Chigawo 9
Mmene Tidziŵira Kuti Tiri mu “Masiku Otsiriza”
1, 2. Kodi tikakhoza kuzindikira bwanji kuti tili m’masiku otsiriza?
KODI tingatsimikizire motani kuti tikukhala ndi moyo panthaŵi imene Ufumu wa Mulungu udzachitapo kanthu motsutsana ndi dongosolo la zinthu lilipoli la ulamuliro wa anthu? Kodi tingadziŵe bwanji kuti tayandikira kwambiri nthaŵi pa imene Mulungu adzathetsa kuipa konse ndi kuvutika?
2 Ophunzira a Yesu Kristu anafuna kudziŵa zinthu zimenezo. Iwo anafunsa chimene chikakhala “chizindikiro” chakukhalapo kwake m’mphamvu ya Ufumu ndi cha mapeto a dongosolo la zinthu.” (Mateyu 24:3, NW) Yesu anayankha mwakundandalika zochitika zogwedeza dziko ndi mikhalidwe imene ikapanga chiungwe chosonyeza kuti mtundu wa anthu waloŵa “nthaŵi yamapeto,” “masiku otsiriza” a dongosolo lino la zinthu. (Danieli 11:40; 2 Timoteo 3:1) Kodi ife m’zaka za zana lino tawona chizindikiro chachiungwe chimenecho? Inde, tatero, mosaphonyetsa!
Nkhondo za Dziko
3, 4. Kodi nkhondo za zana lino zikuyenerana motani ndi ulosi wa Yesu?
3 Yesu ananeneratu kuti “mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina.” (Mateyu 24:7) Mu 1914 dziko linaloŵetsedwa m’nkhondo imene inachititsa mitundu ndi maufumu kuvala zilimbe mwanjira imene inali yosiyana ndi nkhondo iliyonse isanachitike imeneyi. Povomereza chenicheni chimenecho, olemba mbiri apanthaŵiyo anaitcha Nkhondo Yaikulu: inali nkhondo yoyamba yamtundu umenewo m’mbiri, nkhondo yoyamba yadziko. Asilikali ankhondo okwanira 20,000,000 ndi anthu wamba anafa, chiŵerengero chachikulu koposa cha m’nkhondo iliyonse kalelo.
4 Nkhondo Yoyamba I inali chizindikiro cha kuyamba kwa masiku otsiriza. Yesu ananena kuti chochitika ichi ndi zina chikakhala “zowawa zoyamba.” (Mateyu 24:8) Zimenezo zinatsimikizira kukhala zowona, chifukwa chakuti Nkhondo Yadziko II inali yakupha mowonjezerekadi, asilikali ankhondo okwanira 50,000,000 ndi anthu wamba anafa. M’zaka za zana la 20 lino, anthu oposa 100,000,000 aphedwa m’nkhondo, okwanira kuŵirikiza nthaŵi zinayi kuposa zaka 400 zapitazo zitaikidwa pamodzi! Ndikutsutsidwa kwakukulu chotani nanga kwa ulamuliro wa anthu!
Maumboni Ena
5-7. Kodi ndi ati amene ali ena amaumboni akuti tili m’masiku otsiriza?
5 Yesu anaphatikizamo zochitika zina zimene zikatsagana ndi masiku otsiriza. “Kudzakhala zivomezi zazikulu, ndi njala ndi miliri [nthenda za mliri] mmalo akutiakuti.” (Luka 21:11) Zimenezo zikuyenerana ndendende ndi zochitikazo chiyambire 1914, popeza kuti kwakhalapo kuwonjezereka kwakukulu kwa masautso ochokera m’masoka amenewo.
6 Zivomezi zazikulu zikuchitika mwakaŵirikaŵiri, zikumawononga miyoyo yambiri. Fuluwenza ya Spanya yokha inapha anthu 20,000,000 pambuyo pa Nkhondo Yadziko I—ena akuyerekezera chiwerengelocho kukhala 30,000,000 kapena kuposa. AIDS yapha anthu zikwi mazana ambiri ndipo ikakhoza kupha mamiliyoni ambiri owonjezereka posachedwapa mtsogolo muno. Chaka chilichonse mamiliyoni ambiri amafa ndi nthenda zamtima, kansa, ndi nthenda zina. Mamiliyoni owonjezereka amafa ndi imfa yapang’onopang’ono ya njala. Mosakayikira ‘apakavalo a Chivumbulutso’ limodzi ndi nkhondo zawo, kupereŵera kwa zakudya, ndi miliri ya matenda akhala akupha ziŵerengero zazikulu za banja laumunthu chiyambire 1914.—Chivumbulutso 6:3-8.
