawiyi, ndinkakhala kunyumba kwa a Cripps ndipo ndinadziwana ndi mwana wawo dzina lake Sheila. Kenako tinayamba chibwenzi. Nditangotsala pang’ono kumupempha kuti tikwatirane, zikalata za ulendo zija zinatuluka. Ine ndi Sheila tinaipempherera kwambiri nkhaniyi ndipo tinasankha kuti ndipite ku utumiki wanga. Koma tinagwirizana kuti tizilemberana makalata kuti tione ngati tingadzakwatirane m’tsogolo. Zimenezi sizinali zophweka koma pamapeto pake, tinaona kuti tinasankha bwino.
Nditayenda kwa mwezi pasitima yapamtunda, sitima yapamadzi yonyamula katundu komanso pandege, ndinafika mumzinda wa Accra ku Ghana. Kumeneku ndinaikidwa kukhala woyang’anira chigawo. Ndinkayendera dziko lonse la Ghana komanso mayiko oyandikana nalo monga ku Ivory Coast (panopa ndi Côte d’Ivoire) ndi Togoland (panopa ndi Togo). Nthawi zambiri ndinkayenda ndekha pagalimoto ya ku ofesi ya nthambi. Ndinkasangalala kwambiri ndi maulendowa.
Kumapeto kwa mlungu, ndinkachititsa misonkhano yadera. Pa nthawiyo, kunalibe Nyumba za Msonkhano choncho abale ankamanga denga pogwiritsa ntchito nsungwi ndi nthambi za kanjedza kuti anthu adzatetezeke ku dzuwa. Popeza kuti kunalibe mafiliji, ankasunga ziweto zamoyo pamalo pomwepo n’cholinga choti adzaphe pa nthawi yokonzera chakudya anthu omwe abwera pamsonkhano.
Pamisonkhanoyi pankachitikanso zinthu zina zoseketsa. Pa nthawi ina, mmishonale mnzanga dzina lake Herb Jenningsc akukamba nkhani, ng’ombe inathawa kumalo omwe ankaisunga n’kubwera pakati pa pulatifomu ndi anthu. Herb anasiya kaye kukamba nkhani. Ng’ombeyo inkaoneka kuti yasokonezeka kwambiri. Kenako abale 4 amphamvu anaigwira n’kukaibwezera kumalo ake, kwinaku anthu akukuwa mosangalala.
Mkati mwa mlungu ndinkapita m’midzi yapafupi kukaonetsa filimu yonena za ntchito yathu yolalikira padziko lonse. (The New World Society in Action.) Ndinkagwiritsa ntchito pulojekita komanso chinsalu choyera chomwe ndinkachimanga pakati pa mitengo iwiri. Anthuwo ankaikonda filimuyi, chifukwa ambiri kanali koyamba kuonera filimu. Iwo ankaomba m’manja mosangalala akaona anthu mufilimuyi akubatizidwa. Anthu omwe anaonera filimuyi anazindikira kuti ndife anthu ogwirizana padziko lonse.
Nditakhala ku Africa kwa zaka pafupifupi ziwiri, mu 1958 ndinasangalala kukapanga nawo msonkhano wa mayiko ku New York. Zinali zosangalatsa kwambiri kukumana ndi Sheila, yemwe anabwera kuchokera ku Quebec, komwe ankatumikira monga mpainiya wapadera. Tinkalemberana makalata koma popeza tsopano tinakumananso, ndinamupempha ngati tingakwatirane ndipo anavomera. Ndinalembera kalata M’bale Knorrd yowafunsa ngati Sheila angakalowe Sukulu ya Giliyadi kenako n’kubwera kuti tizidzatumikira limodzi ku Africa. Iwo anavomera ndipo pamapeto pake, Sheila anabwera ku Ghana. Tinakwatirana ku Accra pa 3 October 1959. Tinaona kuti Yehova anatidalitsa kwambiri chifukwa chomuika pamalo oyamba pa moyo wathu.
