Mutu 7
Kodi Pali Mizimu Yoipa?
1. (a) Kodi Yesu anakhulupirira kuti mizimu yoipa iripo? (b) Kodi Yesu anamucha Mdierekezi kukhala ciani?
YESU KRISTU, amene anadza pa dziko lapansi kucokera ku malo a mizimu, anakudziwa kukhalapo kwa mizimu yoipa. Inu mungakumbukire kuti iye nthawi zonse anali kulankhula za Mdierekezi, ndi kuti anamucha iye “atate wabodza” ndi “wambanda.” (Yohane 8:44) Kaamba ka cinjirizo lathu mu nthawi iyi pamene kunama ndi kuphana zikumaonjezerekaonjezereka, ife tingacite bwino kuipenda nkhani iyi.
2. (a) Mosiyana ndi zimene Yesu anaziphunzitsa, kodi anthu ena amakhulupirira kuti Mdierekezi ndi ciani? (b) Kodi ndi cokumana naco cotani cimene Yesu anakhala naco ndi Mdierekezi?
2 Ndithudi, anthu ambiri samakhulupirira kuti pali mizimu yoipa. Ngakhale ena amene amanena kuti amagwiritsira nchito Baibulo amanena kuti Satana Mdierekezi wangokhala kokha mkhaklidwe wa kuipa, osati munthu wosaoneka wauzimu. Koma kodi zenizeni zimagwirizana ndi cikhulupiriro caoco? Bwanji ponena za cokumana naco ca Yesu Kristu mwiniyo pamene Mdierekezi anamuyesa iye? Baibulo limatiuza ife kuti Mdierekezi anamsonyeza Yesu maufumu onse a dziko lapansi ndipo anati kwa iye: “Zonse ndikupatsani Inu, ngati mudzagwa pansi ndi kundigwadira Ine.” Yesu anamyankha Mdierekeziyo kuti: “Coka satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, ndipo Iye yekha yekha udzamlambira.” Pamenepo Mdierekeziyo anamsiya Yesuyo.—Mateyu 4:1-11.
3. (a) Kodi ndi motani mmene cokumana naco cimeneco cimasonyezera kuti Mdierekezi sangakhale kokha mkhalidwe wa kuipa? (b) Pamenepo, nanga Satana Mdierekezi ndi ciani?
3 Mkati mwa cokumana naco cimeneco, kodi Yesu Kristu anali kuyesedwa ndi yani? Kodi anali munthu weniweni? Kapena ndi mkhalidwe waucimo cabe? Ngati iye anayesedwa ndi mkhalidwe wa ucimo cabe, kodi mkhalidwe umenewu unali kukhala mwa ndani? Kodi ucimo uwu unali mwa Yesu Kristu? Ngati kuli tero pamenepo sikungakhale koona kuti mwa iye munalibe ucimo. Komabe Baibulo, Mau a Mulungu a coonadi, limakupangitsa kukhala koonekera bwino kuti Yesu anali “wopanda coipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ocimwa.” (Ahebri 7:26) Baibulo limanenanso kuti: “Sanacite cimo, ndipo m’kamwa mwace sicinapezeka cinyengo.” (1 Petro 2:22) Cotero Yesu sakanakhala ndi “kuipa” kokhala mkati mwa iye mwini. Iye anali kulankhulana ndi colengedwa ca mzimu camoyo. Cotero Malemba limodzi ndi kulingalira kwanzeru zimakupangitsa kukhala komvekera bwino kuti Satana ali munthu weniweni wamoyo wokhala m’malo a mizimu.—1 Pet. 5:8.
MDIEREKEZI WODZIPANGA YEKHA
4. Kucokera ku zimene tikuzidziwa ponena za Mulungu, kodi ndi motani mmene tingakhalire otsimikizira kuti iye sakadalenga wina wace woipa?
4 Koma kodi Mdierekezi anafikira kukhalapo motani? Moonekera bwino, Mulungu ‘amene nchito yace iri yangwiro’ sakanamlenga wina wace amene anali woipa. (Deuteronomo 32:4) Iye sakanalenga zolengedwa zanzeru zimene sakanagwirizana nazo. Kuteroko kukanakhala kosiyana ndi kulingalira bwino ndi cikondi ca Mulungu.—Salmo 5:4-6 [5:5-7, Dy].
