Mutu 11
Khalani ndi Moyo Moyembekezera Kukwaniritsidwa kwa Lonjezo
1, 2. (a) Kodi nchiyani chimene chidzachitikabe malinga ndi kunena kwa “mawu a Mulungu” osasinthawo, chikumachititsa kubuka kwa mafunso otani? (b) Kodi ndi motani m’mene mtumwi Petro akufotokozera chimene chidzachitikira dongosolo liripoli?
DONGOSOLO lathunthu la dziko lonse latsala pang’ono kusintha. Mbali iriyonse ya kakhalidwe ka anthu iyenera kuyambukiridwa. Kusintha kumeneku nkosapeweka popeza kuti “mawu a Mulungu” osalepherawo alengeza mapeto a miyamba ndi dziko lapansi zimene ziripozi ndi kulowedwa ,m’malo mwake ndi miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano zaulemerero. Kodi zochitika zimenezi zidzatanthauzanji kwa ife? Kodi ndi motani mmene tingasonyezere kuti tikukhala ndi moyo moyembekezera kukwaniritsidwa kwa zimene Yehova Mulungu walonjeza?
2 Atatha kutchula za chigumula cha pa dziko lonse lapansi cha m’masiku a Nowa, mtumwi Petro akulemba kuti: “Miyamba ndi dziko lapansi zimene ziripo zasungidwira kumoto ndipo zikusungidwa kufikira tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu opanda umulungu.” (2 Petro 3:7, NW) Mtumwiyo akupitirizabe kunena kuti: “miyamba idzachoka ndi phokoso loti fwaa, koma zinthuzo pokhala zotentha kwambiri zidzasungunuka, ndipo dziko lapansi ndi ntchito zokhala momwemo zidzabvumbulutsidwa.”—2 Petro 3:10, NW.
3. Polingalira cholembedwa cha Genesis, kodi nchiyani chimene moyenerera tiyenera kunena ponena za chilengedwe chakuthupi, kuphatikizapo dziko lathu lapansili?
3 Kuchokera m’mawu ouziridwa amenewa, kodi tiyenera kunena kuti dziko lathu lapansi lenilenili kudzanso dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zidzawonongedwa? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyenera kulingalira lingaliro la Mulungu la ntchito zake za iye mwini. Ponena za mapeto a nyengo ya kulenga, cholembedwa cha Genesis chimatiuza kuti: “Anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu.” (Genesis 1:31) Chiyembekezo chimene chinali pamaso pa anthu oyambirira chinali kukhala ndi moyo kwachimwemwe kosatha pa dziko lapansi, malinga ngati iwo anakhalabe omvera. (Genesis 2:16, 17; 3:3) Palibe chirichonse m’cholembedwa cha Genesis chimene chimasonyeza kuti dziko lapansi lidzakhala malo okhala a munthu akanthawi, potsirizira pake ndi kuwonongedwa pa tsiku lina la chiweruzo la mtsogolo. Moyenerera kuyenera kukhala kwakuti chifuno cha Mulungu nchakuti chilengedwe chakuthupichi kuphatikizapo dziko lathu lapansi, chipitirizebe kukhalapo kosatha.
4. (a) Kodi ndi kusiyanitsa kotani kumene petro anapanga ponena za mkhalidwe wa Chigumula chisanachitike ndi pambuyo pake? (b) Kodi Chigumula sichinachitenji?
4 Ndiponso, mtumwi Petro anasiyanitsa pakati pa (1) “miyamba kuyambira kale ndi dziko lapansi linamangika mwamphamvu pa madzi” ndi (2) “miyamba ndi dziko lapansi zimene ziripozi.” (2 Petro 3:5, 7, NW) Komabe, dziko lapansi limene linalipo Chigumula chisanachitike ndi planeti limodzimodzilo limene likalipobe. Zowona, chigumula chinadzetsa masinthidwe mu mkhalidwe wa mapiri sanalinso kulenjekeka kumwamba kwa dziko lapansi, kumeneku kunayambukira kawonekedwe ka chilengedwe chowoneka mwa lingaliro la wopenyerera waumunthu. Komabe, masinthidwe amenewa anali zotsatirapo chabe za Chigumula. Chifuno chake sichinali kuwononga planeti lenilenili koma kuwononga chitaganya cha anthu chopanda umulungu chimene chinali kunja kwa chingalawa. Mwa njira ya chigumula, ntchito zonse ndi malinganizidwe zimene chitaganya cha anthu opanda umulungu chinazipanga zinawonongeka.
5. Kuti pakhale kufanana ndi chigumula cha pa dziko lonse, kodi nchiyani chimene chiyenera kuchitika pa tsiku la mlandu?
5 Chifukwa cha chimenecho, kuti pakhale kufanana ndi chigumula cha pa dziko lonsecho, chiri chonse chogwirizana ndi chitaganya cha anthu oipa chiripochi chiyenera kuwonongeka, monga ngati chapserezedwa ndi moto. Inde, mpangidwe wonse wathunthu wa zochitika za anthu umene unakhalapo pambuyo pa tsiku la Chigumula wasungidwira chiwonongeko ndi tsiku la chiweruzo kapena la mlandu.
