Tsiku Lachiweruzo Nthaŵi ya Chiyembekezo!
NGATI lingaliro la tsiku lachiweruzo limakuchititsani mantha, bwanji osasanthula zimene Baibulo limanena ponena za ilo? Mwachitsanzo, kodi nzowona kuti pamene Mulungu amapereka chiweruzo pa ochimwa, iwo amaponyedwa m’moto wa helo?
Eya, chochitika choyamba kulembedwa cha chiweruzo chaumulungu chinali pachiyambi penipeni pa mbiri ya munthu. Adamu ndi Hava adali ndi mwaŵi wakukhala ndi moyo kosatha pa dziko lapansi laparadaiso. (Genesis 1:26-28; 2:7-9, 15-25) Komabe, iwo anachimwa, ndipo anayang’anizana ndi chiweruzo choopsa cha Mulungu. Ndi chotulukapo chotani? Mulungu anawalanda mphatso ya moyo. M’mawu ena, iwo anafa. Mulungu adawauza kuti: ‘M’thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka; chifukwa kuti m’menemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.’—Genesis 3:16-19.
Chimenechi chinali chiweruzo choopsa, koma chinali cholungama. Ndipo mosakaikira icho sichinaphatikizepo moto wa helo. Pamene Adamu ndi Hava anamwalira, iwo anabwerera ku fumbi. Analeka kukhalako. Kulibe pamene Baibulo limapereka lingaliro lakuti mbali ya Adamu kapena ya munthu wina aliyense inapulumuka paimfa kukazunzidwa kwinakwake kwa umuyaya wonse. Mmalomwake, timaŵerenga kuti: ‘Amoyo adziŵa kuti adzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi.’—Mlaliki 9:5.
Kodi munalikudziŵa kuti Baibulo limanena zimenezi? Ndiponso, kodi munalikudziŵa kuti Baibulo silimagwiritsira ntchito konse mawu akuti “moyo wosakhoza kufa”? Mmalomwake, ilo limati: “Moyo umene umachimwa, udzafa.” (Ezekieli 18:4, King James Version) Izi nzogwirizana kotheratu ndi lamulo lamakhalidwe abwino la Baibulo lakuti: “Malipiro a uchimo ndiwo imfa.” (Aroma 6:23, KJ) Lamulo limeneli limatiyambukira tonsefe. Tonsefe ndife mbadwa za Adamu wochimwa, choncho tonsefe timachimwa ndipo timalandira malipiro a uchimo, imfa. Monga momwe Baibulo limanenera kuti: “Mwa munthu mmodzi uchimo unaloŵa m’dziko, ndi imfa mwa uchimo; ndipo motero imfa inafalikira pa anthu onse, chifukwa cha chimenecho onse anachimwa.” (Aroma 5:12, KJ) Tsiku Lachiŵeruzo ndilo mbali yaikulu ya makonzedwe a Mulungu akutipulumutsa ku mkhalidwe umenewu.
Maziko a Tsiku Lachiweruzo
Malinga nkunena kwa Baibulo, zinali pafupifupi zaka 2,000 zapitazo pamene Mulungu anakhazikitsa maziko a zimene zidzachitika pa Tsiku Lachiweruzo. Ndipamene Yesu anadza padziko lapansi ndi kupereka moyo wake waumunthu wangwiro mmalo mwathu. Yesu mwini yekha anafotokoza kuti: ‘Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asataike, koma akhale nawo moyo wosatha.’—Yohane 3:16.
Ngati tisonyeza chikhulupiriro mwa Yesu, timapindula ndi nsembe yake ngakhale tsopano mwanjira yauzimu. Mulungu amakhululuka machimo athu ndi kutilola kumfikira iye. (Yohane 14:6; 1 Yohane 2:1, 2) Koma tidakali opanda ungwiro, ochimwa, ndipo pokhala otero, timadwalabe mwakuthupi ndipo potsirizira pake nkumwalira. Sitinakhalebe ndi moyo wosatha umene Yesu analonjeza. Uwo udzabwera monga chotulukapo cha Tsiku Lachiweruzo.