5. (a) Kodi ndi motani mmene colengedwa ca mzimu cimene cinafikira kukhala Mdierekezi cinakatengera kacitidwe kolakwa? (b) Kodi inali njoka cabe imene inaliika lingaliro la cipanduko m’maganizo mwa Hava?
5 Motero, mzimu wosaonekawo umene pambuyo pace unafikira kukhala Mdierekezi pa nthawi yina unayenera kukhala unali wangwiro, wopanda cirema monga colengedwa ca Mulungu, mofanana ndi mamiliyoni enawo a “ana a Mulungu “aungelo. (Yobu 38:7) Pamenepo, kodi iye anaipa bwanji? Mwamuna ndi mkazi oyambawo atalengedwa, colengedwa ca mzimu icico cinayamba kupandukira Mulungu. Ico cinayamba kucikulitsa cikhumbo cakuti cizilambiridwa ndipo motero cinamnyenga Adamu ndi Hava kuti apandukire Mulungu. Kodi cinacita bwanji zimenezi? Baibulo limasonyeza kuti njoka inalankhula ndi Hava, kumamuuza mkaziyo bodza. Mwa cotsatirapo cace iye sanamvere Mulungu. Pamenepo anamcititsa mwamunace kugwirizana naye mu kupandukira Mulungu kwaceko. Koma kodi ndani kwenikweni amene anaika ganizo la cipanduko m’malingaliro a Havayo? Kodi inali njoka wamba yopanda ziwalo za kulankhulira? Ai, panali wina wace kumbuyo kwa cinjokaco amene anacipangitsa ico kuonekera ngati cikulankhula. Ife timadziwa kuti anthu ena aluso angalankhule mau atapunamiza milomo yao, kumacita ngati kuti nyama imene yayandikana nawo kapena munthu wosalankula akulankhula. Ndi kosabvuta cotani nanga kwa munthu wokhala ndi mphamvu yoposa yaumunthu wosaonekayo mmene kungakhalire kucicita ici! Mulungu anampangtisa buru wa Balamu kulankhula. (Numeri 22:28) Mu Edene, Satana anagwiritsira nchito cinjoka. Ndipo motero Baibulo limamdziwikitsa Mdierekezi, kapena Satana, kukhala “njoka yakaleyo,” motero kukhala amene anaciyambitsa cipanduko ndi kuipa mu cilengedwe caponseponse.—Cibvumbulutso 12:9; 2 Akorinto 11:3.
6. Kodi ndi motani mmene colengedwa cangwiro cikanatembenukira ku kuipa?
6 Koma inu mungadabwe kuti, ngati mzimu wanzeru zapamwambamwamba uwu unalidi wangwiro, kodi ndi motani mmene unatembenukira ku kuipa pamene panalibe wina aliyense wakuuyesa uwo? Baibulo limayankha kuti kunali mwa kulingalira kwace pa zinthu zolakwika. (Yakobo 1:14, 15) Palibe cinthu colakwika mu kumaziona zinthu zimene zingakhale zotheka m’mikhalidwe yina. Mwacitsanzo, munthu amene ali m’nyumba ya wina angazione ndarama ziri pa tebulo. Kuthekera kwakuti azitenge ndi kuziika m’thumba lace kulipo. Koma, popeza kuti kuteroko kudzakhala kuba, iye sayenera kuyesa kulingalira kumene za ico. Kapena, ngati lingalirolo lidza m’maganizo mwace, iye ayenera kulicotsa ilo. Koma ngati alisunga lingalirolo m’maganizo mwace ndi kulilola ilo kukula, pamenepo cikhumbo colakwa cimakula. Posacedwa cimeneci cidzamsonkhezera iye ku kucita macitidwe oipa.
7. (a) Cotero ndi motani mmene colengedwa ca mzimu ici cinafikira kukhala coipa? (b) Pamenepo, ndani amene anampanga Satana Mdierekezi?
