Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Kulota Uli Maso Nkolakwa?
Chinthu chotsiriza chimene mukukumbukira chinali phokoso la mawu a mphunzitsi wanu akungobwebweta za yankho la masamu a algebra, komatu inu simuli m’kalasimo; maganizo anu ali kugombe la nyanja kumene munapita ndi a m’banja lanu tchuthi chathacho. Mukumva kutentha kwa mchenga ndi dzuŵa lothumirira. Mukumva phokoso la madzi amafunde pagombelo, mawu a ana oseŵera, mawu . . . a anzanu a m’kalasi oseka phwitiphwiti? Inde, loto lanu lokondweretsalo labalalika ndipo mmalomwake muona mphunzitsi, amene wagwirira manja m’chuuno, akumafuna kuti mumuuze yankho la funso limene simunamve.
KULOTA uli maso—nkofala pakati pa anthu onse, achichepere ndi achikulire, kwakuti wofufuza wina wotchuka anakutcha “mbali imodzi yaikulu ya moyo wa munthu.” Ena amakhulupirira kuti gawo limodzi mwa zitatu za maola a kugalamuka kwathu imatengedwa ndi kulota uli maso kwa mitundu yosiyanasiyana. Asayansi samadziŵa bwino mmene ndi chifukwa chake malingaliro opyola mwamsanga ameneŵa amaumbidwira, ndiponso samagwirizana onse ponena za chimene chili kulota uli maso. Dikishonale ina inafotokoza kulota uli maso kukhala “masomphenya osangalatsa . . . kupangika kwa choyerekezeredwa.” Komabe, ofufuza ambiri mokulira amakufotokoza kukhala kukuphatikiza pafupifupi mtundu uliwonse wa kuyerekezera uli maso kapena lingaliro loumirizidwa m’maganizo—kaya kukhale kosangalatsa kapena kosasangalatsa. M’nkhani ino, tidzagwiritsira ntchito liwulo m’lingaliro lake lenileni lalikulu, kuphatikizapo osati kokha kuyerekezera kwachibadwa komanso kwadala.
Pamenepo, sikulota uli maso konse kumene kuli kuyerekezera kodabwitsa ndi kokondweretsa. Kulota uli maso kochuluka kwangokhala kubwerera mmbuyo kunthaŵi yakale ya munthu m’malingaliro kwakanthaŵi. M’nkhani ina yotulutsidwa m’maganizi akuti Parents, Dr. James Comer akutchula za chochitika cha iye mwini cha kulota ali maso—monga ngati poyendetsa galimoto kumka kunyumba atagwira ntchito yatsikulo mu ofesi, maganizo ake ankabwerera kumbuyo pokumbukira chigoli chake cha kupambana pabwalo la maseŵera a basketball pamene anali wachichepere. “Mwinamwake zimenezo nzopanda pake, komabe zimandithandiza kupeza bwino,” iye akutero. Komabe ena amagwiritsira ntchito kulota uli maso kuti kuwathandize kulinganiza mtsogolo mwawo. “Ndinkalota ndili maso kwambiri ponena za kukhala katswiri wodziŵa kuimba wodziŵika padziko lonse,” akukumbukira motero mwamuna wina amene, ndithudi, anakhala katswiri wopeka ndi kuimba nyimbo za jazz.
Komabe, kulota uli maso kochuluka kumaonekera kukhala kutasumika pazochitika za tsiku ndi tsiku—kusukulu, pomacheza, pochita homuweki. Nthaŵi zina anthu angayerekezere mwadala malingaliro otero kuti athetse kunyong’onya kwa phunziro lotopetsa la sukulu kapena ntchito yotopetsa ya panyumba. Kulota kwina uli maso kumangochitika mwadzidzidzi. Liwu, phokoso, kapena chithunzithuzi cha m’maganizo mwadzidzidzi chimawakumbutsa za nkhaŵa ina imene ilipo, kanthu kena kokondweretsa kalelo, kapena kanthu kodzachitidwa mtsogolo, ndipo maganizo awo amayamba kuyendayenda. Baibulo limati: “Pakuti loto lafika mwakuchuluka ntchito.” (Mlaliki 5:3) Ndithudi, munthu amene ali wotanganitsidwa ndi nkhaŵa zake ndi zikhumbo, kwenikweni angakhale atamizidwa ndi kulota ali maso kwa kukondetsa zinthu zakuthupi.
Komabe, ngakhale kuti kulota uli maso kungakhale kosangalatsa, kungadodometsenso kusumika maganizo kwanu pamisonkhano Yachikristu, kusukulu, kapena pantchito. Maloto ena angakhaledi osayenera—kapena aupandu. Pamenepa, kodi kulota uli maso kuli chizoloŵezi chimene muyenera kuthetsa?