Tsiku la Kuweruza
Mtumwi Yohane anawona masomphenya a Tsiku Lachiweruzo, ndipo analilongosola motere: “Ndinawona chimpando chachifumu chachikulu choyera, ndi yemwe anakhalapo, amene dziko lapansi ndi thambo zinachoka pankhope pake; ndipo sipanapezeka malo awo. Ndipo ndinawona akufa, aang’ono ndi aakulu, akuimirira pamaso pa Mulungu; ndipo mabuku anatsegulidwa: ndipo bukhu lina linatsegulidwa, limene liri bukhu la moyo: ndipo akufawo anaweruzidwa mwa zinthu zimene zinalembedwa m’mabukuwo, malinga ndi ntchito zawo.”—Chibvumbulutso 20:11, 12, KJ.
Inde, mogwirizana ndi masomphenya a Yohane, Tsiku Lachiweruzo lidzatsogozedwa ndi Mulungu iyemwini. Koma winawake akuloŵetsedwamo. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “[Mulungu] anaika tsiku, m’limene adzaweruza dziko m’chilungamo mwa munthuyo amene wamuika.” (Machitidwe 17:31, KJ)Kodi munthuyo anali ndani? Yesu, amene iye mwini anati: “Atate saweruza munthu aliyense, koma waika kuweruza konse pa Mwanayo.” (Yohane 5:22, KJ) Choncho Yesu adzakhala Woweruza woikidwa ndi Mulungu pa Tsiku Lachiweruzo.
Iyi ndimbiri yabwino kwa anthu. Uthenga Wabwino umavumbula Yesu kukhala munthu wachifundo chachikulu. Iye siwodzikweza kapena wotsendereza koma ‘wofatsa ndi wodzichepetsa mtima.’ (Mateyu 11:29; 14:14; 20:34) Ndife achimwemwe kukhala m’manja mwa woweruza woteroyo.
Kodi Lidzakhalako Liti?
Komabe, kodi ndiliti pamene Tsiku la Kuweruza lidzakhalako? Chibvumbulutso chimati lidzakhala pamene “dziko lapansi ndi thambo [zachoka].” Izi zimatikumbutsa mawu a mtumwi Petro akuti: ‘Miyamba ndi dziko la masiku ano, ndi mawu omwewo zaikika kumoto, zosungika kufikira tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osapembedza.’ (2 Petro 3:7) Kodi dziko lapansi lenilenili lidzatenthedwa? Ayi, Baibulo nlomvekera bwino pa mfundo imeneyi. Dziko lapansi lenileni silidzawonongedwapo konse. “Dziko lapansi . . . sili[dza]chotsedwapo kunthaŵi zonse.” (Salmo 104:5, KJ) Mawu a Petro apambuyo ndi apatsogolo amasonyeza kuti ndidongosolo lazinthu liripoli la dziko losapembedza limene lidzawonongedwa. Anthu osapembedza, osati pulaneti Dziko Lapansi, ndiwo adzafafanizidwa.—Yohane 12:31; 14:30; 1 Yohane 5:19.
Anthu osapembedza ameneŵa adzawonongedwa pa nkhondo imene Baibulo limaitcha Armagedo—imene, monga momwe magazini ano asonyezera kaŵirikaŵiri, idzachitika posachedwapa. (Chibvumbulutso 16:14, 16) Pambuyo pake, Satana weniweniyo adzaponyedwa m’phompho ndi kutsekerezedwa kudodometsa anthu kwa zaka chikwi, ndipo zaka chikwi zimenezi ndizo nyengo yeniyeniyo ya Tsiku Lachiweruzo. (Chibvumbulutso 19:17–20:3) Kodi nchiyani chimene chidzachitika kwa okhulupirika pamene anthu osapembedza awonongedwa pa Armagedo? Iwo adzapulumuka kuloŵa m’Tsiku Lachiweruzo. Timaŵerenga kuti: ‘Oongoka mtima adzakhala m’dziko [lapansi]. Angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.’—Miyambo 2:21, 22.