7 Kunalinso cimodzimodzi ndi colengedwa ca mzimu cangwiroco. Kuthekera kunalipo kwa kuwagwiritsira nchito anthu awiriwo pa cifuno ca iye mwini m’malo mwa kucita zimene Mulungu anazifuna. Monga wokhala ndi kuthekera kwa kucita zimene iye anafuna mwaufulu, iye sanangolingalira kokha komanso analephera kuzicotsa izo m’maganizo mwace, ndipo zinamtsogolera iye ku kucimwa. Monga momwe munthu amene poyambapo anali woona mtima angadzipangitse yekha kukhala mbala cifukwa ca kuba, coteronso colengedwa ca mzimu ici cinadzipangitsa cokha kukhala Satana mwa kumacita monga wotsutsana ndi Mulungu; ndipo anadzipangitsa iye mwini kukhala Mdierekezi mwa kumafikira kukhala womnamizira Mulungu, cifukwa cakuti cimeneco ndico cimene maina amenewo amatanthauza.
8. Kodi ncifukwa ninji sikunangokhala kuphonya cabe kumene Satana anakupangako?
8 Ndithudi, wina anganene kuti, “Kodi sikunangokhala kuphonya cabe kumene iye anakucita? Kodi iye sakanapepesa ndi kuithetsera nkhaniyo pamenepo?” Poyankha, tiyenera kukumbukira kuti munthu wangwiro ali wosiyana ndi ife. Pamene iye agwiritsira nchito maganizo ace monga momwe afunira, cosankha cimene amacipangaco sicimakhala cifukwa ca kuperewera kapena kupanda ungwiro. Anthu opanda ungwiro nthawi zonse amazipanga zolakwa cifukwa ca kuperewera kwa colowa. Iwo angazibvomereze zolakwa zao, kupepesa ndi kusintha kacitidwe kao. Koma pamene colengedwa cangiro cisankha kucimwa, ico cimakucita iko mwadala ndipo pambuyo pace sicitembenukira ku kumacita zabwino. Icico ndico cimene cinamcitikira uyo amene anadzipangitsa kukhala Mdierekeziyo.
ZOLENGEDWA ZINA ZA MIZIMU ZIMADZIPANGITSA ZOKHA KUKHALA ZIWANDA
9. Kodi ndi motani mmene ena a angelo oyera a Mulungu anadzipangira okha kukhala ziwanda?
9 Mdierekezi sanali colengedwa ca mzimu cokha cimene cinatembenukira ku kuipa ndi kusamvera. Mulungu anali atalenga ciwerengero cacikuru ca angelo oyera, mamiliyoni ambirimbiri. Danieli 7:10 amaibvumbula mbali yina ya iwo kukhala 100,000,000. Colembedwa ca Baibulo pa Genesis 6:1-5 cimalongosola kuti cigumula cisanadze ca mu tsiku la Nowa ena a “ana a Mulungu” a mzimu amenewa anali kudzibveka matupi monga anthu, ndiko kuti, anasiya malo ao kumwamba monga zolengedwa za mizimu nadzibveka matupi. Cifukwa ninji? Kuti akasangalale ndi zilakolako zaumunthu mwa kumakwatira ana akazi a anthu okongola. Aka kanali kacitidwe ka kusamumvera Mulungu, ndipo Baibulo limakagwirizanitsa ndi macitidwe a anthu a mu Sodomu ndi Gomora amene ‘anafunafuna thupi kuti aligwiritsire nchito mosakhala mwacibadwidwe.’ (Yuda 6, 7) Coteronso, kunali kotsutsana ndi cikhalidwe cao ca kumwamba kuti angelo azidza pansi kudzafunafuna matupi aumunthu kuti agonane nawo. Kacitidwe kaoko kanapereka zotsatirapo zoipa, kuphatikizapo ana aucilangwaleza, “amphamvu” ochedwa Anefili. Mwa macitidwe ao opanduka, ana a Mulungu amenewo a mizimu anadzisandutsa okha kukhala ziwanda nadziphatika okha ku mbali ya Mdierekezi, amene ali “mfumu ya ziwanda.”—Mateyu 9:34.
