Mutu 1
Yesu, Mphunzitisi Wamkuru
Kodi mukufuna kumva nkhani?—Eya, chabwino, ndikuuzani imodzi yonena za munthu wina amene anasimba nkhani zabwino kwambiri koposa munthu wina ali yense amene wakhala pa dziko lapansi chiyambire. Dzina lache ndilo Yesu Kristu.
Iye anakhala pa dziko lapansi ili pafupifupi zaka zikwi ziwiri zapitazo. Limenelo ndi kale kwambiri. Ndi kale kwambiri gogo wanu wachikazi kapena gogo wachimuna asanabadwe. Ndipo ndi kale kwambiri anthu asanakhale ndi magalimoto kapena sitima za pa mtunda kapena mawailesi kapena zinthu zina za lero lino.
Pamene Yesu anakamba nkhani ina iyo inampangitsa munthu kuganizira. Ngati munthu anaiganizira iyo kwa nthawi yaitali ndithu, chimene Yesu anachinenacho chinkathadi kusintha njira imene munthuyo analingalilira ponena za zinthu. Chinkatha kulisintha lingaliro lonse la munthuyo la moyo. Ndipo chiri chonse chimene Yesu anachinena chinali choona.
Yesu anadziwa koposa munthu wina ali yense. Iye anali mphunzitsi wabwino kwambiri amene anakhalako chiyambire. Ife timaphunzira zinthu zambiri kuchokera kwa anthu ena. Koma ife tingathe kuphunzira zinthu zofunika kopambana kuchokera kwa Yesu.
Chifukwa chimodzi chimene Yesu analiri mphunzitsi wamkuru motero ndicho chifukwa chakuti iye anamvetsera. Iye anadziwa mmene kuliri kofunika kumvetsera. Koma kodi Yesu anamvetsera kwa yani? Kodi ndani amene anamphunzitsa iye?—Atate wa Yesu anamphunzitsa. Ndipo Atate wa Yesu ndiye Mulungu.
Asanadze ku dziko lapansi monga munthu, Yesu anali atakhala ndi moyo kumwamba limodzi ndi Mulungu. Chotero Yesu anali wosiyana ndi anthu ena. Pakuti palibe munthu wina ali yense amene anakhala kumwamba asanabadwe pa dziko lapansi. Kumwambako Yesu anali Mwana wabwino amene anamvetsera kwa Atate wache. Chotero Yesu anali wokhoza kuwaphunzitsa anthu zimene iye anaziphunzira kuchokera kwa Mulungu. Mwa kumawamvetsera atate ndi mai wanu inu mungamtsanzire Yesu.
Chifukwa china chimene Yesu analiri mphunzitsi wamkuru ndicho chakuti iye anawakonda anthu. Iye anafuna kuwathandiza iwo kuphunzira za Mulungu. Yesu anawakonda akulu. Koma kodi iye anawakondanso ana?—Inde, iye anawakonda. Ndipo ana anakonda kukhala limodzi ndi Yesu chifukwa chakuti iye ankalankhula nawo ndi kuwamvetsera iwo.
Tsiku lina makolo anawabweretsa ana ao ang’ono kwa Yesu. Koma mabwenzi a Yesu anaganizira kuti Mphunzitsi Wamkuruyo anali wotanganitsidwa kwambiri kuti sangalankhule ndi ana ang’onowo. Chotero mabwenziwo anawauza iwo kuchoka. Koma kodi Yesu anabvomereza?—Ai. Iye anati: ‘Tilekeni tiana, musatikanize kudza kwa Ine.’ Ngakhale kuli kwakuti iye, anali munthu wanzeru kwambiri ndi wofunika, Yesu anakhala ndi nthawi kuwaphunzitsa ana ang’ono.—Mat. 19:13, 14.
Yesu anali mphunzitsi wamkuru chifukwa chakuti iye anadziwa kuzipanga zinthu kukhala zokondweretsa. Iye analankhula ponena za mbalame ndi maluwa ndi zinthu zina kuwathandiza anthu kuzindikira Mulungu. Tsiku lina iye anakamba ulaliki kapena nkhani ku khamu lalikuru la anthu amene anadza kwa iye pamene iye anali m’mbali mwa phiri. Iyo imachedwa Ulaliki wa pa Phiri.
Yesu anawauza anthu kuti: ‘Onani mbalame m’mlengalenga. Izo sizibzala mbeu. Izo sizimakundika chakudya m’nyumba. Koma Mulungu wakumwamba amazidyetsa izo. Kodi inuyo simuli oziposa izo?
Yesu ananenanso kuti: ‘Phunzirani kuchokera ku akakombo a ku thengo.’ Kodi ndi phunziro lotani limene mukuganiza kuti tingaliphunzire kuchokera kwa iwo? Eya, Yesu anati: ‘Iwo samapanga zobvala. Ndipo taonani mmene iwo aliri okongola! Ngakhale Mfumu Solomo yolemerayo siinabvale mokongola kwambiri koposa akakombo a ku thengowo. Chotero ngati Mulungu amawasamalira maluwa amene amamera, kodi iye sadzakusamaliraninso inu?’
Kodi mukulizindikira phunziro limene Yesu anali kumaliphunzitsa pamenepo?—Iye sanafune kuti iwo ade nkhawa ponena za kumene iwo akapeza chakudya choti adye kapena zobvala zoti abvale. Mulungu amadziwa kuti anthu amazifuna zinthu zimenezi. Yesu sananene kuti ife sitiyenera kugwira nchito kaamba ka chakudya ndi zobvala. Koma iye ananena kuti ife tiyenera kumuika Mulungu patsogolo. Ngati ife tichita chimenecho, Mulungu adzaona kuti ife tiri ndi chakudya choti tidye ndi zobvala zoti tibvale. Kodi mukuchikhulupilira chimenecho?—Mateyu 6:25-33, NW.
Anthu anaikonda njira imene Yesu anaphunzitsira. Iwo anadabwa. Kunali kokondweretsa kumumvetsera iye. Ndipo zimene iye anazinena zinawathandiza anthu kuchita chimene chiri choyenera.
Kuli kofunika kuti nafenso timumvetsere iye. Koma kodi ndi motani mmene tingachichitire chimenecho? Ife tiri ndi miyambi ya Yesu yolembedwa m’bukhu. Kodi inu mukulidziwa bukhu limenelo?—Ilo ndilo Baibulo Loyera. Chotero ife tingathe kumumvetsera Yesu mwa kumalimvetsera Baibulo.
Mulungu mwiniyo amanene kuti ife tiyenera kumumvetsera Yesu. Tsiku lina pamene Yesu anali limodzi ndi atatu a mabwenzi ache pamwamba m’phiri lalitari, mau ochokera kumwamba anati: ‘Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye.” Kodi mukumdziwa amene anali mwini wa mau amenewo?—Iwo anali a Mulungu! Mulungu ananena kuti ife tiyenera kumumvetsera Mwana wache. —Mateyu 17:1-5.
Kodi inu mudzamumvetsera Mphunzitsi Wamkuruyo? —Chimenecho ndicho chimene ife tonse tiyenera kuchichita. Ife tidzakhala achimwemwe ngati titero. Ndipo kudzatipatsano ife chimwemwe ngati ife tiwauza mabwenzi athu zinthu zabwino zimene ife tikuziphunzira.
(Kaamba ka malingaliro abwino kwambiri oonjezereka onena za mapindu amene amachokera m’kumamumvetsera Yesu, tsegulani Baibulo lanu ndi kuwerenga pamodzi Yohane 8:28-30; 3:16; Machitidwe 4:12.)