Kupanga Ophunzira Enieni Lerolino
YESU KRISTU analamula kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo.” (Mateyu 28:19) Everyman’s Encyclopedia imanena kuti ntchito imeneyi “yachitidwa ndi Akristu m’nyengo iliyonse,” komabe imawonjezera kuti, “koma nthaŵi zina mofooka.” Buku lakuti The Missionary Myth limafunsa kuti: “Kodi nyengo yaumishonale yatha?”
Mu January wa chaka chatha, magazini a Newsweek anasimba kuti: “Papa John Paul II akutengera Chiroma Katolika kumakwalala.” Magaziniwo anafotokoza kuti: “Iye akutumiza alaliki wamba 350 kukafunafuna otembenuza m’malo a disco a Rome, m’ma supermarket ndi m’masiteshoni a sitima zoyenda pansi panthaka. Programu yongoyesayo idzayamba pa Ash Wednesday (Feb. 16). Ngati idzayenda bwino, papa adzayambitsa ntchito ya padziko lonse—mchitidwe umene ungapangitse amishonale Achikatolika kumagogoda pamakomo kuyambira ku Buenos Aires kufikira ku Tokyo.”
Komabe, Mboni za Yehova zamvetsetsa kwanthaŵi yaitali za thayo lawo la kuchita ntchito yaulaliki. (2 Timoteo 4:5) Zoonadi, si onse amene amalalikira monga amishonale m’maiko achilendo. Koma iwo angathe—ndipo amatha—kulalikira kulikonse komwe ali. M’lingaliro limeneli, iwo onse ndi amishonale.
Sukulu ya Mtundu Wapadera
Kuchiyambiyambi kwa ma 1940, Watch Tower Society inakhazikitsa sukulu yophunzitsa atumiki aluso kukatumikira monga amishonale kumaiko achilendo kumene chithandizo chinafunika mwamsanga. M’kupita kwa zaka maphunziro ake asinthidwa, komano sanapatuke pa chonulirapo chake chachikulu chogogomezera phunziro la Baibulo ndi kuchitidwa kwa ntchito yofunika ya kulalikira.
Dzina losankhidwira sukulu yatsopanoyo linali lakuti Gileadi, limene m’Chihebri limatanthauza kuti “Mulu wa Umboni.” Mwakuthandiza kuunjika mulu wa umboni kuulemerero wa Yehova, Gileadi yachita mbali yofunika kwambiri pa kuchitidwa kwa ntchito yolalikira ya padziko lonse imene Yesu ananeneratu kuti ikachitika m’tsiku lathu.—Mateyu 24:14.
Polankhula ndi kalasi yoyamba ya Sukulu ya Gileadi mu 1943, Nathan H. Knorr, amene panthaŵiyo anali pulezidenti wa Watch Tower Society, anati: “Mukukonzekeretsedwa mowonjezereka kaamba ka ntchito yofanana ndi ija ya mtumwi Paulo, Marko, ndi Timoteo, ndi ena amene anayendayenda kumbali zonse za ufumu wa Roma akumalengeza uthenga wabwino wa Ufumu. . . . Ntchito yanu yaikulu ndiyo ija ya kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu kunyumba ndi nyumba monga momwe Yesu ndi atumwi anachitira.”
Pamene kalasi yoyamba inamaliza maphunziro ake, omaliza maphunziro akewo anatumizidwa kumaiko asanu ndi anayi a ku Latin America. Kufikira lerolino, ophunzira oposa 6,500 akumaiko oposa 110 aphunzitsidwa pa Sukulu ya Gileadi ndipo atumizidwa kumaiko oposa 200 ndi zisumbu monga amishonale.
Amishonale Amitundu Yosiyana
Amishonale ambiri a Dziko Lachikristu kalelo, monga awo amene anatumizidwa ku Greenland, anatembenuzira Baibulo kapena mbali zake zina m’chinenero cha kumaloko. Komabe, amishonale oyambirira amenewo kaŵirikaŵiri anali okondweretsedwa ndi zinthu zina osati kuphunzitsa anthu Baibulo.
