Zimene Baibulo Limanena
Kodi Chidzachitike N’chiyani pa Tsiku Lachiweruzo?
Baibulo limanena kuti Mulungu ‘wakhazikitsa tsiku limene akufuna kudzaweruza dziko lapansi kumene kuli anthu.’ (Machitidwe 17:31) Koma anthu ambiri akamva za Tsiku Lachiweruzo amaopa kwambiri. Kodi inunso mumaopa?
NGATI Tsiku Lachiweruzo limakuchititsani mantha, dziwani tsiku limeneli ndi labwino kwambiri chifukwa lidzabweretsa madalitso aakulu kwa anthu, kuphatikizapo amene anafa. (Mateyo 20:28; Yohane 3:16) N’chifukwa chiyani Tsiku Lachiweruzo ndi lofunika? Kodi chidzachitike n’chiyani pa “tsiku” limeneli?
Tsiku Lachiweruzo ndi Lofunika Kwambiri
Mulungu analenga anthu n’kuwaika padziko lapansi kuti akhale ndi moyo kosatha, osati ndi cholinga choti awayese ndipo kenako n’kuwatengera kumalo ena. Komabe, ngakhale kuti anthu awiri oyamba anali angwiro, iwo sanamvere Mulungu. Choncho, anataya mwayi umene anali nawo wokhala ndi moyo kosatha ndipo anabweretsa uchimo ndi imfa kwa ana awo onse.—Genesis 2:15-17; Aroma 5:12.
Tsiku Lachiweruzo lidzakhala la zaka 1,000 ndipo panthawi imeneyi anthu adzakhala ndi mwayi wosonyeza ngati ali oyenerera kupatsidwa moyo wofanana ndi umene Adamu ndi Hava anali nawo asanachimwe.a Onani kuti lemba la Machitidwe 17:31, limene taligwira mawu pamwambapa, limanena kuti zimene zidzachitike pa Tsiku Lachiweruzo zidzakhudza anthu onse okhala padziko. Anthu amene adzachite zabwino panthawiyi adzalandira dziko lapansi ndipo adzakhala ndi moyo wosatha komanso wosangalala. (Chivumbulutso 21:3, 4) Choncho Tsiku Lachiweruzo ndi lofunika kuti cholinga choyambirira chimene Mulungu anali nacho polenga anthu ndi dziko lapansi chikwaniritsidwe.
Mulungu wasankha Yesu Khristu kuti adzaweruze anthu pa tsiku limeneli. Baibulo limanena kuti Yesu “adzaweruza amoyo ndi akufa.” (2 Timoteyo 4:1) Kodi “amoyo” amenewa ndi ndani? Nanga akufa adzakhalanso bwanji ndi moyo ‘m’dziko lapansi kumene kuli anthu’?
Yesu Adzaweruza “Amoyo”
Tatsala pang’ono kufika kumapeto kwa dziko la Satanali, pamene Mulungu adzawononga anthu onse oipa ndi kuchotsa zinthu zonse zoipa. “Amoyo” amene adzaweruzidwe ndi anthu amene adzapulumuke mapeto a dongosololi.—Chivumbulutso 7:9-14; 19:11-16.
Panthawi ya chiweruzo imeneyi, yomwe idzakhale ya zaka 1,000, Khristu Yesu limodzi ndi anthu okwana 144,000 amene adzaukitsidwe n’kukakhala kumwamba, adzalamulira dziko lapansi. Anthu amenewa adzakhala mafumu ndi ansembe ndipo adzathandiza anthu kupindula ndi nsembe ya dipo ya Yesu. Pang’onopang’ono anthu okhulupirika adzakhala angwiro.—Chivumbulutso 5:10; 14:1-4; 20:4-6.
Mu Tsiku Lachiweruzo, Satana ndi ziwanda sadzaloledwa kusokoneza anthu kuti azichita zoipa. (Chivumbulutso 20:1-3) Komabe, kumapeto kwa Tsiku Lachiweruzo, Satana adzaloledwa kuyesa munthu aliyense. Anthu onse amene adzakhale okhulupirika kwa Mulungu adzasonyeza kuti apambana chiyeso chimene Adamu ndi Hava anagonja nacho m’munda wa Edeni. Iwo adzalandira moyo wosatha padziko lapansi la Paradaiso. Anthu onse amene sadzafuna kumvera Mulungu adzawonongedwa limodzi ndi Satana ndiponso ziwanda zake.—Chivumbulutso 20:7-9.
