MUTU 9
Kodi Tilidi ‘M’masiku Otsiriza’?
Kodi Baibulo linaneneratu mavuto ati omwe akuchitika masiku ano?
Kodi Baibulo linaneneratu kuti anthu adzakhala ndi makhalidwe otani m’masiku otsiriza?
Kodi ndi zinthu zabwino ziti zimene Baibulo linaneneratu kuti zidzachitika ‘m’masiku otsiriza’?
1. Kodi ndi buku liti limene lingatithandize kudziwa za m’tsogolo?
KODI nthawi ina mutamvetsera nkhani pa wailesi kapena pa TV, munadzifunsapo kuti, ‘Kodi dzikoli likupita kuti?’ Masiku ano anthu amangokumana ndi mavuto mosayembekezereka ndipo palibe amene angadziwiretu kuti mawa tikumana ndi zotani. (Yakobo 4:14) Koma Yehova amadziwa zimene zidzachitike m’tsogolo. (Yesaya 46:10) Iye ananeneratu m’Baibulo zinthu zabwino komanso zoipa zimene zikuchitika masiku ano ndiponso ananeneratu za zinthu zosangalatsa zomwe zichitike posachedwapa.
2, 3. Kodi ophunzira a Yesu anamufunsa funso loti chiyani, nanga iye anawayankha bwanji?
2 Yesu Khristu analankhula za Ufumu wa Mulungu umene udzathetse zinthu zonse zoipa ndi kukonzanso dzikoli kuti likhale paradaiso. (Luka 4:43) Anthu ankafuna kudziwa kuti Ufumuwo udzabwera liti, n’chifukwa chake ophunzira a Yesu anam’funsa kuti: “Kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a nthawi ino chidzakhala chiyani?” (Mateyu 24:3) Poyankha, Yesu anawauza kuti ndi Yehova Mulungu yekha amene akudziwa nthawi yeniyeni imene mapeto adzafike. (Mateyu 24:36) Koma Yesu ananeneratunso zinthu zimene zidzachitike padziko lapansi Ufumu wa Mulungu usanabweretse mtendere kwa anthu. Ndipo zimene ananenazo ndi zomwe zikuchitika masiku ano.
3 Tisanaone umboni wosonyeza kuti tili m’nthawi ya “mapeto,” tiyeni tikambirane kaye mwachidule za nkhondo inayake yomwe palibe munthu aliyense amene anaiona ikuchitika. Nkhondoyi inachitikira kumwamba koma zotsatira zake zimatikhudza.
NKHONDO IMENE INACHITIKA KUMWAMBA
4, 5. (a) Kodi n’chiyani chinachitika kumwamba Yesu atangokhala Mfumu? (b) Malinga ndi lemba la Chivumbulutso 12:12, kodi zotsatira za nkhondo imene inachitika kumwamba n’zotani?
4 Mutu wapitawu unafotokoza kuti Yesu Khristu anayamba kulamulira monga Mfumu mu 1914. (Werengani Danieli 7:13, 14.) Yesu atangokhala Mfumu anayamba kugwira ntchito yake. Baibulo limati: “Kumwamba kunabuka nkhondo. Mikayeli [dzina lina la Yesu] ndi angelo ake anamenyana ndi chinjoka [Satana Mdyerekezi]. Chinjokacho ndi angelo ake chinamenya nkhondo.”a Satana ndi angelo ake oipa, kapena kuti ziwanda, anagonja pa nkhondoyo ndipo anachotsedwa kumwamba n’kuponyedwa padziko lapansi. Angelo okhulupirika anasangalala chifukwa choti Satana ndi ziwanda zake anachotsedwa kumwamba. Koma anthu sakanatha kusangalala ngati mmene anachitira angelo kumwamba chifukwa Baibulo linaneneratu kuti: “Tsoka dziko lapansi . . . chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, ndipo ali ndi mkwiyo waukulu podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.”—Chivumbulutso 12:7, 9, 12.