7 Yesu ananeneratunso kuwonjezereka kwa upandu umene ukuchitika m’maiko onse. Iye anati: “Chifukwa cha kuchuluka kwa kusayeruzika, chikondano cha anthu aunyinji chidzazirala.”—Mateyu 24:12.
8. Kodi ulosi wa pa 2 Timoteo chaputala 3 umayenerana motani ndi nthaŵi yathu?
8 Ndiponso, ulosi wa Baibulo unaneneratu kunyonyotsoka kwa makhalidwe abwino kumene kukuwonekera kwambiri padziko lonse lapansi lerolino: “Masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zowawitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu, akukhala nawo mawonekedwe achipembedzo, koma mphamvu yake adaikana . . . koma anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire.” (2 Timoteo 3:1-13) Zonsezo taziwona ndi maso athuwa.
Chinthu China
9. Kodi chinachitika n’chiyani kumwamba chimene chinachitikira pamodzi ndi kuyamba kwa masiku otsiriza padziko lapansi?
9 Pali chinthu china chochititsa kuwonjezereka kwakukulu kwa kuvutika m’zaka za zana lino. Panthaŵi imodzimodzi ndi chiyambi cha masiku otsiriza mu 1914, chinthu china chinachitika chimene chinaika anthu paupandu wokulirapodi. Panthaŵiyo, monga momwe ulosi wa buku lomalizira la Baibulo umasimbira: “Munali nkhondo m’mwamba. Mikayeli [Kristu ali mu ulamuliro wakumwamba] ndi angelo ake akuchita nkhondo ndi chinjoka [Satana], chinjokanso ndi angelo ake [ziŵanda] chinachita nkhondo ndipo sichinalakika, ndipo sanapezekanso malo awo m’mwamba. Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iyo yotchedwa mdyerekezi ndi Satana wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi padziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.”—Chivumbulutso 12:7-9.
10, 11. Kodi mtundu wa anthu unayambukiridwa motani pamene Satana ndi ziŵanda zake anaponyeredwa kudziko lapansi?
10 Kodi zotulukapo zinali chiyani ku banja laumunthu? Ulosiwo ukupitiriza kuti: “Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.” Inde, Satana amadziŵa kuti dongosolo lake lili pafupi kutha, chotero iye amachita zonse zimene angathe kuchititsa anthu kupandukira Mulungu iye ndi dziko lake asanawonongedwe. (Chivumbulutso 12:12; 20:1-3) Zolengedwa za uzimu zimenezo zili zoluluzika chotani nanga chifukwa chakuti zinagwiritsira ntchito molakwa ufulu wawo wakusankha! Mikhalidwe yakhala yochititsa mantha chotani nanga padziko lapansi mwachisonkhezero chawo, makamaka chiyambire 1914!
11 Nkosadabwitsa kuti Yesu ananeneratu za nthaŵi yathu kuti: “Kudzakhala zowopsa ndi zizindikiro zazikulu zakumwamba.”—Luka 21:11.
Mapeto Aulamuliro wa Anthu ndi Auchiŵanda Ayandikira
12. Kodi ndi uti umene uli umodzi wa maulosi omalizira otsala umene ufunikira kukwaniritsidwa dongosolo lino lisanathe?
12 Kodi ndi maulosi a Baibulo angati amene atsala kuti akwaniritsidwe Mulungu asanawononge dongosolo lilipoli la zinthu? Oŵerengeka kwambiri! Umodzi wa omalizira uli pa 1 Atesalonika 5:3, umene umati: “Ali chilankhulire za mtendere ndi chisungiko, mwadzidzidzi tsoka lidzakhala pa iwo.” (The New English Bible) Zimenezi zisonyeza kuti mapeto a dongosolo lino adzayamba “pamene ali chilankhulire.” Mosawonedweratu ndi dziko, chiwonongeko chidzakantha pamene sichikuyembekezeredwa konse, pamene chisamaliro cha anthu chidzasumikidwa pamtendere wawo ndi chisungiko zoyembekezeredwazo.
13, 14. Kodi ndi nthaŵi yachivuto iti imene Yesu adaneneratu, ndipo kodi idzatha bwanji?
