Mutu 10
Tetezerani Chiyembekezo Chanu Chachikristu
1. Kodi nchiyani chimene chidzapangitsa ‘miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano’ kukhala zofunika kwambiri?
HA, ndi kwabwino kwambiri chotani nanga mmene kuliri kulingalira za chiyembekezo cha moyo wopanda zopweteka, chisoni kapena imfa! Ndipo komabe, kwenikweni, kuli kwabwinodi kwambiri kuti kumasuka kwathu ku zinthu zimenezi kudzadza kupyolera mwa kuchotsedwa kwa kupanda ungwiro ndi uchimo. Ha, ndi dalitso lotani nanga m’mene lidzakhalira kusalimbana zikhoterero zolakwa ndi zizolowezi zimene ife tikudziwa kuti zimangochititsa chibvulazo kwa ife eni ndi ena! Kudzakhaladi kosangalatsa pamene liwu liri lonse limene tikulankhula, lingaliro liri lonse limene tikuganiza, chiri chonse cha machitidwe athu, zidzakhala kaamba ka ubwino wa onse, zosonyeza kwenikweni kuti Atate wathu wakumwamba ali wotani, zosachokera m’zolinga zadyera. Inde, ndithudi, chilungamo chidzachuluka ‘M’miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano’ zopangidwa ndi Mulungu. Zowonadi chimenechi ndi chiyembekezo choyenera kuchititezera.—2 Petro 3:13.
2. (a) Kuti tikhale ndi kukwaniritsidwa kwa chiyembekezo chathu Chachikristu, kodi nchiyani chimene tiyenera kuchita? (b) Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kudabwa kuti anthu ofuna zawo zokha akatha kupezeka pakati pa odzitcha kukhala Akristu?
2 Kuona kukwaniritsidwa kwa chiyembekezo chathu Chachikristu, tifunikira kuchikumbukira nthawi zonse ndi kukhala ndi moyo mogwirizana nacho. Tingachite zimenezo kokha ngati tikaniza zisonkhezero zonse zimene zikatha kuphimba kapena kuononga chiyembekezo chathu. Nthawi zina chisonkhezero chobvulaza choterocho chingachokere kwa anthu opanda uzimu ofuna zawo zokha ogwirizana ndi mpingo wa anthu a Mulungu. Zimenezi siziyenera kutidabwitsa, pakuti mtumwi Petro analemba kuti: “Panakhalanso aneneri onyenga pakati pa anthu [Israyeli], monga momwenso padzakhalira aphunzitsi onyenga pakati panu [Akristu].” (2 Petro 2:1a, NW) Monga momwedi zinaliri ndi Israyeli wachibadwidwe, Akristu ali okhoza kuipa kuchokera mkati mwa mpingo.
“ADZALOWETSAMO MWAKACHETECHETE MIPATUKO YOWONONGA”
3, 4. Kodi ndi motani m’mene mtumwi Petro akufotokozera mmene aphunzitsi onyenga amafalitsira cholakwa?
3 Ponenapo mawu ponena za m’mene malingaliro olakwa amagwirira ntchito, mtumwi Petro akupitirizabe kuti: “Amenewawo adzalowetsamo mwakachetechete mipatuko yoononga.” (2 Petro 2:1b, NW) Mtumwiyo sanali kunena za anthu amene anangokhala ndi bvuto la kumvetsetsa chabe nkhani zina, kapena anthu amene malingaliro awo, osungidwa mowona mtima, sangagwirizane m’mbali zonse ndi aja a ochuluka. (Yerekezerani Aroma 14:1-6.) Iye mmalo mwake amachita ndi awo amene mwadala amayesayesa kugawanitsa kapena kuipitsa.
4 Anthu otero sikawirikawiri kuti amakhala osabisa, onena zowona kapena olunjika. Kawirikawiri iwo ‘amalowetsamo’ malingaliro awo osagwirizana ndi Malemba mwakachetechete, mwa njira yobisika. M’Chigriki choyambirira chogwiritsiridwa ntchito ndi mtumwi Petro, mawuwo “adzalowetsamo mwakachetechete” ndiro kwenikweni “kutsogolera kumbali, kapena kutsagana ndi.” Imeneyi ndiyo njira yawo. Limodzi ndi chiphunzitso china chabwino Chamalemba, iwo mwapang’onopang’ono ndi mwamachenjera amalowetsamo malingaliro awo ogawanitsa ndi oipisa. Mwa kukonzekeretsa choyamba maganizo a omvetsera awo ndi chowonadi chowonekera bwino, kapena ngakhale mwa mtandadza wautali ndi wocholowanacholowana wa zigomeko, iwo kawirikawiri angawachititse kubvomereza malamulo a khalidwe ena amene angangotsogolera ku cholakwa basi. Iwo angagwiritsire ntchito Baibulo, koma iwo samaliphunzitsa kwenikweni, akumagwiritsira ntchito chiri chonse chimene iwo achiona kukhala choyenera ndi kukhotetsa ziphunzitso zake kuti ziyenerane ndi zimene iko, kaamba ka phindu la munthu mwini, akuyesa kupititsa patsogolo. Motero, chimene kwenikweni chiribe maziko olimba Amalemba chimapangidwa kuonekera kukhala chowona.
5. Kodi ndi motani m’mene njira ya Satana m’kunyenga Hava imasonyezera njira za mphunzitsa wa chinyengo?
5 Njira yochitira zinthu imeneyi ikusonyezedwa bwino lomwe mwa njira imene Satana ananyengera Hava mwa njira ya chinjoka. Poyambirira, funso lowonekera kukhala lopanda cholakwa linafunsidwa: “Eya! kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m’mundamu?” (Genesis 3:1) Funso limenelo linakhotetsa chowonadi. Iro linapereka lingaliro lakuti Wam’mwambamwambayo anali woletsa mosayenera, kukaniza anthu oyambirirawo kanthu kena kamene iwo anali okayenerera. Mawu a chinjokacho ayenera kukhla atachititsa Hava kudabwa chifukwa chenicheni chimene iye sakanadyera za mu “mtengo wa kudziwitsa zabwino ndi zoipa.” Mwa njira imeneyi Satana anakonzekeretsa maganizo ake kufuna kupeza yankho. Ndiyeno panadza yankho lachindunji la chinjoka lakuti: “Kufa simudzafai; chifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadye umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.”—Genesis 3:4, 5.
6. (a) Kodi ndi zinthu zotani zimene zingapangitsa Hava kunyengekera ku kubvomereza cholakwa? (b) Kodi ndi motani mmene gulu lokhala ndi liwongo linapangidwira monga chotulukapo cha bodza la Satana?
6 Popeza kuti maganizo a Hava anali atakonzekeretsedwa mwamachenjera za iro, yankho lonamalo silinadze monga chodabwitsa. Chenicheni chakuti “njoka inali yakuchenjera” yoposa zamoyo zonse chinaonekera kukhala chikupereka lingaliro lakuti cholengedwa choterocho sichikanakhala konse magwero a chidziwitso chonyenga. (Genesis 3:1) Ndiponso, mtengowo unali wokoma m’maso ndipo zipatso zake zinapereka chisonyezero cha kukhala zabwino kuzidya. Hava ananyengedwa kotheratu. Pambuyo pa kudya chipatso chokanizidwacho, iye anakakamiza Adamu kugwirizana naye m’kupandukira Mulungu. (Genesis 3:6) Mwa njira imeneyi mawu onamawo a chinjoka anapambana m’kuchititsa anthu oyambawo kutalikirana ndi Atate wawo wakumwamba. Kwenikweni, gulu lopangidwa ndi anthu awiri lokhala ndi liwongo linapangidwa.
7. (a) Kodi nchifukwa ninji awo amene amachititsa magawano mu mpingo amakana Kristu? (b) Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti iwo ‘amadzidzetsera chionongeko chofulumira’?
7 Mwa njira zofananazo, anthu angayambitse mzimu wogawanitsa mu mpingo, mzimu wa “chipani” wopikisana. Popeza kuti liri lonse la magulu opanduka oterowo liri ndi mizu yake m’cholakwa ndipo mwadala likuyesa kuchititsa kusagwirizana, kaimidwe kake ndi ziphunzitso zimanamizira Mwana wa Mulungu, amene anagula mpingo Wachikristu ndi mwazi wake. Chifukwa cha chimenecho, mtumwi Petro akunena za aphunzitsi onyenga oterowo kukhala ‘akukana ngakhale mbuye amene anawagula, akumadzidzetsera chionongeko chofulumira.’ Inde, pamene anthu angoleka kumamatira zolimba kwa Kristu monga mutu, iwo amamkana ndi kudzilowetsa m’njira imene iri yatsoka mwamakhalidwe ndi mwauzimu. Pangangokhala chotulukapo chimodzi chokha—chionongeko. Pamene nthawi ya kupereka chiweruzo chachitsutso ifika, sipadzakhala kuchedwa. Chiweruzo cholungama chidzaperekedwa mofulumira. Mwa kulandira cholakwa mofunitsitsa, anthu olowetsedwamowo ‘amadzidzetsera chionongeko chofulumira.’—2 Petro 2:1, NW.