6. Kodi “moto” umene ukuthetsa dongosolo lakaleli, uli weniweni?
6 Chakuti “moto” pano ukugwiritsiridwa ntchito monga woimira kutheratu kwa chiwonongekocho chikutsimikiziridwa m’bukhu la Baibulo la Chibvumbulutso, kumene Ambuye Yesu Kristu akusonyezedwa kukhala mfumu yochita nkhondo. Kachitidwe kake ka nkhondo kakunenedwa kukhala kakusiya mitembo iri mbwee pa nkhope ya dziko lapansi, kuti idyedwe ndi mbalame zodya mitembo. (Chibvumbulutso 19:15-18) Chithunzi choterocho sichikanakwaniritsidwa muli monse ngati planeti lino likanasandutsidwa kwenikweni kukhala phulusa lopanda chamoyo.
7. Kodi mawu a pa 2 Petro 3:10 amasonyezanji ponena za chionongeko chikudzacho?
7 Chotero, pamenepa, kufotokoza kwa Petro chionongeko cha dziko lapansi ndi miyamba kumanena za kufafanizidwa kwa chitaganya cha anthu opanda umulungu. Maboma opangidwa ndi anthu amene alamulira chitaganya cha anthu monga “miyamba” adzafafanizidwa. (Yerekezerani ndi Yesaya 34:2-5; Mika 1:3, 4.) Phokoso la kusungunuka kwake kukhala mabwinja, lofotokozedwa kukhala ngati “phokoso loti fwaa” monga ngati ya kutuluka mwamphamvu kwa nthunzi, lidzakula kwambiri mu mphamvu yake, “Zinthu,” ndiko kuti, mzimu umene umasonkhezera anthu opanda umulungu kuganiza, kulinganiza, kulankhula ndi kuchita m’njira yawo yonyoza Mulungu zidzasungunulidwa kapena kufafanizidwa kosakhalako. (Yerekezerani ndi Machitidwe 9:1; Aefeso 2:1-3.) Kumeneku kudzachititsa mapeto a ziphunzitso zonse, nthanthi, malinganizidwe ndi makonzedwe zimene zimasonyeza mzimu wa mtundu wa anthu wotalikirana ndi Wam’mwambamwambayo, “Dziko lapansi ndi ntchito zimene ziri mmenemo zidzabvumbulutsidwa” kapena kuonetsedwa poyera kukhala zoyenera chionongeko. Sipadzakhala kupulumuka kuli konse kwa chiwalo chirichonse cha chitaganya cha anthu choipachi, “dziko lapansi.” (Yerekezerani ndi Genesis 11:1; Yesaya 66:15, 16; Amosi 9:1-3; Zefaniya 1:12-18.) Ntchito zonse za anthu osaweruzika-magulu ndi mabungwe kudzanso chimene chamangidwa mogwirizana ndi amenewa-zidzabvumbulidwa kukhala zotsutsidwa ndi Mulungu, zoyenera kutayidwa monga zapadzala zopanda pake.
8. Popeza kuti mbali iri yonse ya dongosolo liripoli idzaonongedwa, kodi ndi uphungu wotani wa Petro umene tiyenera kuukumbukira?
8 Chifukwa cha chimenecho, ife atumiki a Mulungu, timafuna kukhala ndi moyo mu mkhalidwe wosonyeza kuti timakhulupiriradi kuti mbali iri yonse ya dongosolo liripo lopamda umulunguli idzaonongeka kotheratu. Zimenezi ndizo zimene mtumwi Petro akutifulumiza kuchita, pamene akuti:
“Popeza kuti zinthu zonsezi zidzasungunuka motero, kodi inu muyenera kukhala anthu a mtundu wotani m’khalidwe la machitidwe oyera ndi ntchito za kudzipereka kwaumulungu, oyembekezera ndi kukumbukira kwambiri kudza kwa tsiku la Yehova, mwa limene miyamba pokhala iri pamoto idzasungunuka ndi zinthu pokhala zotentha kwambiri zidzasungunuka!”- 2 Petro 3:11, 12, NW.
9. Kodi ndani okha amene adzapulumuka chionongeko chikudzacho, ali ndi chiyembekezo cha madalitso osatha?
9 Pamene mbali iriyonse ya dongosolo lino isungunulidwa ndi “moto” wa mkwiyo wa Mulungu wosonyezedwa kupyolera mwa Ambuye Yesu Kristu, anthu okhala ndi mbiri ya khalidwe lolungama ndi kudzipereka kwaumulungu adzapulumuka. Kulambiri kowona sikuli kosachita kanthu, komangodzisonyeza kokha m’kupewa kwa munthuyo zolakwa zina. Pamene kuli kwakuti kusunga chiyero cha makhalidwe ndi chauzimu nkofunika kwambiri, tirinso ndi thayo la kusonyeza kukonda kwathu anthu anzathu mwa kukhala ofunitsitsa ndi amphamphu kulabadira ku zosowa zawo zakuthupi ndi zauzimu. Ndipo kumeneku kumathandizira kukhala ndi chisangalalo chachikulu, pakuti “muli chimwemwe chambiri m’kupatsa koposa ndi chimene chiri m’kulandira.”—Machitidwe 20:35, NW.
