MUTU 17
Mose Anasankha Kuti Azilambira Yehova
Ku Iguputo, anthu a m’banja la Yakobo anayamba kudziwika kuti Aisiraeli. Yakobo ndi Yosefe atamwalira, Farao wina anayamba kulamulira. Iye ankachita mantha chifukwa Aisiraeli anali amphamvu kuposa Aiguputo. Choncho Farao ameneyu anachititsa kuti Aisiraeli akhale akapolo. Anawalamula kuti aziumba njerwa komanso kugwira ntchito zotopetsa kumunda. Koma ngakhale kuti ankazunzidwa kwambiri ndi Aiguputo, Aisiraeli anapitirizabe kuchulukana. Popeza Farao sankafuna zimenezi, analamula kuti ana onse aamuna a Aisiraeli aziphedwa akangobadwa. Ukuganiza kuti Aisiraeli anamva bwanji lamuloli litaperekedwa?
Izi zitachitika, mayi wina wa Chiisiraeli, dzina lake Yokebedi anabereka mwana wamwamuna wokongola kwambiri. Pofuna kuteteza mwanayo, mayiyo anamuika m’basiketi n’kukamubisa m’mabango, mumtsinje wa Nailo. Mchemwali wake wa mwanayo, dzina lake Miriamu, anakhala chapafupi kuti azimuyang’anira.
Ndiyeno mwana wamkazi wa Farao anabwera kuti adzasambe ndipo anaona basiketi ija. Atatsegula basiketiyo anapeza kuti munali mwana. Mwanayo ankalira ndipo anamumvera chisoni. Miriamu anafunsa mwana wamkazi wa Faraoyo kuti: ‘Kodi mungakonde kuti ndikakufufuzireni mzimayi woti azimusamalira?’ Mwana wa Farao atavomera, Miriamu anapita n’kukauza amayi ake, a Yokebedi. Atabwera, mwana wa Faraoyo anawauza kuti: ‘Tengani mwanayu, muzikamusamalira ndipo ndizikulipirani.’
Mwana uja atakula, Yokebedi anakamupereka kwa mwana wa Farao ndipo anamupatsa dzina loti Mose n’kumakhala naye ngati mwana wake. Mose analeredwa ngati mwana wa mfumu ndipo akanatha kupeza chilichonse chimene ankafuna. Koma iye sanaiwale Yehova. Ankadziwa kuti anali wa ku Isiraeli osati wa ku Iguputo ndipo anasankha kuti azitumikira Yehova.
Ali ndi zaka 40, Mose ankafuna kuthandiza Aisiraeli anzake. Choncho ataona munthu wa ku Iguputo akumenya munthu wa Chiisiraeli, Mose anamenya munthu wa ku Iguputoyo mpaka kumupha. Atatero anakwirira munthu wakufayo mumchenga. Farao atadziwa zimenezi, ankafuna kupha Mose. Choncho Mose anathawira ku Midiyani. Kumeneko, Yehova anali naye.
“Chifukwa cha chikhulupiriro, Mose . . . anakana kutchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao, ndipo anasankha kuzunzidwa limodzi ndi anthu a Mulungu.”—Aheberi 11:24, 25