Mbali 3
Magwero Apadera a Nzeru Yapamwamba
1 Kodi Baibulo ncholembedwa cha nzeru yapamwamba imeneyo? Kodi lingatipatse mayankho owona a mafunso ofunika koposa a chifuno cha moyo?
2 Ndithudi nkofunika kuti tipende Baibulo. Chifukwa chimodzi nchakuti ndibuku lapadera kwambiri lomwe linalembedwapo, losiyana kwambiri ndi buku lina lililonse. Tapendani mfundo zotsatirazi.
Buku Lakale Koposa, Lofalitsidwa Kopambana
3 Baibulo ndibuku lakale koposa onse olembedwapo, mbali zake zina zinalembedwa pafupifupi zaka 3,500 zapitazo. Lakhalako kwa zaka mazana ambiri kuposa buku lina lililonse lolingaliridwa kukhala lopatulika. Loyambirira pamabuku ake 66 linalembedwa pafupifupi zaka chikwi chimodzi Buddha ndi Confucius asanakhaleko ndi pafupifupi zaka zikwi ziŵiri Muḥammad asanakhaleko.
4 Mbiri yolembedwa m’Baibulo imabwerera kumbuyo mpaka pachiyambi cha banja la anthu ndipo imafotokoza mmene tinafikira kukhalapo padziko lapansili. Imatiperekanso ngakhale ku nthaŵi yakumbuyo pamene anthu anali asanalengedwe, kutiuza zochitika zenizeni ponena za kupangidwa kwa dziko lapansi.
5 Mabuku ena achipembedzo, ndi osakhala achipembedzo, ali ndi makope oŵerengeka okha a malembo apamanja akale amene alipo. Pafupifupi makope olembedwa pamanja 11,000 a Baibulo kapena mbali zake alipo m’Chihebri ndi Chigiriki, ena a iwo ali ndi madeti osonyeza nthaŵi yoyandikana ndi nthaŵi imene analembedwa. Makopewa akhalapobe ngakhale kuti zoyesayesa zamphamvu zinachitidwa kuyesa kutsutsa Baibulo.
6 Ndiponso, Baibulo ndibuku lofalitsidwa kwambiri kuposa mabuku ena m’mbiri. Pafupifupi Mabaibulo kapena mbali zake zokwanira mamiliyoni zikwi zitatu afalitsidwa m’zinenero pafupifupi zikwi ziŵiri. Kukunenedwa kuti 98 peresenti ya banja la anthu ali ndi Baibulo m’chinenero chawo. Palibe buku lina limene limayesa kufanana nalo m’kufalitsidwa kwakeko.
7 Kuwonjezerapo, palibe buku lina lakale limene limalingana ndi Baibulo m’kulondola kwake. Asayansi, olemba mbiri, ofukula za m’mabwinja, openda malo, akatswiri a zinenero, ndi ena akupitirizabe kutsimikizira kulondola kwa mbiri ya m’Baibulo.
Kulondola Kwake m’za Sayansi
8 Mwachitsanzo, ngakhale kuti Baibulo silinalembedwe monga buku lophunzitsa sayansi, limagwirizana ndi sayansi yowona pamene linena nkhani zasayansi. Koma mabuku ena akale olingaliridwa kukhala opatulika ali ndi nthanthi za sayansi, siolondola, ndipo ngabodza. Tawonani zitsanzo zinayi zokha mwa zambiri za kulondola kwa Baibulo m’za sayansi:
9 Mmene dziko lapansi limalenjekekera m’mlengalenga. Nthaŵi zamakedzana pamene Baibulo linali kulembedwa, panali malingaliro ambiri onena za mmene dziko lapansi linalenjekekera m’mlengalenga. Ena anakhulupirira kuti dziko lapansi linachilikizidwa ndi njovu zinayi zoimirira pa kamba wamkulu wa m’madzi. Aristotle, wanthanthi ndi wasayansi Wachigiriki wa m’zaka za zana lachinayi B.C.E., anaphunzitsa kuti dziko lapansi silingakhoze kulenjekeka m’mlengalenga. M’malomwake, anaphunzitsa kuti zinthu zakuthambo zinamamatizidwa pa mbulunga zolimba zowonekera ngati galasi, ndipo iliyonse ya mbulungazo inali mkati mwa inzake. Dziko lapansi linalingaliridwa kukhala mbulunga yamkati kwambiri, ndipo mbulunga yakunja ndiyo inamamatiridwa ku nyenyezi.