Mwachitsanzo, amishonale a Dziko Lachikristu ku Japan anadziloŵetsa mu “mabungwe a zamaphunziro ndi m’sukulu,” ikutero Kodansha Encyclopedia of Japan. Iyo ikuti: “Amishonale ambiri adzipatula mwa kuphunzira kwawo kwambiri.” Anakhala akatswiri achinenero kapena maprofesa, akumaphunzitsa maphunziro onga kulemba mabuku, chinenero, mbiri yakale, nthanthi, zipembedzo za ku East Asia, ndi nthano Zachijapani. “Magulu antchito zachifundo ndi othandiza anthu osauka analinso mbali yofunika ya ntchito ya umishonale,” ikuwonjezera motero insaikulopediyayo.
Kulalikira uthenga wabwino sikunakhale chinthu choyamba kwa amishonale ambiri. Kaŵirikaŵiri iwo ankaika chigogomezero pa kukhutiritsa zosoŵa zakuthupi m’malo mwa zosoŵa zauzimu. Kulondola zinthu zaumwini kunakhala nkhaŵa yawo yaikulu. Motero, mmishonale wina wa Tchalitchi cha England amene anatumizidwa ku Japan mu 1889 lerolino amadziŵika bwino kwambiri kukhala “woyambitsa kukwera mapiri m’Japan.”
Amishonale ophunzitsidwa ku Gileadi amasiyana kwambiri ndi awo a Dziko Lachikristu. Buku lakuti Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom, mutu 23, limati: “Amishonale omaliza maphunziro a Sukulu ya Gileadi amaphunzitsa anthu Baibulo. M’malo mwa kumanga matchalitchi ndi kuyembekezera anthu kudza kwa iwo, iwo amapita kunyumba ndi nyumba . . . , osati kukatumikiridwa, koma kukatumikira.”
Kodi Zipatso Zake Zakhala Zotani?
Pambuyo pa kukhala ndi nthaŵi ya zaka mazana ambiri ya kupanga ophunzira Achikristu ku Ulaya, kodi amishonale a Dziko Lachikristu akhala achipambano motani? Buku lakuti A Global View of Christian Missions likuyankha kuti: “Chiŵerengero cha anthu choyerekezeredwa kukhala 160 miliyoni mu Ulaya samadzinenera kuti ali a chipembedzo chinachake. Pakati pa awo amene amadzinenerabe kukhala omamatira ku Chikristu pali oŵerengeka okha amene amaona chipembedzo chawo mwamphamvu. . . . Kunena zoona Ulaya sangatchedwe kontinenti Yachikristu.”
Bwanji nanga za mkhalidwe wa ku Asia? Kodansha Encyclopedia of Japan ikuyankha kuti: “Kwa anthu Chikristu chidakaonedwabe kukhala chikhulupiriro ‘chachilendo,’ . . . chosayenerera anthu wamba Achijapani. . . . Ntchito za Chikristu sizinayambukirebe anthu Achijapani.” Ndithudi, ku Japan anthu osafika pa 4 peresenti amanena kuti ali Akristu, ku India osafika pa 3 peresenti, ku Pakistan osafika pa 2 peresenti, ndipo ku China osafika pa 0.5 peresenti.
