Mutu 44
Mabwenzi Athu Azikhala Okonda Mulungu
MABWENZI athu, kapena kuti anzathu, ndi anthu amene timakonda kucheza nawo ndi kuchitira nawo zinthu limodzi. Komatu tifunika kukhala ndi mabwenzi abwino. Kodi ukuganiza kuti ndani amene angakhale bwenzi lathu labwino kwambiri?— Inde, ndi Yehova Mulungu.
Kodi zingathekedi kuti Mulungu akhale bwenzi lathu?— Chabwino, Baibulo limanena kuti Abrahamu, yemwe anali ndi moyo kalekalelo, anali “bwenzi la Mulungu.” (Yakobo 2:23) Kodi ukudziŵa chifukwa chake iye anali bwenzi lake?— Baibulo limanena kuti ndi chifukwa chakuti Abrahamu anamvera Mulungu. Iye anamvera ngakhale pamene anauzidwa kuchita chinthu chovuta kwambiri. Ndiye kuti tikhale bwenzi la Yehova, tiyenera kuchita zimene zimamukondweretsa, monga mmene anachitira Abrahamu komanso monga amachitira nthaŵi zonse Mphunzitsi Waluso.—Genesis 22:1-14; Yohane 8:28, 29; Ahebri 11:8, 17-19.
Yesu anauza atumwi ake kuti: ‘Muli mabwenzi anga inu, ngati muchita zimene ndikulamulirani inu.’ (Yohane 15:14) Popeza kuti zonse zimene Yesu anauza anthu zinachokera kwa Yehova, Yesu anali kunena kuti mabwenzi ake anali anthu amene anachita zimene Mulungu anawauza kuti azichita. Inde, anzake onse anali kukonda Mulungu.
Anthu ena amene anali anzake kwambiri a Mphunzitsi Waluso anali atumwi ake, omwe patsamba 75 la buku lino ungaone zithunzi zawo. Anali kuyenda naye ndi kumuthandiza ntchito yolalikira. Yesu nthaŵi zambiri anali kukhala ndi anthu ameneŵa. Anali kudyera pamodzi. Anali kukambirana za Mulungu. Ndipo analinso kuchitira limodzi zinthu zina. Komatu Yesu anali ndi mabwenzi enanso ambiri. Nthaŵi zina anali kukhala kwa mabwenzi ake amenewo, ndipo anali kusangalala.
Banja lina limene Yesu anali kukonda kukakhalako linali kumudzi waung’ono wa Betaniya, womwe unali pafupi ndi mudzi waukulu wa Yerusalemu. Kodi ukulikumbukira?— Linali banja la Mariya ndi Marita ndi mlongo wawo Lazaro. Yesu ananena kuti Lazaro anali bwenzi lake. (Yohane 11:1, 5, 11) Yesu anali kukonda banja limeneli ndipo anali kukonda kukhala nalo chifukwa chakuti linali kukonda Yehova ndi kumutumikira.
Koma zimenezi sizikutanthauza kuti Yesu sanakomere mtima anthu amene sanali kutumikira Mulungu. Anali kuwakomeranso mtima. Anali kupita ngakhale kunyumba kwawo ndi kukadya nawo limodzi chakudya. Anthu ena ataona zimenezi ananena kuti Yesu anali “bwenzi la amisonkho ndi ochimwa.” (Mateyu 11:19) Koma mfundo ndi yakuti Yesu sanapite kunyumba za anthu ameneŵa chifukwa chakuti khalidwe lawo linali kumusangalatsa. Iye anali kukawachezera ndi cholinga chakuti alankhule nawo za Yehova. Anafuna kuwathandiza kusintha khalidwe lawo loipa kuti azitumikira Mulungu.
Zoterezi zinachitika tsiku lina mu mudzi wa Yeriko. Yesu anali kungodutsa mu mudzimo popita ku Yerusalemu. Tsono panali anthu ambiri, ndipo mmodzi wa iwo anali mwamuna wina dzina lake Zakeyu. Iye anafuna kuona Yesu. Komano Zakeyu anali wamfupi ndipo sanathe kumuona chifukwa cha anthuwo. Ndiye iye anathamangira patsogolo ndi kukakwera mumtengo kuti Yesu akamadutsa amuone bwino.