10 Komabe, m’malo mosonyeza malingaliro opeka, osagwirizana ndi sayansi amene analipo nthaŵi imene linali kulembedwa, Baibulo linanena mosavuta (pafupifupi m’chaka cha 1473 B.C.E.) kuti: “ [Mulungu] alenjeka dziko pachabe.” (Yobu 26:7) Mu Chihebri choyambirira, liwu lakuti “pachabe” logwiritsiridwa ntchito panopo limatanthauza “popanda kanthu,” ndipo ndipokhapa pamene limapezeka m’Baibulo. Chithunzi chimene limapereka cha dziko lapansi lozunguliridwa ndi mlengalenga wopanda kanthu chimavomerezedwa ndi akatswiri kukhala chidziŵitso chodabwitsa cha m’nthaŵi yake. Buku lakuti Theological Wordbook of the Old Testament limati: “Modabwitsa kwambiri lemba la Yobu 26:7 limasonyeza dziko lodziŵika lapanthaŵiyo kukhala lolenjekeka m’mlengalenga, motero kuneneratu zodzatulukiridwa ndi sayansi mtsogolo.”
11 Ndemanga yolondola ya Baibulo inanenedwa zaka zoposa 1,100 Aristotle asanakhaleko. Komabe, malingaliro a Aristotle anapitiriza kuphunzitsidwa monga zenizeni pafupifupi kwa zaka 2,000 iye atafa! Pomalizira pake, mu 1687 C.E., Bwana Isaac Newton anafalitsa zopeza zake zakuti dziko lapansi linalenjekedwa m’mlengalenga mogwirizana ndi zinthu zina zakuthambo mwakukokana, kutanthauza mphamvu yokoka. Koma pamenepo panali pafupifupi zaka 3,200 Baibulo litanena kale momvekera bwino kuti dziko lapansi lilenjekeka “pachabe.”
12 Inde, pafupifupi zaka 3,500 zapitazo, Baibulo molondola linanena kuti dziko lapansi lilibe chochilikiza chowoneka, mfundo imene imagwirizana ndi malamulo amene azindikiridwa posachedwapa a mphamvu yokoka ndi kuyenda. Katswiri wina anati: “Funso lakuti kodi Yobu anadziŵa motani chowonadi nlovuta kuyankhidwa ndi amene samavomereza kuti Malemba Oyera ngouziridwa.”
13 Mpangidwe wa dziko lapansi. The Encyclopedia Americana imati: “Chithunzi chakale kwambiri chimene anthu anali nacho cha dziko lapansi chinali chakuti dziko lapansi linali malo olimba athyathyathya, okhala pakati penipeni pa chilengedwe. . . . Lingaliro lakuti dziko lapansi nlobulungira silinavomerezedwe mofala kufikira nyengo ya kuyambitsidwanso kwa maluso yotchedwa Renaissance.” Amalinyero ofufuza malo oyambirira anawopa kuti angagwere kuphedi kwa dziko lapansi lathyathyathyalo. Ndiyeno kupangidwa kwa chiwiya chotchedwa compass ndi zipangizo zina kunatheketsa kuyenda maulendo apanyanja aatali. Buku lina la nazonse likufotokoza kuti “maulendo otumba malo” ameneŵa, “anasonyeza kuti dziko nlobulungira, osati lathyathyathya monga momwe anthu ambiri anakhulupirira.”
14 Komabe, kale kwambiri maulendo amenewo asanapangidwe, pafupifupi zaka 2,700 zapitazo, Baibulo linati: “Pali Uyo amene amakhala pamwamba pa mbulunga ya dziko lapansi.” (Yesaya 40:22, NW) Liwu Lachihebri lotembenuzidwa panopo kuti “mbulunga” lingatanthauzenso “kukwetera,” monga momwe mabuku amaumboni ambiri amasonyezera. Chotero, matembenuzidwe ena a Baibulo amati, “mbulunga ya dziko lapansi” (Douay Version) ndi, “dziko lapansi lozungulira.”—Moffatt.