10. (a) Pamene cigumula ca m’tsiku la Nowa cinadza, kodi ndi ciani cimene cinawacitikira angelo osamverawo amene anali atakwatira ana akazi a anthu? (b) Kodi kuonjezereka kwa kucimwa kwa m’tsiku lathu lino kuyenera kutizindikiritsa ife za ciani?
10 Pamene cigumula ca pa dziko lonse ca mu tsiku la Nowa cinaononga anthu onse oipa, angelo osakhulupirika anawacotsa matupi ao aumunthuwo nabwerera ku malo a mizimu. Koma iwo sanaloledwe kuti akhale mbali ya gulu la Mulungu la angelo oyerawo. M’malo mwace, iwo anabindikiritsidwa mu mkhalidwe woluluzidwa wa mu mdima wauzimu. (2 Petro 2:4) Ciyambire Cigumulaco, Mulungu sanawalole angelo auciwanda amenewa kudzibveka matupi aumunthu monga momwe anacitira kalelo. Komabe iwo angagwiritsire nchito mphamvu yao yoopsayo pa amuna ndi akazi. Ndithudi, mwa cithandizo ca ziwanda zimenezi Satana ‘akumalisoceretsa dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu.’ (Cibvumbulutso 12:9) Kuonjezereka kwakukuru mu kulakwa kumene tikukuonaku pa dziko lonse lapansi lerolino kuyenera kutigalamutsira ife ku kufunika kwa kukhala amaso kuti tisasocezedwe nazo.
MDIEREKEZI ALI “WOLAMULIRA WA DZIKO ILI”
11 Kodi ndi malo otani amene Satana ali nawo ponena za mitundu yonse?
11 Nthawi zitatu m’bukhu la Baibulo la Yohane timawerenga za Ambuye Yesu Kristu kuti anamucha Mdierekezi kukhala “wolamulira wa dziko ili.” (Yohane 12:31; 14:30; 16:11, NW) Pa 2 Akorinto 4:4 iye akuchulidwapo kukhala “mulungu wa nthawi yino ya pansi pano.” Pamenepo, kodi cimeneci cimatanthauza kuti mitundu yonse ya pa dziko lapansi iri kulamuliridwa ndi Satana Mdierekezi? Baibulo limayankha kuti: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Motero Mdierekezi, monga “wolamulira wa dziko ili,” ali ndi cisonkhezero cacikuru pa anthu, cowapitirira iwo ndipo ngakhale kumawalamulira maboma a ndale za dziko.—Cibvumbulutso 16:13, 14.
12 (a) Malinga ndi kunena kwa Cibvumbulutso 13:1, 2, kodi Mdierekeziyo amapereka mphamvu ndi ulamuliro kwa ciani? (b) Kodi ndi motani mmene copereka ca Mdierekeziyo ca kwa Yesu cimatithandizira ife kucizindikira “cirombo” cimeneco? (c) Popeza kuti colembedwa conena za “cirombo” ca mu Cibvumbulutso 13:1, 2 ndi cija conena za zirombo za mu masomphenya a Danieli zonse ziwirizo zimanena za nyama za mitundu yofananayo, kodi nciani cimene “cirombo” cimeneco cikuphiphiritsira?