13 Nthaŵi ikuthera dziko lino losonkhezeredwa ndi Satana. Posachedwa lidzatha m’nthaŵi yachivuto chimene Yesu anati: “Kudzakhala chinsautso chachikulu chimene sichinachitike chiyambire chiyambi chadziko kufikira tsopano, inde, ndipo sichidzachitikanso.”—Mateyu 24:21.
14 Chimake cha “chinsautso chachikulu” chidzakhala nkhondo ya Mulungu ya Armagedo. Ndiyo nthaŵi yonenedwa ndi mneneri Danieli pamene Mulungu ‘adzakantha ndi kutha maufumu awo onse.’ Izi zidzatanthauza mapeto a maulamuliro onse alipowa a anthu osadalira pa Mulungu. Pamenepo Ulamuliro Wake wa Ufumu udzaloŵa mmalo kotheratu kuyendetsa zochitika zonse za anthu. Danieli adaneneratu kuti, ulamuliro sudzasiidwiranso “mtundu wina wa anthu.”—Danieli 2:44; Chivumbulutso 16:14-16.
15. Kodi chidzachitika n’chiyani kuchisonkhezero cha Satana ndi ziŵanda zake?
15 Ndiponso, panthaŵiyo, chisonkhezero chonse cha Satana ndi ziŵanda chidzatha. Zolengedwa zauzimu zopanduka zimenezo zidzawonongedwa kotero kuti sizidzakhozanso ‘kusokeretsa mitundu.’ (Chivumbulutso 12:9; 20:1-3) Iwo apatsidwa chiweruzo cha ku imfa ndipo akuyembekezera chiwonongeko. N’chimasuko chotani nanga kwa mtundu wa anthu kumasuka kuchisonkhezero chawo choluluzika!
Kodi Adzapulumuka Ndani? Kodi Ndani Sadzatero?
16-18. Kodi ndani adzapulumuka mapeto a dongosolo lino, ndipo kodi ndani amene sadzatero?
16 Pamene ziŵeruzo za Mulungu ziperekedwa motsutsana ndi dziko lino, kodi adzapulumuka ndani? Kodi ndani sadzatero? Baibulo limasonyeza kuti awo amene amafuna ulamuliro wa Mulungu adzatetezeredwa ndipo adzapulumuka. Awo amene safuna ulamuliro wa Mulungu sadzatetezeredwa ndipo adzawonongedwa limodzi ndi dziko la Satana.
17 Miyambo 2:21, 22 imati: “Pakuti owongoka mtima [ogonjera ku ulamuliro wa Mulungu] adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa [awo amene samagonjera ku ulamuliro wa Mulungu], adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.”
18 Salmo 37:10, 11 nalonso limati: “Katsala kanthaŵi ndipo oipa adzatha psyiti . . . Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” Vesi 29 limawonjezera kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”
19. Kodi ndi uphungu wotani umene tiyenera kuulabadira?
19 Tiyenera kulabadira uphungu wa Salmo 37:34, umene umati: “Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo iye adzakukweza kuti ulandire dziko: Pakudulidwa oipa udzapenya.” Vesi 37 ndi 38 limati: “Tapenya wangwiro, ndipo tawona wowongoka mtima! Pakuti kumatsiriziro ake a munthuyo kuli mtendere. Koma olakwa adzawonongeka pamodzi: matsiriziro a oipa adzadulidwa.”
20. Kodi n’chifukwa ninji tinganene kuti zino zili nthaŵi zochititsa nthumanzi zokhalamo ndi moyo?
20 Nkotonthoza chotani nanga, inde, nkosonkhezera chotani nanga kuzindikira kuti Mulungu amasamaliradi ndi kuti mwamsanga iye adzathetsa kuipa konse ndi kuvutika! Nkochititsa nthumanzi chotani nanga kuzindikira kuti tikukhala pafupi penipeni ndi nthaŵi yakukwaniritsidwa kwa maulosi aulemerero amenewo!
[Chithunzi patsamba 20]
Baibulo lidaneneratu zochitika zimene zikapanga “chizindiro” cha masiku otsiriza
[Chithunzi patsamba 22]
Posachedwa, pa Armagedo, awo amene sakugonjera kuulamuliro wa Mulungu, adzadulidwa. Awo amene akugonjera adzapulumuka kuloŵa m’dziko latsopano lolungama