8. Kodi ndi chiyambukiro chotani chimene “khalidwe loipa” la odzitcha kukhala Akristu lingakhale nacho pa anthu a kunja kwa mpingo?
8 Momvetsa chisoni, anthu amenewa, chifukwa chakuti amadzitcha kukhala Akristu pamene akuchita mosadziletsa, amaika chodetsa pa mbiri yabwino ya atumiki okhulupirika a Mulungu. Ambiri amene amaona mkhalidwe woluluzika wa anthu ena odzitcha kukhala Akristu amayamba kulankhula mwamwano kapena mochitira chipongwe onse amene amadzidziwikitsa iwo eni kukhala otero. Imeneyi ndiyo mfundo imene Petro ananena pamene analemba kuti: “Ndipo ambiri adzatsata zonyansa zawo; chifukwa cha iwo njira ya chowonadi idzanenedwa zamwano.”—2 Petro 2:2, NW.
CHENJERANI NDI KUKHALA ‘POPEZERAPO PHINDU NDI MAWU ONYENGA’
9. (a) Kodi nchiyani chimene chimasonkhezera anthu oipa kuyesa kudzisonkhanitsira atsatiri? (b) Kodi nchiyani chimene chidzachitikira anthu amenewo ndi awo amene akunyengedwa nawo?
9 Kodi nchiyani chimene chimasonkhezera anthu oipa kudzichulutsira owatsira? Mtumwi Petro akuyankha kuti: “Mwa chisiriro adzakuyesani popezerapo phindu ndi mawu onyenga.” (2 Petro 2:3a, NW) Anthu amenewa akufunafuna kuzipezera mapindu a zinthu zakuthupi a iwo eni kapena kufuna ulamuliro, ukumu ndi ulemu zimene zimachokera m’kuonedwa kukhala aphunzitsi. Mwa njira ya “mawu onyenga,” ndiko kuti, manenedwe a chinyengo, kuphatikizapo zigomeko zomvekera bwino, iwo amayesa kupeza mapindu pamtu pa ena, akumawadyera masuku pamutu. Popeza kuti zonse ziwiri zisonkhezero ndi ziphunzitso ziri zolakwa, chotulukapo kwa anthu olowetsedwamowo ndicho kuonongeka. Mtumwi Petro akuptirizabe kuti:
“Ponena za iwowa, chiweruzo chakale lomwe sichinachedwa, ndipo chiwonongeko chawo sichiwozera. Ndithudi ngati Mulungu sanaleka kulanga angelo amene anachimwa, koma, mwa kuwaponya iwo mu Dzenje, anawapereka iwo ku maenje a mdima waukulu kuti akasungidwe kaamba ka chiweruzo; ndipo iye sanaleka kulanga dziko lakale, koma anasunga Nowa, mlaliki wa chilungamo, bwino lomwe limodzi ndi ena asanu ndi awiri pamene iye anadzetsa chigumula pa dziko la anthu opanda umulungu; ndipo mwa kusandutsa mizinda ya Sodumu ndi Gomora kukhala phulusa iye anaitsutsa, akumapereka chitsanzo kaamba ka anthu opanda umulungu a zinthu zirikudza; ndipo iye anamlanditsa Loti wolungamayo, amene anasautsidwa kwakukulu ndi kumwerekera kwa anthu onyoza lamulo mu mkhalidwe wachisembwere-pakuti munthu wolungamayo mwa zimene iye anaziona ndi kuzimva pamene anali kukhala pakati pawo tsiku ndi tsiku zinali kumauzunza moyo wake wolungamawo chifukwa cha zochita zawo zosaweruzika-Yehova amadziwa kulanditsa anthu odzipereka mwaumulungu ku chiyeso, koma kuwasunga anthu osalungama kaamba ka tsiku la chiweruzo kuti akadulidwe, komabe, makamaka, awo amene amatsatira thupi limodzi ndi chikhumbo cha kuliipitsa ndi amene amanyozetsa umbuye.”—2 Petro 2:3-10, NW.
10. (a) Kodi ndi liti pamene mawu oyambirira a chiweruzo cha Mulungu pa ‘mbweu ya chinjoka’ ananenedwa? (b) Kodi nchifukwa ninji kuperekedwa kwake ‘sichikuchedwa’?
10 Kuperekedwa kwa chiweruzo cha imfa kumene Mulungu wakulamula ‘kuchokera kale’ motsutsana ndi onse amene afikira kukhala a ‘mbeu ya chinjoka’ chidzachitika mosalephera. (Genesis 3:15; Yohane 8:44, Yuda 14, 15) Ngakhale kuli kwakuti poyambirira chinanenedwa pafupifupi zaka 6,000 zapitazo ndi kubwerezedwa chiyambiri pa nthawi imeneyo, chiweruzo chimenechi ‘sichikuchedwa’ monga ngati kuti sichidzafika. Chionongekocho chiri chotsimikizirika kudza, pakuti icho sichinangoima pa malo amodzi. Chiri chamoyobe kwambiri m’chifuno cha Mulungu.
11. (a) Kodi nchiyani chimene chinachitikira angelo osamvera, ndipo kodi nchiyani chimene chikali kuwayembekezera? (b) Kodi nchiyani chimene chikutsimikiziridwa ndi kulangidwa kwa angelowo, kuonongedwa kwa anthu opanda umulungu m’Chigumula, ndi kufafanizidwa kwa okhala m’Sodomu ndi Gomora?
11 Monga momwe Petro anasonyezera, ngakhale angelo amene anasangalala kukhala pamaso pa Mulungu penipenipo koma amene pambuyo pake anakhala osakhulupirika sanasiyidwe ‘osaponyedwa m’Dzenje,” ndiko kuti kutsitsidwira ku mkhalidwe wotsikitsitsa. Kudulidwa ku chidziwitso chonse chaumulungu, kuletsedwa kusabwereranso ku malo awo oyambirira kumwamba ndi kuchepetseredwa ntchito zawo, angelo osamverawo akudzipeza iwo eni ali mu mkhalidwe wofanana ndi “maenje a mdima waukulu,” akuyembekezera chiweruzo cha imfa choperekedwa ndi Yesu Kristu. (Yerekezerani ndi Chiibvumbulutso 20:1-3, 7-10.) Mofananamo, Yehova Mulungu sanaleka kuononga dziko lonse la anthu oipa m’chigumula cha pa dziko lonse kapena kuchitapo kanthu motsutsana ndi anthu okhala mu Sodomu ndi Gomora achisembwere chonyansawo m’masiku a Loti. Anthu okha olungama onga ngati Nowa ndi banja lake ndi onga Loti angathe kukhala ndi chiyembekezo cha kupulumuka chiweruzo cha Mulungu ndi kulanditsidwa ku chiyeso chochititsidwa ndi kukhala pakati pa anthu osaweruzika. Komabe, kunena kwa kudzitcha kukhala Mkristu sikudzapulumutsa ali yense amene akufunafuna kudetsa thupi la ena mwa kuchita chisembwere.
CHENJERANI NDI AWO AMENE AMANYOZETSA ULAMULIRO
12, 13. Monga momwe kwasonyezedwera pa 2 Petro 2:10b,11, kodi mkhalidwe wa anthu oipa ndi wotani kulinga ku ulamuliro?
12 Kawirikawiri zolinga zoipa za anthu oipa zingathe kuzindikiridwa ndi mkhalidwe wawo kulinga ku ulamuliro. Iwo “amanyozetsa umbuye,” kunyozetsa ulamuliro wa mtundu uli wonse. Mtumwi Petro akupitirizabe kufotokoza kwake: “Osaopa kanthu, otsata zofuna zawo, samanthunthumira ndi anthu olemekezeka koma amalankhula mwamwano, pamene angelo, ngakhale kuli kwakuti ali anyonga ndi amphamvu kwambiri, samadzitengera chitsutso mwa mawu amwano, osatero chifukwa cha kulemekeza Yehova.”—2 Petro 2:10b, 11, NW.
13 Chifukwa cha chimenecho, tikafuna kukhala ochenjera ndi anthu olimba mtima, odzikuza amene samalemekeza “olemekezeka.” Mu mpingo Wachikristu, amuna okhulupirika oikiziridwa thayo samadziona kukhala ali ndi malo apamwamba kapena kukhala okwezeka pamwamba pa okhulupirira anzawo koma modzichepetsa amadziona kukhala atumiki. (Mateyu 23:8, 1 Atesalonika 2:5-12) Komabe, gawo lawo la utumiki liri ‘lolemekezeka,’ popeza kuti iwo anaikidwa ndi mzimu woyera kukhala oyang’anira kapena “abusa” a gulu la nkhosa. (Machitidwe 20:28; yerekezerani ndi Aroma 11:13.) Iwo amaimiranso Ambuye waulemereroyo Yesu Kristu ndi Mbusa Wamkulu Yehova Mulungu. (1 Petro 2:25; 5:4) Ndicho chifukwa chake Malemba amalimbikitsa ziwalo za mpingo kukhala zogonjera kwa amene akutsogolera. (Ahebri 13:17) Pamene kuli kwakuti amuna oterowo, monga Petro iye mwini, angapange zolakwa, zimenezi sizikapangitsa ali yense kupeza chodzikhululukira nacho chowanenera mwamwano. (Yerekezerani ndi Agalatiya 2:11-14; 3 Yohane 9, 10.) “Abusa” ogwira ntchito zolimba mayenerera ulemu wa mpingo. Koma anthu amene amasonkhezera ena kuchita zoipa samaleka kuchitira chipongwe akulu Achikristu. Ngati munthu anenera mwau amwano, achipongwe kwa mbale wake, Yehova Mulungu ndi Mwana wake amaziona monga ngati kuti zachitidwira kwa iwo eniwo.