MACHITIDWE OSONYEZA KUTI IFE TIKUZINDIKIRA KUYANDIKIRA KWA MAPETO
10. Chifukwa cha “mapeto a zinthu zonse” akudzawo, kodi ndi chilangizo chotani chimene Petro anapereka?
10 Mawu otsatirapowa a mtumwi Petro amafutukula chimene tifunikira kukhala tikuchita polingalira kudza kwa “mapeto a zinthu zonse”: “Chifukwa chake, khalani olama maganizo, ndipo khalani amaso ponena za mapemphero. Koposa zonse, mukondane kwambiri wina ndi mnzake, chifukwa chakuti chikondi chimakwirira unyinji wa machimo. Mukhalirane aufulu kwa wina ndi mnzake popanda kudandaula.”—1 Petro 4:7-9, NW.
11. Kodi nchiyani chimene chikufunika kuti ife tikhalebe “olama maganizo”?
11 Mogwirizana ndi chilangizo chimenechi, kuti tikhalebe oyera mwamakhalidwe kapena olungama mu mkhalidwe, ndi kukhala okangalika m’kupititsa patsogolo thanzi lauzimu la ena, tifunikira kukhala “olama maganizo.” Zimenezi zimafunikira kuti tipewe kulola malingaliro athu kulamulira ndi kuwalola kutichititsa kukhala osakhazikika mwamalingaliro. Kuli kofunika kwambiri kuti ife tizindikire zinthu zofunikadi kwambiri m’moyo, kotero kuti tikhale ndi lingaliro lokhazikika la zimene ziyenera kuyambirira.—Afilipi 1:9, 10.
12. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kukhala “amaso ponena za mapemphero”? (b) Kodi ndi motani mmene Petro anafikira pa kuzindikira kufunika kwake kuchokera m’chokumana nacho cha iye mwini?
12 Ngati tikufuna kukhalabe atumiki okhulupirika a Mulungu, sitingayembekezere kupambana m’nyonga ya ife eni. Tifunikira kuyang’ana kwa Yehova Mulungu kaamba ka chithandizo, tikumakhala “amaso ponena za mapemphero.” Kuchokera m’chokumana nacho cha munthu mwini, mtumwi Petro anaphunzira kufunika kwa kukhala “maso,” wodikira kapena wogalamuka ponena za mapemphero. Patangotsala pang’ono kuti Yesu Kristu agwidwe ndi gulu lachiwawa lokhala ndi zida m’munda wa Getsemane, Mwana wa Mulungu anali atalimbikitsa Petro, Yakobo ndi Yohane kupemphera kotero kuti asakhale ogwera mkuyesedwa. Komabe, atumwi onse atatuwo anagona tulo pa nthawi yobvuta kwambiri imeneyi. (Mateyu 26:36-46; Marko 14:32-42; Luka 22:39-46) Atagalamutsidwa ndi kulephera kwake kukhala “maso” ponena za pemphero, Petro pambuyo pake anakana Yesu Kristu katatu. (Yohane 18:17, 18, 25-27) Komabe, kuchiyambiyambi, Petro anali atalengeza modzidalira kuti: “Ambuye ndiri wokonzekera kumka nanu ku ndende ndi kuimfa.” (Luka 22:33, NW) “Ngakhale onse adzakhumudwa chifukwa cha Inu, ine sindidzakumudwa nthawi zonse.”—Mateyu 26:33.
13. Kodi nchiyani chimene tingaphunzire kuchokera m’chokumana nacho cha Petro pamene iye analephera kukhala “wamaso ponena za mapemphero”?
13 Pali phunziro lofunika kwambiri kwa ife m’zimene zinachitikira Petro. Zingathe kugogomezera kwa ife upandu wa kudzidalira mopambanitsa. Chifukwa cha zofooka zathu ndi zoperewera, kuli kokha mwa chithandizo cha Mulungu kuti ife tingathe kupambana m’kukaniza chiyeso. Chifukwa cha chimenecho, tiyenitu, tipitirizebe kupemphera ndi maganizo ogalamuka ndi mtima umene uli wosagwedezeka m’kukonda kwake kwambiri Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu.
14. Kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala cholinga chathu m’kukwaniritsa thayo lathu Lachikristu, ndipo kodi ndi motani mmene chimenechi chimaonekera m’machitidwe athu ndi okhulupirira anzathu?
14 Kuphatikiza pa kukhalabe ogalamuka ndi kukhala okhazikika ponena za kukhala wophunzira Wachikristu, tichita bwino kulingalira kuti tione ngati chikondi chikutisonkhezera kukwaniritsa mathayo athu. (1 Akorinto 13:1-3) Mtumwi Petro anafulumiza kuti tiyenera kukhala ndi “chikondi chachikulu” kwa okhulupirira anzathu. Chikondi chachikulu chimenecho chimasonyezedwa mwa kukhala ndi mzimu wa kukhulukira. Pamene ziri choncho, sitimakulitsa kwambiri zolakwa za abale athu ndiponso sitimayang’anitsitsa kwambiri zolephera zawo. Sitimafunafuna zolakwa, kuika zolakwa za ena poonekera bwino kwambiri monga momwe kungathekere. Mwa kukhala kwathu okhululukira motero, chikondi chathu chidzakwirira unyinji wa machimo m’malo mwa kuwambvumbula kuti awonekere bwino kwa ena.