Pochirikiza zimenezi, Baibulo limatiuza za ‘khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe’ omwe adzawoneka padziko lapansi Armagedo isanaulike. Iwoŵa ‘akutuluka m’chisautso chachikulu’; m’mawu ena, iwo akupulumuka mapeto a dziko lino losapembedza monga momwe Nowa anapulumukira mapeto a dziko la m’tsiku lake. (Chibvumbulutso 7:9-17; 2 Petro 2:5) Kodi munalikudziŵa kuti khamu lalikulu la mitundu yonse limeneli la Akristu okangalika liripo ngakhale tsopanoli? Iwoŵa amayembekezera kupulumuka chisautso chachikulu ndi kukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi. Kukhalapo kwawo kuli umboni wotsimikizirika wa kuyandikira kwa Tsiku Lachiweruzo.
Kodi Ndani Amene Adzaweruzidwa?
Khamu lalikulu limeneli lidzaweruzidwa pa Tsiku Lachiweruzo. Koma sadzakhala okha. Cholembedwa cha Yohane chimapitiriza kuti: “Nyanja inapereka akufa omwe anali m’menemo; ndipo imfa ndi helo zinapereka akufa omwe anali mwa izo: ndipo iwo anaweruzidwa munthu aliyense malinga ndi ntchito zawo.” (Chibvumbulutso 20:13, KJ) Umenewu ndiumboni wowonjezereka wakuti anthu samazunzika kosatha m’helo. Ngati helo amapereka akufa okhala m’menemo, kodi ndimotani mmene wina angakhalire m’menemo ku umuyaya wonse? Kwenikweni, helo wa Baibulo ali manda wamba a anthu, kumene akufa amakhala opanda chikumbukiro akuyembekezera chiukiriro. Patsiku Lachiweruzo, helo adzachotsedwamo akufa ake onse.—Mlaliki 9:10.
Kodi ndani amene adzaukitsidwa kwa akufa pa Tsiku Lachiweruzo? Mtumwi Paulo anati: “Padzakhala chiukiriro cha akufa, ponse paŵiri olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15, KJ) Chotero, atumiki a Mulungu okhulupirika, “olungama,” adzaukitsidwa. Koma adzateronso ena osaŵerengeka, “osalungama.” Mowonekeratu, chiukirirocho chidzaphatikizapo onse amene anafa ndipo adakali m’manda—kusiyapo alionse amene machimo awo anali aakulu kwakuti Mulungu anawaweruza kale kukhala osayenerera moyo khotheratu.—Mateyu 12:31.
Chiweruzocho
Komabe, kodi nchiyani chimene chidzachitikira khamu lalikulu la opulumuka ndi oukitsidwa pa Tsiku Lachiweruzo? Baibulo limati: “Akufa anaweruzidwa mwa zinthu zolembedwa m’mabukuwo, malinga ndi ntchito zawo.” Iyi ndinthaŵi yakupenda kosamalitsa. Onse ofunitsitsa kuchita mogwirizana ndi ‘zinthuzo zolembedwa m’mabukuwo’—zimene mowonekeratu ndiziyeneretso za Mulungu kaamba ka anthu panthaŵiyo—adzalembedwa mu “bukhu la moyo.” (Chibvumbulutso 20:12, KJ) Iwo adzakhala panjira yakupeza moyo wosatha!