14. Kodi ndi motani mmene angelo okhulupirika amasonyezera mkhalidwe wosiyana kotheratu ndi uja wa aphunzitsi onyenga?
14 Ha, ndi osiyana chotani nanga mmene aliri aphunzitsi otsata zofuna zawo a chinyengowo ndi angelo okhulupirika! Angelo ali ndi changu pa chilungamo. Koma iwo samagwiritsira ntchito kanenedwe kaukali, kamwano ngakhale pamene akuchita ndi otsutsa. Mwa chitsanzo, “Mikayeli mkulu wa angelo, pakuchita makani ndi mdierekezi anatsutsana za thupi la Mose, sanalimbika mtima kumtchulira chifukwa chomchitira mwano, koma anati, Ambuye akudzudzule.” (Yuda 9) Kuchokera m’zimenezi tinganene kuti angelo ena okhulupirika sakatembenukira konse ku kuunjika zitonzo pa ali yense koma modekha, komabe mwamphamvu, akasonyeza zenizeni. Iwo ali ndi ulemu woyenera kwa Mlengi wawo, akumazindikira kuti kulankhula kwamwano sikuli konse kogwirizana ndi kupatulika kwake kapena chiyero.
15. Mogwirizana ndi uphungu wa Petro, kodi ife tiyenera kuchenjerera mtundu wotani wa anthu?
15 Tiyenera kukhala ochenjera ndi anthu amene moipa amanyoza ena ndiyeno napitiriza kudzipititsa patsogolo iwo eni. Chenicheni chakuti anthu oterowo sadzapulumuka chiweruzo chachitsutso kaamba ka machitidwe awo chiyenera kukumbukiridwa nthawi zonse ndi ife. Kutereku kungatithandize kukhala okondweretsedwa ndi ena koma, kwenikweni, akufunafuna phindu la iwo eni. Mtumwi Petro ananenapo mawu ponena za chotulukapo cha anthu ofunafuna za iwo okha, kuti:
“Anthu amenewa, mofanana ndi nyama zopanda nzeru zobadwa mwachibadwa kuti zigwidwe ndi kuphedwa, mu zinthu zimene sakudzidziwa ndi kulankhula monyoza, adzaonongedwadi mu njira yawoyawo ya chionongeko, akumadzilakwira monga mphotho ya kulakwa.”—2 Petro 2:12, 13a, NW.
16 Kodi ndi motani mmene anthu oipa aliri ngati “nyama zopanda nzeru”?
16 Anthu amene akulamulidwa ndi zikhumbo zoipa amachita ngati “nyama zopanda nzeru.” Ponena za zinyama Yehova Mulungu anati: “Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu.” (Genesis 9:3) Mwa kukhala ngati “nyama zopanda nzeru” motero, anthu olankhula monyozawo samalamuliridwa ndi zolamula za chikumbu mtima chawo chabwino ndipo chotero samasonyeza chiyamikiro kaamba ka njira za Mulungu, machitidwe ndi ntchito. Pokhala osakhoza kuwerengera mtengo woyenera wa zinthu zamtengo wapatali zauzimu, iwo anganene za izo kukhala ngati zopanda pake. Malingaliro awo olakwa adzakhala chowaononga. Iwo amakhala ndi malingaliro onama amenewa modzibvulaza okha ndipo ali otsimikizirika kukumana ndi zotulukapo zoipa za njira yawo yosalungama. Ndithudi, timafuna kugwiritsa chiyembekezo chathu ndi kupewa kugawana nawo m’chionongeko chawo.
CHENJERANI NDI AWO AMENE AMAFUNAFUNA CHISANGALALO CHADYERA NDI PHINDU LA IWO ENI
17. Malinga ndi kunena kwa 2 Petro 2:13b-15a, kodi ndi iti imene iri ina ya mikhalidwe yodzikwikitsa anthu oipa?
17 Pakati pa mikhalidwe ina yoipa, anthu opanda uzimuwo ali ndi chikhumbo chachikulu cha kukhala mosabvutikira ndi chisangalalo. Mtumwi Petro analemba kuti:
“Iwo amalingalira kukhala ndi moyo kosangalatsa kukhala chikondwerero. Iwo ali mawanga ndi zoipitsa, akumasangalala mosaletseka m’ziphunzitso zao zonyenga pamene akuchita nanu phwando. Iwo ali ndi maso odzala chigololo ndi osakhoza kusiya tchimo, ndipo Iwo amasonkhezera miyoyo yosakhazikika. iwo ali ndi mtima wophunzitsidwa chisiriro. Iwo ali ana otembereredwa. Atasiya njira yolunjika, iwo asocheretsedwa.”—2 Petro 2:13b-15a. NW.
18. Kodi ndi motani mmene anthu opanda uzimu aliri ofanana ndi Aisrayeli osakhulupirika ofotokozedwa mu Yesaya 5:11, 12?
18 Mkati mwa maora a usana, pamene iwo akanakhala akuchita kaamba ka kulimbikitsidwa kwa ena, anthu opanda uzimu mmalo mwake angakhale otanganitsidwa m’kuchita mapwando aphokoso, kudzichititsa iwo eni kupambanitsa m’kudya ndi kumwa. Iwo ali ofanana kwambiri ndi Aisrayeli ena amene anangokhalira moyo kusangalala chabe. Vinyo anali kupezeka mosabvuta kwambiri pa mapwando awo. Pamene tsikulo liyendabe mpaka kufika usiku, mapwando ophokoserawo akakhala aphokoso moonjezereka ndi osalamulirika moonjezereka, akumaphatikiza kuchita phwando kwao kwaphokoso ndi nyimbo zodzutsa chilakolako. Mnereri Yesaya akunena za anthu oterowo kuti:
“Tsoka kwa iwo amene adzuka m’mamawa kuti atsate zakumwa zaukali; amene achezera usiku kufikira vinyo awaledzeretsa! Ndipo zeze ndi mngoli, ndi lingake ndi chitoliro, ndi vinyo, ziri m’mapwando ao; koma iwo sapenyetsa ntchito ya Yehova; ngakhale kuyang’ana pa machitidwe a manja ake.” (Yesaya 5:11, 12)
Ofunafuna zosangalatsawo motero anachita monga ngati kuti panalibe umboni ponena za ntchito zazikulu za Mlengi. Iwo sanachite kudzilamulira kuli konse, kuiwala kukhala kwao ndi mlandu konse kwa Yehova Mulungu, ndipo chifukwa cha chimenecho, sakanayembekezera kupulumuka chiweruzo chake.
19. Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti anthu ena ogwirizana ndi mpingo ali okonda zokondweretsa?
19 Siziyenera kutidabwitsa ngati zinthu zofananazo zichitika pakati pa anthu ena amene amadzitcha kukhala atumiki a Mulungu lero lino. Mapwando a ukwati ndi masiku okumbukira tsiku la ukwati angasandutsidwe kukhala nthawi ya kubvina kosonkhezera maganizo kosalamulirika pa kumveka kwa nyimbo zodzutsa chilakolako. Pa mapwando oterowo, zakumwa zoledzeretsa zingakhale zikungopezeka mosabvuta kwambiri. Kuchita madyerero kwaphokoso ndi kosalamulirikako kungakhale kusakutha mpaka kumbandakucha kapena kufikira mmamawa. M’maiko ena, kutchula dzina mwana wobadwa chatsopano, kutseguliridwa kwa nyumba yatsopano, maliro ndi kutseguliridwa kwa nyumba yatsopano, maliro ndi kutsegulilirdwa kwa nyumba zogwiritsiridwa ntchito kaamba ka kulambira kungasandutsidwe kukhala nthawi za kuchita misonkhano imene amafikira kukhala yosalingalira, yobvutitsa maganizo ngakhale kwa anansi audziko ndi kuwachititsa kupempha mpumulo ku phokoso lopambanitsalo. Ngakhale m’maiko kumene anthu mwachisawawa amadziwika kukhala odziletsa, kumwa kopambanitsa kungakule pakati pa mabwenzi apamtima m’njira imene imachititsa chowonadi chonena za “mbiri yabwino” kunenedwa monyoza. Ndithudi, Akristu owona ayenera kuchenjerera kupambanitsa koteroko.—1 Petro 4:3.
20. (a) Kodi ndi chiyambukiro chotani chimene awo amene ali opambanitsa ali nacho pa mpingo? (b) Kodi ndi motani mmene ngakhale zochitika zolemekezeka zimasandutsidwira kukhala zaphokoso?