15. Kodi nchifukwa ninji kungakhale kofunika kusonyeza ufulu, ndipo kodi uwo uyenera kusonyezedwa ndi kaimidwe ka maganizo kotani?
15 Kusonyeza ufulu kulinso chisonyezero cha chikondi. Ha, ndi kwabwino kwambiri chotani nanga m’mene kumakhalira pamene tigawana ndi ena chakudya chathu ndi zofunika, makamaka awo amene ali osowa! (Luka 14:12-14) Pamene okhulupirira anzathu atayikiridwa ndi chirichonse kupyolera mwa masoka a chilengedwe kapena chizunzo, zimenezi zingatanthauze kutsegulira amenewa nyumba zathu kwa nyengo ya nthawi yotalikirapo. Kumeneku kungakhale kosapezetsa bwino kwambiri kwa ife, ndipo tingayedzamire ku kudandaula ponena za zofunika zoonjezereka zimene zikuikidwa pa chuma chathu ndi nyonga. Pa nthawi zoterozo tichita bwino kutetezera kudandaula nako kukhala titasonyeza ufulu nthawi ndi nthawi, tikamuzindikira kuti imeneyi ndi njira yabwino kwambiri imene tingasonyeze nayo kukonda kwathu awo amene Mulungu amawakonda.
16, 17. (a) Kodi ndi motani mmene tiyenera kuonera mphatso zimene tiri nazo? (b) Kodi ndi kaimidwe ka maganizo kotani kamene Paulo ananena kuti ndi kabwino ndipo iye mwiniyo anakasonyeza?
16 Tonsefe tiri ndi mphatso kapena maluso zimene tingathe kuzigwiritsira ntchito kaamba ka phindu la ena. Kukhalabe kwathu atumiki obvomerezeka a Mulungu kumadalira pa kugwiritsira ntchito kwathu mphatso zimenezi mofunitsitsa ndi mosangalala. Mwanzeru, tidzapewa kudziyerekezera ife eni ndi ena. Kumeneku kungapewetse kukhala kwathu ogwetsedwa ulesi pamene tiona kuti ena angathe kuchita zochuluka kwambiri koposa zimene ife tingachite. Ku mbali ina, sitikagonjera ku malingaliro alionse a kukhala wapamwamba pamene tingathe kuchita zochuluka kwambiri m’mbali ina ya ntchito koposa m’mene ena angachitire. (Agalatiya 6:3, 4) Onani zimene mtumwi Petro ananena: “Monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundu mitundu cha Mulungu.” (1 Petro 4:10) Chifukwa cha chimenecho, tiri ndi thayo la kugwiritsira ntchito mokwanira mphatso zirizonse zimene tingakhale nazo. Mwa chisomo cha Mulungu tiri chimene ife tiri ndipo ndi zimene tiri nazo. Chotero, nyonga zathu zonse, maluso ndi kukhoza zinthu zingathe kuonedwa monga mphatso zimene ife tapatsidwa ndi Yehova mwa kukoma mtima kwake kwapadera, kuti zigwiritsiridwe ntchito kuperekera chitamando ndi ulemu kwa Wam’mwambamwambayo.
17 Mtumwi Paulo anagogomezera kaimidwe ka maganizo koyenera mwa njira ya mafunso otsatirapowa: “Akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli nacho chiyani osati wachilandira? Koma ngati wachilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunachilandira?” (1 Akorinto 4:7) Ngakhale kuli kwakuti Paulo iye mwini ananena zimenezo iye “anagwira ntchito koposa” onse a atumwi ena, iye sanadzitengera thamo koma anaonjeza kuti,” si ine, koma chisomo cha Mulungu chakukhala ndi ine.”—1 Akorinto 15:10.
18. Kodi tiyenera kukhala tikugwiritsira ntchito mphatso zathuzo mu mkhalidwe wotani?
18 Monga adindo okhulupirika, tidzafuna kukhala odera nkhawa ndi kugwiritsira ntchito kwathu mphatso ziri zonse zimene tingakhale nazo m’kuthandiza ena mwauzimu ndi mwakuthupi. Mkhalidwe umene tikuchitira zimenezo ulinso wofunika kwambiri. Ponena za zimenezi, Petro analemba kuti:
“Akalankhula wina, alankhule ngati manenedwe a Mulungu; wina akatumikira, achite ngati mu mphamvu imene Mulungu apatsa, kuti m’zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Kristu, amene ali nawo ulemerero ndi mphamvu ku nthawi za nthawi. Amen.”—1 Petro 4:11.
