Mutu 44
“Iwe Udzakhala ndi Ine m’Paradaiso”
KODI INU mumazikonda zinyama?—Kodi inuyo mungakonde kusewera ndi mkango? Kapena kodi inuyo mungakonde kukhala ndi chimbalangondo monga chiweto?—
Nthawi irinkudza pamene inu mudzakhala okhoza kuchita chimenecho. Tengani Baibulo lanu ndipo tiyeni tiwerenge ponena za icho limodzi.
Lembalo liri m’bukhu la Yesaya, chaputara 11, vesi 6. Ilo limati: “Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wa ng’ombe ndi mwana wa mkango ndi choweta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera.”
Kodi nchiani chimene chikachitika lero lino ngati mmbulu utafika pa mwana wa nkhosa?—Ukamdya iye, kodi sichoncho? Ndipo kodi nchiani chimene chikanachitika ngati nyalugwe anali limodzi ndi mwana wa mbuzi?—Mbuzi yaing’ono imeneyo ikakhala chakudya cha nyalugweyo.
Koma Baibulo limanena kuti zimenezo zidzasintha. Mulungu adzazichititsa nyama zimenezo kudya udzu, m’malo mwa kumadyana. Pamene nyama zonse ziri zaubwenzi, kudzakhala kokondweretsa kukhala ndi mkango monga chiweto, ati?—Zimenezo zidzachitika m’Paradaiso.
Kodi inu mukuchidziwa chimene Paradaiso ali?—Paradaiso ndiye munda wokongola kapena paki. Ndiye malo a mtendere ndi chikondwelero.
Mulungu anampatsa mwamuna woyambayo, Adamu, ndi mkazi wache Paradaiso kuti akhalemo. Iye anali kuchedwa Munda wa Edene. Munali zinyama m’munda umenewo. Koma palibe iri yonse ya izo inabvulaza zinazo. Munalinso mitengo yokhala ndi zipatso zochuruka zokoma pa iyo. Ndipo munali mtsinje. Anali malo odabwitsa kukhalamo.
Koma Adamu ndi Hava anamtaya Paradaiso ameneyo. Iwo sanamumvera Mulungu, chotero iwo sakadathanso kukhala m’Paradaiso. Kulibe Munda wa Edene tsopano. Chotero, kodi ndi mwai wotani umene ife tiri nao wa kukhala m’Paradaiso?—
Eya, iye asanafere pa mtengo wozunzirapowo, Mphunzitsi Wamkuruyo analankhula za Paradaiso watsopano. Munthu wina anali atangonena kwa iye kuti: “Yesu, ndikumbukireni ine pamene inu mulowa mu ufumu wanu.” Yesu anayankha kuti: “Zoonadi ndikuuza iwe lero, Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.”—Luka 23:42, 43, NW.
Yesu sananene kuti iwo anali kunka kukakhala m’Paradaiso tsiku limenelolo. Awiri onse a iwo anafa ndipo anaikidwa pa tsiku lomwelo. Koma Yesu anali kumalankhula za chimene chikachitika iye ‘atalowa mu ufumu wache.’ Pamenepo kudzakhala Paradaiso kachiwiri. Paradaiso watsopanoyo adzakhala kosatha.
Kodi Paradaiso ameneyo adzakhala kuti?—Paradaiso woyambayo anali pa dziko lapansi pompano, kodi sichoncho? Motero Paradaiso watsopanoyo adzakhalanso pa dziko lapansi pompano. Chimenecho ndicho chifukwa chache chimene Yesu anatiphunzitsira ife kuchipempha chifuniro cha Mulungu kuti chichitidwe pa dziko lapansi. Pamene nthawi imeneyo ifika, dziko lonse lapansi lidzakhala Paradaiso.
Mu Paradaiso mudzapangidwa masinthidwe akuru. Mpweya udzakhala woyera ndi wabwino ndi wokondweretsa kuupuma. Madzi m’mitsinje adzakhala oyera ndi abwino. Nthaka idzabala zakudya zochuruka kotero kuti palibe ali yense akukhala ndi njala. Dziko lonse lapansi lidzakhala ngati paki. Ilo lidzakhala lamoyo ndi mbalame ndi zinyama, mitengo ndi maluwa a mtundu uli wonse.
Koma masinthidwe akuru kopambana adzakhala mwa anthu. Ndi anthu amene amaliipitsa dziko lapansi, ati?—Ena a iwo amakhala m’nyumba zoipa kwambiri. Ndipo iwo amataya zinyalala pali ponse pamene iwo akupita. Koma Paradaiso sadzakhala wotero. Adzakhala malo oyera ndi okondweretsa kukhalamo. Chotero ngati ife tikufuna kukhala m’Paradaiso, kodi inuyo simunganene kuti tsopano ndiyo nthawi ya kuphunzira kuzisunga zinthu kukhala zaudongo ndi zoyera?—Imeneyo ndiyo njira imodzi ya kusonyezera kuti ife tikulifunadi dziko lapansi kukhala Paradaiso, eti?—
Anthu adzasintha m’njira zinanso. Paradaiso adzakhala malo a mtendere. Koma si munthu ali yense lero lino ali wamtendere. Anthu ena amawakalipira anzao. Iwo amamenya ndi kuwabvulaza anthu ena. Iwo amachita mofanana kwambiri ndi zinyama. Iwo afunikira kuphunzira kukhala mu mtendere. Mu Paradaiso, iwo “sadzachita upandu uli wonse kapena kuchititsa chionongeko chiri chonse.”—Yesaya 11:9, NW.
Kodi inu muli masiku onse amtendere ndi ena?—Ngati ife titi tikakhale ndi moyo m’Paradaiso, ife tifunikira kuphunzira kukhala amtendere, kodi sichoncho?—
Chidzakhala chinthu chodabwitsa kukhala ndi moyo m’Paradaiso. Mulungu amalonjeza kuti iye adzatichitira ife zinthu zodabwitsa pa nthawi imeneyo. Bandakulani Baibulo lanu pa Chibvumbulutso chaputara 21, vesi 3 ndi 4, ndipo tiyeni tiwerenge chimene ilo limanena: “Taonani, chihema, cha Mulungu chiri mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ache, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”
Tangoganizirani za chimenecho! Mulungu adzatiyang’anira ife. Ife sitidzafunikira konse kulira chifukwa chakuti ife tiri opanda chimwemwe. Palibe munthu ali yense amene adzamva ululu chifukwa chakuti iye ali kudwala. Ndipo palibe munthu ali yense amene adzafunikira kufa. M’menemo ndimo mmene kuti kudzakhalire m’Paradaiso.
Kodi inu mukufunadi kukhala ndi moyo m’Paradaiso? – Ine ndikufuna. Chimene ife tichichita tsiku liri lonse tsopano chiri ndi chiyambukiro ponena zakuti kaya ife tidzakhalamo. Ngati ife tikufuna kukhala ndi moyo m’Paradaiso, tsopano ndiyo nthawi ya kukonzekera kaamba ka iye.
(Dziko lapansili lidzakhala kosatha ndipo Mulungu adzalipanga ilo kukhala malo odabwitsa kukhalamo. Werengani zochuruka zonena za chimenechi pa Masalmo 104:5 [103:5, MO]; 37:10, 11 [36:10, 11 MO]; Miyambo 2:21, 22; Yesaya 35:5, 6; Mika 4:3, 4.)