Mutu 29
Khalani Mabwenzi a Omamkonda Mulungu
TANDIUZANI amene ali ena a mabwenzi anu. Kodi maina ao ndani?—
Kuli bwino kukhala ndi mabwenzi. Iwo ali anthu amene inu mumakonda kukhala nawo. Inu mumakonda kulankhula nawo ndi kuchita zinthu limodzi.
Kulinso kofunika kukhala ndi mtundu woyenera wa mabwenzi. Kodi ndi motani mmene ife tingadziwire ngati iwo ali mtundu woyenera kapena ai?—
Eya, kodi ndani amene inuyo mukanena kuti ali munthu wofunika koposa m’miyoyo yathu?—Ndiye Yehova Mulungu, kodi sichoncho? Moyo wathu, mpweya wathu ndi zinthu zonse zabwino zimachokera kwa iye. Ife sitifuna konse kuchita kanthu kali konse kamene kakauononga ubwenzi wathu ndi Mulungu, ati?— Koma kodi munadziwa kuti kusankha kwathu mabwenzi kukatha kuuononga ubwenzi umenewo?—Chabwino. Chotero ife tifunikira kuwasankha mabwenzi mosamala kwambiri.
Mphunzitsi Wamkuruyo anatisonyeza ife kuchita kwache chimenecho. Iye anali ndi mtundu woyenera wa mabwenzi. Iye anati: “Inu muli mabwenzi anga ngati inu muchita chimene ine ndikulamulirani inu.” Kodi nchifukwa ninji zinali choncho?—Chifukwa chakuti chinthu chiri chonse chimene Yesu anawauza anthu chinachokera kwa Mulungu. Chotero Yesu anali kumanena kuti mabwenzi ache anali anthu amene anachita chimene Mulungu ananena kuti iwo ayenera kuchichita.—Yohane 15:14, NW.
Ichi sichimatanthauza kuti Yesu sanali wokoma mtima kwa anthu amene sanali otanganitsidwa mu utumiki wa Mulungu. Iye anali. Iye ankapitadi ku nyumba zao ndi kukadya nawo. Anthu ena amene anamva za chimenechi ananena kuti Yesu anali ‘bwenzi la ochimwa.’ Koma kodi chimenechi chinalidi choona?— —Mateyu 11:19.
Ai, sichinali choona. Yesu sanapite ku nyumba zao chifukwa chakuti iye anaikonda njira imene iwo anakhalira ndi moyo. Iye anwachezera iwo kotero kuti iye akadatha kulankhula nawo ponena za Mulungu. Iye anayesayesa kuwathandiza iwo kusintha kuchokera ku njira zao zoipa ndi kumtumikira Mulungu.
Ichi chinachitika tsiku lina mu mzinda wa Yeriko. Yesu ankapita ndi njira pa ulendo wache wa ku Yerusalemu. Munali khamu la anthu m’menemo, ndipo m’kati mwa khamulo munali munthu wina wochedwa Zakeyu. Iye anafuna kumuona Yesu. Koma Zakeyu anali wamfupi kwambiri ndipo iye sakadatha kumuona Yesu chifukwa cha khamulo. Chotero iye anathamangira kutsogolo kwa mseuwo nakwera mu mtengo m’malo mwakuti aone bwino bwino pamene Yesu anadutsa.
Pamene Yesu anafika ku mtengo umenewo iye anayang’ana m’mwamba nati: ‘Fulumira nutsike. Lero ndidzafika ku nyumba kwako.’ Koma Zakeyu anali munthu wolemera amene adachita zinthu zoipa. Kodi nchifukwa ninji Yesu anafuna kupita ku nyumba ya munthu woteroyo?—
Sichinali chifukwa chakuti Yesu anaikonda njira imene munthu ameneyo anakhalira ndi moyo. Iye anapita kumeneko kukalankhula ndi Zakeyu ponena za Mulungu. Iye anaona mmene munthu ameneyo anayesayesera zolimba kumuona iye. Chotero iye anadziwa kuti Zakeyu mwinamwache akamvetsera. Imeneyi ikakhala nthawi yabwino kulankhula naye ponena za njira imene Mulungu amanena kuti ife tiyenera kukhalira ndi moyo.