19. Kodi ndi motani mmene tingalemekezere Mulungu pamene tikuthandiza ena mwauzimu ndi mwazinthu zakuthupi?
19 Chifukwa cha ichi, ngati tikuthandiza ena mwauzimu, tidzafuna kulankhula m’njira yakuti idzasonyeza kuti magwero a mawu athu otonthoza, achikondiwo ndiwo Yehova Mulungu. Pamene ziri choncho, kulalikira ndi kuphunzitsa kwathu zidzakhala zolimbikitsa sizidzachititsa malingaliro a kudziona kukhala wotsika ndi kuchita manyazi mwa awo amene tikuyesayesa kuwathandiza. Mofananamo, ngati tipereka nthawi yathu ndi nyonga m’kupereka chithandizo chakuthupi, tidzafuna kudalira pa Mulungu kaamba ka nyonga. Kumeneku kudzakhala kuchepetsa kugogomezera maluso a ife eni ndi kugogomezera kugwiritsira ntchito kwa Mulungu maluso athu a kuchita zinthu zabwino. Mwa njira imeneyi, Atate wathu wakumwamba adzalemekezedwa. (1 Akorinto 3:5-7) Popeza kuti kulemekeza kapena ulemu woterowo zikuperekedwa kwa Atate chifukwa cha kukhala kwathu ophunzira a Mwana wake, Yehova Mulungu ‘akulemekezedwa kupyolera mwa Yesu Kristu.’ Inde, Wam’mwambamwambayo ali wathayo kaamba ka kutipatsa kukhoza ndi nyonga yochitira zabwino.
20. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuyang’ana mtsogolo ku kudza kwa tsiku lalikulu la Yehova, ndipo chotero kodi nchiyani chimene tiyenera kukhala tikuchita?
20 Mwa kugwiritsira ntchito nthawi yathu, chuma ndi nyonga kuthandiza ena, timasonyeza kuti ife tiri mu mkhalidwe wa kukhala okonzekera mwauzimu, achire kukumana ndi tsiku lalikulu la Yehova. Kunena zowona, kuzindikira kwathu kuti Ambuye Yesu Kristu angadze pa nthawi iri yonse monga wochita kubwezera kwa Mulungu kungatisonkhezere kukhalabe amaso mwauzimu. Ndicho chifukwa chake tifunikira kukumbukira nthawi zonse kutsimikizirika kwa kudza kwa tsiku lalikulu la Yehova. Chifukwa chakuti lidzatsegula mwayi waukulu wa ophunzira onse okhulupirika a Yesu Kristu, tingathe moyenerera kuyang’ana mtsogolo ku iro mwa chiyembekezo chaphamphu. Tsiku la Yehova lidzatanthauza kumasulidwa kosatha ku chisalungamo ndi zitsenderezo za dongosolo la zinthu liripoli, kusangalala ndi madalitso a “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano.” Ha, ndi kofunika chotani nanga m’mene kuliri kuti ‘tikumbukire nthawi zonse’ tsiku limeneli, tikumalilakalaka motenthedwa manganizo! (2 Petro 3:12, 13) Kukhala kwathu ndi phande mokangalika m’kubukitsa chifuno cha Mulungu kwa ena kumapereka umboni wa kaimidwe ka maganizo koyenera. Kumasonyeza kuti ife tiri okhutiritsidwa maganizo kuti tsiku la Yehova lidzadza ndi kuti ena afunikira kudziwa ponena za iro ndi kuchita mogwirizana ndi chidziwitso chofunika kwambiri chimenechi.
21. (a) Kodi ife tingathe kukhala otsimikizira za chiyani ponena za lonjezo la Mulungu la “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano”? (b) Kodi ndi motani mmene kumeneku kuyenera kutiyambukirira?
21 Lonjezo la Mulungu la “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano” lonenedwa choyamba kupyolera mwa mnereri Yesaya, lidzakwaniritsidwa m’tanthauzo lake lotheratu. (Yesaya 65:17; 66:22) Ulamuliro wolungama wokhala m’manja mwa Yesu Kristu ndi mafumu ndi ansembe anzake pa chitaganya cha pa dziko lapansi chochita mogwirizana ndi lamulo la Mulungu uyenera kukhala weniweni. (Chibvumbulutso 5:9, 10; 20:6) Kutsimikizirika kwa zimenezi kungathe kutisonkhezera kugwira ntchito, kukumatisonkhezera kuchita zonse zimene tingathe kukhala pakati pa awo amene akugawana nawo madalitso amene adzatulukapo. Mtumwi Petro analangiza kuti: “Okondedwa, popeza muyembekezera zinthu zimenezi chitani zotheka kuti mupezedwe potsirizira pake opanda banga ndi opanda chirema ndi mu mtendere.” (2 Petro 3:14, NW) Monga atumiki a Mulungu, nkhawa yathu ndiyo kukhala obvomerezedwa ndi Ambuye Yesu Kristu, osachititsidwa kukhala ndi mawanga kapena zirema ndi makhalidwe audziko, njira ndi machitidwe. Timafuna kukhala omasuka ku chodetsa cha uchimo. Popeza kuti uchimo umadodometsa mtendere wathu ndi Mulungu, kokha mwa kukhalabe mu mkhalidwe umene machimo athu akutetezeredwa tingathe kupezedwa mu “mtendere” pa kudza kwa tsiku lake lalikulu.
YAMIKIRANI KUDEKHA KWA MULUNGU
22. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kukhala osadekha ponena za kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Mulungu?