12 Ngati mutsegula Baibulo lanu pa Cibvumbulutso 12:9, mudzaona kuti Mdierekezi akulongosoledwa kukhala “cinjoka cacikuru.” Mu caputara cotsatirapoco, vesi 1 ndi 2, ife tikuuzidwa kuti cinjoka cacikuru ici, Mdierekezi, cinapereka mphamvu ndi mpando wacifumu ndi ulamuliro waukuru ku cimene cikuchedwa mophiphiritsira kukhala “cirombo” coturuka m’nyanja. Kodi “cirombo” cophiphiritsira cimeneci nciani? Eya, kodi Satanayo akulamulira ciani? Kodi nciani cimene analonjeza kuti adzampatsa Yesu Kristu? “Maufumu onse a dziko lokhalamo anthu.” (Luka 4:5-8) Yesu mwamsanga anakana mphatsoyo, koma iye sanakane kuti Mdierekezi analamulira maufumu a ndale za dziko a pa dziko lapansi. Mogwirizana ndi cimeneci, Cibvumbulutso 13:7 cimati ponena za “cirombo” cophiphiritsiraco kuti “anacipatsa ulamuliro wa pa pfuko lirilonse, ndi anthu, ndi manenedwe, ndi mitundu.” Kuonjezerapo, kodi mneneri Danieli anazidziwikitsa zirombo zina ndi ciani? Ndi “maufumu,” kapena maboma a ndale za dziko. (Danieli 7:2-7, 17, 23) Kunena kuti zirombo zophiphiritsira za m’masomphenya za Danieli ndi “cirombo” ca mu Cibvumbulutso ziri ndi tanthauzo lofananalo kwaonekera kucokera mu ceniceni cakuti zolembedwa zonse ziwirizo zimanena za zolengedwa za mitundu yofananayo: mkango, cimbalangondo, nyalugwe ndi cirombo ca nyanga khumi. (Cibvumbulutso 13:1, 2) Cotero “cirombo” cimatanthauza gulu lonse la ndale za dziko la Mdierekezi limene lakucita kulamulira konga ngati kwaucinyama pa dziko lapansi kupyolera mu zaka mazana onse apitawo kufikira tsopano. Mposadabwitsa kuti Yesu Kristu anati: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi.” Ndipo mposadabwitsa kuti atsatiri ace sadzakhalanso a mbali iyi ya dziko lapansi, ndiko kunena kuti, iwo adzapewa kulowa mu zocitika zace.—Yohane 18:36; 17:14-16.
DZIPATULENI KU MPANGIDWE ULIWONSE WA KUKHULUPIRIRA MIZIMU
13. Kodi kukhulupirira mizimu ndi ciani, ndipo kodi ncifukwa ninji Baibulo limaticenjeza ife kusakhala ndi phande mu iko?
13 Imodzi ya njira zimene mizimu yoipa imawasocezera anthu amuna ndi akazi iri kupyolera mwa kukhulupirira mizimu. Kodi kukhulupirira mizimu ndi ciani? Kuli kulankhulana ndi zolengedwa zoipa za mizimu, kumasocezedwa nazo kaya kukhale mwacindunji kapena kupyolera mwa munthu wina kapena kupyolera mu njira ina. Baibulo limaticenjeza ife kusacita ciriconse cogwirizana ndi mizimu, cifukwa cakuti kukhulupirira mizimu kumamlowetsa munthu m’cisonkhezero ca ziwanda.—Agalatiya 5:19-21; Cibvumbulutso 21:8.
14. Kodi ndi macitacita ena ati amene agwirizanitsidwa ndi kukhulupirira mizimu, ndipo kodi ndi motani mmene Mulungu amawalingalirira awo amene amawagwiritsira nchito macitacita amenewo?
14 Mulungu amautsutsa mtundu uliwonse wa kukhulupirira mizimu. Baibulo limatiuza ife za zimene zinthu zosabvomerezeka zimenezi ziri: Kuombeza ula, matsenga, kufunafuna tanthauzo la malodza, kubwebweta, kutsirika (cidima, kulodza, ndi zina zotero), kupita kwa wopenduza kapena mlauli ndi kukafunsira kwa akufa. (Deuteronomo 18:10-12; Yesaya 8:19) Zonsezi ziri uciwanda, ndipo awo amene amawacita macitidwe oterowo amadzipangitsa okha kukhala adani a Mulungu.—Levitiko 19:31; 1 Mbiri 10:13, 14.a
15. (a) Kodi kuombeza ula nciani, kodi njira zina ndi zotani zimene anthu amazigwiritsira nchito lerolino? (b) Kodi ndi kuti kumene kupenda nyenyezi ndi matsenga zinayambirako?