15 Chotero, Baibulo silinayambukiridwe ndi malingaliro osagwirizana ndi sayansi amene anali otchuka a panthaŵiyo ponena za chochilikiza dziko lapansi ndi mpangidwe wake. Chifukwa chake nchokhweka: Woyambitsa Baibulo ndiye Mpangi wa chilengedwe. Iye analenga dziko lapansi, chotero ayenera kudziŵa pamene linalenjekeka ndi mpangidwe wake. Chifukwa chake, pamene anauzira Baibulo, anatsimikizira kuti malingaliro osagwirizana ndi sayansi sanaphatikizidwemo, mosasamala kanthu kuti ndimalingaliro ochuluka motani amene anakhulupiriridwa ndi anthu ena panthaŵiyo.
16 Kapangidwe ka zinthu zamoyo. Lemba la Genesis 2:7 limati: “Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi.” The World Book Encyclopedia imati: “Zinthu zonse za makemikolo zimene zimapanga zinthu zamoyo zimapezekanso m’zinthu zopanda moyo.” Chotero makemikolo onse amene amapanga zinthu zamoyo, kuphatikizapo munthu, amapezekanso m’dziko lapansi lenilenilo. Zimenezi zimagwirizana ndi ndemanga ya Baibulo imene imatchula zinthu zimene Mulungu anagwiritsira ntchito polenga anthu ndi zinthu zina zonse zamoyo.
17 “Monga mwa mitundu yawo.” Baibulo limanena kuti Mulungu analenga anthu aŵiri oyamba ndi kuti anthu ena onse anachokera kwa iwo. (Genesis 1:26-28; 3:20) Limanena kuti zinthu zamoyo zina, monga ngati nsomba, mbalame, ndi nyama zoyamwitsa, zinachita zofananazo, zinakhalako “monga mwa mitundu yawo.” (Genesis 1:11, 12, 21, 24, 25) Zimenezi nzomwe asayansi apeza m’chilengedwe chachibadwa, kuti chinthu chamoyo chilichonse chimabadwa kwa kholo la mtundu wake. Kusasiyapo chilichonse. Pankhani imeneyi katswiri wa physics Raymo anati: “Moyo umapanga moyo unzake; zimachitika nthaŵi zonse m’selo lililonse. Koma kodi chopanda moyo chinapanga motani moyo? Limenelo nlimodzi la mafunso aakulu osayankhidwa m’sayansi ya zamoyo, ndipo pakali pano akatswiri a sayansi ya zamoyo amapereka mayankho ongopeka. Amati mwanjira inayake zinthu zopanda moyo zinadzilinganiza kupanga chinthu chamoyo. . . . Ndiiko komwe, mlembi wa Genesis angakhale analongosola molondola nkhaniyo.”
Kulondola kwa Mbiri
18 Baibulo lili ndi mbiri yamakedzana yolondola kwambiri kuposa buku lina lililonse limene lilipo. Buku lakuti A Lawyer Examines the Bible limagogomezera kulondola kwake kwa mbiri mwanjira iyi: “Pamene kuli kwakuti nkhani zolembedwa, nthano zoperekedwa ndiponso umboni wonama zimakhala zaluso kugwirizanitsa zochitika zosimbidwazo ndi malo akutali ndi nthaŵi zosadziŵika, mwakutero kuswa malamulo oyambirira amene ife maloya timaphunzira akutsatira bwino mlandu, akuti ‘mlandu uyenera kutchula nthaŵi ndi malo,’ nkhani za Baibulo zimatchula molondola bwino lomwe deti ndi malo a zinthu zonenedwazo.”
19 The New Bible Dictionary ikupereka ndemanga yakuti: “ [Amene analemba Machitidwe] anapereka nkhani yake mogwirizana ndi mbiri yapanthaŵiyo; nkhani yake njodzaza ndi maumboni a olamulira amizinda, akazembe azigawo, mafumu olamulira milaga, ndi zina zotero, ndipo nthaŵi zonse maumboni ameneŵa amatsimikizira kukhala oyenerera malo ndi nthaŵi yotchulidwayo.”