22 Pamene kuli kwakuti moyenera tikuyembekezera “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano,” sitikufuna kukhala osadekha ponena za kukwaniritsidwa kwa lonjezo. Chenicheni chakuti tsiku la Yehova lalikululo silinadze kalelo chatheketsa chipulumutso chathu cha ife eni. Mtumwi Petro anafotokoza kuti:
“Lingalirani kudekha kwa Ambuye wathu monga chipulumutso, monga momwedi mbale wathu wokondedwa Paulo monga mwa nzeru yoperekedwa kwa iye anakulemberaninso, kunena za zinthu zimenezi monga momwe amachitiranso m’makalata ake onse. Komabe, mmenemo, muli zinthu zina zobvuta kuzimvetsetsa, zimene osaphunzitsidwa ndi osakhazikika akuzipotoza, monga momwe amachitiranso ndi Malemba ena onse, modziononga okha.”—2 Petro 3:15, 16, NW.
23. (a) Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kulingalira molakwa kudekha kwa Mulungu? (b) Kodi ndi motani mmene ena m’zaka za zana loyamba analepherera m’kuzindikira chifukwa cha kudekha kwa Mulungu?
23 Monga anthu amene amayamikira kudekha kwa Yehova, tidzafuna kukhala osamala kuti tisakulingalire molakwa, tikumalungamitsa njira ina yadyera pa maziko akuti tsiku lalikulu la Mulungu lingakhale likali kutalibe kwambiri. M’zaka za zana loyamba C.E. panali okhulupirira amene mwachionekere anachita zimenezi. Mtumwi Petro akuwafotokoza kukhala “osaphunzitsidwa ndi osakhazikika,” opanda kumvetsetsa bwino Mawu a Mulungu ndi osakhazikika ponena za chiphunzitso Chachikristu ndi kachitidwe. Anthu amenewa anayesa ngakhale kugwiritsira ntchito mawu ochokera m’makalata a mtumwi wouziridwa Paulo ndi mbali zina za Malemba kulungamitsira khalidwe lawo loipa. Mwina mwake kungakhale kuli kwakuti iwo anasonya ku zimene Paulo analemba ponena za kugwiritsira ntchito chikumbu mtima ndi ponena za kulengezedwa kukhala wolungama mwa chikhulupiriro ndipo osati ndi ntchito za chilamulo cha Mose kukhala zikupereka ufulu kaamba ka mitundu yonse ya machitidwe amene anali osemphana ndi chifuniro cha Mulungu. (Yerekezerani ndi Aroma 3:5-8; 6:1; 7:4; 8:1, 2; Agalatiya 3:10.) Iwo angakhale atagwiritsira ntchito molakwa mfundo zonga ngati zotsatirapozi:
“Kristu anatisandutsa mfulu, chifukwa chake chirimikani, musakodwenso ndi gori la ukapolo.” (Agalatiya 5:1) “Zinthu zonse ziloledwa kwa ine.” (1 Akorinto 6:12) “Zonse ziyera kwa iwo amene ayera mtima.” (Tito 1:15)
Komabe, iwo ananyalanyaza kuti Paulo anatinso:
“Musachita nawo ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwa chikondi chitiranani ukapolo. Pakuti mawu amodzi akwanaritsa chilamulo chonse ndiwo; Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.” (Agalatiya 5:13, 14) “Munthu asafune zake za iye yekha, koma za mnzake.”—1 Akorinto 10:24.
24. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuchenjerera mayanjano athu ngakhale mkati mwa mpingo?
24 Monga momwe zinaliri mu mpingo wa m’zaka za zana loyamba, momwemo lero lino pali awo amene akafutukula malire a ufulu Wachikristu mpaka kufika pa kukhalitsidwa akapolo ku uchimo. Chifukwa cha chimenecho, tichita bwino kuchenjerera mayanjano athu, kuchitira kuti tingalowe m’chisonkhezero choipa ndi kusocheretsedwa. Pokumbutsa chenicheni chimenechi, mtumwi Petro analemba kuti: “Inu, tsono, okondedwa, pozizindikiratu izi, chenjerani, kuti potengedwa ndi kulakwa kwa iwo osayeruzika, mungagwe kusiya chikhazikiko chanu.”—2 Petro 3:17.
PANGANI KUPITA PATSOGOLO MONGA MKRISTU
25, 26. Titapeza chikhulupiriro, kodi nchiyani chimene tiyenera kukhala tikuchita mogwirizana ndi 2 Petro 1:5-7?
25 Kuti tipewe kutayikiridwa madalitso amene Yehova Mulungu watisungira, tiyenera kufuna kupanga kupita patsogolo m’kukhala ndi ntchito Zachikristu. (2 Petro 3:18) Kuchita kwathu motero kumagwirizana ndi chilimbikitso cha mtumwi Petro:
“Inde, pa chifukwa cha ichi, pa kuonjezerapo changu chonse, onjezerani ku chikhulupiriro chanu ukoma, pa ukoma wanu chidziwitso, pa chidziwitso chanu kudziletsa, pa kudziletsa kwanu chipiriro, pa chipiriro chanu kudzipereka kwaumulungu, pa kudzipereka kwanu kwaumulungu chikondi chaubulu, pa chikondi chanu chaubale chikondi.”—2 Petro 1:5-7, NW.
