Kusamalira Okalamba—Vuto Lomakulakulabe
PALI nkhani yosimbidwa ya msungwana wachichepere yemwe anafunsa amayi ŵake kuti: “Kodi nchifukwa ninji Agogo amadyera m’ndilo pamene enafe timadyera m’mbale zathu zabwino?” Amayi ŵake anafotokoza kuti: “Manja a amayi ngamanjenje, ndipo angatigwetsere mbale zathu zabwino ndi kuziswa, ndicho chifukwa chake amagwiritsira ntchito ndilo.” Ataganizira za ichi kwakamphindi, msungwana wachichepereyo anafunsa kuti: “Pamenepo kodi mudzandisungira ndilo yoti ndidzikakupatsiranimo nditakula?” Kuwoneratu zomadza mtsogolo kwa mwanayo kuyenera kuti kunazizwitsa amayiwo, ngakhale kuwawopsako ndithu. Koma posinkhasinkha, kuyenera kuti kunawatsimikizira chinthu china—kuti msungwana wawo wachichepereyo ankakonzekera kuwasamalira!
Okalamba ambiri angakhale opanda chiyembekezo chotsimikizirika. Iwo akhala gulu la anthu omachuluka mofulumira m’mbali zambiri zadziko. World Press Review ya mu August 1987 inasimba kuti anthu okwanira 600 miliyoni, yomwe inali 12 peresenti ya anthu a papulaneti panthaŵiyo, adali atapyola pamsinkhu wa zaka 60.
Mu United States, okalamba akuchuluka kuposa achichepere kwanthaŵi yoyamba. Mkonzi wasayansi wa nyuzipepala ya ku New York City anasimba kuti: “Anthu a ku Amereka mamiliyoni makumi atatu tsopano ali ndi zaka 65 kapena kuposapo—mmodzi mwa asanu ndi atatu alionse a ife, kuposa ndi kalelonse, ndipo: Chiŵerengero cha okalamba chikukula paliŵiro loŵirikiza kaŵiri kuposa misinkhu yonse. . . . Avereji ya utali wa moyo kwa anthu a ku Amereka inali 35 mu 1786. Kwa mwana wa ku Amereka wobadwa mu 1989, utali wake ngwazaka 75.”
Mu Canada chiŵerengero cha okalamba kwambiri, amsinkhu wa zaka 85 kunka pamwamba, chikuyembekezeredwa kuŵirikiza katatu podzafika kumapeto kwa zaka za zana lino.
Mu Yuropu zaka zana limodzi zapitazo, okalamba adali 1 peresenti yokha ya chiwonkhetso cha anthu onse. Lerolino chiŵerengero chawo chakula kufika 17 peresenti.
Lipoti la U.S. Census Bureau pamutu wakuti “Kukalamba m’Maiko Otukuka Kumene” lidati: “Chiwonjezeko cha mbali ya zinayi mwa zisanu za okalamba chikuchitika m’Maiko Otukuka Kumene.”
Zaka makumi anayi zapitazo utali wa moyo wotsimikizirika wa anthu a ku China unali pafupifupi zaka 35. Podzafika mu 1982 chiŵerengerocho chinakwera kufika pa zaka 68. Lerolino anthu a ku China oposa 90 miliyoni akulingaliridwa kukhala okalamba, ndipo kwayerekezeredwa kuti podzafika kumapeto kwa zaka za zana lino, chiŵerengerocho chidzakwera kufika pa 130 miliyoni, kapena 11 peresenti ya anthu onse.
