NKHANI 28
M’mene Mose Anapulumutsidwira
MUKUONA khanda likulira’lo, litagwira chala cha mai’yo. Uyu ndi Mose. Kodi amai wokongola’yo mukumudziwa? Ndiye mwana wamkazi, wa Farao wa Igupto.
Mai wa Mose anam’bisa mpaka atakwana miyezi itatu, chifukwa sanafune kuti aphedwe ndi Aigupto. Koma anadziwa kuti Mose angapezedwe, chotero nazi zimene anachita kum’pulumutsa.
Anatenga mtanga naukonza kuti madzi asalowemo. Naikamo Mose, naika mtanga’wo m’maudzu atali m’mbali mwa Mtsinje wa Nile. Mlongo wa Mose, Miriamu, anauzidwa kuima chapafupi ndi kuona chimene chikachitika.
Posapita nthawi mwana wamkazi wa Farao akudza ku Nile kudzasamba. Modzidzimuka anaona mtanga’wo m’maudzu. Anaitana mmodzi wa adzakazi nati: ‘Kanditengere mtanga’wo.’ Pamene anautsegula, munali khanda lokongola kwambiri limene analionamo! Khanda Mose anali kulira, ndipo mwana wa mfumu’yo anamumvera chisoni. Sanafune kuti aphedwe.
Miriamu anadzapo. Mungamuone m’chithunzimo. Miriamu anafunsa mwana wamkazi wa Farao’yo kuti: ‘Kodi ndikakuitanireni mkazi Wachiisrayeli akuyamwitsireni khanda’lo?’
‘Inde chonde,’ anatero mwana wamkazi’yo.
Chotero Miriamu akuthamanga kukauza mai wake. Atadza mai wa Mose kwa mwana wamkazi wa mfumu’yo, mwana’yo anati: ‘Tenga nundiyamwitsire khanda’li, ndipo ndidzakulipira.’
Chotero mai wa Mose analera mwana wake. Kenako Mose anakula mokwanira, namka naye kwa mwana wamkazi wa Farao, amene anam’landira monga mwana wake. Ndimo m’mene Mose anakulira m’nyumba ya Farao.