20 Monga momwe mtumwi Petro ananenera, awo omachita mwanjira imeneyi ali ngati mawanga ndi zodetsa pa mpingo Wachikristu. Iwo amaipitsa kaonekedwe kaudongo ka atumiki oona a Mulungu. Iwo ali ngati mawanga pa malaya oyera kapena ofanana ndi chodetsa chiri chonse chooneka moipa pa chinthu chimene pakadapanda icho chikanakhala chokongola. Chifukwa chakuti cholinga cha anthu ena ndicho “kuchita zonse zimene angathe’ kukhutiritsa chikhumbo chawo cha zosangalatsa, iwo amasandutsa ngakhale nthawi ya zochitika zabwinobwino mwachizolowezi kukhala zaphokoso. Iwo amayesa kusonkhezera kapena kuphunzitsa ena kugwirizana nawo m’kubvina kosadzilamulira ndi kumwa kopambanitsa mwa kunena kuti ‘ndi kusangulutsa komasula thupi chabe.’ “Maso odzala chigololo” amene Petro akuwatchula angakhale ali oonekera. Pa zochitika za kucheza, maso a amuna angayambe kuyang’ana mwa chikondwerero choipa pa akazi okongola amene alipo. Zikhumbo zoipazo zingakhale zamphamvu kwambiri kwakuti ngakhale maso a amuna okwatira sangathe konse kulephera kukhala ndi liwongo la kuchimwa. (Yerekezerani ndi Mateyu 5:28; Marko 9:47.) Akazi amene sali okhazikika mwamphamvu m’malamulo a khalidwe labwino Achikristu, monga ‘miyoyo yosakhazikika,” mosabvuta angakhale mikhole ya amuna oipawa.—Yerekezerani ndi 2 Timoteo 3:6, 7.
21. Kodi nchifukwa ninji anthu amene akalowetsa ena m’moyo wa kupambanitsa ali upandu weniweni ku mpingo Wachikristu?
21 Amuna amenewa ali upandu weniweni, pakuti iwo amasonyeza luso m’kunyengerera ofooka. Mtumwi Petro akuwafotokoza kukhala ‘ataphunzitsa mtima wao chisiriro.’ Chonulirapo chawo kapena cholinga chathunthu m’moyo chimaonekera kukhala kukhutiritsa zilakolako za chisiriro, ndipo iwo amafikira kukhala akatswiri m’kufikira zonulirapo zawo. Wophunzira Yuda nayenso ananena za anthu oterowo kukhala anthu amene ‘amakwawiramo’ nasandutsa kukoma mtima kwapadera kwa Mulungu kukhala ‘chochitira khalidwe losadziletsa,’ motero kudzitsimikizira kukhala onyenga kwa Mbuye wathu mmodzi yekha, Yesu Kristu. Iye akusonyeza kuti iwo kawirikawiri ‘amasirira anthu chifukwa cha phindu la iwo eni chabe,’ ndi kuti awo ochititsa magawano ali “anthu auchinyama, opanda mkhalidwe wauzimu.” (Yuda 4, 16, 19, NW) Ngati ena alionse atampambana, kaya mwa mawu oshashalika kapena mwa kusonyeza kwina changu choonekera, m’kupeza ulamuliro kapena kutchuka mu mpingo, iwo amapanga upandu waukulu. Moyenerera oterowo ali otembereredwa ndi Mulungu ndipo ali oyenerera chionongeko, monga momwedi mtumwi Petro ananenera. Chimene chiri chowona ponena za amuna amene akutsatira njira yogawanitsa ndi yoipa imeneyi chidzakhala chowona mofananamo kwa akazi amene akuchita motero.- Yerekezerani ndi Chibvumbulutso 2:20-23.
22, 23. Kodi ndi motani mmene awo amene amaipitsa ena aliri ofanana ndi Balamu?
22 Mtumwi Petro anayerekezeranso anthu oipa ndi Balamu, kuti:
“Atatsata njira ya Balamu mwana wa Beori, amene anakonda mphotho ya chosalungama; koma anadzudzulidwa pa kulakwa kwake mwini; buru wopanda mawu, wolankhula ndi mawu a munthu, analetsa kuyaruka kwa mneneriyo.” (2 Petro 2:15b, 16)
Wopenduza ameneyu anadziwa bwino lomwe kuti kunali kosemphana ndi chifuniro cha Mfumu Yaikuluyo kutemberera Aisrayeli. Pamene kuli kwakuti iye anali kusonyeza kuti iye sakapitirira zimene Yehova akamsonkhezera kulankhula, Balamu chamkati anali kukulitsa chikhumbo cha kutemberera Israyeli. Iye anafuna mphotho imene Mfumu ya Moabu Balaki inalonjeza. Koma Mulungu Wamphamvuyonse anadzudzula Balamu mwa njira ya bulu wa Balamu iye mwini. Mwa chozizwitsa, Wamphamvuyonseyo anachititsa nyama yopanda nzeru yonyamula katundu kunena mawu omveka bwino lomwe. (Numeri 22: 1-35) Chimenechi sichinali chinthu chobvuta kwa munthu amene akatha kupangitsa ngakhale miyala kupfuula. (Luka 19:40) Polingalira kukhumba phindu kwambiri kwa Balamu, Yehova Mulungu moyenerera anagwiritsira ntchito njira yachilendo imeneyi ya chidzudzulo. M’kuyesa kukaniza chifuniro cha Mulungu ponena za Israyeli, Balamu anachita monga munthu wopanda nzeru. Kwa kanthawi, chidzudzulo cha chifuyo chimenechi chinamletsa kulondola njira yake, pakuti chinasonyeza kuti iye sakapambana konse m’kutemberera Israyeli.—Numeri 23:1-24:9.
23 Komabe, Balamu anali woyedzamirabe ku kupeza mphothoyo. Potsirizira pake, iye anatulutsa kakonzedwe kamene kakachititsa Aisrayeli kudzidzetsera okha temberero la Mulungu. Iye analangiza Balaki ponena za m’mene akagwiritsirira ntchito akazi Achimoabu ndi Achimidyani kuchititsa amuna Achiisrayeli kuchita kulambira mafano ndi kuchita chigololo. (Numeri 31:16; Chibvumbulutso 2:14) Njira ya chiwembuyo inakhala ndi chipambanodi ndipo inachititsa imfa ya Aisrayeli 24,000.—Numeri 25:1-9.
24. Kodi chitsanzo cha Balamu chikuthandiza kuonanji ponena za anthu amene ali ofuna za iwo okha?
24 Ha, ndi mwamphamvu chotani nanga m’mene chochitika cha Balamu chikusonyezera njira ya amuna amene amasiya chimene chiri choyenera kaamba ka phindu la iwo eni! Ngakhale chozizwitsa sichikawaletsa kuyesa kukhutiritsa umbombo wao. Chifukwa cha chimenecho, tiyenera kupewa kuyanjana mwathithithi ndi aliyense amene mkhalidwe wake, kulankhula ndi khalidwe zimabvutitsa kwambiri chikumbu mtima chathu. Anthu ofuna za iwo okha samabvutika maganizo ndi kubvulaza ena kuti afikire zonulirapo za iwo eni.
25. Kodi nchiyani chimene chikugogomezeredwa ndi mawu a 2 Petro 2:17?
25 Popitirizabe kufotokoza anthu oipa amenewo, Petro akulongosola kuti: “Iwo ndiwo akasupe opanda madzi, nkhungu yokankhika ndi mkuntho, amene mdima wakuda bii uwasungikira.” (2 Petro 2:17) Palibe chiri chonse chopindulitsa chimene chikapezedwa mwa kugwirizana thithithi ndi anthu odetsedwa. Iwo ali ngati zitsime kapena akasupe amene munthu wotopa wapaulendo angafike ali ndi chiyembekezo cha kupeza madzi opha ludzu, ndi kugogwiritsidwa mwala chabe kupeza kuti chitsimecho madzi anaumamo. Iwo ali ngatinso mitambo younjika, yonga nkhungu imene munthu angayang’aneko akuyembekezera mvula yofunika yothirira mbeu zimene zirinkukula koma imene imangokankhiridwa kutali mwamsanga ndi mphepo. Aphunzitsi a chinyengo sali magwero a kuunika kuli konse kapena chidziwitso. Iwo eniwo akumka ku “mdima wakuda bii,” mdima wotheratu woimira chiweruzo chachitsutso chimene chikuwayembekezera.
SAMALANI NDI “MAWU OTUKUMUKA”
26. Kodi ndi motani mmene mtumwi Petro akufotokozera njira imene anthu oipa amapezera zolinga zawo?
26 Chiri chifukwa cha kwaonekedwe kawo kakunja kachinyengo chakuti ife tiyenera kukhala ochenjera ndi anthu aupandu mu mpingo. Makamaka awo amene sali okhazikika bwino m’chowonadi ndi kakhalidwe Kachikristu ayenera kukhala osamala. Njira zogwiritsiridwa ntchito ndi anthu ofuna za iwo okha zingakhale zogwira mtima kwambiri. Koma tsoka kwa awo amene anyengedwa ndi mawu awo okopa otukumukawo! Mtumwi Petro akuti:
“Polankhula mawu otukumuka opanda pake, anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, iwo amene adayamba kupulumukira a mayendedwe olakwawo; ndi kuwalonjezera iwo ufulu, pokhala iwo okha ali akapolo a chibvundi; pakuti iye amene munthu agonjetsedwa naye, ameneyonso adzakhala kapolo wake.”—2 Petro 2:18, 19.
