Anthu Achilungamo Zinthu Zimawayendera
“Ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.”—Luka 12:15.
NDALAMA n’zofunika kwambiri pa moyo wathu. Mwachitsanzo, timafunika ndalama kuti tikwaniritse udindo umene Mulungu anatipatsa wosamalira mabanja athu.—1 Timoteyo 5:8.
Koma bwanji ngati munthu wafika pokonda kwambiri ndalama, moti cholinga chake pa moyo n’kupeza ndalama basi? Munthu wotere amayamba kuchita zinthu zachinyengo. Ndipo amadzazindikira mochedwa kuti kuchita zimenezi n’kosathandiza. Ndiponso, mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena, kukonda ndalama kumabweretsa mavuto ambiri.—1 Timoteyo 6:9, 10.
M’ndime zotsatirazi muli zitsanzo za anthu anayi omwe amaona kuti pali zinthu zina zofunika kwambiri kuposa kukhala ndi ndalama. Zinthu zimenezi ndi:
Kudzisungira Ulemu
“Zaka zingapo zapitazo, ndinakambirana ndi munthu wina yemwe ankafuna kugula inshuwalansi ya ndalama zambiri. Chifukwa chopeza kasitomala ameneyu, kampani ya Inshuwalansiyo ikanandipatsa ndalama zambiri zondithokoza. Koma kasitomalayo anandiuza kuti ngati ndikufuna ndimuthandize, ndimupatse hafu ya ndalama zomwe kampaniyo ikanandipatsa, apo ayi talepherana. Zimene iye ankafunazi zinali zopanda nzeru komanso zosemphana ndi malamulo, ndipo ndinamuuza mosapita m’mbali kuti sindingachite zimenezo.
“Pofuna kumuthandiza kuona kuti zimene akufunazo n’zosayenera, ndinamufunsa ngati iyeyo angalole kuuza munthu wachinyengo zinthu zokhudza ndalama zimene ali nazo komanso zinthu zina zachinsinsi zokhudza iyeyo. Ndinabwereza kumuuza kuti sindingachite zimene iye akufunazo ndiponso ndinamuuza kuti akadzakhala wokonzeka kuchita zinthu mwachilungamo adzandipeza. Kuyambira nthawi imeneyo sanaonekenso.
“Ndikanachita zimene ankafunazo, ndikanawononga mbiri yanga ndipo anthu akanasiya kundilemekeza monga Mkhristu. Ndiponso ndikanamvera zofuna za munthu wachinyengoyu, ndikanakhala kapolo wake.”—Anatero Don, wa ku United States.
Mtendere wa Mumtima
Monga mmene nkhani yoyambirira ija yasonyezera, Danny anauzidwa kuti apatsidwa ndalama zambiri ndi mwini fakitaleyo ngati atakanena kwa mabwana ake zabwino zokhazokha zokhudza katundu amene fakitaleyo imapanga. Kodi iye anatani?
Iye anati: “Ndinathokoza munthuyo chifukwa chondiitanira chakudya koma ndinamubwezera envulopuyo. Anandikakamiza kuti ndilandire ndalamazo komanso anandilonjeza kuti fakitale yake ikavomerezedwa andipatsa ndalama zinanso, koma ndinakanitsitsa.
“Ndikanalandira ndalamazo, bwenzi ndikungokhalira kuda nkhawa kuti tsiku lina zidzaululika kuti ndinachita zachinyengo. Ndipotu patapitadi nthawi, bwana wanga anadzadziwa za nkhaniyi. Ndinasangalala kwambiri kuti ndinachita zinthu mwachilungamo. Ndinakumbukira lemba la Miyambo 15:27, limene limati: ‘Munthu wopeza phindu mwachinyengo amabweretsa tsoka panyumba pake, koma wodana ndi ziphuphu ndi amene adzakhalebe ndi moyo.’”—Anatero Danny, wa ku Hong Kong.
Banja Losangalala
“Ndili ndi kampani yanga ya zomangamanga. Ngati nditafuna, ndikhoza kumabera makasitomala komanso kuzemba msonkho. Koma ndikuona kuti banja langa lapindula kwambiri chifukwa chakuti ndimayesetsa kuchita zinthu mwachilungamo.