26 Kupyolera mwa Mwana wake, Yehova Mulungu watipatsa kukhoza kukhala ndi chikhulupiriro. Chifukwa cha chimenecho, molabadira, kapena chifukwa cha, zimene zachitidwa kaamba ka ife, tifunikira kukulitsa mikhalidwe ina yabwino imene imapereka umboni wa kukhala kwathu ndi chikhulupiriro chenicheni. Kumeneku timakuchita mwa kulola Mawu a Mulungu ndi mzimu wake kusonyeza mphamvu yake yokwanira m’miyoyo yathu. (2 Petro 1:1-4) Mtumwi Petro analangiza kuti ‘tionjezere changu chonse’ kupanga kuyesetsa kwamphamphu ndi nyonga yonse imene tiri nayo, mogwirizana ndi ntchito imene Atate wathu wakumwamba akuchita m’kutipangitsa kukhala Akristu achikwanekwane.—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 3:6, 7; Yakobo 1:2-4.
27. Kodi nchiyani chimene chikutanthauzidwa mwa kuonjezera ukoma ku chikhulupiriro chathu?
27 Kuonjezera kwathu ukoma ku chikhulupiriro kumatanthauza kuyesayesa kukhala anthu a makhalidwe abwino kwambiri m’kutsanzira Wopereka chitsanzo wathu, Kristu. Ukoma woterowo kapena ubwino wa makhalidwe uli mkhalidwe wotsimikizirika. Wokhala nawo wake si kokha kuti amapewa kuchita zoipa kapena kubvulaza anthu anzake komanso amafunafuna kuchita zabwino, akumayankha motsimikizira zosowa zauzimu, zakuthupi ndi za malingaliro za ena.
28. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kukula m’chidziwitso?
28 Ubwino wa makhalidwe sungakhalepo popanda chidziwitso. Tifunikira chidziwitso kuti tilekanitse chabwino ndi choipa. (Ahebri 5:14) Nchofunikanso kutsimikizira mmene ubwino wotheratu uyenera kusonyezedwera mu mkhalidwe woperekedwa. (Afilipi 1:9, 10) Mosafanana ndi kungokhulupirira ziri zonse, kumene kumapepuza kapena ngakhale kukaniza chidziwitso, chikhulupiriro chokhazikika zolimba chimakhala ndipo nthawi zonse chimapindula ndi chidziwitso. Chifukwa cha chimenecho, kukhala kwathu akhama m’kugwiritsira ntchito Malemba Oyera kudzalimbikitsa chikhulupiriro chathu pamene tikupitirizabe kukula m’chidziwitso chonena za Yehova Mulungu ndi Mwana wake.
29. (a) Kodi nchifukwa ninji chidziwitso chiri chofunika kwambiri m’kukulitsa kudziletsa? (b) Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa kudziletsa ndi chipiriro?
29 Chidziwitso chimenechi chimatumikira kutiletsa kugonjera ku zilakolako zochimwa, kukhala wosakhala wachikatikati ndi kusadziletsa m’khalidwe, kapena m’njira zina kukhala ndi liwongo la kulephera kwakukulu kusonyeza chifanizo chaumulungu m’khalidwe, mawu ndi kachitidwe. Chidziwitso chimathandizira kukhala kwathu ndi kudziletsa, kukhoza kudziletsa munthu mwiniwe, machitidwe ndi kulankhula. Mwa kupitirizabe kusonyeza kudziletsa, tidzakhala ndi mkhalidwe wofunika kwambiriwo wa chipiriro. Nyonga ya m’kati imene chipiriro chimatulutsa ingatithandizenso kuletsa kugonjera ku zilakolako zochimwa, kulolera molakwa pamene tikubvutika ndi chizunzo kapena kukhala otanganitsidwa ndi nkhawa za tsiku ndi tsiku, zosangalatsa kapena chumba chakuthupi. Chipiriro chimenechi chimachokera m’kudalira pa Wam’mwambamwambayo kaamba ka nyonga ndi chitsongozo.—Yerekezerani ndi Afilipi 4:12, 13; Yakobo 1:5.
30. (a) Kodi kudzipereka kwaumulungu nchiyani, ndipo kodi ndi motani mmene kumadzisonyezera? (b) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti umulungu sungathe kukhalapo mosiyana ndi chikondi chaubale?
30 Kudzipereka kwaumulungu kapena kupembedza kuyenera kuwonjezeredwa ku chipiriro. Mkhalidwe umenewo umadziwikitsa mkhalidwe wathunthu wa moyo wa Mkristu wowona. Umadzisonyeza m’kulemekeza ndi kuopa Mlengi ndi ulemu waukulu ndi kulemekeza ndi kuopa Mlengi ndi ulemu waukulu ndi kudera nkhawa ndi makolo kapena ena amene ali oyenerera kudziperekako. (1 Timoteo 5:4) Komabe, popanda chikondi chaubale, kukhala waumulungu sikungakhalepo. Mtumwi Yohane akulongosola kuti:
“Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wake, ali wabodza; pakuti iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sakhoza kukonda Mulungu amene sanamuona.” (1 Yohane 4:20)
Ali yense wodzinyadira pa kupembedza kwake ndi kudzipereka akakhalabe woperewera momvetsa chisoni ngati iye analephera kusonyeza chikondi, kukoma mtima ndi ubwenzi kwa abale ake. Sitingathe kukhala ofunda kwa Mulungu ndi kukhala ozizira kwa abale athu.