27. Kodi nchiyani chimene chimasonyezedwa ndi kulankhula ndi mkhalidwe za anthu amene amapereka chiyambukiro choipitsa?
27 Awo amene amasonkhezera ena kuchita cholakwa kapena kutsatira njira yosemphana ndi chikumbu mtima choyera kawirikawiri amalankhula mokuthiritsa maganizo kwambiri. Akumadziganizira kwambiri iwo eniwo ndi mawu awo, akumatamanda zokamba zawo. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 10:10, 12; 11:3-6, 12, 13.) M’malo mwa kupereka zifukwa zabwino Zamalemba mu mzimu wa kudzichepetsa, iwo anganyoze ndi kulankhula mwamphamvu ndi modzitukumula, akumabisa kufooka kwa chigomeko chawo monyada. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 4:2) Pamene apendedwa mothandizidwa ndi Malemba Oyera, mawu awo ogwira mtimawo amasonyezedwa kukhala opanda pake kapena osapindulitsa kwa ali yense.
28. Kodi ndani amene kwenikweni ali otsimikizirikadi kusonkhezeredwa ndi anthu oipa mu mpingo?
28 Momvetsa chisoni, awo amene sali okhazikika zolimba m’Mawu a Mulungu sangazindikire upanduwo. ‘Mphamvu zawo za kulingalira siziri zophunzitsidwa kusiyanitsa chabwino ndi choipa.’ (Ahebri 5:14) Popeza kungakhale kuli kwakuti osakhazikika amenewa angakhale atangodzipatula posachedwapa ku machitachita onyoza Mulungu amene akuchitidwa m’dziko, machitachita oterowo angakhale akali okondweretsa kwa iwo.
29. Kodi lingaliro la Malemba ndi lotani ponena za zosangalatsa kapena kusangulutsa, ndipo kodi ndi liti pamene kwenikweni tifunikira kukhala ochenjera?
29 Mwachiwonekere, pali kufunika kwa kukhazikika m’kulingalira kwathu nkhani za zosangalatsa ndi kusangulutsa. Malemba samapempha kuti atumiki a Mulungu akhale ndi moyo wa kudzilanga, ndiponso iwo samasonyeza kudzimana kukhala kuli koyenera mwa iko kokha koma kokha pamene kuchitidwa tikulingalira cholinga chabwino. (Yerekezerani ndi Mlaliki 2:24; 3:1, 4, 13; 8:15; 1 Akorinto 13:3, Akolose 2:20-23.) Koma zimenezi sizikupereka chowiringulira chochitira mopambanitsa, kulola thupi lochimwali kulamulira ndi kugwiritsira ntchito ufulu Wachikristu kukhala chophimbira choipa. (Agalatiya 5:13, 14; 1 Petro 2:16) Njira yoteroyo singathe konse kugwirizanitsidwa ndi kukonda Mulungu ndi kukonda mnansi monga munthu mwini, “lamulo lachifumu” limene ife tiri pansi pake. (Yakobo 2:8, 12) Awo amene amanena mosiyana, ndi awo amene amatsutsa awo amene samagwirizana nawo m’kupambanitsa kwaoko, amasonyeza kuti akali akapolo ku zikhoterero za iwo eni zadyera.
30. Kodi nchiyani chimene chingachitike potsirizira pake chifukwa cha chisonkhezero choipa mu mpingo?
30 Chotero pali kufunika kwa kusunga malingaliro athu ndi kupewa kupambanitsa kulikonse. Pali upandu wosakanika wa kuchititsidwa kulowa m’njira yosalabadira ya kulondola zosangalatsa. Munthu angathe mwapang’onopang’ono kukokeredwa ku mapawando osiyanasiyana kwakuti, m’kupita kwa nyengo ya nthawi, mkhalidwe wake umaipaipa, akumalowa moonjezerekaonjezereka m’kumpambanitsa m’kubvina kapena kumwa, kapena m’kuonera zosangalatsa zimene zimatamanda chisembwere ndi kukondweretsedwa ndi zankhanza. Kuli kusalingalira abwino kunena kuti zisonkhezero zoipa zimenezi sizimapanga upandu. Sizingathandize konse koma kukhala ndi chiyambukiro cholefula pa chikumbu mtima cha Mkristu, zikumafooketsa mphamvu ya malingaliro ya munthu. Anthu amene amayerekezera kukhala osiyana ndi zimenezi kawirikawiri amatsirizira atakhala ogonjera ku uchidakwa ndi chisembwere.—Miyambo 13:20.
31, 32. Kodi nchiyani chimene ziwalo zina za mpingo zidzapitirizabe kuchita mpaka pa “tsiku la chiweruzo” ndipo ndi kukhala ndi zotulukapo zotani?
31 Zowonadi, mtumwi Petro ananasonyeza kwenikweni chimene chikapitirizabe kuchitika pakati pa atumiki a Mulungu kufikira “tsiku la chiweruzo [kuti anthu osalungama] akadulidwe.” (2 Petro 2:9, NW) Nthawi zonse padzakhala anthu amene amayesa kutanimphitsa malire a ufulu Wachikristu kupyola pamene pali poyenera kotero kuti akhutiritse zikhumbo zawo kaamba ka chisangalalo cha malingaliro. Iwo samafuna kutsatira chilangizo cha Babulo chakuti: “Chifukwa chake fetsani ziwalozo ziri padziko; dama, chidetso, chifunitso cha manyazi, chilakolako choipa chisiriro.” (Akolose 3:5) M’malo mwake, iwo amasankha kusangulutsa kwenikweniko kumene kumasonkezera zilakolako zoipa zimenezi. Polowetsamo ena, iwo anganene kuti: ‘Ngati chikumbu mtima chathu chikulola, palibepo cholakwa.’ Koma iwo amalephera kuzindikira kuti chikumbu mtima choipitsidwa, sichiri chitsogozo chopanda upandu. Anthu amenewa akugonjera ku zilakolako zawo zolakwa ndipo, chifukwa cha chimenecho, ali mu ukapolo ku zimenezi. Malonjezo awo a “ufulu” kwa ena ali osocheretsa.
32 Chotulukapo kwa awo amene akulowetsedwa kachiwirinso m’moyo wa kuchita zolakwa ndithudi chiri chatsoka. Mtumwi Petro analemba kuti:
“Pakuti ngati, adatha kuthawa zodetsa za dziko lapansi mwa chizindikiritso cha Ambuye ndi Mpulumutsi Yesu Kristu, akodwanso nazo nagonjetsedwa, zotsiriza zawo zidzaipa koposa zoyambazo. Pakuti pakadakhala bwino kwa iwo akadakhala osazindikira njira ya chilungamo, ndi poizindikira, kubwerera kutaya lamulo lopatulika lopatsidwa kwa iwo. Chidawayenera iwo cha nthanthi yowona, Garu wabwerera ku masanzi ake, ndi nkhumba idasambayi yabwerera kukunkhulira m’thope.”—2 Petro 2:20-22.
33. (a) Kodi ndi masinthidwe otani amene munthu angapange pamene wapeza chidziwitso cha chowonadi? (b) Kodi nchifukwa ninji kubwerera ku njira za dziko kuli nkhani yoopsya kwambiri?
33 Kodi nchifukwa ninji mtumwi Petro ananena zimenezi? Pamene munthu wagopeza chidziwitso cholongosoka chonena za Ambuye Yesu Kristu, iye amayamba kuona kufunika kwa kupanga masinthidwe. Iye angasiye kumwa kwambiri, moyo wa chisembwere, kuchobva juga ndi zoipa zina. Mwa kudziyeretsa iye mwini kuti agwirizane ndi zimene zikuyembekezeredwa kwa wophunzira wa Yesu Kristu, munthuyo amathawa kapena amapulumuka “zodetsa za dziko lapansi,” ku machitachita amene iye wafikira pa kuwadziwa kukhala otsutsidwa mwaumulungu. Komabe, pokhala wokodwa kachiwirinso m’machitachita onyoza Mulungu, iye mwadala amakankhira pambali zimene iye akuzidziwa kukhala zoyenera. Kudziwa kwake Yesu Kristu ndi chikumbu mtima chake chophunzitsidwa ndi Baibulo poyambirira chimatumikira monga choletsa kuchita cholakwa. Pomasuka ku chiletso chabwino chimenecho, iye angafikiredi pa kuipa kwambiridi koposa kale asanatenge njira ya kukhala wophunzira wa Kristu. Iye angapitirire zimene anthu amachita amene alibe chidziwitso cha njira ya chilungamo. Izi ziri chifukwa chakuti chikumbu mtima chake chaipitsidwa, kapena ngakhale kulochedwa-monga ngati balima. (Yerekezerani ndi 1 Timoteo 4:2.) Akadapanda kudziwa konse njira yoyenera, khalidwe lake loipa silikananyozetsa moopsa kwambiri dzina la Kristu, uchimo wake sukanakhala ndi ukulu wofananawo, ndipo chiweruzo cha Mulungu pa iye sichikanafunikira kukhala champhamvu kwambiri.—Yerekezerani ndi Luka 12:45-48; 1 Timoteo 1:13, 15, 16.
34, 35. (a) Kodi nchiyani chimene tingapeze kuchokera ku mwambi wonena za galu wautchisi ndi nkhumba? (b) Kodi mwambi umenewu uyenera kukhomereza chiyani pa ife?