“Timafunika kukhala anthu achilungamo pa chilichonse, osati kuntchito kapena pa bizinezi pokha. Munthu ukadziwa kuti mkazi kapena mwamuna wako amatsatira malamulo a Mulungu moti sangachite zinthu zachinyengo zivute zitani, umamudalira kwambiri. Ndipo mkazi kapena mwamuna wako akadziwa kuti umayesetsa kutsatira chilungamo nthawi zonse ngakhale pamene zinthu zavuta, sada nkhawa kuti ukumana ndi mavuto chifukwa chochita chinyengo.
“Munthu akhoza kukhala ndi kampani yaikulu kwambiri padziko lonse koma n’kukhala ndi banja losasangalala. Ndine wa Mboni za Yehova ndipo ndimaona kuti kutsatira mfundo za m’Baibulo kumathandiza kuti banja liziyenda bwino komanso lisamasowe kanthu. Ndimakhala ndi nthawi yosangalala ndi banja langa, popanda kusokonezedwa ngakhale pang’ono ndi mtima wokonda kwambiri ndalama.”—Anatero Durwin, wa ku United States.
Ubwenzi Wabwino ndi Mulungu
“Ndikapita kukagula katundu wa kampani yathu, anthu ena amandiuza kuti ndikawagula katundu wawo andipatsa ndalama zoti zikhale zanga m’malo moichotsera kampani yathuyo mtengo wa katunduyo. Koma ndinkaona kuti kumeneku ndi kubera kampani yathu.
“Ndimalandira malipiro ochepa kwambiri ndipo ngati nditamalandira ndalama zimene anthuwa amafuna kundipatsa zikhoza kundithandiza kwambiri. Koma ndimakana ndalamazo chifukwa ndimaona kuti kukhala ndi chikumbumtima chabwino komanso kukondweretsa Yehova Mulungu ndi kofunika kwambiri. Choncho, ndimayesetsa kutsatira lemba la Aheberi 13:18, limene limatilimbikitsa ‘kuchita zinthu zonse moona mtima.’”—Anatero Raquel, wa ku Philippines.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 9]
Mfundo za m’Baibulo Zimene Tingatsatire Pochita Bizinezi
Mayiko osiyanasiyana amatsatira mfundo zosiyanasiyananso pochita bizinezi. Komabe, mfundo za m’Baibulo zikhoza kuthandiza anthu a m’mayiko onsewa pochita bizinezi. Taganizirani mfundo 6 zotsatirazi:
Kupewa Kunena Bodza
Mfundo ya m’Baibulo: “Musamanamizane.”—Akolose 3:9.
Kusunga Lonjezo
Mfundo ya m’Baibulo: “Tangotsimikizani kuti mukati Inde akhaledi Inde, ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi.”—Mateyu 5:37.
Kusunga Chinsinsi
Mfundo ya m’Baibulo: “Usaulule chinsinsi cha munthu wina.”—Miyambo 25:9.
Kukana Ziphuphu
Mfundo ya m’Baibulo: “Usalandire chiphuphu chifukwa chiphuphu chimachititsa khungu anthu amaso akuthwa.”—Ekisodo 23:8.
Kuganizira Ena
Mfundo ya m’Baibulo: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.”—Mateyu 7:12.
Kutsatira Malamulo
Mfundo ya m’Baibulo: “Perekani kwa onse zimene amafuna. Amene amafuna msonkho, m’patseni msonkho.”—Aroma 13:7.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 9]
Zinthu Zokuthandizani Kupewa Chinyengo Pochita Bizinezi
● Dziwiranitu Zinthu Zofunika Kwambiri. Mwachitsanzo, kodi chofunika kwambiri n’chiyani kwa inu pakati pa kukhala ndi chuma chambiri ndi kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu?
● Muzidziwiratu Zochita Kapena Zonena. Yesani kuganizira zinthu zimene munganene kapena kuchita ngati munthu wina akufuna kuti muchite zachinyengo.
● Ena Azidziwiratu Mfundo Zimene Mumatsatira. Mukamayamba kuchita bizinezi ndi anthu ena, athandizeni mosamala kudziwa mfundo zimene mumatsatira.
● Muzipempha Malangizo kwa Ena. Ngati simukudziwa chochita pamene munthu wina akufuna kuti muchite zachinyengo, pemphani malangizo kwa anthu ena amene amatsatira mfundo za m’Baibulo.
[Chithunzi patsamba 8]
Munthu amene amachita zinthu zachilungamo amakhala ndi mtendere wa mumtima