Kuyesayesa Kwapadera kwa Kuwasamalira Okalamba Anu
Pamene chiŵerengero cha okalamba kwambiri chikukulakula padziko lonse, funso lozizwitsa lonena za kuŵasamalira likuvutiravutirabe. M’nthaŵi za Baibulo vutoli silinali lalikulu motero. Iwo anali ndi banja lalikulu, mmene ana, makolo, ndi agogo anakhalira pamodzi. Ana ndi agogo anagaŵana mapindu, ndipo makolo anagaŵira zinthu zakuthupi zofunikira ndipo anatsimikiziranso kuti chisamaliro chapadera chirichonse chofunikira kwa okalamba m’banja chinalipo. Mabanja aakulu oterowo osamalira okalamba akadali mwambo wotsatiridwa m’maiko ena lerolino. (Mwachitsanzo, chonde onani bokosi patsamba 24.) Koma siziri choncho m’maiko okhupuka kwambiri kumene banja limalekezera kwa makolo ndi ana awo okha basi. Anawo atakula ndi kukwatira ndi kubala ana awo, kaŵirikaŵiri amayang’anizana ndi vuto la kusamalira makolo awo okalamba, ofooka, ndipo kaŵirikaŵiri odwala matenda osapola.
M’dongosolo la zinthu liripoli, kuchita chimenechi kungakhaledi vuto lalikulu! Ngakhale nchosayanjidwa, m’mikhalidwe yamakono yachuma, kungakhale kofunika kuti makolo onse aŵiri agwire ntchito. Chakudya nchodula, lendi njodula, ngongole zingobwera. Ngakhale ndalama za malipiro a anthu aŵiri zingathe msanga. Ngati mkazi wapanyumbapo samagwira ntchito kwina, iye angakhale wotanganitsidwa ndi kulera ana, kugula, kuyeretsa—nayonso ndintchito yeniyeni payokha. Pano sitikunena kuti kholo lokalamba, kapena makolo okalamba, sayenera kusamaliridwa panyumba. Tangoti ingakhale ntchito yovuta zedi. Okalamba ali ndi mavuto awo, ndipo momvekera bwino nthaŵi zina angamadandaule ndikung’ung’udza, kaŵirikaŵiri okhala ndi malingaliro oipidwa ndi osagwirizanika. Izi sizimatanthauza kuti kuyesayesa kwamphamvu kusamalira kholo lokalamba panyumba sikuyenera kuchitidwa.
Kaŵirikaŵiri, thayo limakhala pa ana aakazi otsala. Kufufuza kwambirimbiri kwavumbula kuti chinkana kuti amuna angapereke thandizo landalama, kwakukulukulu ali akazi amene amapereka chisamaliro chachikulu chachindunji. Iwo amawaphikira chakudya okalamba—kaŵirikaŵiri amaŵadyetsa ngati khanda—amaŵasambika ndi kuŵaveka, amaŵasintha zovala, amawaperekeza kwa adokotala ndi kuchipatala, amasamalira kuŵapatsa mankhwala awo. Kaŵirikaŵiri ndiwo amakhala maso, makutu, ndi malingaliro a makolo awo okalamba. Ntchito yawo njaikulu, ndipo kufunitsitsa kwawo kuichita mosasamala kanthu za kuvuta kwake nkoyamikirikadi ndi kokondweretsa Yehova Mulungu.
Kukhulupirira kuti ana achikulire ambiri amatumiza makolo awo okalamba kukatsirizira zaka zawo zaukalamba m’nyumba zolelera sikowona, mogwirizana ndi Carl Eisdorfer, M.D., Ph.D., mtsogoleri wa Center on Adult Development and Aging pa Yunivesite ya Miami, Florida, U.S.A. “Kufufuza kwasonyeza kuti kusamalira anthu okalamba kwakukulu kumachitidwa ndi mabanja awo,” iye anatero.
Mapendedwe akuchilikiza zonena zake. Mwachitsanzo, mu United States, 75 peresenti ya anthu amene anafunsidwa anati akafuna kukhala ndi makolo awo ngati afikira pamsinkhu wosakhoza kukhala okha. “Ichi chikutsimikizira kuti mabanja amafuna kusamalira okalamba awo,” anatero Dr. Eisdorfer. Ndipo lipoti lopezeka m’magazini a Ms. linati: “Maperesenti 5 okha a anthu a msinkhu wa zaka zoposa 65 ndiwo ali m’nyumba zolerera okalamba nthaŵi zonse chifukwa chakuti ponse paŵiri okalamba ndi achibale awo ambiri amakonda chisamaliro chapanyumba mmalo mwa ku nyumba zolerera.”
