Kodi Zingatheke Bwanji Kuti Mudzakhale ndi Moyo Wosatha?
Yankho la m’Baibulo
Baibulo limatilonjeza kuti: “Wochita chifuniro cha Mulungu adzakhala kosatha.” (1 Yohane 2:17) Ndiye kodi Mulungu amafuna kuti inuyo muzichita chiyani?
Muziphunzira za Mulungu komanso za Mwana wake, Yesu. Nthawi ina Yesu akupemphera ananena kuti: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.” (Yohane 17:3) Ndiye kodi tingatani ngati tikufuna “kudziwa” za Mulungu ndi Yesu? Timafunika kuphunzira Mawu a Mulungu komanso kuyesetsa kugwiritsa ntchito zimene timaphunzirazo.a Baibulo limatithandiza kudziwa zimene Yehova yemwe ndi Mlengi wathu, amafuna kuti tizichita. (Machitidwe 17:24, 25) Limatiuzanso za Yesu yemwe ndi Mwana wake. Yesu anaphunzitsa anthu “mawu amoyo wosatha.”—Yohane 6:67-69.
Muzikhulupirira nsembe yomwe Yesu anapereka ngati dipo. Yesu anabwera padziko lapansi “kudzatumikira ndi kudzapereka moyo wake dipo.” (Mateyu 20:28) Nsembe ya dipo yomwe Yesu anapereka inathandiza kuti anthu akhale ndi mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padzikoli.b (Salimo 37:29) Yesu ananena kuti: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Komabe tifunika kudziwa kuti pali zambiri zomwe zimafunika kuposa kungonena kuti timakhulupirira Yesu. Timafunika kusonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro, kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene amatiphunzitsa komanso zimene Atate wake amafuna.—Mateyu 7:21; Yakobo 2:17.
Muyenera kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu. Mulungu amafuna kuti tiyandikirane naye komanso kuti tizimuona ngati mnzathu. (Yakobo 2:23; 4:8) Popeza Mulungu sangafe, amafunanso kuti anthu amene ali naye pa ubwenzi adzakhale ndi moyo wosatha. N’chifukwa chake m’Mawu ake, iye anafotokoza zimene amafuna kudzachitira anthu onse amene amamufunafuna kuti: “Mitima yanu ikhale ndi moyo kosatha.” Salimo 22:26.
Maganizo Olakwika pa Nkhani Yokhala ndi Moyo Wosatha
Maganizo olakwika: Zimene akatswiri akuyesetsa kuchita zidzatithandiza kudzakhala ndi moyo wosatha
Zoona zake: Ngakhale kuti akatswiri a zachipatala akuyesetsa kupeza njira zotalikitsira moyo, zimenezi sizingadzachititse anthu kuti adzakhale ndi moyo wosatha. Mulungu yekha ndi amene angatipatse moyo wosatha chifukwa iyeyo ndi “kasupe wa moyo.” (Salimo 36:9) Ndipotu akutilonjeza kuti “adzameza imfa kwamuyaya” komanso kudzapereka moyo wosatha kwa anthu omwe amamukhulupirira.—Yesaya 25:8; 1 Yohane 2:25.
Maganizo olakwika: Anthu a mitundu inayake okha ndi omwe adzakhale ndi moyo wosatha.
Zoona zake: Mulungu sakondera anthu a mtundu winawake. Ndipotu Baibulo limanena kuti, “iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.” (Machitidwe 10:34, 35) Choncho, ngati anthu a mitundu komanso zikhalidwe zosiyanasiyana amamvera Mulungu, akhoza kudzakhala ndi moyo wosatha.
Maganizo olakwika: Moyo wosatha udzakhala wotopetsa.
Zoona zake: Mulungu amatikonda ndipo amafuna kuti tizisangalala. Ndipo iye watipatsa mwayi woti tidzakhale ndi moyo wosatha. (Yakobo 1:17; 1 Yohane 4:8) Iye amadziwanso kuti anthufe timakhala osangalala tikamagwira ntchito yabwino. (Mlaliki 3:12) N’chifukwa chake akulonjeza kuti anthu amene adzakhale ndi moyo wosatha, adzasangalala ndi ntchito yomwe azidzagwira chifukwa izidzathandiza iwowo komanso okondedwa awo.—Yesaya 65:22, 23.
Kuwonjezera pamenepo, anthu amene adzakhale ndi moyo wosatha adzapitirizabe kuphunzira zinthu zatsopano zokhudza Mlengi komanso zinthu zosiyanasiyana za m’chilengedwechi. Mulungu anatilenga ndi mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale ngakhale kuti sitidzakwanitsa kudziwa ntchito yonse “imene Mulungu woona wagwira, . . . kuyambira pa chiyambi mpaka pa mapeto.” (Mlaliki 3:10, 11) Choncho nthawi zonse anthu amene adzakhale ndi moyo wosatha azidzachita zinthu zosangalatsa komanso kuphunzira zinthu zochititsa chidwi.
a A Mboni za Yehova amaphunzira Baibulo ndi anthu kwaulere. Kuti mudziwe zambiri onerani kavidiyo kakuti Kodi Phunziro la Baibulo Limachitika Bwanji?
b Werengani nkhani yakuti “Kodi Yesu Amatipulumutsa Bwanji?”