Pambuyo pa zaka mazana ambiri za ntchito ya amishonale a Dziko Lachikristu mu Afirika, kodi mkhalidwe wake kumeneko ngwotani? M’lipoti lonena za msonkhano wa mabishopu a ku Afirika wochitidwa m’ngululu yapitayi ku Rome, magazini ena Achijeremani a Focus anasimba kuti: “Zipembedzo za mu Afirika sizikutsutsidwanso konse monga zolambira mafano zachikunja. Chikalata china chalamulo chimene chikuyembekezera kufalitsidwa, chikuika ‘zipembedzo za mwambo za mu Afirika’ pa malo a kukhala mabwenzi oyenerera ndi ofunika. Ziŵalo zawo ziyenera kulemekezedwa. Sinodiyo inazindikira kuti zipembedzo zimene poyamba zinatsutsidwa kukhala zamatsenga ‘nthaŵi zambiri zalamulira ngakhale moyo wa Mkatolika wamphamvu kwambiri.’”a
Pambuyo pa kukhala ndi nthaŵi ya zaka mazana ambiri ya kupanga ophunzira Achikristu ku maiko a ku America, kodi amishonale a Dziko Lachikristu akhala ndi chipambano chotani? Buku lakuti Mission to the World likuyankha kuti: “‘Latin America’ amayenererabe kutchedwa ‘kontinenti yonyalanyazidwa’ mosasamala kanthu za kupita patsogolo kwambiri mu ntchito yaumishonale m’zaka makumi angapo zaposachedwapa.” Ponena za United States, Newsweek ikunena kuti kufufuza kwaposachedwapa “kukusonyeza kuti pamene kuli kwakuti chipembedzo chili m’dziko lonse la America, anthu ochepa okha ndiwo amene amachiona mwamphamvu. . . . Theka la anthu amene amauza ofufuzawo kuti amathera masiku a Sande m’tchalitchi sakunena choonadi. . . . Pafupifupi chigawo chimodzi mwa zitatu cha Amereka a zaka 18 ndi okulirapo ali ndi malingaliro adziko kotheratu . . . Ndi 19 peresenti yokha . . . amene amatsatira chipembedzo chawo nthaŵi zonse.”
Mwachidule, pa kuyesayesa kwawo kuchepetsa umphaŵi, kudwaladwala, ndi umbuli, amishonale a Dziko Lachikristu, monga gulu, achirikiza makonzedwe aumunthu amene kwenikweni angodzetsa chitonthozo chakanthaŵi ndi chapang’ono. Komabe, amishonale enieni Achikristu, amatsogolera anthu ku Ufumu wokhazikitsidwa wa Mulungu, umene udzadzetsa chitonthozo chachikulu ndi chosatha. Sudzangochepetsa mavuto; udzawathetsa. Inde, Ufumu wa Mulungu udzadzetsa ku mtundu wa anthu thanzi langwiro, kusungika kwenikweni kwachuma, mipata yosatha ya ntchito yopindulitsa kwa onse, ndi moyo wopanda mapeto!—Salmo 37:9-11, 29; Yesaya 33:24; 35:5, 6; 65:21-23; Chivumbulutso 21:3, 4.
Amishonale a Dziko Lachikristu angasonye kwa onena kuti ali Akristu amene panthaŵi ndi nthaŵi amafika pa mapemphero achipembedzo kukhala umboni wakuti ‘aphunzitsa anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza.’ Koma maumboni akusonyeza kuti amishonale ameneŵa alephera kuphunzitsa anthu obatizidwa ameneŵa ‘kusunga zinthu zonse zimene Yesu analamulira.’—Mateyu 28:19, 20.
Komabe, ntchito yophunzitsa ya Akristu oona idzapitirizabe mpaka m’dziko latsopano la Mulungu. Idzafalikira kwa mamiliyoni a oukitsidwa amene adzafunikira malangizo m’njira za Mulungu. Pamenepo, popanda chidodometso chausatana, Akristu adzakhala ndi mwaŵi wabwino kwambiri wa kupitirizabe kupanga ophunzira—monga momwedi akhala akuchitira kwa zaka makumi ambiri.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “Tchalitchi cha Katolika mu Afirika,” patsamba 18.
[Bokosi patsamba 24]
Mmene Athandizira Anthu
Otsatirawa ndi mawu onenedwa ndi awo amene apindula ndi thandizo la amishonale ophunzitsidwa ku Gileadi.