5 Taonani zotsatira za nkhondo yomwe inachitika kumwambayo. Chifukwa chokwiya, Satana anabweretsa tsoka, kapena kuti mavuto padziko lapansi. Monga mmene muonere m’nkhaniyi, panopa tikukhala m’nthawi ya mavuto imeneyi. Koma zimenezi sizitenga nthawi yaitali, ndi za “kanthawi kochepa,” ndipo ngakhale Satanayo amadziwa zimenezi. Baibulo limatchula nthawi imeneyi kuti ndi “masiku otsiriza.” (2 Timoteyo 3:1) N’zosangalatsa kudziwa kuti posachedwapa Mulungu achotsa mavuto onse amene Mdyerekezi akuchititsa padziko lapansili. Tsopano tiyeni tikambirane zinthu zina zimene zikuchitika masiku ano zomwe Baibulo linaneneratu kuti zidzachitika. Zinthu zimenezi zimatitsimikizira kuti tikukhala m’masiku otsiriza ndiponso kuti Ufumu wa Mulungu watsala pang’ono kubweretsa madalitso kwa anthu amene amakonda Yehova. Choyamba tiyeni tikambirane zinthu 4 zimene Yesu anatchula ngati chizindikiro cha masiku otsiriza.
ZINTHU ZIKULUZIKULU ZOCHITIKA M’MASIKU OTSIRIZA
6, 7. Kodi mawu a Yesu onena za nkhondo ndi njala akukwaniritsidwa bwanji masiku ano?
6 “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina.” (Mateyu 24:7) Anthu mamiliyoni ambiri aphedwa pa nkhondo m’zaka 100 zapitazi. Katswiri wina wolemba mbiri yakale wa ku Britain analemba kuti: “Zaka za m’ma 1900 ndi nthawi imene anthu anaphedwa kwambiri kuposa zaka zina zonse m’mbuyomu. . . . Nkhondo zinkangotsatizana moti pafupifupi nthawi ina iliyonse pankakhala dera kapena dziko linalake kumene kunali nkhondo.” Lipoti la bungwe lina linati: “Anthu amene anafa pa nkhondo m’zaka za m’ma 1900 ndi ochuluka kuwirikiza katatu kuposa amene anafa pa nkhondo zonse zimene zinachitika pa zaka zoposa 1,800 za m’mbuyo mwa nthawi imeneyi.” (Worldwatch Institute) Anthu oposa 100 miliyoni aphedwa pa nkhondo zimene zamenyedwa kuyambira m’chaka cha 1914. Zimakhala zopweteka mnzathu kapena m’bale wathu mmodzi akaphedwa pa nkhondo. Ndiye tangoganizani chisoni chimene achibale komanso anzawo a anthu mamiliyoni amenewa anakhala nacho.
7 “Kudzakhala njala.” (Mateyu 24:7) Kafukufuku amasonyeza kuti chakudya chimene anthu akhala akukolola m’zaka 30 zapitazi, n’chochuluka kwambiri kuposa chimene amakolola m’mbuyomu. Komabe anthu ambiri akuvutikabe ndi njala chifukwa chakuti alibe ndalama zogulira chakudya kapena malo olima. Anthu oposa 1 biliyoni a m’mayiko osauka amapeza ndalama yosakwana 1 dola patsiku. Ambiri mwa anthu amenewa amakhala ndi njala nthawi zonse. Malinga ndi Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse, ana oposa 5 miliyoni amamwalira chaka chilichonse chifukwa chosowa zakudya.
8, 9. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti maulosi a Yesu onena za zivomezi ndi miliri akukwaniritsidwa?
8 “Kudzachitika zivomezi zamphamvu.” (Luka 21:11) Malinga ndi bungwe lina la ku United States, chaka chilichonse padziko lapansi pamachitika zivomezi zikuluzikulu pafupifupi 19. (U.S. Geological Survey) Zivomezi zimenezi zimakhala zamphamvu moti n’kuwononga nyumba komanso kung’amba nthaka. Ndipo pafupifupi chaka chilichonse kumachitika zivomezi zamphamvu kwambiri zomwe zimatha kuwonongeratu nyumba. Anthu ena ofufuza apeza kuti zivomezi zapha anthu oposa 2 miliyoni kuyambira mu 1900. Nkhani ina inati: “Kupita patsogolo kwa sayansi kwangochepetsako pang’ono chiwerengero cha anthu amene amafa pakachitika chivomezi.”
9 “Kudzakhala miliri.” (Luka 21:11) Ngakhale kuti luso lachipatala lapita patsogolo, matenda akale komanso atsopano akupitirizabe kuvutitsa anthu. Lipoti lina linanena kuti matenda oposa 20 odziwika bwino, kuphatikizapo chifuwa chachikulu cha TB, malungo ndi kolera, achuluka kwambiri zaka zapitazi ndipo mitundu ina ya matenda yayamba kusamva mankhwala. Ndiponso kwabwera matenda ena atsopano pafupifupi 30. Ena mwa matendawa alibe mankhwala ndipo ndi oopsa komanso amapha mosavuta.