15 Kuombeza ula kuli umodzi wa mipangidwe yofala kwambiri ya kukhulupirira mizimu. Kuli kuyesayesa kwa kupeza cidziwitso ca zinthu zosadziwika kapena za mtsogolo mwanjira ya malodza kapena mphamvu ya ziwanda. (Macitidwe 16:16) Pali njira zambiri mu zimene kuombeza kumacitikira lerolino, monga ngati namlondola, thabwa loombezera, mpira woombezera, matabwa a Ouija, ESP, kumaipenda mizera ya m’manja (kupenda cikhatho), kupenda kaulukidwe ka mbalame zina, kufunafuna tanthauzo m’maloto ndi mu zocitika zina za m’moyo ndi kuyesa kumazigwirizanitsa zimenezi ndi nthawi za mtsogolo. Palinso kuombeza mwa nyenyezi, kumene mofala kumachedwa kupenda zam’mwamba. Zimenezi zinayambira mu Babulo wakale, monga momwe inacitira mipangidwe yosiyanasiyana ya macitacita a matsenga. Baibulo limasonyeza kuti onse amene amagwiritsira nchito kuombeza amacimwira Mulungu.—1 Samueli 15:22, 23.b
16. Kodi nciani cimene tinayenera kucicita ngati tingamve “mau” ocokera kosaoneka akulankhula nafe?
16 Imodzi ya njira zofala mu imene mizimu yoipa imawasocezera anthu ndiyo mwa kumalankhula nawo, kaya kukhale kupyolera mwa kubwebweta kapena mwa “mau” ocokera ku malo osaoneka. Mauwo amayerekeza kukhala a wacinansi amene anafa kapena mzimu wabwino; koma cimeneci ciri cinyengo! Mauwo amakhala kwenikweni mzimu woipa umene umalankhula! Kodi nciani cimene munayenera kucicita ngati “mau” oterowo alankhula nanu? Eya, kodi nciani cimene Kristu Yesu anacicita pamene wolamulira wa mizimu yoipayo analankhula naye? Yesu anawakana malingaliro a Mdierekeziyo, akumati: “Coka Satana.” (Mateyu 4:10) Inunso mungatero. Ndiponso, mungaitanire pa Yehova kaamba ka cithandizo, mukumapemphera mopfuula ndi kumagwiritsira nchito dzina lace. Katsatireni kacitidwe aka kanzeru, ndipo musamamvetsera mau amenewo ocokera ku malo osaoneka.—Miyambo 18:10; Yakobo 4:7.
17. Kodi ndi motani mmene munthu angakucotsere kukhulupirira mizimu lerolino ngati atsatira citsanzo ca Akristu a ku Efeso oyambirira?
17 Koma bwanji ngati munthu anali atalowa mu zina za zipembedzo za mizimu kapena masayansi ndipo tsopano akufuna kukusiya kukhulupirira mizimu? Eya, kodi nciani cimene ambiri a Akristu oyambirira pa Efeso anacicita pamene anafuna kuwacotsa macitacita a matsenga? Baibulo limatiuza ife kuti, atalandira “mau a ambuye” amene analalikidwa ndi mtumwi Paulo, iwo “anasonkhanitsa mabuku ao, nawatentha pamaso pa onse,” ngakhale kunali kwakuti anali okwanira mtengo wa ndarama za siliva 50,000! (Macitidwe 19:19, 20) Citsanzo cao ca kuononga zipangizo zogwirizana ndi macitacita a mizimu ndico cimene ciri canzeru kucitsatira.
18. (a) Kodi nciani cimene cidzaicitikira mizimu yonse yoipa? (b) Pomalingalira za ici, kodi nciani cimene tiyenera kucicita ngati tifuna moyo wamuyaya?
18 Musanyengedwe ndi cionjezeko comakulakula mu cikondwerero ca zinthu zonena za mizimu. Zolengedwa zoipa za mizimu zikukupititsa patsogolo kukhulupirira m’mizimu koteroko. Koma magulu oipa a mizimu oterowo, kuphatikizapo Mdierekezi, adzaonongedwa potsirizira pace. (Mateyu 25:41) Ngati mufuna moyo wamuyaya muyenera kukhala osakhudzana ndi cisonkhezero cace mwa kumaupewa mtundu uliwonse wa kukhulupirira m’mizimu.
