Amishonale—Kodi Ayenera Kukhala Otani?
LIWU lakuti “mishonale” lingayambukire mtima kwambiri. Mwa anthu ena, limasonkhezera ulemu, likumakumbutsa za anthu onga Mayi Teresa kapena malemu Albert Schweitzer.
Mosiyana ndi zimenezo, ena amachita mphwayi, kuipidwa, kapena ngakhale kukwiya pamene nkhani ya amishonale itchulidwa. Kwa iwo liwulo limatanthauza kupotoza maganizo ndipo limakumbutsa za utsamunda.
Ponena za amishonale, funso loyenerera nlakuti, kodi iwo akhala onyamula kuunika kapena onyamula mdima?
Kodi Mmishonale Ndani?
Mmishonale amafotokozedwa kukhala wochita “utumiki wolamulidwa ndi gulu lachipembedzo wa kuwanditsa chikhulupiriro chake kapena kuchita ntchito yothandiza anthu.”
Maziko a ntchito yaumishonale Wachikristu anayalidwa ndi Yesu Kristu pamene anauza otsatira ake kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse.” Zimenezi zimafuna kuti uthenga Wachikristu ulalikidwe padziko lonse.—Mateyu 28:19.
Yesu mwiniyo anali mmishonale, wotumidwa ndi Atate ake, Yehova, kuchokera kumwamba kumka kugawo lachilendo, la dziko lapansi. (Afilipi 2:5-8) Moyenerera, mmishonale Wachikristu ayenera kutsatira mosamalitsa chitsanzo choperekedwa ndi Yesu Kristu. Mmishonale wa m’zaka za zana loyamba amene anachitadi zimenezo anali mtumwi Paulo, amene anakhala chitsanzo choyenera kutsanziridwa ndi amishonale Achikristu a pambuyo pake.—1 Akorinto 11:1.
Ngakhale kuti anachita chisoni ndi mavuto a kakhalidwe okantha mtundu wa anthu, Yesu sanasumike maganizo kwambiri pa kuwathetsa pamene anali padziko lapansi. Kuchita zimenezo kukanangodzetsa mpumulo wakanthaŵi. (Yohane 6:26, 27; 12:8) Kanthu kena kanali kofunika koposa. “Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi,” Yesu anatero kwa Pilato, “kuti ndikachite umboni ndi choonadi.” Phindu la kukhala ndi chidziŵitso cha choonadi chimenecho silingagogomezeredwe mwanjira ina kuposa pamenepa, monga momwe Yesu anatchulira poyambirira m’pemphero kuti: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.”—Yohane 17:3; 18:37.
Kodi amishonale a Dziko Lachikristu atsatira mosamalitsa chitsanzo choperekedwa ndi Yesu? Kodi akhaladi onyamula kuunika monga momwe iye analili, akumaŵalitsa kuunika kwa Mawu a Mulungu, chidziŵitso chimene chimatsogolera ku moyo wosatha? Kapena kodi asiya anthu mumdima? Tonsefe tifunikira kudziŵa yankho la funso limeneli chifukwa chakuti zipatso zotulutsidwa ndi odzitcha kukhala amishonale Achikristu m’zaka mazana ambirizo zimatithandiza kudziŵa chipembedzo choona, ndiponso chipembedzo chonyenga.
Kodi Amishonale Achita Motani?
Amishonale athandizira kwambiri kufalitsa uthenga wa Kristu. Mwachitsanzo, ena atembenuza Baibulo m’zinenero zina, motero akumakhozetsa anthu kudziŵerengera.
Komabe, masiku ano, kukuoneka kuti amishonale ena akuganiza kuti kupereka zosoŵa za chitaganya kuyenera kukhala kofunika kuposa ntchito yolalikira kapena yotembenuza. Nkhani ina m’magazini a Time ya mutu wakuti “Umishonale Watsopano” inati: “Pakati pa Aprotesitanti, pakhala kusintha kulinga ku kutanganitsidwa kwambiri ndi mavuto a anthu a zachuma ndi a kakhalidwe amene amishonale akuyesa kuthetsa.” Ponena za Akatolika, mkulu wa mamishoni a Ajesuit wotumidwa kuchokera ku United States ananena kuti kugaŵana zikhulupiriro Zachikristu “kwakhala pamalo achiŵiri poyerekezera ndi kutumikira anthu.” Ndipo mlembi wa mishoni Yachikatolika ananenetsa kuti: “Kale, tinali ndi chotchedwa cholinga chopulumutsa miyoyo. . . . Tsopano, chifukwa cha kukoma mtima kwa Mulungu, timakhulupirira kuti anthu onse ndi zipembedzo zonse apeza kale chisomo ndi chikondi cha Mulungu ndipo adzapulumuka mwa chifundo cha Mulungu.”
Kodi zimenezi zikutanthauza kuti palibenso chifuno chilichonse cha kuphunzitsa Mawu a Mulungu monga momwe Yesu anachitira?
Kodi Chifuno Chikalipobe?
Mu 1985 mabanja 18,000 ku Hamburg, Germany, anaimbiridwa telefoni ndi antchito odzifunira mazana angapo m’ntchito imene nyuzipepala ina inatcha “ntchito yaumishonale wa makamu yochitidwa pa telefoni.” Mwachionekere inabala zipatso zochepa. M’December wapita The European inalemba kuti: “Tchalitchi cha Chiprotesitanti ku Germany . . . chakhala ndi kutsika kwa ziŵerengero za osonkhana ndi oposa 500,000 kuyambira mu 1991.”
Kuchepachepa kwa mipingo sikuli m’matchalitchi a ku Germany okha. Anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse afulatira chipembedzo, akumachiona kukhala chosafunikanso m’moyo wa m’ma 1990 ofuna zinthu zogwira ntchito. Koma chidziŵitso chonena za Chikristu chili chofunika ngati titi tilimbane mwachipambano ndi mdima wa dziko lamakono ndipo ngati titi tichirikizidwe ndi chiyembekezo cha dziko labwino kwambiri la mtsogolo. Lamulo la Yesu la kupanga ophunzira mwa anthu a mitundu yonse lili njira yoyenera yokhutiritsira chosoŵa cha mwamsanga.
Yesu Kristu anafuna kuti amishonale Achikristu akhale onyamula kuunika, osati onyamula mdima. Kodi amishonale a Dziko Lachikristu achita motani? Kodi atsatira chitsanzo chiti?
[Mawu a Chithunzi patsamba 19]
Culver Pictures