MAKHALIDWE A ANTHU A M’MASIKU OTSIRIZA
10. Kodi anthu masiku ano amasonyeza makhalidwe ati otchulidwa pa 2 Timoteyo 3:1-5?
10 Kuwonjezera pa kufotokoza zinthu zina zimene zikuchitika padziko lonse, Baibulo linaneneratunso kuti m’masiku otsiriza makhalidwe a anthu adzasintha kwambiri. Mtumwi Paulo anafotokoza mmene moyo udzakhalire chifukwa cha kuipa kwa makhalidwe a anthu ambiri. Iye anati: “Masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta.” (Werengani 2 Timoteyo 3:1-5.) Paulo ananena kuti anthu adzakhala
odzikonda
okonda ndalama
osamvera makolo
osakhulupirika
osakonda achibale awo
osadziletsa
oopsa
okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu
ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu koma amakana kuti mphamvu ya kudziperekako iwasinthe
11. Kodi lemba la Salimo 92:7 limafotokoza kuti n’chiyani chidzachitikire anthu oipa?
11 Kodi mmenemu ndi momwe anthu ambiri alili m’dera lanu? Sitikukayikira kuti ali choncho chifukwa kulikonse kumapezeka anthu amakhalidwe oipa. Zimenezi zikusonyeza kuti posachedwapa Mulungu awononga dziko loipali, chifukwa Baibulo limati: “Anthu oipa akamaphuka ngati msipu, ndipo anthu onse ochita zopweteka anzawo akamaphuka ngati maluwa, amatero kuti awonongeke kwamuyaya.”—Salimo 92:7.
ZINTHU ZABWINO ZIMENE ZIKUCHITIKA M’MASIKU OTSIRIZA
12, 13. Kodi ulosi woti anthu adzadziwa “zinthu zambiri zoona” wakwaniritsidwa bwanji ‘m’nthawi yamapeto’ ino?
12 Monga mmene Baibulo linafotokozera, m’masiku otsiriza ano mavuto achulukadi. Komabe pali zinthu zina zabwino zimene zikuchitika pakati pa anthu amene amalambira Yehova.
13 Buku la Danieli linaneneratu kuti anthu “adzadziwa zinthu zambiri zoona.” Koma kodi zimenezi zidzachitika liti? Zidzachitika “nthawi yamapeto.” (Danieli 12:4) Makamaka kuyambira mu 1914, Yehova anathandiza anthu ofunitsitsa kumutumikira kuti amvetse bwino mfundo za m’Baibulo. Anthu amenewa amvetsa bwino zoona zenizeni za dzina la Mulungu ndi cholinga chake, nsembe ya dipo ya Yesu Khristu, zimene zimachitika munthu akamwalira komanso za kuukitsidwa kwa akufa. Ndiponso olambira Yehova aphunzira kukhala ndi makhalidwe amene amawathandiza kukhala ndi moyo wabwino komanso kuchititsa kuti Mulungu alemekezedwe. Amvetsanso zimene Ufumu wa Mulungu udzachite pokonza zinthu padziko lapansili. Ndiyeno kodi amachita chiyani ndi zinthu zimene adziwazi? Funso limeneli likutifikitsa pa ulosi winanso umene ukukwaniritsidwa m’masiku otsiriza ano.
14. Kodi ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu yafalikira bwanji masiku ano, nanga ndi ndani amene akulalikira uthengawu?
14 Yesu Khristu anafotokoza mu ulosi wake wonena za “mapeto a nthawi ino” kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Werengani Mateyu 24:3, 14.) Uthenga wabwino wa Ufumu ukulalikidwa padziko lonse m’mayiko oposa 235 komanso m’zinenero zoposa 600. Uthenga wake ndi wonena za Ufumu wa Mulungu, zimene udzachite komanso zimene tingachite kuti tidzalandire madalitso amene Ufumuwo udzabweretse. A Mboni za Yehova omwe alipo mamiliyoni ambiri amagwira mwakhama ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Iwo amachokera “m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse.” (Chivumbulutso 7:9) A Mboni amaphunzira Baibulo ndi anthu mamiliyoni ambiri omwe amafuna kudziwa zenizeni zimene Baibulo limaphunzitsa ndipo amachita zimenezi kwaulere. Kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewu n’kochititsa chidwi kwambiri makamaka tikaganizira kuti Yesu ananeneratu kuti Akhristu oona adzadedwa ndi “anthu onse.”—Luka 21:17.