TINATUMIKIRA LIMODZI KU CAMEROON
Mu 1961, tinatumizidwa ku Cameroon. Kumeneko anandipempha kuti ndikakhazikitse ofesi ya nthambi yatsopano ndipo ndinkatanganidwa kwambiri. Popeza ndinali ndisanakhalepo mtumiki wa nthambi, panali zambiri zoti ndiphunzire. Kenako mu 1965 tinazindikira kuti Sheila ndi woyembekezera. Zinanditengera nthawi yaitali kuti ndivomereze kuti tidzakhala makolo. Koma titangoyamba kusangalala ndi udindo watsopano tinkayembekezerawu komanso kukonzekera zobwerera ku Canada, panachitika zomvetsa chisoni.
Sheila anapita padera. Madokotala anatiuza kuti mwana amene tinkayembekezerayo anali wamwamuna. Izi zinachitika zaka 50 zapitazo koma sitimaiwala. Ngakhale kuti tinamva chisoni kwambiri ndi zomwe zinachitikazi, tinapitirizabe kuchita utumiki wathu womwe tinkaukonda ku Cameroon.
Ku Cameroon, nthawi zambiri abale athu ankazunzidwa chifukwa chokana kulowerera ndale. Zinthu zinkavuta kwambiri makamaka pa nthawi ya zisankho za pulezidenti. Zimene tinkaopa kwambiri zinachitika pa 13 May 1970, pamene ntchito ya Mboni za Yehova inaletsedwa m’dzikoli. Boma linalanda ofesi yathu yokongola, yomwe tinali titangokhalamo kwa miyezi 5 yokha. Mlungu umodzi usanathe, amishonale tonse kuphatikizapo ine ndi Sheila, tinathamangitsidwa m’dzikolo. Zinali zovuta kusiya abale ndi alongo athu chifukwa tinkawakonda. Tinkadera nkhawa posadziwa zomwe ziwachitikire.
Kwa miyezi 6 tinakhala tili ku ofesi ya nthambi ya ku France. Tili kumeneko, ndinkachita zonse zomwe ndingathe pothandiza abale athu ku Cameroon. Mu December chaka chomwecho, tinatumizidwa ku nthambi ya ku Nigeria, yomwe inayamba kuyang’anira ntchito ya ku Cameroon. Abale ndi alongo a ku Nigeria anatilandira bwino ndipo tinasangalala kutumikira kumeneko kwa zaka zingapo.
KUSANKHA ZOCHITA PA NKHANI YOVUTA
Mu 1973 tinkafunika kusankha zochita pa nkhani ina yovuta kwambiri. Sheila ankavutika ndi matenda enaake aakulu. Tili kumsonkhano ku New York, iye anangoyamba kulira n’kundiuza kuti: “Sindingathenso kupitiriza. Nthawi zambiri ndimakhala ndikudwala ndipo ndimatopa kwambiri.” Tinali titatumikira limodzi ku West Africa kwa zaka zoposa 14. Ndinkayamikira kuti ankatumikira Yehova mokhulupirika koma tsopano tinkafunika kusintha. Titakambirana nkhaniyi komanso kuipempherera kwa nthawi yaitali, tinaganiza zobwerera ku Canada kuti azikalandira thandizo la mankhwala. Kusiya umishonale komanso utumiki wa nthawi zonse kunali kovuta kwambiri.
Titafika ku Canada, ndinapeza ntchito kwa mnzanga wina yemwe ankagulitsa magalimoto m’tauni ina kumpoto kwa mzinda wa Toronto. Tinakwanitsa kuchita lendi nyumba komanso kugula mipando yakale popanda kutenga ngongole. Tinkafuna kukhalabe ndi moyo wosalira zambiri kuti mwina tsiku lina tingadzayambirenso utumiki wa nthawi zonse. Tinadabwa kuti zimene tinkayembekezerazi zinachitika mwamsanga kuposa mmene tinkaganizira.
Loweruka lililonse ndinkakathandiza pa ntchito yomanga Nyumba ya Msonkhano yatsopano ya ku Norval ku Ontario. Kenako ndinapemphedwa kuti ndizikatumikira monga woyang’anira Nyumba ya Msonkhano. Sheila anayamba kupeza bwino ndipo tinaona kuti angakwanitse kuchita utumiki umenewu. Choncho mu June 1974, tinasamukira kunyumba imene inali pamalo a msonkhano. Tinasangalala kwambiri kuyambiranso utumiki wa nthawi zonse.