Yesu atafika pamtengopo anayang’ana m’mwamba ndi kunena kuti: ‘Fulumira tsika, chifukwa lero ndipita kunyumba kwako.’ Tsonotu Zakeyu anali munthu wolemera amene anachita zinthu zoipa. Ndiye ukuganiza kuti ndi chifukwa chiyani Yesu anafuna kupita kunyumba kwa munthu woteroyo?—
Sichinali chifukwa chakuti Yesu anali kusangalala ndi khalidwe la munthuyu. Anapita kwa Zakeyu kuti akakambirane naye za Mulungu. Yesuyo anazindikira kuti Zakeyu anali kufunitsitsa kwambiri kuti amuone. Ndiye Yesu anadziŵa kuti Zakeyu angathe kumvetsera. Imeneyi inali nthaŵi yabwino yokambirana naye zimene Mulungu amanena kuti anthu azichita.
Tsono chinachitika ndi chiyani?— Zakeyu anasangalala ndi zimene Yesu anali kuphunzitsa. Anamva chisoni kwambiri chifukwa chakuti anali kubera anthu, ndipo analonjeza kubwezera ndalama zimene anali kulanda anthu. Atatero anakhala wotsatira wa Yesu. Zakeyu atachita zimenezi ndi pamene anakhala bwenzi la Yesu.—Luka 19:1-10.
Ngati titengera Mphunzitsi Waluso, kodi tidzapita kukacheza kwa anthu amene si anzathu?— Inde. Koma sikuti tidzapita kunyumba kwawo chifukwa chakuti khalidwe lawo limatisangalatsa. Ndiponso sitidzachita nawo zinthu zoipa zimene amachita. Tidzapita kukacheza nawo kuti tiwauze za Mulungu.
Koma mabwenzi athu apamtima ndi anthu amene timakonda kucheza nawo kwambiri. Kuti akhale mabwenzi abwino, ayenera kukhala anthu amene Mulungu amawakonda. Ena angakhale kuti sakumudziŵa n’komwe Yehova. Koma ngati akufuna kuphunzira za iye, tingawathandize. Akadzafika pokonda Yehova mofanana ndi ifeyo, pamenepo akhoza kukhala mabwenzi athu apamtima.
Palinso njira ina imene ungadziŵire ngati munthu angakhale mnzako wabwino. Uziona zimene iye amachita. Kodi amachita zinthu kuti apweteke ena kenako ndi kumasekerera? Zimenezi si zabwino, si choncho?— Kodi amachita zinthu zimene zimamubweretsera mavuto? Ife sitingafune kuti tizivutika naye limodzi, si choncho kodi?— Kapena kodi iye amachitira dala zinthu zoipa ndiyeno ndi kumaganiza kuti ndi wochenjera chifukwa chakuti sanamugwire? Komatu ngakhale kuti iye sanamugwire, Mulungu anaona zimene anachitazo, eti?— Kodi ukuganiza kuti anthu amene amachita zoterezi angakhale mabwenzi abwino?—
Tatenga Baibulo lako kuti tione zimene limanena pankhani yakuti anzathu amatha kusintha khalidwe lathu. Lemba lake ndi 1 Akorinto chaputala 15, vesi 33. Kodi walipeza?— Limanena kuti: “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” Izi zikutanthauza kuti ngati timacheza ndi anthu oipa, ifenso tikhoza kukhala oipa. Ndiponso ndi zoona kuti tikakhala ndi anzathu abwino amatithandiza kukhala ndi makhalidwe abwino.
Tisaiwale kuti Munthu wofunika kwambiri pamoyo wathu ndi Yehova. Ife sitikufuna kuwononga ubwenzi wathu ndi iye, ndi choncho eti?— Ndiyetu tifunika kukhala osamala kwambiri kuti mabwenzi athu azikhala anthu okhawo amene amakonda Mulungu.
Malemba aŵa akusonyeza kuti tifunika kukhala ndi mabwenzi abwino: Salmo 119:115; Miyambo 13:20; 2 Timoteo 2:22; ndi 1 Yohane 2:15.