34 Polingalira mwambi umene Petro waugwira mawu, awo amene amakhala ndi moyo wa uchimo mwachionekere amalephera kugwiritsira ntchito mwai wao kuti apite patsogolo m’kukhala ndi moyo Kwachikristu. (2 Petro 1:2-11) Ena mwakunja kokha angaleke zizolowezi zoipa koma osafika pa kuzida. Iwo angakhale asanafulatire “masanzi,” zodetsa za dziko. Kwa iwo, pakali kanthu kena kokondweretsa ponena za icho, ndipo chotero iwo angathe kunyengedwa kuti abwerereko. Iwo angakhale ndi chikhumbo cha m’kati cha kukukhunizika m’matope a dziko a kululuzika kwa makhalidwe. Ponena za ena, iwo angalephere kuwonjezeka m’kuzindikira phindu la kukhala wophunzira Wachikristu, ndipo potsirizira pake zimene dziko lingapereke zimakhala zokondweretsa kwambiri. Ha, ndi koopsa chotani nanga m’mene kumakhalira kugwa kwa awo amene anyengeka motero kubwerera ku mkhalidwe umene pa nthawi ina unali wobvutitisa maganizo kwa iwo.
35 Mwambi wouziridwawo uli ngati phunziro la chenjezo kwa onse amene amadzitcha kukhala Akristu. Ngati sitikulitsa chiyero cha makhalidwe ndi chauzimu m’mitima yathu ndipo tiri opanda kunyansidwa kwenikweni ndi zodetsa za dziko lino, tiri mu upandu waukulu wa kuwonogeka kwauzimu. Akristu sangathe konse kuleka kukhala kwao maso m’kukaniza zonyengerera za dziko loipali. Tiyenera kufetsa zilakolako zathu zolakwa, osazilola kutilamulira, ndiponso sitiyenera kuzisonkhezera mwa kuyang’ana mokhumbira zimene dziko limapereka.—1 Akorinto 10:12; Akolose 3:5.
KHALANI MASO!
36. Kuphatikiza pa kukhala woyera mwamakhalidwe ndi mwauzimu, kodi nchiyani chimene tifunikira kuchita kuti tikondweretse Mbuye wathu?
36 Kuphatikiza pa kukhala woyera mwamakhalidwe ndi mwauzimu, tifunikiranso kukhala okangalika mu utumiki wa Mbuye wathu, kuthandizira ena mwauzimu kudzanso mwakuthupi. Njira yathu yonse yathunthu ya moyo iyenera kusonyeza kukhala ogalamuka mwauzimu ndi kukangalika. Pogogomezera kufinika kwa zimenezi, mtumwi Petro akufotokoza kuti:
“Okondedwa, iyi tsopano ndi kalata yanga yachiwiri imene ndikukulemberani, mu imene, mofanana ndi m’yanga yoyamba ija, ndikudzutsa mphamvu zanu za kulingalira bwino mwa njira ya chokumbutsira, kuti muyenera kukumbukira mawu onenedwa kale ndi aneneri oyera ndi lamulo la Ambuye ndi Mpulumutsi kupyolera mwa atumwi anu. Pakuti inu mudziwa ichi choyamba, kuti m’masiku otsiriza kudzadza onyoza ndi kunyoza kwawo, akumapitirizabe mogwirizana ndi zilakolako zawo za iwo eni ndi kunena: “Kuli kuti kukhala pafupi kwake kolonjezedwako? Inde, kuyambira m’nthawi imene makolo athu anagona mu imfa, zinthu zonse zikupitirizabe monga momwedi zinaliri pa chiyambi cha chilengedwe.”—2 Petro 3:1-4, NW.
37. (a) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupangitsa ‘mphamvu zathu za kulingalira kudzutsidwa’? (b) Kodi aneneri analoza ku chochitika chofunika kwambiri chotani?
37 Ndithudi ife lero lino timapindula nako kuchititsidwa kwa ‘mphamvu zathu za kulingalira kudzutsidwa’ kotero kuti tithe kupanga kutsimikizira koyenera chimene chiri chofunika kwambiri kaamba ka kupeza chibvomerezo cha Mulungu. (Yerekezerani ndi 2 Petro 1:12-15.) “Aneneri oyera,” kalelo mpaka kwa Enoke anachenjeza za tsiku la chiweruzo. Pa Yuda 14,15, timawerenga kuti: “inde, wachisanu ndi chiwiri mu mzera wochokera kwa Adamu, Enoke, ananenera nayenso ponena za iwo, pamene iye ananena kuti, ‘Taonani! Yehova anadza ndi oyera ake miyanda miyanda, kudzapereka chiweruzo kwa onse, ndi kudzatsutsa onse opanda umulungu ponena za ntchito zawo zonse zopanda umulungu zimene iwo anazichita m’njira yopanda umulungu, ndi ponena za zinthu zonse zobvutitsa maganizo zimene anthu ochimwa opanda umulungu analankhula momtsutsa.’” Zaka mazana ochuluka pambuyo pake, aneneri Achihebri onga ngati Yesaya, Danieli, Yoweli, Habakuku, Zefaniya, Hagai, Zekariya ndi Malaki anasonkhezeredwa kunena maulosi ofananawo.- Yesaya 66:15, 16; Danieli 7:9-22; Yoweli 3:9-17; Habakuku 3:16-18; Zefaniya 1:14-18; Hagai 2:21,22; Zekariya 14:6-9; Malaki 4:1-6.
38. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuyesayesa kukhala mkhalidwe wa kukonzekera?
38 Chiweruzo cha Mulungu chonenedweratu ndi aneneri onsewa ndi ena chiyenera kukwaniritsidwa mosalephera. Zimenezi zikufunikiritsa kuti ife nthawi zonse tiyeseyese kukhala mu mkhalidwe wokonzekera ndi kusaika pa ngozi kaimidwe kathu koyera pamaso pa Wam’mwambamwambayo.
39. Kodi ndi uthenga wotani umene ukuperekedwa ndi lamulo la Yesu Kristu?
39 Uthenga wa aneneri kwa ife uli wofanana ndi uja umene unaperekedwa ndi lamulo la Ambuye wathu Yesu Kristu, monga momwe linabwerezedwera ndi atumwi, kuphatikizapo Paulo. Ife ophunzira a Mwana wa Mulungu tiyenera kukhala okangalika mu utumiki wake, tikumakhala oyera mwamkhalidwe ndi mwauzimu, ndi kukhala okonzekera nthawi zonse kulandira Mbuye wathu pamene adza kudzapereka chiweruzo motsutsana ndi opanda umulungu. Mwana wa Mulungu anafotokoza kuti:
“Dzipenyereni inu eni kuti mitima yanu isalemetsedwe ndi kudya kopambanitsa ndi kumwa kopambanitsa ndi nkhawa za moyo, ndipo mwadzidzidzi tsikulo nalikufikirani modzidzimutsa monga msampha. Pakuti lidzafika pa onse okhala pa nkhope ya dziko lapansi. Pamenepo, khalani maso, nthawi zonse mukumapemphera kuti inu mukapambane m’kupulumuka zinthu zonse zimenezi zimene zaikidwiratu kuchitika, ndi m’kuima pamaso pa Mwana wa munthu.”—Luka 21:34-36, NW.
40. Kuti tipewe kulowetsedwa m’tulo tauzimu, kodi nchiyani chimene tiyenera kuchita?
40 Inde, tiyenera kuchenjera kuti tisalowetsedwe m’tulo tauzimu. Kumeneku kumafunikira kupewa kudya, kumwa ndi zosangalatsa mosadziletsa. Kupambanitsa koteroko kumafooketsa mphamvu ya kulingalira ya malingaliro ndi yauzimu ndi kulemeza mtima ndi malingaliro a liwongo. Izo zimayangirira zolinga zoyenera za mtima. Mofananamo, nkhawa yosayenera ponena za kupeza zofunika za moyo ingathe kuchotera mtima chitsimikiziro chotonthoza chakuti Yehova Mulungu adzapereka chiri chonse chimene ife tikuchifunikira kwenikweni. (Mateyu 6:25-34) Pamene cholinga chachikulu cha mtima chileka kukhala chikhumbo cha kupezedwa tiri obvomerezeka ndi Ambuye Yesu Kristu pa nthawi yake ya chiweruzo, munthu amalowa mu mkhalidwe wa upandu waukulu wauzimu. Iye angapezedwe ali mu mkhalidwe wosabvomerezeka ndi Mbuyeyo, Yesu Kristu.
41. Kodi nchifukwa ninji kukhulupirira kutsimikizirika kwa kudza kwa Kristu mu ulemerero nthawi zonse kwakhala chithandizo m’kukhala kwa munthu wokhulupirika kwa iye?