Chochitika chotsatirachi chimasonyeza kuyesayesa kumene ena amakuchita m’kusamalira makolo okalamba. Lipotili likuchokera kwa woimira Mboni za Yehova woyendayenda yemwe amachezetsa mipingo mu United States yonse. Iye akufotokoza mmene iye ndi mkazi wake analiri otsimikiza mtima kusunga amayi a mkazi wake azaka 83 zakubadwa mmalo moŵaika m’nyumba yolerera. Iye anathirira ndemanga kuti: “Ndinakumbukira mwambi wakuti,” iye anatero, “mayi mmodzi anatha kusamalira ana 11, koma ana 11 sanathe kusamalira mayi mmodzi. Eya, aŵirife tinali otsimikiza mtima kusamalira mayi mmodzi wokalambayo. Ngakhale kuti iwo ankayamba kudwala matenda a Alzheimer, anayenda nafe m’kalavani.
“Poyamba iwo anayenda nafe pamene tinkalalikira uthenga wa Ufumu kukhomo ndi khomo. Pambuyo pake tinafunikira kuwatengera panjinga yamagudumu. Eninyumba anawoneka kuyamikira mmene tinawasamalirira. Panthaŵi zina amayiwo ankanena zinthu zosalongosoka, koma sitinawachititse manyazi mwakuwawongolera. Komabe, iwo anali akadali ndi nthabwala zawo. Nthaŵi zina ndinkawachenjeza kuti, ‘Mponde bwino Amayi’ ndipo iwo ankayankha nati, ‘Sindinakupondereni amayi ŵanu.’ Tinawasamalira kufikira pamene anamwalira, pamsinkhu wa zaka 90.”
Pamene Nyumba Zolerera Zikhala Zofunikira
Pafupifupi okalamba okwanira mamiliyoni aŵiri amakhala m’nyumba zolerera mu United States. Komabe, m’zochitika zambiri, izo siziri “nyumba zosungiramo nkhalamba mopanda chifundo monga katundu,” monga momwe ena amakunenera kuwaika m’nyumba zolerera. Mmalomwake, kaŵirikaŵiri ndiyo imakhala njira yokha yotsalapo yoperekera chisamaliro chokwanira kwa osakhoza kudzisamalira okha. Nthaŵi zambiri, ana a okalamba samakhoza kusamalira makolo awo okalamba, ambiri a iwo angakhale akudwala matenda oopsa a Alzheimer kapena kubindikiritsidwa ndi matenda ena olemaza omwe amafuna chisamaliro cha tsiku lonse lathunthu. M’zochitika zoterozo nyumba zolerera zingakhale malo okha okwaniritsira zosoŵa zapadera zimenezi.
Mishonale wa Watch Tower Society m’Sierra Leone, Afirika, anasimba za kupweteka kumene amayi ŵake anayang’anizana nako pamene anafunikira kuika amayi ŵawo m’nyumba yolerera: “Posachedwapa amayi m’Florida anaika amayi ŵawo, a Helen, m’nyumba yolerera. Chinali chosankha chovuta kwenikweni kwa iwo. Iwo anawasamalira amayi ŵawo a Helen kwa zaka zinayi, koma tsopano a Helen anafunikira chisamaliro chanthaŵi yonse. Mabwenzi a amayi, banja, ndi antchito yakakhalidwe ndi adokotala onseŵa anachirikiza chosankha chakuika a Helen m’nyumba yolerera, komabe chinali chosankha chovuta kuchipanga. Amayi analingalira kuti popeza kuti amayi ŵawo adawasamalira iwo pamene adali mwana, tsopano kunali kolondola kuti iwonso asamalire amayi ŵawo muukalamba wawo—kulipira, kapena ‘kubwezera koyenera,’ kumene mtumwi Paulo anakunena. Komabe, monga momwe zinaliri, a Helen anasamaliridwa bwinopo m’nyumba yolerera kuposa mmene zikanakhalira kunyumba kwa amayi.”—1 Timoteo 5:4.