Kodi Nkwaupandu Pathanzi Lanu la Maganizo?
Kalelo, kulota uli maso kunaonedwa moipa ndi ogwira ntchito za thanzi la maganizo, madokotala, ndi ophunzitsa ena. Chifukwa chake, mnyamata wina anauzidwa ndi katswiri wa zamaganizo kuti: “Tiyenera kukuthandiza kuti uleke kulota uli maso.” Malinga ndi kunena kwa wofufuza Dr. Eric Klinger, uphungu wotero kwakukulukulu unazikidwa panthanthi ya munthu wotchedwa kuti atate wa ukatswiri wa zamaganizo, Sigmund Freud, amene anaona kulota uli maso monga chibwana ndi kusokonezeka maganizo. Motero, buku lina la phunziro la zamaganizo linati: “Kaŵirikaŵiri kulota uli maso ndiko chotulukapo cha kulephera kapena kusakondweretsedwa ndi malo a munthuwe, ndipo kulidi kupeŵa zenizeni.” Mbadwo wa anthu ophunzitsa anzawo ndi ogwira ntchito zosamalira odwala maganizo anaphunzitsidwa kuti kulota uli maso kuyenera kulamuliridwa. Kunanenedwa kuti kulota uli maso konkitsa kungachititse kusokonezeka maganizo kotchedwa schizophrenia.
Komabe, nthanthi za Freud zagonjetsedwa ndi zopezedwa zenizeni za kufufuza kwakukulu. M’buku lake lakuti Daydreaming, Dr. Eric Klinger akunena kuti mwa zinthu zina, ofufuza akunena kuti:
Kulota uli maso nkofala ndipo kuli chochitika chachibadwa.
Anthu ambiri amene amalota ali maso mwakaŵirikaŵiri amakhala ndi mkhalidwe wabwino wa maganizo mosiyana ndi amene samatero.
Kulota uli maso sikumachititsa kubwebweta.
Kulota uli maso sikumachititsa “schizophrenia.” Anthu ovutika ndi “schizophrenia” amalota ali maso mofanana ndi munthu aliyense.
Kugwiritsira Ntchito Kuyerekezera Kwanu Mopindulitsa
Pamenepo, mposadabwitsa kuti palibe paliponse m’Baibulo pamene limatsutsa kugwiritsiridwa ntchito kwabwino kwa kuyerekezera kwa munthu. Ndithudi, kukhoza kwa maganizo athu kuona ndi kuyerekezera ndiko umboni wakuti, ‘chipangidwe chathu nchowopsa ndi chodabwitsa,’ monga momwe wamasalmo ananenera. (Salmo 139:14) Kutagwiritsiridwa ntchito mopindulitsa, kukhoza kumeneku kungakhale chuma chapadera. Akristu akuuzidwa “kuyang’ana ndi maso [awo] osati pazinthu zooneka, koma pazinthu zosaoneka.” (2 Akorinto 4:18, NW) Zimenezi zidzaphatikizapo kuyesa kuona dziko latsopano lolungama la Mulungu ndi maso a maganizo. Mafotokozedwe a Baibulo a Paradaiso wa padziko lonse wa mtsogolo ameneyu amasonkhezera kuyerekezera kwathu ponena za nkhaniyi!—Yesaya 35:5-7; 65:21-25; Chivumbulutso 21:3, 4.
Kuyerekezera kwanu kungakhalenso kothandizadi ngati muti muchite ntchito yovuta. Mwachitsanzo, achichepere amene ali pakati pa Mboni za Yehova kaŵirikaŵiri amapatsidwa gawo la kupereka ulaliki m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki. Kuwonjezera pakuyeseza ndi pakamwa, yesani kuyeseza ulaliki wanu m’maganizo. Yerekezerani omvetsera mmene akuchitira ndi chidziŵitso chanu ndi kaperekedwe kanu ka nkhani. Zimenezi zingakuthandizeni kukonzetsera ulaliki wanu ndi kukupatsani chidaliro chowonjezereka.
Mungayesezenso m’maganizo mmene mungachitire ndi mikhalidwe yovuta. Mwinamwake mukudziŵa kuti Mkristu mnzanu ali ndi chifukwa ndi inu, ndipo mukufuna kukambitsirana za nkhaniyo. (Mateyu 5:23, 24) Mmalo mwa kufikira munthuyo popanda kukonzekera, mungapende nkhaniyo m’maganizo mwanu, mukumayeseza mafotokozedwe osiyanasiyana pankhaniyo. Zimenezi zikakhala zogwirizana ndi lamulo la mkhalidwe la Baibulo lakuti: “Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe.”—Miyambo 15:28.