20 Polemba mu The Union Bible Companion, S. Austin Allibone anati: “Bwana Isaac Newton . . . analinso wotchuka kukhala wosuliza zolembedwa zamakedzana, ndipo anapenda mosamalitsa Malemba Oyera. Kodi ananenanji pankhaniyi? Iye anati, ‘Ndikupeza umboni wochuluka wodalirika m’Chipangano Chatsopano kuposa m’mbiri [yakudziko] iliyonse.’ Dr. Johnson akuti tili ndi umboni wochuluka wakuti Yesu Kristu anafera pa Kalivali, monga momwe Mauthenga Abwino amanenera kuposa wakuti Julius Caesar anafera ku Capitol. Tilidi ndi umboni wochuluka kwambiri.”
21 Buku limodzimodzili limawonjezera kuti: “Funsani aliyense amene amanena kuti amakayikira chowonadi cha mbiri ya Uthenga Wabwino kuti ali ndi chifukwa chotani chokhulupirira kuti Caesar anafera ku Capitol, kapena kuti Mfumu Charlemagne anaikidwa kukhala Mfumu ya chigawo cha Kumadzulo cha Roma ndi Papa Leo III. mu 800? . . . Kodi mumadziŵa bwanji kuti munthu wonga Charles I. [wa ku Mangalande] anakhalako, ndi kuti anadulidwa mutu, ndi kuti Oliver Cromwell anakhala wolamulira amene anamuloŵa m’malo? . . . Bwana Isaac Newton amanenedwa kukhala anatulukira lamulo la mphamvu yokoka . . . Timakhulupirira zonenedwa zonsezo za amuna ameneŵa; ndi chifukwa chakuti tili ndi umboni wa m’mbiri wa kuwona kwake. . . . Ngati ena akanabe kukhulupirira, pambuyo popatsidwa umboni wonga umenewu, timawaleka kukhala anthu ouma khosi mwautsiru kapena mbuli zopanda pake.”
22 Ndiyeno buku limeneli likumaliza kuti: “Pamenepo, kodi tinene chiyani, za awo amene, mosasamala kanthu za umboni wochuluka umene ulipo tsopano wonena za kudalirika kwa Malemba Oyera, amanenabe kuti sakukhutiritsidwa? . . . Ndithudi tili ndi chifukwa chonenera kuti mtima wawo ndiwo wolakwa osati maganizo;—kuti samafuna kukhulupirira zinthu zimene zimawachititsa manyazi, ndi kuwakakamiza kukhala ndi miyoyo yosiyana.”
Kugwirizana kwa Nkhani Zake ndi Kuwona Kwake
23 Tayerekezerani kuti buku linayamba kulembedwa m’nthaŵi ya ufumu wa Roma, kupitiriza mpaka m’Nyengo Zapakati, ndi kumalizidwa m’zaka za zana la 20 zino, likumalembedwa ndi alembi ambiri osiyana. Kodi mukanayembekezera chotulukapo chotani ngati ntchito za olembawo zinali zosiyanasiyana monga asilikali, mafumu, ansembe, asodzi, abusa, ndi asing’anga? Kodi mukanayembekeza bukulo kukhala logwirizana ndi lomvekera bwino? ‘Kutalitali!’ mungayankhe motero. Eya, Baibulo linalembedwa pansi pa mikhalidwe imeneyi. Komabe, ilo lonse nlogwirizana, osati kokha pa mfundo zazikulu koma m’tsatanetsatane wochepetsetsa.
24 Baibulo ndimpukutu wa mabuku 66 wolembedwa pa nyengo ya zaka 1,600 ndi alembi 40 osiyanasiyana, kuyambira mu 1513 B.C.E. ndi kumalizira mu 98 C.E. Olembawo anali ndi ntchito zosiyanasiyana, ndipo ambiri sanadziŵane nkomwe. Komabe, buku lomwe linatulukapo limatsatira mutu waukulu, wogwirizana, ngati kuti linalembedwa ndi munthu mmodzi. Ndipo mosemphana ndi zimene ena amakhulupirira, Baibulo silinalembedwe ndi anthu a Kumadzulo, koma linalembedwa ndi anthu a Kum’maŵa.