Mboni ina, yogwira ntchito ku malikulu apadziko lonse a Mboni za Yehova, inasimba za kudwala kansa kwa atate ŵake. “Abambo ŵanga adali Mboni yachangu kwa zaka zopasa 30. Kwa zaka zisanu ndi zinayi zotsirizira za moyo wawo, adali ndi kansa. Mkazi wanga ndi ine tinakhala nawo panthaŵi ya machuti athu ndipo tinatenga machuti aatali kuti tikhale nawo ndikuwathandiza. Achibale ena anathandiza m’njira zosiyanasiyana. Koma mbali yaikulu yanthaŵiyo, iwo ankasamaliridwa ndi akazi awo ndi mwana wawo wamkazi wokwatiwa yemwe ankakhala m’nyumba yotsatira. Iwo anachezeredwanso ndi ziŵalo za mpingo wa Mboni kumene ankasonkhana. Kwa zaka ziŵiri zotsirizira, iwo anali akabwerebwere m’chipatala, ndipo miyezi isanu yotsirizira anaithera ku malo opereka chisamaliro chowonjezereka kumene ankalandira chisamaliro chapadera chimene anachifunikira.
“Kuwachotsa kunyumba kuti apite ku malowo kunali chosankha chabanja, nawonso akugaŵanamo. Iwo anati kuwasamalira kunayamba kukhala kothodwetsa kwambiri, ngakhale kosatheka, kwa banja panyumba. ‘Kudzakutopetsani nonsenu!’ iwo anadandaula motero. ‘Ndinthaŵi yanga yakuti ndipite ku malo opereka chisamaliro chowonjezereka ameneŵa. Ziribwino kwa inu; ziri bwinonso kwa ine.’
“Chotero iwo anapita. Banja lidawasamalira kwa mbali yaikulu m’zaka zisanu ndi zinayi, ndipo iwo anapita ku malo opereka chisamaliro chowonjezereka kokha monga njira yokha yotsalapo yopezera chisamaliro chapadera, cha tsiku lonse lathunthu chofunikiracho.”
Pamene nyumba yolerera ikhala yofunikira kaamba ka chisamaliro chokwanira, monga njira yokha yotsalapo, banja liyenera kufunafuna yaudongo ndi yokhala ndi antchito opereka chisamaliro mwachifundo ndi mwaluso. Ngati nkotheka, pangani makonzedwe akuti pakhale wokawachezetsa tsiku lirilonse—chiŵalo chabanja, winawake wa mumpingo, ngakhale foni yokha—kotero kuti munthu wokalambayo sadzimva kuti wataidwa, kuiŵalidwa, kukhala yekha, ndikumaganiza kuti palibe amene amamsamalira. Pamene ena m’nyumba yolerera akhala ndi owachezetsa, koma palibe amene amabwera kudzawona wokondedwa wanu—zingakhale zomkhwethemula kwambiri. Chotero yesani kumamuwona munthuyo mokhazikika. Mchezereni. Mvetserani kwa iye. Pempherani naye. Chotsirizirachi nchofunika kwambiri. Ngakhale ngati awoneka kukhala akuthatha ndi moyo, pempheranibe. Simungadziŵe kuti ndi kumlingo wotani umene iye angakhale akumva zinthu!
Pamene mupanga zosankha ponena za makolo, yesani kuchita zimenezo limodzi nawo mmalo mowachitira. Aloleni adzimve kuti akuilamulirabe miyoyo yawo. Perekani chithandizo chofunikira ndi chikondi chonse ndi kuleza mtima ndi kuwamvetsetsa kothekera. Imeneyo ndiyo nthaŵi ya kubwezera, mangawa athu kwa makolo ndi agogo athu, monga momwe mtumwi Paulo analembera.
