Kodi Yesu Anapereka Lamulo Lotani Lokhudza Kuchita Zinthu ndi Ena?
Yankho la m’Baibulo
Pa ulaliki wake wapaphiri, Yesu anapereka lamulo lakuti: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.”—Mateyu 7:12; Luka 6:31.
Kodi lamuloli limatanthauza chiyani?
Lamulo limene Yesu anaperekali limatilimbikitsa kuti tizichita zinthu ndi ena mmene tikufunira kuti iwo azichita zinthu ndi ife. Mwachitsanzo, ambirife timafuna kuti anthu azichita nafe zinthu mwaulemu, mokoma mtima komanso mwachikondi. Choncho tiyenera kuchita “zomwezo” kwa ena.—Luka 6:31.
N’chifukwa chiyani lamuloli ndi lothandiza?
Lamulo la Yesuli lingathandize pa zinthu zambiri pa moyo. Mwachitsanzo, likhoza . . .
Kulimbitsa mabanja.—Aefeso 5:28, 33.
Kuthandiza makolo kuti azilera bwino ana awo.—Aefeso 6:4.
Kuthandiza anthu kuti azigwirizana ndi maneba awo, anzawo akuntchito ndi anzawo ena.—Miyambo 3:27, 28; Akolose 3:13.
Lamulo limene Yesu anaperekali ndi lofanana ndi mfundo imene imapezeka kwambiri m’malemba amene anthu ambiri amati Chipangano Chakale. Baibulo limati lamuloli “n’zimene Chilamulo [mabuku 5 oyambirira a m’Baibulo] ndi Zolemba za aneneri [mabuku olembedwa ndi aneneri] zimafuna.” (Mateyu 7:12) M’mawu ena, tinganene kuti lamulo la Yesuli ndi lofanana ndi mfundo yaikulu ya m’Chipangano Chakale yakuti: muzikonda anzanu.—Aroma 13:8-10.
Kodi muzitsatira lamuloli pokhapokha ena akakuchitirani zabwino?
Ayi. Cholinga cha lamuloli n’chakuti inuyo muzithandiza anthu ena. Pamene Yesu anapereka lamuloli, ankanena za mmene tiyenera kuchitira zinthu ndi anthu onse, ngakhale adani athu. (Luka 6:27-31, 35) Choncho lamuloli limalimbikitsa anthu kuti azichitira anthu ena onse zabwino.
Kodi mungatsatire bwanji lamuloli?
1. Muzikhala tcheru. Muziona zimene anthu ena akuchita. Mwachitsanzo, mwina mungaone munthu akuvutika kunyamula katundu, mungamve za munthu amene ali kuchipatala kapena mwina mungaone mnzanu wakuntchito yemwe wakhumudwa. Mukamakhala tcheru kuti muone zimene zikuchitikira anthu ena, mukhoza kumapeza mipata yonena kapena kuchita zinthu zowathandiza.—Afilipi 2:4.
2. Muzimvera ena chisoni. Muziyesetsa kumvetsa mmene anthu ena akumvera. Kodi mukanamva bwanji ngati zikanakuchitikirani zimene zikuchitikira iwowo? (Aroma 12:15) Mukamayesetsa kumvetsa mmene anthu ena akumvera, mungafune kuwathandiza.
3. Muzikumbukira kuti anthu amasiyana. Zimene anthu ena angafune kuti muwachitire mwina sizingakhale zimene inuyo mungafune kuti ena akuchitireni. Choncho, pa zonse zimene mungasankhe kuchitira munthu wina, yesetsani kusankha zimene munthuyo angafune kwambiri.—1 Akorinto 10:24.