25 Pamene kuli kwakuti olemba ambiri amakedzana anasimba za zipambano ndi maubwino awo okha, olemba Baibulo anavomereza poyera zophophonya zawo, limodzinso ndi zolakwa za mafumu ndi atsogoleri awo. Malemba a Numeri 20:1-13 ndi Deuteronomo 32:50-52 amasimba zolakwa za Mose, ndipo ndiye analemba mabuku amenewo. Malemba a Yona 1:1-3 ndi 4:1 amandandalitsa zolakwa za Yona, amene analemba nkhani zimenezo. Malemba a Mateyu 17:18-20; 18:1-6; 20:20-28; ndi 26:56 amasimba za mikhalidwe yoipa imene inasonyezedwa ndi ophunzira a Yesu. Chotero, kuwona mtima ndi kunena zowona kwa olemba Baibulo kumachilikiza kudzinenera kwawo kwakuti anauziridwa ndi Mulungu.
Mbali Yake Yapadera Kwambiri
26 Baibulo lenilenilo limavumbula chifukwa chake lili lolondola kwambiri pankhani za sayansi, mbiri, ndi zina ndi chifukwa chake zili zogwirizana ndi zowona. Limasonyeza kuti Wokhalako Wamkulu, Mulungu wamphamvuyonse, Mlengi amene anapanga chilengedwe chonse, ndiye Woyambitsa Baibulo. Iye anangogwiritsira ntchito anthu kulemba Baibulo monga alembi ake, akumawasonkhezera mwamphamvu ndi mphamvu yake yogwira ntchito kulemba zimene anawauzira.
27 M’Baibulo, mtumwi Paulo amati: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.” Ndipo mtumwi Paulo ananenanso kuti: “Pakulandira mawu a uthenga wa Mulungu, simunawalandira monga mawu a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mawu a Mulungu.”—2 Timoteo 3:16, 17; 1 Atesalonika 2:13.
28 Motero, Baibulo limachokera m’maganizo a Woyambitsa mmodzi—Mulungu. Ndipo ndi mphamvu yake yochititsa mantha, kunali kosavuta kwa iye kutsimikizira kuti chowonadi cha zimene zinalembedwa chinasungidwa kufikira m’tsiku lathu. Ponena za zimenezi mkulu wotsogolera wa malembo apamanja a Baibulo, Bwana Frederic Kenyon, ananena mu 1940 kuti: “Maziko otsirizira a chikayikiro chilichonse chakuti Malemba afika kwa ife monga momwe iwo analembedwera kwenikweni tsopano achotsedwa.”
29 Anthu ali ndiluso lakutumiza kudziko lapansi mauthenga a wailesi ndi wailesi yakanema kuchokera pamtunda wa makilomita zikwi zambiri m’mlengalenga, ngakhale kuchokera ku mwezi. Zombo zopita m’mlengalenga zatumiza kudziko lapansi chidziŵitso ndi zithunzithunzi zochokera ku mapulaneti amene ali pamtunda wa makilomita mamiliyoni mazana ambiri. Ndithudi Mlengi wa munthu, Mlengi wa mphamvu ya mawu a wailesi, angakhoze kuchita zoposapo. Ndithudi, kunali kosavuta kwa iye kugwiritsira ntchito mphamvu yake yaikulu kutumiza mawu ndi zithunzithunzi m’maganizo mwa amene anawasankha kuti alembe Baibulo.
30 Ndiponso, pali zinthu zambiri zokhudza dziko lapansi ndi moyo umene uli padziko zimene zimapereka umboni wa kukondwera kwa Mulungu ndi anthu. Chifukwa chake, nkomvekera bwino kuti amafuna kuthandiza anthu kudziŵa amene iye ali ndi chifuno chake kwa iwo mwakufotokoza zinthu zimenezi momvekera bwino m’buku—cholembedwa chachikhalire.