‘Choyenera Anthu Onse’
M’dziko lamakono lotangwanidwa ndi zochitachita, nkosavuta kunyalanyaza makolo m’moyo. Makamaka, achichepere omwe angoloŵa kumene pampikisanowo ndikuthamangira kupeza bwino m’moyo wawo amakhoterera kulingalira kuti okalamba ali chopinga m’njira yawo ya moyo, kuti anatha kale ntchito. Mwinamwake tonsefe tiyenera kuima ndi kulingalira kuti: Ndiiko komwe, kodi nchiyani chimene chimapangitsa moyo kukhala wantchito nanga? Nkosavuta kwa achichepere kuchepsa mtengo wa miyoyo ya okalamba ndikuwona moyo wawo kukhala wamtengo kwenikweni.
Komabe, siokalamba kapena ofooka okha amene amachita zochepera kapena kusapereka chirichonse ku chimene chikuwoneka kukhala tanthauzo la moyo. Mfumu Solomo m’bukhu la Mlaliki mobwerezabwereza anasonya ku ntchito za anthu mwachisawawa kukhala zachabe. Iye analankhula za achichepere ndi nyonga yawo yapakanthaŵi ndikusonyeza mmene zaka zomapita zidzanyonyotsolera matupi awo monga momwe zachitira kale ku matupi a anthu ena mamiliyoni ochuluka. Zonse zimathera m’fumbi ndipo zimayenerera mawu aŵa: ‘Chabe zachabetu,’ anatero Solomo. ‘Zonse ndi chabe.’—Mlaliki 12:8.
Komabe iye anathokoza mawu a anzeru ndipo anaika zimene anapenda ponena za moyo m’mawu achidule aŵa: ‘Mawu atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.’ (Mlaliki 12:13) Imeneyo ndiyo njira ya moyo wogwira ntchito, osati kuchepa msinkhu kwanu kapena ukalamba wanu kapena kutchuka kwanu m’dziko lino lokondetsa zinthu zakuthupi limene likupita.
Kuti tilamulire maunansi athu aumunthu, Yesu anapereka muyezo wotsogolera umene ukutchedwa Lamulo Lamakhalidwe Abwino wakuti: “Nthaŵi zonse chitirani ena monga momwe mukafunira iwo kukuchitirani.” (Mateyu 7:12, The New English Bible) Kuti tiligwiritsire ntchito lamulolo, tiyenera kudziika m’malo a munthu mnzathu, kuwona mmene tingafunire kuchitiridwa ngati tinali m’malo ake. Ngati ndife okalamba ndi ofooka ndipo tifunikira thandizo, kodi tingakonde kuchitiridwa motani ndi mmodzi wa ana athu? Kodi tidzawabwezera makolo athu kaamba ka zaka 20 za chisamaliro ndi chichilikizo zimene anatipatsa moolowa manja pamene tinali ana opanda thandizo mwakuwasamalira tsopano pamene ali opanda thandizo muukalamba wawo?
Pamene tisamalira zosoŵa za makolo athu okalamba, mwinamwake tidzakumbukira nthaŵi yaubwana wathu ndi zonse zimene anatichitira pamene tinali makanda, ana, kuleredwa ndi iwo m’matenda apaubwana, kudyetsedwa ndi kuvekedwa ndi iwo, kutipereka kokayendayenda kuzotisangalatsa monga ana. Kenaka, ndi chisamaliro chachikondi kaamba ka ubwino wawo, lingalirani zimene ziri zabwino koposa kuti tizifikire zosoŵa zawo.
Zimenezo zingakhale kupanga makonzedwe akuwasunga panyumba ngati nkotheka. Kumbali ina, makonzedwe abwino koposa kwa onse oloŵetsedwamo, kuphatikizamo makolo okalambawo, angakhale malo achisamaliro chowonjezereka kapena nyumba yolerera. Chosankha chirichonse chimene chingapangidwe, chiyenera kuvomerezedwa ndi ena. Monga momwe timauzidwira kuti: ‘Koma iwe uweruziranji mbale wako? Kapena iwenso upeputsiranji mbale wako?’ Ndiponso: “Iwe woweruza mnzako ndiwe yani?”—Aroma 14:10; Yakobo 4:12.
