Mutu 126
“Zowonadi Uyu Anali Mwana wa Mulungu”
YESU sanakhale pamtengopo nthaŵi yaitali pamene, dzuŵa liri pamutu, mdima wodabwitsa, wamaola atatu ukuchitika. Kumeneku sikuli kaamba ka kukomana kwa dzuŵa ndi mwezi, popeza kuti zimenezi zimachitika kokha panthaŵi imene mwezi wangokhala kumene koma panopa mwezi uli wathunthu panthaŵi ya Paskha. Ndiponso, kukomana kwa dzuŵa ndi mwezi kumakhala mphindi zochepekera zokha. Chotero mdimawo ngwochititsidwa ndi Mulungu! Mwinamwake ukuchititsa onyodola Yesu kuima kaye, kuchititsa zitonzo zawozo kulekekadi.
Ngati chochitika chozizwitsa chochititsa mantha chapaderachi chikuchitika pamene wochita zoipa winayo asanadzudzule bwenzi lake ndi kupempha Yesu kumkumbukira, chingakhale chochititsa kulapa kwake. Mwinamwake ndimkati mwa mdima umenewu pamene akazi anayi, ndiko kuti, amayi wa Yesu ndi mchemwali wawo Salome, Mariya wa Magadala, ndi Mariya amake a mtumwi Yakobo Wamng’ono, akupita pafupi ndi mtengo wozunzirapowo. Yohane, mtumwi wokondedwa wa Yesu, ali nawo pomwepo.
Mmene mtima wa amayi wa Yesu ‘ukupyozedwera’ nanga pamene iwo akuwona mwana wawo amene anamlera ndi kumsamalira ali pachikike pamenepo muululu! Komabe Yesu akuganiza, osati za ululu wake, koma za ubwino wawo. Movutikira, iye akupukusira mutu kwa Yohane nati kwa amakewo: “Mkazi, tawonani, mwana wanu!” Pamenepo, akupukusira mutu kwa Mariya, nati kwa Yohane: “Tawona, amayi wako.”
Pamenepo Yesu akuikizira chisamaliro cha mayi ŵake, amene mwachiwonekere tsopano ali mkazi wamasiye, kwa mtumwi wake wokondedwa mwapadera. Iye akuchita zimenezi chifukwa chakuti ana ena a Mariya sanasonyezebe chikhulupiriro mwa iye. Motero iye akupereka chitsanzo chabwino popanga makonzedwe osati kokha kaamba ka zofunika zakuthupi za amayi wake komanso kaamba ka zofunika zauzimu.
Pafupifupi 3 koloko masanawo, Yesu akuti: “Ndimva ludzu.” Yesu akuzindikira kuti Atate wake, titero kunena kwake, wachotsa chitetezo pa iye kutsata kuti umphumphu wake uyesedwe kumlingo wotheratu. Chotero iye akufuula ndi mawu aakulu nati: “Mulungu wanga, Mulungu wanga mwandisiiranji ine?” Pakumva zimenezi, ena oimirira pafupipo akudzuma kuti: “Tawonani, aitana Eliya.” Mwamsanga mmodzi wa iwo akuthamanga, naika chinkhupule choviikidwa m’vinyo wosasa pabango, nampatsa kuti amwe. Koma enawo akuti: “Lekani; tiwone ngati Eliya adza kudzamtsitsa.”
Yesu atalandira vinyo wosasayo, akufuula kuti: “Kwatha.” Inde, iye wamaliza zonse zimene Atate wake anamtuma kudzachita padziko lapansi. Potsirizira pake, iye akuti: “Atate, m’manja mwanu ndipereka mzimu wanga.” Mwakutero Yesu akupereka mphamvu yake ya moyo kwa Mulungu ndi chidaliro chakuti Mulungu adzaibwezeretsanso kwa iye. Pamenepo akuweramika mutu nafa.
Panthaŵi imene Yesu akutsirizika, chivomezi chowopsa chikuchitika, chikumaswa miyala. Chivomezicho nchachikulu kwambiri kwakuti manda achikumbukiro kunja kwa Yerusalemu akutseguka ndipo mitembo ikuponyedwera kunja. Anthu odutsa m’njira amene akuwona mitembo yofukukayo akuloŵa mumzinda nasimba zochitikazo.
Ndiponso, panthaŵi imene Yesu akufa, chinsalu chachikulu cholekanitsa chipinda Chopatulika ndi Chopatulukitsa m’kachisi wa Mulungu chikung’ambika pakati, kuchokera pamwamba mpaka pansi. Mwachiwonekere chotchinga chokometseredwa mokongola chimenechi chiri chotalika mamitala 18 ndipo ncholemera zedi! Chozizwitsa chochititsa kakasicho sichikusonyeza kokha mkwiyo wa Mulungu wotsutsa akupha mwambanda Mwana Wake komanso chikutanthauza kuti njira yoloŵera ku chipinda Chopatulukitsa, kumwamba kwenikeniko, tsopano yatheketsedwa ndi imfa ya Yesu.
Eya, anthu akumva chivomezi ndi kuwona zinthu zimene zikuchitika, akuchita mantha kwambiri. Kazembe wa gulu lankhondo woyang’anira kuphedwako akulemekeza Mulungu. “Zowonadi uyu anali Mwana wa Mulungu,” (NW) iye akufuula motero. Mwinamwake iye adaalipo pamene nkhani ya kudzinenera kukhala mwana wa Mulungu inakambitsiridwa pamlandu wa Yesu pamaso pa Pilato. Ndipo tsopano ngwokhutiritsidwa kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu, inde, kuti ndiyedi munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako.
Enanso agonjetsedwa ndi zochitika zozizwitsa zimenezi, ndipo ayamba kubwerera kwawo akumadziguguda pachifukwa monga chisonyezero cha chisoni chawo chachikulu ndi manyazi. Owonerera patali chochitika chapaderachi ndiwo ophunzira achikazi a Yesu amene achititsidwa chidwi ndi zochitika zosaiŵalika zimenezi. Nayenso mtumwi Yohane ali pomwepo. Mateyu 27:45-56; Marko 15:33-41; Luka 23:44-49; 2:34, 35; Yohane 19:25-30.
▪ Kodi nchifukwa ninji kukumana kwa dzuŵa ndi mwezi sikunachititse maola atatuwo a mdima?
▪ Mwamsanga imfa yake isanachitike, kodi ndichitsanzo chabwino chotani chimene Yesu akupereka kwa awo amene ali ndi makolo okalamba?
▪ Kodi nziti zimene ziri ndemanga zinayi za Yesu asanafe?
▪ Kodi chivomezi chikukwaniritsanji, ndipo nchiyani chomwe chiri tanthauzo la kung’ambika pakati kwa chotchinga cha m’kachisi?
▪ Kodi kazembe wa gulu lankhondo woyang’anira kuphedwako akuyambukiridwa motani ndi zozizwitsazo?