31 Talingaliraninso kupambana kwa buku lolembedwa ndi Mulungu, moyerekezera ndi chidziŵitso choperekedwa ndi anthu mwa mawu apakamwa. Mawu apakamwa sangadaliridwe, popeza kuti anthu angafupikitse uthengawo, ndipo m’kupita kwa nthaŵi, tanthauzo lake lingapotozedwe. Iwo akapereka chidziŵitso cholankhulidwacho mogwirizana ndi lingaliro lawo. Koma cholembedwa chachikhalire chouziridwa ndi Mulungu, sichingakhale ndi zolakwa. Ndiponso, buku likhoza kusindikizidwanso ndi kutembenuzidwa kotero kuti anthu oŵerenga zinenero zosiyanasiyana akhoze kupindula. Chotero kodi sikwanzeru kuti Mlengi wathu anagwiritsira ntchito njira imeneyo kupereka chidziŵitso? Ndithudi, nkwanzeru kwambiri, chifukwa Mlengiyo amanena kuti zimenezi nzomwe anachita.
Ulosi Wokwaniritsidwa
32 Kuwonjezerapo, Baibulo limasonyeza umboni wa kuuziridwa kwaumulungu mwanjira yapadera kwambiri: Ndibuku la maulosi amene anakwaniritsidwa ndipo akupitiriza kukwaniritsidwa mosalakwika.
33 Mwachitsanzo, kuwonongedwa kwa Turo wamakedzana, kugwa kwa Babulo, kumangidwanso kwa Yerusalemu, ndi kubuka ndi kugwa kwa mafumu a Amedi ndi Perisiya ndi Girisi zinanenedweratu mwatsatanetsatane m’Baibulo. Maulosiwo anali olondola kwambiri kotero kuti osuliza anayesayesa, koma mosaphula kanthu, kunena kuti analembedwa zochitikazo zitachitika kale.—Yesaya 13:17-19; 44:27–45:1; Ezekieli 26:3-6; Danieli 8:1-7, 20-22.
34 Maulosi amene Yesu anapereka onena za chiwonongeko cha Yerusalemu mu 70 C.E. anakwaniritsidwa molondola. (Luka 19:41-44; 21:20, 21) Ndipo maulosi onena za “masiku otsiriza” amene anaperekedwa ndi Yesu ndi mtumwi Paulo akukwaniritsidwa mwatsatanetsatane m’nthaŵi yathu ino.—2 Timoteo 3:1-5, 13; Mateyu 24; Marko 13; Luka 21.
35 Palibe maganizo a munthu, mosasamala kanthu kuti ngwaluntha motani, amene anganeneretu molondola chotero zochitika za mtsogolo. Maganizo a Mlengi wa chilengedwe wamphamvu zonse ndi nzeru zonse okha ndiwo angakhoze, monga momwe timaŵerengera pa lemba la 2 Petro 1:20, 21 kuti: “Palibe chinenero cha lembo chitanthauzidwa pa chokha, pakuti kale lonse chinenero sichinadza ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi mzimu woyera, analankhula.”
Limapereka Yankho
36 Chotero, pali njira zambiri zimene Baibulo limaperekera umboni wakuti lili Mawu ouziridwa a Wokhalako Wamkulu. Motero, limatiuza chifukwa chake anthu ali padziko lapansi, chifukwa chake pali kuvutika kwambiri, kumene tikumka, ndi mmene mikhalidwe idzasinthira kukhala yabwinopo. Limatiuzanso kuti pali Mulungu wamkulu amene analenga anthu ndi dziko lapansili ndi chifuno ndi kuti chifuno chake chidzakwaniritsidwa. (Yesaya 14:24) Baibulo limatiuzanso chimene chili chipembedzo chowona ndi mmene tingachipezere. Chifukwa chake, ndilo magwero okha a nzeru yapamwamba amene angatiuze chowonadi pa mafunso onse ofunika a moyo.—Salmo 146:3; Miyambo 3:5; Yesaya 2:2-4.
37 Pamene kuli kwakuti pali umboni wochuluka wa kudalirika ndi kuwona kwa Baibulo, kodi onse amene amanena kuti amalivomereza amatsatira ziphunzitso zake? Mwachitsanzo, talingalirani za maiko amene amanena kuti Ngachikristu, kutanthauza Dziko Lachikristu. Iwo akhala ndi Baibulo kwa zaka mazana ambiri. Koma kodi kulingalira kwawo ndi zochita zawo zimasonyezadi nzeru yapamwamba ya Mulungu?
