Zimene Owerenga Amafunsa
Kodi Paradaiso Amene Baibulo Limatchula ali Kuti?
▪ Munthu wina atatsala pang’ono kufa anasonyeza molimba mtima kuti ankakhulupirira Yesu. Choncho Yesu anauza munthuyo kuti: “Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” (Luka 23:43) Kodi Yesu ankatanthauza kuti munthu ameneyu adzakhala kuti? Kodi Paradaiso amene Yesu ananenayu ali kumwamba, padziko lapansi kapena kumalo enaake kumene anthu amayembekezera kuti aweruzidwe?
Kumbukirani kuti makolo anthu oyambirira anakhalapo m’Paradaiso. Baibulo limatiuza kuti: “Yehova Mulungu, anakonza munda ku Edeni, chakum’mawa, ndipo m’mundamo anaikamo munthu amene anamuumbayo. . . . Tsopano Yehova Mulungu anatenga munthu uja n’kumuika m’munda wa Edeni kuti aziulima ndi kuusamalira.” (Genesis 2:8, 15) Pamene mawu amenewa anamasuliridwa m’Chigiriki, mawu akuti “munda” anawamasulira kuti pa·raʹdei·sos ndipo ndi kumene kunachokera mawu a Chingelezi akuti “paradaiso.”
Pamene banja lawo linali kukula, makolo athu oyambirira anafunika kukulitsa Paradaiso kuti asangokhala m’munda wa Edeni mokha. Zimenezi ndi zofanana ndi zimene makolo angachite powonjezera malo awo chifukwa chakuti banja lawo likukula. Mulungu anauza makolo athu oyambirirawa kuti: “Mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anire.”—Genesis 1:28.
Apatu ndiye kuti cholinga cha Mlengi wathu chinali chakuti anthu akhale m’Paradaiso padziko lapansi ndi kubereka ana. Iwo akanakhala kwa muyaya ndipo panalibe chifukwa choti akhale ndi manda. Cholinga cha Mulungu chinali chakuti anthu onse azikhala padziko lapansi mpaka kalekale. N’chifukwa chake ndi zosadabwitsa kuti timasangalala ndi zinthu zachilengedwe zimene zili padziko lapansili. Anthufe tinalengedwa kuti tizikhala padziko lapansi lokongolali.
Kodi cholinga cha Mulungu chinasintha? Ayi ndithu. Yehova akutitsimikizira kuti: “Ndi mmenenso adzakhalire mawu otuluka pakamwa panga sadzabwerera kwa ine popanda kukwaniritsa cholinga chake, koma adzachitadi zimene ine ndikufuna ndipo adzakwaniritsadi zimene ndinawatumizira.” (Yesaya 55:11) Patapita zaka 3,000 kuchokera pamene munthu woyamba analengedwa, Baibulo linanena kuti “amene anaumba dziko lapansi ndi kulipanga, . . . sanalilenge popanda cholinga” koma “analiumba kuti anthu akhalemo.” (Yesaya 45:18) Cholinga cha Mulungu sichinasinthe. Dziko lapansi lidzakhaladi paradaiso.
N’zochititsa chidwi kuti mavesi ambiri a m’Baibulo onena za Paradaiso amanena za moyo wapadziko lapansi. Mwachitsanzo, mneneri Yesaya ananena kuti: “Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake.” (Yesaya 65:21) Kodi n’kuti kumene anthu amamanga nyumba, kubzala minda ya mpesa ndiponso kudya zipatso? Zimenezi zimachitika padziko lapansi. Lemba la Miyambo 2:21 limati: “Owongoka mtima ndi amene adzakhale m’dziko lapansi.”
Nayenso Yesu ananena za paradaiso wa padziko lapansi. N’zoona kuti analonjezanso anthu za paradaiso wakumwamba koma ndi wa anthu osankhidwa ochepa chabe. (Luka 12:32) Anthu amenewa akafa amaukitsidwa kupita ku Paradaiso wakumwamba kuti adzalamulire dziko lapansi la Paradaiso limodzi ndi Khristu. (Chivumbulutso 5:10; 14:1-3) Olamulira a kumwamba amenewa adzaonetsetsa kuti zinthu zikuyenda bwino m’Paradaiso wapadziko lapansi mogwirizana ndi zofuna za Mulungu.
Yesu anadziwa kuti zimenezi ndi zimene Mulungu anafuna kuti zichitike padziko lapansili. Ndipotu, iye anali kumwamba ndi Atate wake pamene munda wa Edeni unkalengedwa. Munthu aliyense amene amasonyeza chikhulupiriro mwa Yesu ali ndi mwayi wodzakhala m’paradaiso wa padziko lapansi. (Yohane 3:16) Yesu akulonjeza anthu oterewa kuti: ‘Mudzakhala ndi ine m’Paradaiso.’—Luka 23:43.
[Mawu a Chithunzi patsamba 25]
© FORGET Patrick/SAGAPHOTO.COM/Alamy