Kusamalira Makolo Okalamba
“NDINALI kukhala maso usana ndi usiku, koma ndinalingalirabe zimenezo kukhala mwaŵi.” Umo ndimmene mkazi wina wokwatiwa anafotokozera kusamalira amayi ake okalamba. Kwa mkaziyu, ndi kwa ena ambiri, kusamalira makolo okalamba kuli chinthu chabwino.
Iko kukukhalanso chochitika chofala kwambiri. Gulu la msinkhu limene likukula mofulumira koposa mu United States likunenedwa kukhala gulu la azaka zopitirira 75 zakubadwa. Mu 1900, Aamereka azaka 75 kapena kuposerapo anali osafika chiŵerengero cha miliyoni imodzi. Pofika mu 1980 pafupifupi mamiliyoni khumi anali opitirira zaka 75. Anthu okalamba akukhala ndi moyo nthaŵi yotalikirapo, ndipo pafupifupi mmodzi mwa atatu a awo azaka 85 kapena kupitirirapo amafunikira chisamaliro chanthaŵi zonse.
Pamene kuli kwakuti kusamalira munthu wosakhoza kudzichitira zinthu kungakhale chochitika chopindulitsa, kuli ndi zovuta zake. Ngati kholo lanu limodzi kapena onse aŵiri akalamba ndipo akufunikira chisamaliro chanu, mungapeze mbali zina kukhala zovuta. Kungoona kuti thanzi lawo likufookerafookera kumakupwetekanidi mtima. Ndipo ngati mupatsidwa chithandizo chochepa kapena ngati simupatsidwa chilichonse ndi ziŵalo zina za banja, pamenepo mumasiyiridwa mtolo waukulu wa kupereka chisamalirocho.
Mungapezenso kuti mosasamala kanthu za msinkhu wanu, simumadziona kukhala wamkulu pamaso pa makolo anu. Iwo angakhale ndi chikhoterero cha kukuchitirani monga mwana wamng’ono, ndipo chikhoterero chanunso chingakhale cha kuchita mogwirizana ndi zimenezo. Kusoŵeka kwa chichirikizo cha malingaliro cha mabwenzi kungawonjezere kupsinjika pa kupereka chisamaliro kwanu.
Komabe, zovuta za kupereka chisamaliro siziyenera kudodometsa kusunga unansi wanu wapafupi ndi makolo anu. Malemba amalangiza achikulire momvekera bwino “ [kusonyeza kudzipereka kwaumulungu, NW ] m’banja lawo, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu.” Kumbali ina, “wopitikitsa amayi, ndiye mwana wochititsa manyazi ndi wogwetsa nkhope.”—1 Timoteo 5:4; Miyambo 19:26.
Kudzipereka kwaumulungu kosonyezedwa mwa kupereka chisamaliro kungakhale chinthu cholemeretsa. Koma choyamba, muyenera kudziŵa zimene makolo anu amafunikira kwenikweni monga chithandizo chanu. Nkhani zotsatirazi zingakuthandizeni kudziŵa ndi kukwaniritsa zosoŵa zimenezo. Ndipo pamene kuli kwakuti nkhanizi zikusumika kwambiri pazimene zingachitidwe m’nyumba, ndikodziŵika kuti m’zochitika zina, chifukwa cha kukhala ndi thanzi lofooka kwambiri kapena kukalamba, kholo lingafunikire chithandizo cha akatswiri, monga chija chopezeka m’nyumba zosamalira okalamba.