[Study Questions]
1, 2. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupenda Baibulo?
3, 4. Kodi Baibulo lakhalako kwa utali wotani?
5. Kodi ndimalembo apamanja akale angati a Baibulo amene alipo, poyerekezera ndi zolembedwa zina zamakedzana zakudziko?
6. Kodi Baibulo lafalitsidwa mofala chotani?
7. Kodi tinganenenji za kulondola kwa Baibulo?
8. Kodi Baibulo nlolondola motani pankhani za sayansi?
9, 10. M’malo mosonyeza malingaliro osagwirizana ndi sayansi a m’nthaŵi yake, kodi Baibulo linanenanji ponena za chochilikiza dziko lapansi?
11, 12. Kodi ndiliti pamene anthu anamvetsetsa chowonadi cha lemba la Yobu 26:7?
13. Kodi zaka mazana apitawo anthu analingalira motani za mpangidwe wa dziko lapansi, koma nchiyani chinasintha malingaliro awo?
14. Kodi Baibulo linafotokoza motani mpangidwe wa dziko lapansi, ndipo liti?
15. Kodi nchifukwa ninji Baibulo silinayambukiridwe ndi malingaliro osagwirizana ndi sayansi onena za dziko lapansi?
16. Kodi kapangidwe ka zinthu zamoyo kamagwirizana motani ndi ndemanga ya Baibulo?
17. Kodi chowonadi nchiti ponena za mmene zinthu zamoyo zinakhalirako?
18. Kodi loya akunenanji za kulondola kwa mbiri ya m’Baibulo?
19. Kodi buku lina lamaumboni limanena ndemanga yotani pa maumboni a mbiri ya Baibulo?
20, 21. Kodi katswiri wa Baibulo ananenanji ponena za mbiri ya Baibulo?
22. Kodi nchifukwa ninji ena amakana kuvomereza kuti Baibulo nlodalirika?
23, 24. Kodi nchifukwa ninji kugwirizana kwa nkhani za Baibulo kuli kodabwitsa?
25. Kodi kuwona mtima ndi kunena zowona kwa Baibulo kumachilikiza ndemanga yotani ya olemba Baibulo?
26, 27. Kodi nchifukwa ninji Baibulo lili lolondola kwambiri m’nkhani zasayansi ndi nkhani zina?
28. Pamenepo, kodi Baibulo linachokera kuti?
29. Kodi kukhoza kwa Mulungu kwa kulankhulana kungafaniziridwe motani?
30. Kodi Mulungu amafuna kuti anthu adziŵe chifuno chake kwa iwo?
31. Kodi nchifukwa ninji uthenga wolembedwa mouziridwa uli wapamwamba kuposa wopatsiridwa mwa pakamwa?
32-34. Kodi Baibulo lili ndi chiyani chimene buku lina lililonse lilibe?
35. Kodi nchifukwa ninji ulosi wa m’Baibulo ungachokere kwa Mlengi yekha?
36. Kodi Baibulo limatiuzanji?
37. Kodi tiyenera kufunsanji ponena za Dziko Lachikristu?
[Pictures on page 11]
Bwana Isaac Newton anakhulupirira kuti dziko lapansi linachilikizidwa m’mlengalenga mogwirizana ndi zinthu zina zakuthambo mwa mphamvu yokoka
Chithunzi chimene Baibulo limapereka cha dziko lapansi lozunguliridwa ndi mlengalenga wopanda kanthu chimawonedwa ndi akatswiri kukhala chidziŵitso chodabwitsa cha m’nthaŵi yake
[Picture on page 12]
Amalinyero ofufuza malo oyambirira anawopa kuti angagwere kuphedi kwa dziko lapansi lathyathyathyalo
[Picture on page 13]
Pali umboni wochuluka wakuti Yesu Kristu anakhalako kuposa umene ulipo wakuti Julius Caesar, Mfumu Charlemagne, Oliver Cromwell, kapena Papa Leo III anakhalako
[Picture on page 15]
Maulosi amene Yesu anapereka onena za kuwonongedwa kwa Yerusalemu mu 70 C.E. anatsimikiziridwa ndi zolembedwa pa chipata cha Arch of Titus mu Roma