31. Kodi chikondi chathu chiyenera kusonyezedwa kwa yani, ndipo chifukwa ninji?
31 Chikondi ndicho mkhalidwe wapadera umene uyenera kukhala woonekera kwenikweni m’miyoyo yathu. Mtundu umenewu wa chikondi suyenera kuongolekezera kwa abale athu Achikristu okha. Pamene kuli kwakuti tiyenera kukhala ndi chikondi kwa abale athu auzimu, chikondi chiyenera kusonyezedwa kwa anthu onse. Chikondi chimenechi sichiri chodalira pa kaimidwe ka makhalidwe abwino ka munthuyo. Chiyenera kusonyezedwa ngakhale kwa adani, makamaka chikumadzisonyeza m’chikhumbo cha kuwathandiza mwauzimu.—Mateyu 5:43-48.
32. Kodi nchiyani chimene chimatukukapo pamene tigwiritsira ntchito uphungu wa pa 2 Petro 1:5-7?
32 Kodi nchiyani chimene chimatulukapo pamene ukoma, chidziwitso, kudziletsa, chipiriro, kudzipereka kwaumulungu, chikondi chaubale ndi chikondi zionjezeredwa ku chikhulupiriro? Mtumwi Petro akuyankha kuti: “Pakuti izi zikakhala ndi inu, ndipo zikachuluka, zidzachita kuti musakhale aulesi kapena opanda zipatso pa chizindikiritso cha Ambuye wathu Yesu Kristu.” ( 2 Petro 1:8) Pamenepo ife sitidzakhala titangoyima malo amodzi, osagwira ntchito, akufa mwauzimu. Titakhala ndi mikhalidwe yaumulungu ikukhala m’mitima yathu, ikumakhaladi mbali ya ife, tidzasonkhezeredwa kuganiza, kulankhula ndi kuchita m’njira yobvomerezedwa ndi Mulungu. (Yerekezerani ndi Luka 6:43-45.) Pamene zimenezi ziri choncho ponena za ife, kudza kwa Ambuye Yesu Kristu kudzakhala ndi ulamuliro wotheratu pa zochitika za dziko lapansi kudzakhala kuyamba kwa madalitso akulu kopambana amene tikuwalingalira pa tsopano lino.
33-35. Kodi ndi motani mmene timapindulira nako kukhala ndi moyo monga ophunzira a Yesu Kristu?
33 Chifukwa cha chimenecho, tiyenitu, tisakhale konse osasamala ponena za khalidwe lathu kapena m’kuchita mathayo athu Achikristu, kuphatikizapo ntchito yofunika kwambiri ya kubukitsa uthenga wa Mulungu kwa ena. Ngati tasankha moyo wa kukhala wophunzira wa Yesu Kristu tingathe kusangalala ndi chikumbu mtima choyera ndi utsamwali wabwino ndi okhulupirira anzathu. Tingathe kukhala ndi chithandizo chopatsa nyonga cha Mulungu m’nthawi za chiyeso, ndipo unansi wathu ndi ena udzaongokera pamene ife mosamalitsa tikugwiritsira ntchito malamulo a khalidwe labwino a Baibulo.
34 Palibe mbali ina m’moyo—pa nyumba, pa ntchito, m’kuchita kwathu ndi akuluakulu a boma okhala pa ma udindo onse-imene sidzakhudzidwa bwino ngati tiyesayesa kutsatira Mawu a Mulungu. Kudzachitititsanso kukhala ozindikira bwino kwambiri kufunika kwa kukhala wa mtima wonse m’kufikira anthu ochuluka monga momwe kungathekere ndi uthenga wotonthoza wa Baibulo. Tidzapeza chimwemwe chachikulu ndi lingaliro lowona la chipambano m’kulabadira zosowa za anthu anzathu, makamaka ku zosowa zao zauzimu.
35 Chofunika kopambana koposa zonse, kukhala ndi moyo monga ophunzira enieni a Yesu Kristu ndiko njira yokha imene iri ndi lonjezo la mtsogolo mwamuyaya mwa kukhala ndi moyo kwachimwemwe. Ndithudi sitikafuna kutayikiridwa ndi zimene tapeza. Tiyenitu kupita kwa tsiku liri lonse kutipeze tiri mu mkhalidwe wa kukhala okonzekera kudza kwa Mbuye wathu mu udindo wa kukhala mfumu yopambana kotheratu. Ndi pamenepo pokha pamene ife tingathe kukhala ndi phande m’chisangalalo chopanda malire chochokera m’kukhala kwathu titasankha kumamatira ku thayo lathu la kutumikira Yehova Mulungu mokhulupirika.