Timayamikira kuti Sheila anapitiriza kupeza bwino. Patatha zaka ziwiri, tinapemphedwa kuti tikatumikire monga woyang’anira dera. Dera lomwe tinatumizidwa linali ku Manitoba ku Canada, komwe ndi kozizira kwambiri. Koma tinkasangalala kwambiri chifukwa abale ndi alongo ankatilandira bwino. Tinazindikira kuti chofunika kwambiri si kumene tikutumikira koma kupitirizabe kutumikira Yehova kulikonse kumene tili.
NDINAPHUNZIRA PHUNZIRO LOFUNIKA KWAMBIRI
Titatumikira mudera kwa zaka zingapo, mu 1978 tinaitanidwa kukatumikira ku Beteli ya ku Canada. Pasanapite nthawi yaitali, ndinaphunzira phunziro lofunika kwambiri koma m’njira yowawa. Ndinapemphedwa kuti ndikakambe nkhani ya ola limodzi ndi hafu mu Chifulenchi pamsonkhano wapadera ku Montreal. Koma nkhani yanga inali yosafika pamtima ndipo m’bale wina wa mu Dipatimenti ya Utumiki anandipatsa malangizo. Kunena zoona, ndinkafunika kuzindikira kuti ndilibe luso lokamba nkhani. Pa nthawiyo sindinasangalale ndi malangizowo. Sitinkagwirizana kwenikweni ndi m’baleyo. Ndinkaona kuti anali wokhwimitsa zinthu komanso wosayamikira. Ndinalakwitsa kwambiri posalandira malangiziwo chifukwa choganizira munthu amene anawapereka komanso mmene anawaperekera.
Patangopita masiku angapo, m’bale wina wa m’Komiti ya Nthambi anakambirana nane zokhudza nkhaniyo. Ndinavomereza kuti sindinalandire bwino malangizowo ndipo ndinapepesa. Kenako ndinakakambirana ndi m’bale amene anandipatsa malangizo uja. Iye anavomereza ndi mtima wonse kupepesa kwanga. Zimene zinachitikazi zinandiphunzitsa phunziro lofunika kwambiri pa nkhani ya kudzichepetsa, lomwe sindidzaiwala. (Miy. 16:18) Ndakhala ndikupemphera kwa Yehova za nkhaniyi mobwerezabwereza ndipo ndatsimikiza kuti ndizilandira bwino malangizo omwe ndingapatsidwe.
Ndakhala ndikutumikira ku Beteli ya ku Canada kwa zaka zoposa 40, ndipo kuchokera mu 1985 ndi pamene ndinakhala ndi mwayi wotumikira m’Komiti ya Nthambi. Mkazi wanga Sheila anamwalira mu February 2021. Kuwonjezera pa chisoni chomwe ndili nacho chifukwa cha imfa ya mkazi wanga, ndikumadwaladwala. Koma kutanganidwa ndi kutumikira Yehova kumandithandiza kukhala wosangalala moti ndimaona kuti ‘masiku akudutsa mofulumira kwambiri.’ (Mlal. 5:20) Ngakhale kuti ndakhala ndikukumana ndi mavuto, zosangalatsa zimene ndapeza ndi zochuluka kwambiri. Kuika Yehova pamalo oyamba komanso kumutumikira mu utumiki wa nthawi zonse kwa zaka zoposa 70, kwandithandiza kukhala ndi moyo wabwino kwambiri. Ndimapempherera achinyamata kuti nawonso apitirize kuika Yehova pamalo oyamba chifukwa sindikukayikira kuti angakhale ndi moyo wabwino komanso wosangalala pokhapokha ngati akutumikira Yehova.
a Onani mbiri ya moyo wa M’bale Marcel Filteau mu nkhani yakuti “Yehova Ndiye Pothawirapo Panga ndi Mphamvu Yanga” mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 2000.
b Dera limeneli la ku Africa linali pansi pa ulamuliro wa dziko la Britain mpaka mu 1957, ndipo linkatchedwa Gold Coast.
c Onani mbiri ya moyo wa M’bale Herbert Jennings mu nkhani yakuti “Simudziwa Chimene Chidzagwa Mawa” mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 2000.
d M’bale Nathan H. Knorr ndi amene ankatsogolera ntchito yathu pa nthawiyo.