MDIEREKEZI AMACIPITITSA PATSOGOLO CIPEMBEDZO CONYENGA
19. (a) Kodi njira yaikurukuru ndi yotani imene mdierekezi amawafufunutsira anthu kwa Mulungu? (b) Kodi cipembedzo conyenga ndi ciani? (c) Ngati munthu acicita cipembedzo conyenga, kodi munthuyo akutumikira kwenikweni ndani?
19 Sikuyenera kutidabwitsa ife kuti Mdierekezi limodzi ndi ziwanda zace ali ndi njira zambiri za kusocezera mtundu wa anthu, kukhulupirira mizimu kumakhala njira imodzi cabe ya zimenezi. Pamenepo, kodi ndi njira yaikurukuru yotani imene Mdierekeziyo, “atate wa bodza,” amaucotsera mtundu wa anthu kwa Mulungu? (Yohane 8:44) Kuli mwa njira ya cipembedzo conyenga! Cipembedzo conyenga ciri kulambira kumene kwamangidwa pa zinyengo ndi kumene kuli koombana ndi Mau a Mulungu a coonadi, Baibulo. Cimeneco ndico cifukwa cimodzi cifukwa cace Baibulo limanena kuti ngati munthu alambira mu njira imene siri yogwirizana ndi Mau a Mulungu, iye kwenikweni akutumikira ziwanda, cifukwa cakuti akucita mogwirizana ndi zimene izo zimafuna mosemphana ndi Mulungu.—Deuteronomo 32:16, 17; 1 Akorinto 10:20.
20. Mofanana ndi atsogoleri aciwembu, kodi ndi motani mmene a gulu la Mdierekezi amawanyengera anthu?
20 Ngakhale kuli kwakuti zipembedzo zonyenga zingaonekere kukhala zolemekezeka, ife tiyenera kuzindikira kuti Mdierekezi ali wofanana ndi atsogoleri a maupandu okhala m’malo obisala lerolino amene amabisala mwa kudzipatsa dzina lolemekezeka. Kodi ndi njira yocenjera yotani imene ingakhalepo yakuti iye awanyengere anthu ndi kuwapangitsa iwo kumtumikira iye koposa ndi kugwiritsira nchito cipembedzo cimene kunja kwace cimadzionetsera kukhala ciri ndi cilungamo? Kunena kuti Mdierekezi adzawasoceza anthu mwa cipembedzo cimene mwa kunja kwace cimadzisonyeza kukhala comamtumikira Mulungu kwasonyezedwa m’Baibulo. (Mateyu 7:22, 23) Ponena zoona, mtumwi Paulo Wacikristu ananena kuti “Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wakuunika” ndipo “atumiki ace adzionetsa monga atumiki a cilungamo.”—2 Akorinto 11:14, 15.
21. (a) Kodi Baibulo limasonyezanji ponena za nthawi imene yaitsalira mizimu yoipayo? (b) Kodi ncifukwa ninji munthu ayenera kusiya kukhulupirira mizimu ndi cipembedzo conse conyenga?
21 Cotero Yesu Kristu sanali kuganizira kanthu kena pamene iye anamchula Mdierekeziyo kukhala “wolamulira wa dziko ili lapansi.” (Yohane 12:31, NW) Ndithudi iripo mizimu yoipa imene ikulisoceza “dziko lonse.” Koma pangotsala “kanthawi” cabe Mdierekeziyo limodzi ndi angelo ace oipa asanaletsedwe kucita kanthu kalikonse. (Cibvumbulutso 12:9, 12) Pa nthawi yino, usiyeni mtundu uliwonse wa kukhulupirira mizimu ndipo cisiyeni cipembedzo cimene cingaonekere kukhala colemekezeka koma ciri cozikidwadi pa cinyengo. Inu simungamamatire ku kukhulupirira mizimu kapena cinyengo ca cimpembedzo ca mtundu uli wonse ndi kupeza moyo wamuyaya mu dongosolo latsopano la Mulungu la zinthu, cifukwa cakuti ciri coonadi cokha cimene cimatsogolera ku moyo wamuyaya.—Aefeso 6:12, 16.
[Mawu a M’munsi]
a 1 Paralipomenon 10:13, 14, Dy.
b 1 Mafumu 15:22, 23, Dy.