Kuweruza “Akufa”
Baibulo limanena kuti pa Tsiku Lachiweruzo akufa “adzaimirira” kapena kuti adzauka. (Mateyo 12:41) Yesu ananena kuti “idzafika nthawi pamene onse ali m’manda a chikumbutso adzamva mawu ake ndipo adzatuluka. Amene anali kuchita zabwino adzauka kuti alandire moyo, amene anachita zoipa adzauka kuti aweruzidwe.” (Yohane 5:28, 29) Lembali silikunena za mizimu ya anthu amene anafa. Anthu akufa sadziwa kalikonse ndipo alibe mzimu umene umapulumuka iwo akafa. (Mlaliki 9:5; Yohane 11:11-14, 23, 24) Yesu adzaukitsa anthu amene anagona mu imfa kuti akhalenso ndi moyo padziko lapansi.
Kodi anthu oukitsidwa adzaweruzidwa potengera zinthu zimene anachita asanamwalire? Ayi, chifukwa Baibulo limaphunzitsa kuti “munthu amene wafa wamasuka ku uchimo wake.” (Aroma 6:7) Choncho, mofanana ndi anthu amene adzapulumuke mapeto a dongosolo lino, iwo adzaweruzidwa “mogwirizana ndi ntchito” zimene adzachite mu Tsiku Lachiweruzo. (Chivumbulutso 20:12, 13) Malinga ndi chiweruzo chimene adzalandire mogwirizana ndi zochita zawo m’tsiku limeneli, Baibulo limanena kuti ena adzauka kuti alandire moyo wosatha ndipo ena adzauka kuti aweruzidwe, kapena kuti awonongedwe. Kwa anthu ambiri amene adzaukitsidwe, umenewu udzakhala mwayi wawo woyamba wophunzira za Yehova Mulungu ndiponso malamulo ake. Iwo adzakhala ndi mwayi wochita zimene Mulungu amafuna ndiponso wolandira moyo wosatha padziko lapansi.
Palibe Chifukwa Choopera Tsiku Lachiweruzo
Pa Tsiku Lachiweruzo anthu adzalandira malangizo kuchokera kwa Mulungu ndipo adzakhala ndi mwayi wogwiritsa ntchito zimene akuphunzira komanso wodalitsidwa ndi Mulungu. Taganizirani mmene mudzasangalalire mukadzakumananso ndi achibale anu komanso anzanu omwe adzaukitsidwe ndiponso kuona kuti inu ndi anzanuwo mukusintha n’kukhala angwiro.
Kumapeto kwa Tsiku Lachiweruzo, Mulungu adzalola Satana kuyesa anthu onse. Koma palibe chifukwa choopera zimenezi. Tsiku Lachiweruzo likamadzatha, anthu onse adzakhala ali okonzeka kukumana ndi chiyeso chomaliza chimenechi. Tsiku Lachiweruzo lidzathandiza kukwaniritsa chifuniro cha Mulungu chochotsa mavuto onse obwera chifukwa cha kuchimwa kwa Adamu ndi Hava.
[Mawu a M’munsi]
a M’Baibulo mawu akuti “tsiku” angatanthauze nthawi yaitali mosiyanasiyana. Mwachitsanzo, onani Genesis 2:4.
KODI MWAGANIZIRAPO IZI?
● Kodi n’chiyani chidzachitike pa Tsiku Lachiweruzo?—Machitidwe 17:31.
● Kodi ndi ndani amene adzaweruzidwe?—2 Timoteyo 4:1.
● Kodi Tsiku Lachiweruzo lidzatenga nthawi yaitali bwanji?—Chivumbulutso 20:4-6.
[Mawu Otsindika patsamba 11]
Taganizirani mmene mudzasangalalire mukadzakumananso ndi achibale anu komanso anzanu omwe adzaukitsidwe
[Zithunzi patsamba 10]
Mu ulamuliro wa Khristu, anthu amene anafa adzaukitsidwa n’kukhalanso ndi moyo padziko lapansi la paradaiso