41 Mofanana ndi Petro, atumwi ena okhulupirika anaphunzitsa okhulupirira anzawo kukumbukira nthawi zonse kutsimikizirika kwa kudza kwa Kristu kudzapereka chiweruzo ndi kudzafupa ophunzira ake okhulupirika. Cholinga chachikulu cha kuphunzitsa koteroko chinali kuthandiza Akristu kupezedwa ali obvomerezeka pa kufika kwa Mwanayo “mu mphamvu ndi ulemerero waukulu.” (Mateyu 24:30, NW) Monga momwe Yesu anachitira, atumwi anapitirizabe kugogomezera kufunika kwa kutsimikizira kukhala okhulupirika kufikira mapeto. Mapeto amenewo angadze kaya pa imfa yawo kapena pa “kudza kwa tsiku la Yehova.” (2 Petro 3:12) Popeza kuti ngakhale pa chiukiriro cha olowa nyumba limodzi ndi Kristu chikugwirizanitsidwa ndi kubweranso kwake m’Malemba, ziyembekezo za ophunzira onse oona zamangidwa pa kubweranso kwa Mwana wa Mulungu ali mu udindo wa Mfumu yaulemerero yakumwamba. (Mateyu 10:28; 24:13, 36-44; 1 Atesalonika 1:9, 10; 4:14-17) Chotero, mkati mwa mbiri yonse ya mpingo Wachikristu, chikhulupiriro chosagwedezeka m’kudza kwa Mbuyeyo “mu mphamvu ndi ulemerero waukulu” chakhala chithandizo m’kutsimikizira kwa munthu kukhala wokhulupirika kwa iye.
MUSANYENGEDWE NDI OSEKA
42. (a) Kodi nchifukwa ninji tikumva mawu a otsutsa lero lino? (b) Kodi kutsutsa kwawo nkotani?
42 Mbali ina chifukwa cha kufunitsitsa kukhala ali ndi moyo pa nthawi imene Yesu Kristu akudzibvumbula mu ulemerero, pakhala okhulupirira m’kati mwa zaka mazana ochuluka zonsezi amene anayamba kuyang’ana ku nyengo yakuti yakuti kapena chaka kaamba ka kutha kwa dongosolo la zinthu lopanda umulungu. Zimenezi zachitika mpaka kudzafika “masiku otsiriza” ano. Popeza kuti ziyembekezo zina sizinakwaniritsidwe, ambiri anakhumudwa nabwerera ku njira za dziko. M’kukwaniritsidwa kwa mawu a Petro, ngakhale lero lino timamva mawu a oseka. (2 Petro 3:3, 4) Chifukwa cha chimenecho, iwo amenena, kuti: ‘Pali chifukwa chotani chokhulupiririra kuti Mwana wa Mulungu adzapha opanda umulungu ndi kufupa ophunzira ake? Inde, palibe chiri chonse chimene chasintha chiyambire pa nthawi ya chilengedwe. Kayendedwe koyambirira ka moyo kakupitirizabe ndipo sikakupereka chisonyezero chiri chonse cha kufika pa mapeto a tsoka mtsogolo muno posachedwapa. Amuna akukwatira, ndipo akazi akukwatitsidwa, ana akubadwa, ndipo anthu akupitirizabe kukalamba ndi kufa.’ Motero iwo amasonyeza kuti Ambuye Yesu Kristu sadzabwera konse kudzapereka chiweruzo kapena kuti chochitika chimenechi chiri kutali kwambiri m’tsogolo kwakuti sinkhani yoti nkudera nayo nkhawa pa tsopano lino.
43. Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti nthawi yonse pakhala kufunika kwa ophunzira a Kristu kukhala akhama m’kuchita mathayo awo?
43 Onyoza oterowo ataya kapenyedwe kotheratu ka chenicheni chakuti kaya imfa kapena “tsiku la Yehova” lidzawafikira mosapeweka asakudziwa. M’chochitika chiri chonse cha zimenezo, iwo sadzakhala ndi mwai wina wa kukundika chuma kumwamba mu mpangidwe wa ntchito zabwino. (Luka 12:15-21, 31, 33-40) Chotero, kwa ophunzira a Yesu Kristu sipanakhale nthawi ya mu mbiri pamene iwo akanatha kukhala onyozera mathayo ao. Ndithudi, upandu wa kuchita motero uli wokuliradi kwambiri m’nthawi yathu.
44. Kodi ndi mathayo akulu otani amene ife tiyenera kuchita?
44 Pamenepotu, lero lino, kodi ndi mathayo otani kwenikweni amene ife tiyenera kukhala tikuchita? Choyamba, talamulidwa “kupanga ophunzira mwa anthu a mitundu yonse, tikumawabatiza m’dzina la Atate ndi la Mwana ndi la mzimu woyera, tikumawaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndakulamulirani.” (Mateyu 28:19, 20, NW) Inde, pa mapeto a dongosolo la zinthu, tiri ndi mwayi wa kukhala ndi phande pa dziko lonse m’kulalikira kwa” mbiri yabwino ya ufumu.” (Mateyu 24:14, NW) Chofunika kopambanadi kwenikweni pa nthawi ino ndicho thayo lathu la kusonyeza chikondi kwa abale athu onse, tikumalabadira zosowa zawo za chithandizo, kumvera chifundo ndi chilimbikitso. (Yerekezerani ndi Mateyu 25:35-40; Ahebri 13:1-3; 1 Yohane 3:16-18.) Ndiponso tifunikira kupanga kuyesetsa mosalekeza kuti tikhale oyera ku ntchito zoluluza za thupi.—Mateyu 7:21-23; Agalatiya 5:19-21.
YEHOVA WATSIMIKIZIRA ONYOZA KUKHALA OLAKWA
45, 46. Kodi ndi umboni wotani umene Yehova wapereka kusonyeza kuti onyozawo ndi olakwa?
45 Pamene tikupitirizabe kukhala ndi moyo umene umagwirizana ndi kukhala kwathu ophunzira a Yesu Kristu, tidzafuna kukumbukira nthawi zonse kuti Yehova Mulungu kalelo anapereka umboni umene mosakanika umatsimikizira onyozawo kukhala olakwa. Pokumbutsa chenicheni chimenechi, mtumwi Petro analemba kuti:
“Mogwirizana ndi kufuna kwawo, chenicheni ichi chikuiwalidwa, kuti panali miyamba kuyambira kale ndi dziko lapansi linamangika mwamphamvu pa madzi ndi m’kati mwa madzi ndi mawu a Mulungu; ndipo mwa njira zimenezo dziko la nthawiyo limene linanonongeka pamene linamizidwa ndi madzi.”—2 Petro 3:5, 6.
46 Chenicheni chakuti Yehova Mulungu pa nthawi ina kalelo anaononga dziko la anthu opanda umulungu chimasonyeza kuti onyozawo ali olakwa m’kunena kuti sipadzakhala kusintha kwakukulu kuli konse m’zochitika za anthu koma kuti zinthu zonse zidzapitirizabe ‘monga momwedi zinaliri pa chiyambi cha chilengedwe.’ Tiri ndi mawu a Mulungu mwini a lonjezo lakuti, mwa njira ya Mwana wake, iye adzachitapo kanthu motsutsana ndi anthu opanda umulungu. Mawu amenewo ali amphamvu kwambiri kwakuti palibe kuthekera kwa kulephera kwake kukwaniritsidwa.
47. Kodi ndi motani m’mene cholembedwa chonena za chilengedwe chimabvumbulira mphamvu ya “mawu” a Mulungu?
47 M’mene Baibulo limanenera za ntchito za kulenga za Yehova limabvumbula mphamvu ya “mawu” ake. Kuyambira pa Genesis chaputala 1, timaphunzira kuti, pamene Wam’mwambamwamba anena mawu kapena apereka lamulo, chifuno chake chiri monga ngati kuti chachitika kale. (Yerekezerani ndi Salmo 148:1-6.) Ponena za tsiku lachiwiri, tikuuzidwa kuti: “Anati Mulungu, pakhale thambo pakati pa madzi, lilekanitse madzi ndi madzi. Ndipo Mulungu anapanga thambo, nalekanitsa madzi anali pansi pa thambolo ndi madzi anali pamwamba pa thambolo: ndipo kunatero.” (Genesis 1:6, 7) Ndiyeno, pa tsiku lachitatu, “anati Mulungu, Madzi a pansi pa kumwamba asonkhane pamodzi pa malo amodzi, uoneke mtunda: ndipo kunatero.”—Genesis 1:9.
48. Kodi ndi motani mmene dziko lapansi ‘linamangikira zolimba pa madzi’ ndi “pakati pa madzi”?
48 Zimene cholembedwa cha Genesis chimanena ziri zogwirizana kotheratu ndi kufotokoza kumene kukuperekedwa ndi mtumwi Petro. Chifukwa chakuti mtunda unatuluka pamwamba pa madziwo, ‘dziko lapansi linamangika zolimba pa madzi.’ Komabe, chifukwa cha kuzungulira dziko lapansi kwa madzi pamwamba pa thambo (limene liri ndi mipweya yofunika kaamba ka kuchirikiza moyo), dziko lapansi linaimanso “pakati pa madzi.” (Yerekezerani ndi Miyambo 8:24-29.) Kakonzedwe kameneka kanakhalako mwa “mawu a Mulungu.”
49. (a) Kodi ndi motani mmene zinachitikira kuti “mwa njira zimenezo dziko la nthawi imeneyo linaonongeka”? (b) Kodi ndi chochitika cha mtsogolo chotani chimene “mawu a Mulungu” amphamvuwo amachitsimikizira?
