Yohane
12 Kutangotsala masiku 6 kuti pasika ayambike, Yesu anafika ku Betaniya+ kumene kunali Lazaro,+ uja amene Yesu anamuukitsa kwa akufa. 2 Choncho anamukonzera chakudya chamadzulo kumeneko, ndipo Marita+ anali kutumikira.+ Lazaro anali mmodzi wa anthu amene anali kudya naye.+ 3 Pamenepo Mariya anatenga mafuta onunkhira. Mafutawa anali nado+ weniweni, okwera mtengo kwambiri okwana magalamu 327. Mariya anathira mafutawo pamapazi a Yesu ndi kupukuta mapaziwo ndi tsitsi lake.+ M’nyumba monsemo munangoti guu kafungo kabwino ka mafutawo. 4 Koma Yudasi Isikariyoti,+ mmodzi wa ophunzira ake, amene anali pafupi kumupereka anati: 5 “N’chifukwa chiyani mafuta onunkhirawa+ sanagulitsidwe madinari 300 ndi kupereka ndalamazo kwa anthu osauka?”+ 6 Koma iye ponena izi sikuti anali kudera nkhawa osauka ayi, koma chifukwa anali wakuba.+ Iye anali wosunga bokosi la ndalama,+ ndipo anali kutengamo ndalama zimene zinali kuponyedwa m’bokosilo. 7 Choncho Yesu anati: “M’lekeni, achite mwambo umenewu pokonzekera tsiku limene ndidzaikidwe m’manda.+ 8 Pakuti osaukawo+ muli nawo nthawi zonse, koma ine simudzakhala nane nthawi zonse.”
9 Tsopano khamu lalikulu la Ayuda linadziwa kuti Yesu ali kumeneko. Choncho linafika, osati chifukwa cha Yesu yekha ayi, komanso kuti lidzaone Lazaro, amene iye anamuukitsa kwa akufa.+ 10 Pamenepo ansembe aakulu anasonkhana pamodzi ndi kupangana zakuti aphenso Lazaro,+ 11 chifukwa Ayuda ambiri anali kupita kumeneko ndi kukhulupirira Yesu chifukwa cha Lazaroyo.+
12 Tsiku lotsatira, khamu lalikulu la anthu amene anabwera ku chikondwererocho, atamva kuti Yesu akubwera ku Yerusalemuko, 13 anatenga nthambi za kanjedza+ ndi kutuluka kukamuchingamira. Ndipo anayamba kufuula kuti:+ “M’pulumutseni!+ Wodalitsidwa iye wobwera m’dzina la Yehova,+ amenenso ndi mfumu+ ya Isiraeli!” 14 Koma pamene Yesu anapeza bulu wamng’ono,+ anakwera pa iye monga mmene Malemba amanenera kuti: 15 “Usaope mwana wamkazi wa Ziyoni. Taona! Mfumu yako ikubwera.+ Ikubwera itakwera bulu wamng’ono wamphongo.”+ 16 Poyamba ophunzira akewo sanazindikire zimenezi.+ Koma pamene Yesu analandira ulemerero,+ iwo anakumbukira kuti zimenezi zinalembedwa ponena za iye. Anakumbukiranso kuti anamuchitira zimenezi.+
17 Tsopano anthu ambiri amene analipo pamene iye anaitana Lazaro+ kuti atuluke m’manda achikumbutso ndi kumuukitsa, anali kumuchitira umboni.+ 18 Pa chifukwa chimenechi, anthu onsewo anamuchingamira, chifukwa anamva kuti anachita chizindikiro+ chimenechi. 19 Pamenepo Afarisi+ anayamba kuuzana kuti: “Apa ndiye mukudzionera nokha kuti palibiretu chimene tikuphulapo. Onani! Dziko lonse lakhamukira kwa iye.”+
20 Pakati pa obwera kudzalambira ku chikondwereroko panalinso Agiriki.+ 21 Amenewa anafika kwa Filipo+ wa ku Betsaida ku Galileya, ndipo anayamba kumupempha kuti: “Bambo, ife tikufuna kuona Yesu.”+ 22 Filipo anapita kukauza Andireya zimenezo. Andireya ndi Filipo anapita kukauza Yesu.