Zirizonse zimene zingathandize makolo okalamba, kaya kukhala ndi ana awo kapena m’nyumba yolerera, ngati mphamvu zawo zakulingalira zikadali bwino, iwo angakhale akadali ndi moyo watanthauzo. Iwo angaphunzire chifuno cha Yehova kaamba ka anthu onse omvera chakukhala ndi moyo kosatha ndi thanzi labwino padziko lapansi laparadaiso. Iwo angapeze ntchito yatsopano, yosangalatsa ndi yokhutiritsa yakutumikira Mlengi wawo, Yehova Mulungu. Chotero imeneyi imakhala nthaŵi yatanthauzo koposa ndi yachimwemwe m’moyo wawo. Ena m’zaka zawo zaukalamba, pamene ena akhala opanda chiyembekezo m’moyo, adziŵa malonjezo a Yehova a moyo wosatha m’dziko latsopano lolungama popanda mapeto ndipo apeza chisangalalo chatsopano m’kulankhula kwa ena ponena za chiyembezo chimenecho.
Timalize ndi mfundo ya nkhaniyi. Mkazi wina wa ku California, pamsinkhu wa zaka 100, anawuzidwa za madalitso olonjezedwa ameneŵa ndi mlezi wa m’nyumba yolerera, ndipo pamsinkhu waukalamba kwenikweni wa zaka 102, anabatizidwa monga mmodzi wa Mboni za Yehova. Iye anamaliza moyo wake, osati monga mapeto a ‘chabe zachabe,’ koma mwakukwaniritsa ‘chofunika chonse cha moyo’ wake, ndicho, ‘kuwopa Mulungu wowona ndi kusunga malamulo ake.’
[Mawu Otsindika patsamba 21]
Zanenedwa kuti zaka zakale mayi mmodzi anatha kusamalira ana 11; tsopano ana 11 satha kusamalira mayi mmodzi
[Bokosi patsamba 24]
Kusonyeza Ulemu Mwakusamalira Okalamba—Ndemanga Zochokera Kumalo Osiyanasiyana m’Dziko
“Mu Afirika muli makonzedwe ochepa aboma kapena mulibiretu alionse kaamba ka okalamba—kulibe nyumba zolerera, kulibe mapindu a Chisamaliro Chazamankhwala kapena Chitetezo Chakhalidwe, palibe mapenshoni. Anthu okalamba amasamaliridwa ndi ana awo.
“Chifukwa chachikulu chimene kubala ana kuliri kofunika kwambiri kwa anthu a m’maiko otukuka kumene nchakuti ana awo adzawasamalire mtsogolo. Ngakhale anthu osauka amabala ana ambiri, akumalingalira kuti akakhala ndi ana ambiri, pamakhalanso mwaŵi waukulu wakuti ena a iwo adzakula ndikuwasamalira.
“Chinkana kuti miyezo ya moyo ikusintha mu Afirika, kwakukulukulu, mabanja amalitenga mosamalitsa thayo la kusamalira okalamba awo. Ngati palibe ana, ziŵalo zina za banja zidzawasamalira. Kaŵirikaŵiri awo omapereka chisamaliro amakhala opanda chuma chokwanira, koma amagaŵana zimene ali nazo.
“Njira ina imene ana amasamalira nayo makolo awo ndiyo kuwasungitsa ana awo. Kaŵirikaŵiri amakhala adzukulu amene amachita ntchito zapanyumba.
“M’maiko otsungula, anthu amakhala ndi moyo kwanthaŵi yaitali chifukwa chakupita patsogolo m’zamankhwala. Koma siziri choncho m’maiko otukuka kumene. Anthu osauka amafa chifukwa chakuti samatha kulipirira ngakhale thandizo lochepera lokhalapo lamankhwala. Mwambi wonenedwa m’Sierra Leone umati: ‘Palibe munthu wosauka wodwala.’ Ndiko kuti, popeza kuti munthu wosauka alibe ndalama zolipirira mankhwala, iye amangokhala alibwino kapena wakufa.”—Robert Landis, mishonale wa mu Afirika.