ZIMENE MUYENERA KUCHITA
15. (a) Kodi mumakhulupirira kuti tili m’masiku otsiriza, ndipo n’chifukwa chiyani? (b) Kodi n’chiyani chidzachitikire anthu amene samvera Yehova ndi amene amamumvera?
15 Popeza maulosi ambiri a m’Baibulo akukwaniritsidwa masiku ano, kodi simukuona kuti tikukhaladi m’masiku otsiriza? Yehova akadzaona kuti uthenga wabwino walalikidwa mokwanira, “mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14) Baibulo likamanena za “mapeto” limakhala likutanthauza nthawi imene Yehova adzachotse zinthu zonse zoipa padziko lapansili. Yehova adzagwiritsa ntchito Yesu komanso angelo ake amphamvu powononga anthu onse amene mwadala amachita zinthu zotsutsana naye. (2 Atesalonika 1:6-9) Satana ndi ziwanda zake sadzasocheretsanso anthu. Pambuyo pake Ufumu wa Mulungu udzabweretsa madalitso ambiri kwa anthu onse amene amagonjera ulamuliro wake wolungama.—Chivumbulutso 20:1-3; 21:3-5.
16. Popeza mapeto ayandikira, kodi muyenera kuchita chiyani?
16 Popeza mapeto a dziko la Satanali ali pafupi, tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndiyenera kuchita chiyani?’ Muyenera kupitiriza kuphunzira za Yehova ndiponso zimene amafuna kuti tizichita. (Yohane 17:3) Muziphunzira Baibulo mwakhama komanso nthawi zonse muzisonkhana ndi anthu amene amayesetsa kuchita zimene Yehova amafuna. (Werengani Aheberi 10:24, 25.) Muyenera kuyesetsa kuphunzira Baibulo kuti mumudziwe bwino Yehova Mulungu ndiponso yesetsani kusintha moyo wanu n’cholinga choti Yehova Mulungu azisangalala nanu.—Yakobo 4:8.
17. N’chifukwa chiyani kuwonongedwa kwa anthu oipa kudzakhale kodzidzimutsa kwa anthu ambiri?
17 Yesu ananeneratu kuti anthu ambiri adzanyalanyaza umboni wakuti tikukhala m’masiku otsiriza. Kuwonongedwa kwa anthu oipa kudzachitika modzidzimutsa komanso pa nthawi imene anthu samayembekezera. Chiwonongekochi chidzadzidzimutsa anthu ambiri ngati mmene amadzidzimukira kukabwera wakuba usiku. (Werengani 1 Atesalonika 5:2.) Yesu anachenjeza kuti: “Monga mmene analili masiku a Nowa, ndi mmenenso kukhalapo kwa Mwana wa munthu kudzakhalire. M’masiku amenewo chigumula chisanafike, anthu anali kudya ndi kumwa. Amuna anali kukwatira ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m’chingalawa. Anthu ananyalanyaza zimene zinali kuchitika mpaka chigumula chinafika n’kuwaseseratu onsewo. Zidzateronso ndi kukhalapo kwa Mwana wa munthu.”—Mateyu 24:37-39.
18. Kodi Yesu anapereka chenjezo lotani?
18 Choncho Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi kudya kwambiri, kumwa kwambiri, ndi nkhawa za moyo, kuti tsikulo lingadzakufikireni modzidzimutsa ngati msampha. Pakuti lidzafikira onse okhala pankhope ya dziko lonse lapansi. Chotero khalani maso ndipo muzipemphera mopembedzera nthawi zonse, kuti mudzathe kuthawa zinthu zonsezi zimene zikuyembekezeka kuchitika. Kutinso mudzathe kuima pamaso pa Mwana wa munthu.” (Luka 21:34-36) Tiyenera kumvera chenjezo la Yesu limeneli chifukwa anthu amene amasangalatsa Yehova Mulungu komanso “Mwana wa munthu,” Yesu Khristu, ndi amene adzapulumuke pa nthawi imene dziko la Satanali lizidzawonongedwa. Anthu amenewa adzakhala ndi mwayi wokhala ndi moyo mpaka kalekale m’dziko lapansi latsopano lomwe lili pafupi.—Yohane 3:16; 2 Petulo 3:13.
a Kuti muwerenge mfundo zotsimikizira kuti Mikayeli ndi dzina lina la Yesu Khristu, onani Zakumapeto, tsamba 218-219.