“Ndinadabwa ndi khama lawo, akumapirira ndi zinthu zambiri zimene zinali zosiyana ndi zakwawo: mkhalidwe wa mphepo, zinenero, miyambo, chakudya, ndi zipembedzo. Koma anakhalabe m’magawo awo, ena kufikiradi imfa. Zizoloŵezi zawo zabwino za kuphunzira ndi changu muutumiki zinandithandiza kukulitsa mikhalidwe yofananayo.”—J. A., India.
“Ndinachita chidwi ndi kusunga nthaŵi kwa mmishonaleyo pophunzira nane. Anasonyeza kudziletsa kwapadera popirira ndi malingaliro anga olakwa ndi umbuli.”—P. T., Thailand.
“Mkazi wanga ndi ine tinayamikira mkhalidwe wa chiyero umene amishonale a Mboni anasonyeza. Ntchito yawo inatisonkhezera kupanga utumiki wanthaŵi yonse kukhala chonulirapo chathu, ndipo lero tili okondwa kukhala amishonale ife enife.”—A. C., Mozambique.
“Moyo wanga unali wodzidalira. Kukumana ndi amishonale kunapereka nyonga imene ndinafunikira kuti ndisinthe. Mwa iwo ndinaonamo chimwemwe chenicheni osati chonyenga.”—J. K., Japan.
“Amishonale a Dziko Lachikristu anali ndi moyo wapamwamba. Antchito anali kuyeretsa nyumba, kuphika, kuchapa zovala, kusamalira pabwalo, ndi kuwayendetsera galimoto. Ndinadabwa kuona amishonale a Gileadi akumachita bwino lomwe ntchito yawo ya m’nyumba, pamenenso anali kuthandiza anthu akumaloko kuphunzira za Ufumu wa Mulungu.”—S. D., Thailand.
“Alongo ochita umishonale ankakwera njinga pokaonana ndi anthu ngakhale pamene kunatentha kuposa [madigiri 46 a Celsius]. Ubwenzi wawo ndi kusakondera, ndiponso chipiriro chawo, zinandithandiza kudziŵa choonadi.”—V. H., India.
“Amishonalewo sanadzione kukhala apamwamba. Modzichepetsa iwo anatengera kakhalidwe ka anthu akumaloko ndi kulandira mikhalidwe yawo yaumphaŵi. Anadza kudzatumikira, chotero sanadandaule konse koma nthaŵi zonse anaonekera kukhala okondwa ndi okhutira.”—C. P., Thailand.
“Sanasukulutse choonadi cha Baibulo. Komanso sanapangitse anthu akumaloko kulingalira kuti mbali zonse za mwambo wawo zinali zolakwa kapena kuti ayenera kugwiritsira ntchito njira za Akumadzulo. Sanapangitse konse ena kudziona kukhala otsika kapena osayenera.”—A. D., Papua New Guinea.
“Mosiyana ndi amishonale a Dziko Lachikristu, iye anali wofunitsitsa kukhala pansi atapinda miyendo, Mwachikoreya, pamene tinali pa phunziro lathu la Baibulo. Anali wofunitsitsa kulaŵa zakudya zathu Zachikoreya. Chikondi chimene ndinali nacho pa iye chinandithandiza kupita patsogolo.”—S. K., Korea.
“Ndinali ndi zaka khumi ndipo ndinkaŵeruka kusukulu masana. Mmishonale wina ankandipempha kutsagana naye muutumiki wakumunda masana. Anandiphunzitsa malamulo amkhalidwe a Baibulo ambiri ndipo anakhomereza chiyamikiro chenicheni mwa ine kaamba ka gulu la Yehova.”—R. G., Colombia.
“Anandiphunzitsa kumamatira kumagawo, ndikumachita zimene zinafunikira kuchitidwa popanda kudandaula. Ndikuyamika Yehova ndi Yesu Kristu kuchokera pansi pa mtima chifukwa cha kutitumizira amishonale.”—K. S., Japan.
[Chithunzi patsamba 23]
Amishonale ophunzitsidwa ku Gileadi akumaiko 16 akusimba zokumana nazo pa misonkhano yachigawo yaposachedwapa