49 Madziwo analenjekeka kutali ndi nkhope ya dziko lapansi ndi madzi a kunthambo anapanga kuthekera kwa chigumula cha pa dziko lonse ndipo anatsimikizira kukhala njira imene Wam’mwambamwambayo anaonongera dziko lopanda umulungu. Chifukwa cha chimenecho, Chigumulacho chiri ngati chitsanzo cha chenjezo kwa onse amene amanyoza kutsimikizirika kwa kulowera kwa Mulungu mu zochitika za anthu mkati mwa nthawi ya kukhala pafupi kwa Kristu. Mawu amphamvu amene anachititsa kuthekera kwa chigumula cha pa dziko lonse ndiwo mawu amodzimodziwo amene amasonyeza chionongeko cha dongosolo loipali la zinthu. Mtumwi Petro akupitirizabe kuti: “Koma miyamba ndi dziko la masiku ano, ndi mawu omwewo zaikika kumoto, zosungika kufikira tsiku la chiweruzo ndi chionongeko cha anthu osapembedza.”—2 Petro 3:7.
50. (a) Ponena za chionongeko cha dongosolo la zinthu lakale liripoli, kodi ndi lingaliro lotani limene anthu ena amene akugwirizana ndi mpingo Wachikristu atenga? (b) Kodi ndi motani mmene mkhalidwe umenewu ukusonyezedwera?
50 Makamaka chifukwa chakuti zaka mazana ambiri zapitapo chiyambire pamene mtumwi Petro analemba mawu amenewo ndipo chifukwa chakuti ziyembekezo zina sizinakwaniritsidwe, anthu ena ogwirizana ndi mpingo Wachikristu akayikira ponena za kuti kaya chionongeko chimenecho chidzadza. Pamene mwina mwake sakugwirizana mwapoyera ndi onyoza, iwo samaonanso “tsiku la chiweruzo” kukhala chochitika chimene iwo ayenera kuchilingalira. Iwo amakhala onyalanyaza m’kukhala ndi moyo mogwirizana ndi mathayo awo Achikristu, ndipo amagonjera ku mkhalidwe wa kuozera kwauzimu. Iwo amayesayesa kupeza zochuluka monga momwe angathere kuchokera ku dongosolo la zinthu liripoli m’njira ya zosangalatsa ndi chuma.
YAMIKIRANI KUDEKHA KWA YEHOVA
51. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kuganiza kuti kudza kwa Kristu mu udindo wa wolipsira kwachedwa kwambiri?
51 Mwa lingaliro laumunthu, kungaonekere kuti kudza kwa Kristu mu udindo wa wopereka kulipsira kwa Mulungu kwachedwa kudza. Koma sizinakhale choncho m’maso mwa Yehova Mulungu. Chifukwa cha chimenecho, kuti ife tipewe kugona mwauzimu, tifunikira kuona zinthu mwa lingaliro la Wam’mwambamwambayo. Mawu a mtumwi Petro ngatithandize kuchita zimenezo. Timawerenga kuti:
“Koma, ichi chimodzi, musaiwale, okondedwa inu, kuti tsiku limodzi likhala kwa Ambuye ngati zaka chikwi, ndi zaka chikwi ngati tsiku limodzi. Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa. Koma tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala.”—2 Petro 3:8-10.
52, 53. Kodi ndi motani mmene zaka chikwi ziri ngati tsiku limodzi kwa Yehova, ndi tsiku limodzi ngati zaka chikwi?
52 Yehova sali wamphamwayi ponena za nthawi monga momwe ikugwirira ntchito kwa anthu. (Genesis 1:14, 15) Iye anapanga munthu kukhala wosunga nthawi. M’Baibulo, Mulungu anaika nyengo za nthawi zotsimikizirika, zimenezi zikumawerengedwa m’zaka malinga ndi kuwerenga nthawi kwa anthu. (Genesis 15:13-16; Eksodo 12:40,41; Agalatiya 3:17; Numeri 14:33, 34; 32:13; Deuteronomo 2:7; Yoswa 5:6; Machitidwe 13:20) Popeza kuti iye ali Mulungu wopanda chiyambi ndi wopanda mapeto, woyambira ku nthawi yosadziwika kumka ku nthawi yosadziwika, moyo wake sungathe kupimidwa ndi nthawi. (Salmo 90:2, 4) Chotero zimenezi ziri kwa munthu zaka chikwi kapena nyengo ya masiku oposa 365,000 ziri, ponena moyerekezera, ngati tsiku limodzi la maora 24 kwa Mulungu wamuyaya.
53 Pamene Petro wouziridwayo akunena, nayenso, kuti “tsiku limodzi likhala kwa Ambuye ngati zaka chikwi,” sakutanthauza kuti nthawi imangoyenda pang’onopang’ono motopetsa kwa Yehova ponena za zochitika za pa dziko lapansi kapena za pa anthu, M’malo mwake, m’tsiku limodzi la maora 24 Mulungu akatha kuchita zimene zikatengera munthu, mwina mwake, zaka chikwi kuti azichite. Koma Wam’mwambamwambayo sali wochepekedwa nthawi, ngakhale kuli kwakuti angathe kufulumizitsa zinthu. Kombe, ngati iye akufuna kuyembekezera kwa zaka chikwi asanchitepo kanthu kotsimikizirika, iye akuyembekezera kwa “tsiku” limodzi lokha, kunena moyerekezera.
54. (a) Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kuganiza za Yehova Mulungu kukhala wozengeleza? (b) Kodi ndi motani mmene ife tapindulira ndi kudekha kwa Mulungu?
54 Chotero, m’malo mwa kuyang’ana pa zaka mazana ochuluka zimene zapita chiyambire pamene mtumwi Petro analemba kalata yake yachiwiri monga umboni wa kuzengereza kwa Mulungu, tiyenera kulingalira nyengo imeneyi kukhala chisonyezero chodabwitsa cha kudekha kwa Mulungu. Kumatsimikizira mosakanika kuti Atate wathu wakumwamba amafuna kuti anthu kuli konse afike pa kulapa ndi kukhala ndi moyo. Monga momwe Petro anasonyezera, kudekha kwa Mulungu kwapindulitsa Akristu. Pa nthawi ina iwo, nawonso, anali osakhulupirira ndipo anafunikira kulapa m’malo mwakuti apeze kaimidwe kobvomerezeka kwa Wam’mwambamwambayo. Komabe, ngati chiweruzo cha Mulungu chikanakhala chitaperekedwa motsutsa dzko lopanda umulungu, awo amene anali asanafike pa kulapa akanakhala ataonongedwa. Chotero kudekha kwa Yehova kwatheketsa chipulumutso cha Akristu, monga momwedi tsopano ku kupitirizira kutsegulira mwayi enanso kufika pa kulapa ndi kukhala ndi moyo. Komatu kudekha kwa Mulungu sikudzasonyezedwa kosatha. Mosayembekezereka, monga ngati pamene mbala ikudza, ambuye Yesu Kristu adzabvumbulidwa “m’lawi la moto” pamene iye akuyamba ntchito yake ya kupha opanda umulungu.—2 Atesalonika 1:7-9.
55. Kodi nchiyani chimene tiyenera kukhala tikuchita polingalira za kutsimikizirika kwa kudza kwa Kristu kudzapereka chiweruzo, ndipo kodi zimenezi zingatanthauzenji kwa ife?
55 Chifukwa chakuti kubvumbulutsidwa koteroko kwa Ambuye Yesu Kristu kungathe kudza pa nthawi iri yonse, tifunikira kulingalira mwamphamvu ponena za kaimidwe kathu pamaso pa Mulungu ndi Kristu. Ife sitiri ndi nthawi yopanda mapeto ya kupanga mbiri ya ntchito zabwino zimene zidzachititsa kuonedwa kwathu kukhala obvomerezeka ndi iwo. Baibulo limasonyeza bwino lomwe kuti tsiku la Mbuye wathu la chiweruzo lidzafikira modzidzimutsa awo amene sali amaso. Ngati ife tiri onyalanyaza ponena za mathayo athu Achikristu, pamenepo, monga mbala, chochitika chimenecho chikatifikira modzidzimutsa mu mkhalidwe wosakonzekera. Chifukwa cha chimenecho tiyenera kuyesayesa kukhala ndimoyo tsiku liri lonse monga ngati kuti linali tsiku lathu lomaliza, osalola zikhumbo za munthu mwini kapena zosangalatsa kudodometsa kutumikira kwathu mokhulupirika Yehova Mulungu ndi Ambuye wathu Yesu Kristu. Zikatero, sitidzachita chisoni ndi m’mene tinagwiritsira ntchito nthawi yathu, nyonga zathu, ndi chuma chathu chakuthupi. Bvumbulutso la Ambuye Yesu Kristu pamenepo sidzakhala nthawi imene idzatibvumbula kukhala akapolo osakhulupirika oyenerera chilango. Koma idzayambitsa nyengo ya madalitso yosafanana ndi ina iri yonse kwa ife monga mbali ya “miyamba yatsopano” kapena “dziko lapansi latsopano” zopangidwa ndi Mulungu. Ndithudi, chimenechi ndi chiyembekezo chabwino kwambiri chimene chiyenera kutetezeredwa.—2 Petro 3:13.