23 Koma Yesu anawayankha kuti: “Nthawi yafika yakuti Mwana wa munthu alemekezedwe.+ 24 Ndithudi ndikukuuzani, Kambewu ka tirigu kakapanda kugwa m’nthaka ndi kufa, kamakhalabe kamodzi komweko. Koma kakafa,+ kamadzabala zipatso zambiri. 25 Aliyense wokonda moyo wake akuuwononga, koma wodana ndi moyo wake+ m’dziko lino akuusungira moyo wosatha.+ 26 Ngati munthu wafuna kunditumikira ine, anditsatire, ndipo kumene ine ndidzakhala, mtumiki wanga adzakhalanso komweko.+ Aliyense wonditumikira ine, Atate adzamulemekeza.+ 27 Moyo wanga ukusautsika tsopano,+ ndinene chiyani kodi? Atate ndipulumutseni ku nthawi yosautsayi.+ Komabe nthawi imeneyi iyenera kundifikira pakuti ndiye chifukwa chake ndinabwera. 28 Atate lemekezani dzina lanu.” Pamenepo mawu+ anamveka kuchokera kumwamba kuti: “Ndalilemekeza ndipo ndidzalilemekezanso.”+
29 Chotero khamu la anthu amene anali ataimirira pamenepo ndi kumva zimenezi anayamba kunena kuti kwagunda bingu. Ena anayamba kunena kuti: “Mngelo walankhula naye.” 30 Poyankha Yesu anati: “Sikuti mawu amenewa amveka chifukwa cha ine ayi, koma chifukwa cha inu.+ 31 Tsopano dziko ili likuweruzidwa, wolamulira wa dzikoli+ aponyedwa kunja tsopano.+ 32 Koma ine ndikadzakwezedwa+ m’mwamba padziko lapansi, ndidzakokera anthu osiyanasiyana kwa ine.”+ 33 Kwenikweni ananena izi pofuna kusonyeza mtundu wa imfa imene anali pafupi kufa.+ 34 Pamenepo khamu la anthulo linamuyankha kuti: “Ife tinamva m’Chilamulo kuti Khristu adzakhala kosatha.+ Nanga inu mukunena bwanji kuti Mwana wa munthu adzakwezedwa m’mwamba?+ Kodi Mwana wa munthu ameneyo ndani?”+ 35 Pamenepo Yesu anati: “Kuwala kukhalabe pakati panu kanthawi pang’ono. Yendani pamene kuwalako mudakali nako, kuti mdima+ usakugwereni, pakuti woyenda mu mdima sadziwa kumene akupita.+ 36 Pamene kuwala mudakali nako, sonyezani chikhulupiriro mwa kuwalako, kuti mukhale ana ake a kuwala.”+
Yesu atanena zimenezi, anachoka ndi kuwabisalira. 37 Koma ngakhale kuti anachita zizindikiro zambiri pamaso pawo, iwo sanali kukhulupirira iye, 38 moti mawu a mneneri Yesaya anakwaniritsidwa. Iye anati: “Yehova,* kodi ndani wakhulupirira zimene ife tamva?+ Ndipo kodi dzanja la Yehova laonetsedwa kwa ndani?”+ 39 Chifukwa chimene sanakhulupirire n’chimenenso Yesaya ananena kuti: 40 “Wachititsa khungu maso awo ndipo waumitsa mitima yawo,+ kuti asamaone ndi maso awowo, asazindikire ndi mitima yawo ndi kutembenuka kuti ine ndiwachiritse.”+ 41 Yesaya ananena zimenezi chifukwa anaona ulemerero wa Khristu,+ ndipo ananena za iye. 42 Komabe ambiri, ngakhalenso olamulira anamukhulupirira,+ koma chifukwa cha Afarisi sanavomereze poyera, poopa kuti angawachotse musunagoge.+ 43 Pakuti anakonda kwambiri ulemerero wa anthu kuposa ulemerero wa Mulungu.+
44 Koma Yesu anafuula kuti: “Wokhulupirira ine sakhulupirira ine ndekha, komanso amakhulupirira iye amene anandituma ine.+ 45 Amene wandiona ine waonanso amene anandituma.+ 46 Ndabwera monga kuwala m’dziko,+ kuti aliyense wokhulupirira ine asapitirize kukhala mumdima.+ 47 Ngati munthu wamva mawu anga koma osawasunga, ine sindiweruza woteroyo, pakuti sindinabwere kudzaweruza dziko,+ koma kudzalipulumutsa.+ 48 Aliyense wondinyalanyaza ndi kusalandira mawu anga, ali naye mmodzi womuweruza. Mawu+ amene ine ndalankhula ndi amene adzamuweruze pa tsiku lomaliza. 49 Chifukwa sindinalankhulepo zongoganiza pandekha, koma Atate amene ananditumawo anandipatsa lamulo pa zimene ndiyenera kunena ndi zimene ndiyenera kulankhula.+ 50 Komanso ndikudziwa kuti lamulo lake limatanthauza moyo wosatha.+ Choncho zimene ndimalankhula, monga mmene Atate anandiuzira, ndimazilankhula momwemo.”+