Kodi nchiani chimene chinali choturukapo chache? Zakeyu anasintha kuchokera ku njira zache zoipa. Iye anazibweza ndarama zimene iye analibe kuyenera kwa kuzitenga, ndipo iye anakhala mtsatiri wa Yesu. Kunali pa nthawi imeneyoyo yokha chakuti Yesu ndi Zakeyu anakhala mabwenzi.—Luka 19:1-10.
Chotero, ngati ife tiphunzira kuchokera kwa Mphunzitsi Wamkuruyo, kodi ife tidzachezanso ndi anthu amene sali mabwenzi athu?—Inde. Koma ife sitidzapita ku nyumba zao chifukwa chakuti ife tikuikonda njira imene iwo amakhalira. Ndipo ife sitidzachita zinthu zolakwa limodzi ndi iwo. Ife tidzacheza nawo kotero kuti ife tingathe kulankhula nawo ponena za Mulungu.
Koma mabwenzi athu enieni ndiwo amene ife makamaka timakonda kukhala nawo. Ife taona kuti kuti iwo akhale mtundu woyenera wa mabwenzi, iwo ayenera kukhala mtundu umene Mulungu akaukonda. Koma kodi ife tingadziwe bwanji ngati iwo ali?—
Eya, njira imodzi yabwino ndiyo kuwafunsa iwo kuti: Kodi inu mumamkonda Yehova? Ena a iwo sangamdziwedi amene Yehova ali. Koma ngati iwo afuna kuphunzira ponena za iye, ife tingathe kuwathandiza iwo. Ndipo pamene nthawi ifika imene iwo akumkonda Yehova monga momwe ife timachitira, pamenepo ife tingathe kukhala mabwenzi enieni.
Pali njira ina ya kudziwira ngati munthu akakhala bwenzi labwino. Yang’anani zinthu zimene iye amachita. Kodi iye amachita zinthu zosakhala bwino kwa anthu ena ndipo kenako kuziseka izo? Zimenezo siziri zabwino, kodi sichoncho?—Kodi iye masiku onse amalowa m’bvuto?—Ife sitikafuna kulowa m’bvuto limodzi ndi iye, ati?—Kapena kodi iye amachita zinthu zoipa mwadala ndiyeno kuganizira kuti iye ali wochenjera chifukwa chakuti iye sanagwidwe? Ngakhale ngati iye sanagwidwe, Mulungu anachiona chimene iye anachichita, ati?—Kodi inu mukuganizira kuti anthu amene amachita zinthu zoterozo akakhala mabwenzi abwino?—
Bwanji osatenga Baibulo lanu, ndi kuti tione chimene ilo limachinena ponena za mmene atsamwali athu amaiyambukilira miyoyo yathu? Lembali liri pa Akorinto Woyamba chaputura 15, vesi 33. Kodi mwalipeza?—
Ilo limati: “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” Chimenecho chikutanthauza kuti ngati ife timayenda ndi anthu oipa ife tidzakhala oipa. Ndipo kulinso koona kuti atsamwali abwino amatithandiza ife kuwapanga makhalidwe abwino.
Tiyeni tisaiwale konse kuti munthu wofunika koposa m’moyo mwathu ndiye Yehova. Ife sitikufuna kuuononga ubwenzi wathu ndi iye, eti?—Chotero ife tiyenera kukhala osamala kukhala mabwenzi kokha a awo amene amamkonda Mulungu.
(Kufunika kwa mtundu woyenera wa atsamwali kwamveketsedwanso bwino pa 1 Yohane 2:15, 2 Mbiri 19:2 [2 Mbiri 19:2, MO], Salmo 119:115 [118:115, MO] ndi 2 Timoteo 2:22. Awerengeni malemba amenewo limodzi.)