Mutu 2
Alemekezedwa Asanabadwe
PAMBUYO pakuti mngelo Gabrieli wauza Mariya namwaliyo kuti adzabala mwana wamwamuna amene adzakhala mfumu yosatha, Mariya akufunsa kuti: “Ichi chidzachitika bwanji, popeza ine sindidziŵa mwamuna?”
“Mzimu woyera udzafika pa iwe,” Gabrieli akufotokoza motero, “ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe chifukwa chakenso choyeracho chikadzabadwa, chidzatchedwa Mwana wa Mulungu.”
Kuthandiza Mariya kukhulupirira uthenga wake, Gabrieli akupitiriza kuti: “Ndipo tawona Elizabeti mbale wako, iyenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna muukalamba wake; ndipo mwezi uno uli wachisanu ndi chimodzi wa iye ananenedwa wouma. Chifukwa palibe mawu amodzi akuchokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.”
Mariya akukhulupilira mawu a Gabrieli. Ndipo kodi yankho lake nlotani? “Wonani, mdzakazi wa Ambuye!” iye akutero. “Kukhale kwa ine monga mwa mawu anu.”
Mwamsanga pamene Gabrieli achoka, Mariya akukonzekera kupita kukachezera Elizabeti, amene amakhala ndi mwamuna wake, Zakariya, m’dziko lamapiri la Yudeya. Kuchokera kwawo kwa Mariya ku Nazarete umenewo ndiwo ulendo wautali mwinamwake wa masiku atatu kapena anayi.
Potsirizira pake pamene Mariya akufika kunyumba kwa Zakariya, akuloŵa ndi kupereka moni. Pamenepo, Elizabeti akudzazidwa ndi mzimu woyera, ndipo akunena kwa Mariya kuti: “Wodalitsika iwe mwa akazi, ndipo chodalitsika chipatso cha mimba yako. Ndipo ichi chichokera kuti kudza kwa ine, kuti adze kwa ine amake wa Ambuye wanga? Pakuti wona pamene mawu a kulankhula kwako analoŵa m’makutu anga, mwana wosabadwayo anatsalima ndi msangalalo m’mimba mwanga.”
Pakumva zimenezi, Mariya akuyankha ndi mtima woyamikira: “Moyo wanga ulemekeza Ambuye, ndipo mzimu wanga wakondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga. Chifukwa iye anayang’anira umphaŵi wa mdzakazi wake; pakuti tawonani, kuyambira tsopano, anthu amibadwo yonse adzanditchula ine wodala. Chifukwa iye Wamphamvuyo anandichitira ine zazikulu.” Komabe, mosasamala kanthu za chiyanjo chosonyezedwa kwa iye, Mariya akupereka ulemu wonse kwa Mulungu. “Dzina lake liri loyera,” iye akutero, “ndipo chifundo chake chifikira anthu a mibadwomibadwo pa iwo amene amuwopa iye.”
Mariya akupitiriza kutamanda Mulungu mwa nyimbo yake yaulosi wouziridwa, akumalengeza kuti: “Iye anachita zamphamvu ndi mkono wake; iye anabalalitsa odzitama ndi mlingaliro wa mtima wawo. Iye anatsitsa mafumu pamipando yawo yachifumu, ndipo anakweza aumphawi. Anawakhutitsa anjala ndi zinthu zabwino, ndipo eni chuma anawachotsa opanda kanthu. Anathangatira Israyeli mnyamata wake, kuti akakumbukire chifundo, monga analankhula kwa makolo athu kwa Abrahamu ndi kwa mbewu yake kunthaŵi yonse.”
Mariya akukhala ndi Elizabeti kwa pafupifupi miyezi itatu, ndipo mosakayikira iye ali wothandiza kwambiri mkati mwa masabata omalizira ameneŵa a mimba ya Elizabeti. Ndithudi nkwabwino kuti akazi aŵiri okhulupirika ameneŵa, onse aŵiri okhala ndi ana mwa thandizo la Mulungu, angakhale pamodzi panthaŵi yodalitsika imeneyi ya miyoyo yawo!
Kodi mwawona ulemu umene unaperekedwa kwa Yesu ngakhale asanabadwe? Elizabeti anamutcha “Ambuye wanga,” ndipo mwana wake wosabadwa anadumpha ndi chikondwerero pamene Mariya anawonekera poyamba. Kumbali ina, pambuyo pake ena anachitira Mariya ndi mwana wake amene adzabadwa mopanda ulemu, monga momwe tidzawonera. Luka 1:26-56.
▪ Kodi Gabrieli akunenanji kuthandiza Mariya kuti azindikire za mmene adzakhalira ndi pakati?
▪ Kodi Yesu analemekezedwa motani asanabadwe?
▪ Kodi Mariya akunenanji m’nyimbo ya ulosi wolemekeza Mulungu?
▪ Kodi Mariya akukhala kwautali wotani ndi Elizabeti, ndipo nchifukwa ninji kuli koyenerera kuti Mariya akhale ndi Elizabeti mkati mwa nthaŵi imeneyi?