Mutu 127
Kuikidwa m’Manda Lachisanu—Manda Apululu pa Lamlungu
POFIKA tsopano ndi Lachisanu masana, ndipo Lasabata Nisani 15 lidzayamba pakuloŵa kwa dzuŵa. Mtembo wa Yesu uli lenjekeke pamtengopo, koma achifwamba aŵiriwo pambali pake adakali moyobe. Lachisanu masana limatchedwa Lokonzera chifukwa ndipamene anthu amakonza zakudya ndi kutsiriza ntchito iriyonse yofunikira imene singayembekezere kufikira pambuyo pa Sabata.
Sabata limene lidzayamba msanga siliri kokha Sabata lanthaŵi zonse (tsiku lachisanu ndi chiŵiri la mlungu) komanso nloŵirikiza kaŵiri, kapena kuti Sabata “lalikulu.” Limatchedwa motero chifukwa chakuti Nisani 15, limene liri tsiku loyamba la Phwando la Mikate Yopanda Chotupitsa la masiku asanu ndi aŵiri (ndipo nthaŵi zonse ndilo Sabata, mosasamala kanthu kuti limadza tsiku liti lamlungu), limakhala patsiku limodzimodzilo monga Sabata lanthaŵi zonse.
Malinga ndi Chilamulo cha Mulungu, mitembo siyenera kusiidwa iri pachikike pamtengo usiku wonse. Chotero Ayuda akupempha Pilato kuti imfa ya opachikidwawo ifulumizidwe mwa kuthyola miyendo yawo. Chifukwa cha chimenecho, asilikali akuthyola miyendo ya achifwamba aŵiriwo. Koma popeza kuti Yesu akuwonekera kukhala atafa, miyendo yake sikuthyoledwa. Zimenezi zikukwaniritsa lembalo: “Fupa la iye silidzathyoledwa.”
Komabe, kuti achotse chikayikiro chirichonse chakuti Yesu wafadi, mmodzi wa asilikaliwo akumbaya ndi thungo m’nthiti mwake. Nthungoyo ikupyoza pafupi ndi mtima wake, ndipo pomwepo magazi ndi madzi zikuchucha. Mtumwi Yohane, amene ali mboni yowona ndi maso, akusimba kuti zimenezi zikukwaniritsa lemba lina: “Adzayang’ana pa iye amene anampyoza.”
Ndiponso amene alipo pakuphedwako ndiye Yosefe wa kumzinda wa Arimateya, chiŵalo chotchuka cha Sanhedrin. Iye anakana kuchita voti movomereza kachitidwe kopanda chilungamo ka bwalo lamilandu lalikulu kotsutsa Yesu. Kwenikweni Yosefe ali wophunzira wa Yesu, ngakhale kuli kwakuti wakhala akuchita mantha kudziulula monga wotero. Komabe, tsopano iye, akusonyeza kulimba mtima ndipo akumka kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu. Pilato akuitana mkulu wa gulu la ankhondo, ndipo ofesalayo atatsimikizira kuti Yesu wafadi, Pilato akuchititsa mtembowo kuperekedwa.
Yosefe akutenga mtembowo naukulunga m’nsalu yopanda litsiro yabafuta kukonzekerera kuika maliro. Iye akuthandizidwa ndi Nikodemo, chiŵalo china cha Sanhedrin. Nikodemo nayenso walephera kuvomereza kuti amakhulupirira Yesu chifukwa cha kuwopa kutayikiridwa ndi malo ake. Koma tsopano iye akudza ndi nsupa yokhala ndi pafupifupi makilogiramu makumi atatu mphambu atatu a mure ndi aloe wokwera mtengo. Mtembo wa Yesu ukukulungidwa m’milezo yopakidwa zonunkhira zimenezi, monga momwedi uliri mwambo wa Ayuda wa kukonzekeretsa mitembo kaamba ka kuikidwa.
Pamenepo mtembowo ukuikidwa m’manda achikumbukiro atsopano a Yosefe osemedwa pathanthwe m’munda wake pafupipo. Potsirizira pake, mwala waukulu ukukunkhuniziridwa pakhomo la mandawo. Kuti kuika maliroko kumalizidwe Sabata lisanafike, kukonza mtembowo kukuchitidwa mofulumira. Chifukwa cha chimenecho, Mariya wa Magadala ndi Mariya amayi ŵa Yakobo Wamng’ono, amene mwinamwake akhala akuthandiza kukonzako, akupita mofulumira kunyumba kukakonza zonunkhira zina zowonjezereka ndi mafuta onunkhira. Sabata litatha, iwo akulinganiza kukadzozanso mtembo wa Yesu kuti ausungitse kwanthaŵi yaitali.
Tsiku lotsatira, limene liri Loŵeruka (Sabata), akulu ansembe ndi Afarisi akupita kwa Pilato ndi kunena: “Mfumu, takumbukira ife kuti wonyenga uja anati, pamene anali ndi moyo, Ndidzauka pofika masiku atatu. Chifukwa chake mulamule kuti asindikize pamandapo, kufikira tsiku lachitatulo, kuti kapena ophunzira ake angadze, nadzamuba iye, nadzanena kwa anthu, kuti iye anauka kwa akufa: ndipo chinyengo chomaliza chidzaposa choyambacho.”
“Tengani alonda,” Pilato akuyankha motero. “Mukani, kasungeni monga mudziŵa.” Chotero iwo akumka nalonda mandawo mwa kusindikiza mwalawo ndi kuikapo asilikali Achiroma monga alonda.
Lamlungu mmamaŵa Mariya wa Magadala ndi Mariya amayi ŵa Yakobo, limodzi ndi Salome, Yohana, ndi akazi ena, akubweretsa zonunkhira kumanda kuzadzoza mtembo wa Yesu. Ali panjira akufunsana kuti: “Adzatikunkhunizira ndani mwalawo, pakhomo la manda?” Koma atafika, akupeza kuti pachitika chivomezi ndipo mngelo wa Yehova wakunkhuniza mwalawo kuuchotsa. Alonda apita, ndipo mandawo ngapululu! Mateyu 27:57–28:2; Marko 15:42–16:4; Luka 23:50–24:3, 10; Yohane 19:14, 31–20:1; 12:42; Levitiko 23:5-7; Deuteronomo 21:22, 23; Salmo 34:20; Zekariya 12:10.
▪ Kodi nchifukwa ninji Lachisanu limatchedwa Lokonzera, ndipo Sabata “lalikulu” nchiyani?
▪ Kodi ndimalemba ati amene akukwaniritsidwa mogwirizana ndi mtembo wa Yesu?
▪ Kodi Yosefe ndi Nikodemo akuchitanji pakuikidwa kwa Yesu, ndipo unansi wawo ndi Yesu ngwotani?
▪ Kodi ndipempho lotani limene ansembe akupanga kwa Pilato, ndipo kodi iye akuyankha motani?
▪ Kodi nchiyani chikuchitika Lamlungu mmamaŵa?