Ndiyeno, potsirizira pake, imfa yansembe ya Kristu idzabweretsa mapindu akuthupi! Awo ondandalitsidwa m’bukhu la moyo panthaŵi imeneyo sadzagweranso m’kudwala ndi imfa. Mmalomwake, adzabwezeretsedwa pang’onopang’ono ku ungwiro waumunthu, ndi moyo wosatha wolonjezedwa kwa osonyeza chikhulupiriro mwa Yesu. Ha, nchiyembekezo chochititsa chidwi chotani nanga! Chikhalirechobe, ena mwachiwonekere adzakana kumvera ‘zinthuzo zolembedwa m’mabukuwo.’ Kodi nchiyani chidzachitika kwa iwo? Iwo sadzapeza moyo wamuyaya. Mmalomwake, lembalo limati: “Aliyense amene sanapezeka m’bukhu la moyo anaponyedwa m’nyanja ya moto.”—Chibvumbulutso 20:15, KJ.
Kodi umenewo ndiwo moto wa helo umene Chikristu Chadziko chimalankhulapo? Ayi, popeza kuti m’vesi loyambirira, tiŵerenga kuti: “Imfa ndi helo zinaponyedwa m’nyanja ya moto. Iyi ndiyo imfa yachiŵiri.” (Chibvumbulutso 20:14, KJ) Ngati helo aponyedwa m’nyanja ya moto, nyanjayo singakhale moto wa helo. Ndiponso, imfa sichinthu chenicheni chimene chingagwidwe, chimene chingatoledwe ndi kuponyedwa kwinakwake. Choncho nyanja ya moto iyenera kukhala yophiphiritsira. Chiyani? Baibulo limati: “Iyi ndiyo imfa yachiŵiri.” Pamene imfa ndi Hade ziponyedwa m’nyanja ya moto, izo “zifa,” kuleka kukhalako. Mofananamo, anthu opanduka amene pomalizira pake afika kumeneko amafa, kapena kuleka kukhalako. Motero, imeneyi ndiimfa yachiŵiri, yopanda chiyembekezo cha chiukiriro.
Tsiku Lachiweruzo—Nthaŵi ya Chiyembekezo
Choncho pamene tilingalira za Tsiku Lachiweruzo, sitiyenera kuchititsidwa mantha kapena kuipidwa. Tsiku Lachiweruzo ndinthaŵi ya chiyembekezo, nthaŵi yakubwezeretsera anthu moyo wosatha wotaidwa ndi Adamu. Mvetserani madalitso amene lidzabweretsa kwa amene adzaweruzidwa kukhala okhulupirika: ‘Taonani, chihema cha Mulungu chiri mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.’—Chibvumbulutso 21:3, 4.
Podzafika kumapeto kwa Tsiku Lachiweruzo la zaka chikwi, anthu okhulupirika a ku mbali zonse za dziko lapansi pomalizira pake adzakhala angwiro. Iwo ‘adzakhala amoyo’ m’lingaliro lokwanira, ndipo Tsiku Lachiweruzo lidzakhala litakwaniritsa chifuno chake. (Chibvumbulutso 20:5) Ndiyeno, Baibulo limati, Satana adzaloledwa kupita kwa anthu kwanthaŵi yotsirizira. (Chibvumbulutso 20:3, 7-10) Awo amene adzamtsutsa panthaŵi yotsirizira imeneyi adzasangalala ndi kukwaniritsidwa kotheratu kwa lonjezo la Baibulo lakuti: ‘Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.’—Salmo 37:29.
Ha, ndimakonzedwe okongola chotani nanga amene Tsiku Lachiweruzo liri! Ndipo nkwabwino chotani nanga kuti tikhoza kulikonzekera ngakhale tsopano lino, mwakuphunzira Baibulo, kuphunzira chifuniro cha Mulungu, ndi kugwiritsira ntchito chifuniro chaumulungu chimenechi m’miyoyo yathu! Nzosadabwitsa kuti wamasalmo anasonyeza chisangalalo polingalira za chiweruzo cha Mulungu pamene analemba kuti: ‘Kumwamba kukondwere nilisekerere dziko lapansi; nyanja ibume mwa kudzala kwake: munda ukondwere ndi zonse ziri m’mwemo; pamenepo mitengo yonse ya kunkhalango idzafuula mokondwera; pamaso pa Yehova, pakuti akudza; pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi.’—Salmo 96:11-13.