“Mu Mexico anthu ali ndi ulemu waukulu kwa makolo okalamba. Makolo amakhala okha m’nyumba zawo pamene ana awo aamuna akwatira, koma pamene makolo akalamba ndipo ali nako kusoŵa, anawo amawatengera m’nyumba yawo ndikuwasamalira. Iwo amakulingalira kukhala thayo.
“Nkofala kuwona agogo akukhala m’nyumba imodzi ndi ana awo aamuna ndi adzukulu awo. Adzukulu amawakonda ndikuwalemekeza agogo awo. Banjalo limakhala logwirizana kwenikweni.
“Mu Mexico nyumba zolerera okalamba nzakamodzikamodzi chifukwa chakuti ana aamuna ndi aakazi amasamalira okalamba awo. Ngati pali ana aamuna ochulukirapo, nthaŵi zina wotsirizira kukwatira amakhala panyumbapo ndi makolowo.”—Isha Aleman, wa ku Mexico.
“Mu Korea timaphunzitsidwa panyumba ndi kusukulu kulemekeza okalamba. M’banja mwana wamwamuna wamkulu ayenera kusamalira makolo ake okalamba. Ngati satha kuwasunga, mwana wina wamwamuna kapena wamkazi adzatero. Okwatirana ambiri amakhala ndi kumasamalira makolo awo okalamba m’nyumba imodzi. Makolo amayembekezera kukhala ndi ana awo, ndipo amakonda kusamalira adzukulu awo ndikumawapatsa malangizo. Kumawonedwa kukhala chamanyazi kuti okwatirana achichepere atumize makolo awo okalamba kunyumba yolerera.
“Atate ŵanga anali mwana wamwamuna wamkulu, ndipo tinkakhala ndi agogo athu m’nyumba imodzi. Nthaŵi zonse pamene tinachoka panyumba, tinawauza kumene tinkapita ndi pamene tikabwerako. Pamene tinabwera kunyumba, choyamba tinagwada pachipinda chawo ndikuwapatsa moni titaŵeramitsa mitu ndikuwadziŵitsa kuti tinabwerako popeza kuti anali odera nkhaŵa ponena za ubwino wa banja lonse.
“Pamene tinawapatsa chinachake, tinapereka chinthucho ndi manja aŵiri. Kuli kupanda ulemu kupereka chinthu chirichonse ndi dzanja limodzi kwa anthu olemekezeka, monga ngati makolo, agogo, aphunzitsi, kapena nduna zogwira ntchito m’boma. Pamene tinali ndi chakudya china chapadera, choyamba tinachigaŵira agogo athu.
“Kulemekeza okalamba sikumalekezera kwa ziŵalo zabanja zokha koma kumafutukukira kwa okalamba onse. Kuyambira kusukulu ya pulaimale mpaka ku sekondale, pamakhala maphunziro pa zamakhalidwe abwino. Mkati mwa phunziro limenelo, tinaphunzira kupyolera m’nthano kapena nkhani mmene tingalemekezere okalamba.
“Pamene munthu wamkulu aloŵa m’chipinda, achichepere amayembekezeredwa kuimirira. Ngati wachichepere wakhala pampando m’basi ndipo mwamuna kapena mkazi wokalamba alibe mpando, pamenepo uli mwambo kuti wachichepereyo apereke mpando wakewo. Ngati mwamuna wokalamba wasenza katundu wowoneka kukhala wolemera kwambiri, muyenera kuima ndikufunsa ngati akufuna thandizo kapena ayi. Ngati ati inde, mumamsenzera katunduyo mpaka kumene akupitako.
“Monga momwe Baibulo linaloserera, m’masiku otsiriza ano a dongosolo lazinthu, muyezo wa makhalidwe ukanyonyotsoka tsiku ndi tsiku. Korea sakusiidwa ndi chiyambukiro chimenechi. Komabe, mkhalidwe waulemu wa mtunduwu kulinga kwa okalamba ulipobe m’mitima ya anthu ambiri a ku Korea.—(2 Timoteo 3:1-5)—Kay Kim, wa ku Korea.
[Chithunzi patsamba 23]
Kuchezera okalamba kuli kuthera pabwino nthaŵi