Kodi pali munthu amene wakukhumudwitsani kapena kukukwiyitsani? Onani chilangizo choperekedwa pa Salmo 4:4: “Chitani chinthenthe, ndipo musachimwe: nenani mumtima mwanu pakama panu, ndipo mukhale chete.” Zimenezi sizitanthauza kuti mudzingobwerezabwereza nkhaniyo m’maganizo mwanu, kapena kumangoganizira za mmene mungakhaulitsire winayo ndi mawu. Ndiiko komwe, Yesu anachenjeza kuti “yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu,” monga momwenso “amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe” adzachitira. (Mateyu 5:22) Koma kuyeseza m’maganizo zimene mungafune kuchita—kumene kungaphatikizepo kungokhululukira wochimwayo—kungakuthandizeni kuthetsa nkhaniyo ndi iye mumkhalidwe wabwino ndi wamtendere.
Kulota uli maso kungachitenso mbali yabwino yaikulu m’kuthetsa mavuto. Dr. Klinger akuti: “Kulota uli maso kwenikweniko ndiko njira yopezera mayankho othandiza pamavuto. Anthu amene amalota ali maso moyerekezera nthaŵi zina angapeze mayankho amene sakanatha kuwaganizira akanakhala kuti akulimbana ndi mavuto mozoloŵereka.”
Pali umboni wakuti kulota uli maso kungakuthandizeni kuongolera njira imene mumachitira ndi mathayo akuthupi. Mwachitsanzo, mlangizi wina wa maseŵera otchedwa kuti ski, amauza ophunzira kupanga chithunzithunzi cha iwo eni m’maganizo akumayandikira chigwa, nadziyerekezera kuti iwowo akudziongolera m’magulaye monse ndi motsika m’njira yake. Ofufuza amakhulupirira kuti kuchita motero kwenikweni kumasonkhezera mbali ya ubongo imene imalamulira minyewa, kuyambitsa ubongo kuti uchitepo kanthu. Zowona, kuyeseza kwenikweni sikungaloŵedwe mmalo, koma kuyeseza m’maganizo kungakuthandizeni kuongolera kukhoza kwanu kuliza chipangizo choimbira kapena kutaipa. “Kunena mwachidule,” akutero Dr. James Comer, “kulota uli maso sikutaya nthaŵi koma ndiko mpumulo wa kutithandiza kuchita zinthu bwinopo.”
Maupandu
Komabe, “Kanthu kalikonse kali ndi nthaŵi yake.” (Mlaliki 3:1) Pamene kuli kwakuti kulota uli maso kungakhale kwabwino pamene mukupuma m’chipinda chanu, pali nthaŵi zimene pamene kuchita motero kukhala kosayenera kapena kwaupandu. Kodi mumayendetsa galimoto? Pamenepo mufunikira kukhala watcheru kwambiri ndi wa maso kungozi. Bwanji ngati mukuyesedwa mayeso kapena kumvetsera nkhani ya m’Baibulo? Pamenepo mufunikira kukhala ndi “mphamvu zabwino zakuganiza.”—2 Petro 3:1, NW.
Baibulo limatichenjezanso za kupitirizabe kuganiza zosakondweretsa kosafunika. Nkwachibadwa kudera nkhaŵa poyang’anizana ndi mayeso kapena kufunsidwa za ntchito, koma sikungakuthandizeni kuganizira za kulephera chifukwa cha mantha ndi kukanidwa. (Yerekezerani ndi Mlaliki 11:4.) Pa Miyambo 12:25 pamachenjeza kuti: “Nkhaŵa iweramitsa mtima wa munthu.” Yesu analangiza omvetsera ake kuti: “Musadere nkhaŵa za maŵa; pakuti maŵa adzadzidera nkhaŵa iwo okha. Zikwanire tsiku zovuta zake.”—Mateyu 6:34.
Ndiponso, kulota uli maso konkitsa kapena kosayenera kungachititsenso mavuto ena. Mwachitsanzo, achichepere ena, amakulitsa maloto a zakugonana. Ena amaona kuti kulota ali maso kukudodometsa kusumika maganizo kwawo pazinthu. Nkhani yathu yotsatira mumpambo uno idzapereka malingaliro ena okuthandizani kulimbana ndi mavuto otero.
[Zithunzi patsamba 17]
Kuyeseza m’maganizo kungaongolere kuchita zinthu kwa munthu