Mutu 15
Mverani Uphungu, Landirani Mwambo
“TIMAKHUMUDWA tonse pa zinthu zambiri,” limatero Baibulo pa Yakobo 3:2. Tingathe kukumbukira nthaŵi zambiri pamene talephera kukhala ngati munthu amene Mawu a Mulungu amafuna. Ndipo tikuvomereza kuti Baibulo limanena zoona likamatiuza kuti: “Tamvera uphungu, nulandire mwambo, kuti ukhale wanzeru pa chimaliziro chako.” (Miyambo 19:20) Mosakayika, ife tasintha kale moyo wathu kuti ugwirizane ndi ziphunzitso za Baibulo. Koma kodi timatani Mkristu mnzathu akatipatsa uphungu pankhani inayake?
2 Ena amati akawapatsa uphungu amayesa kupereka zifukwa zolungamitsa zimene achita, kapena amayesa kuchepetsa cholakwacho, kayanso kuloza ena chala. Koma njira yabwino ndiyo kumvera uphunguwo ndi kuutsatira. (Ahebri 12:11) Inde, munthu safunika kuyembekeza ena kuchita zinthu mwangwiro. Safunikanso kumangopereka uphungu nthaŵi zonse pa zinthu zazing’onong’ono kapenanso pankhani zimene Baibulo limasiyira munthu kuti adzisankhire. Mwinanso wopatsa mnzake uphunguyo sayang’ana mbali zonse, ndipo ena angamutchulire zimenezo mwaulemu. Koma m’nkhani ino, tiyeni tinene kuti munthu wapatsidwa uphungu kapena mwambo woyenera kuchokera m’Baibulo. Kodi iye ayenera kutani?
Zitsanzo Zotichenjeza
3 Mawu a Mulungu amasimba nkhani za anthu enieni amene analandira uphungu wofunikira. Nthaŵi zina anapatsidwa uphungu ndi chilango chomwe. Munthu wina amene zimenezi zinam’chitikira ndi Mfumu Sauli ya Israyeli. Iye sanamvere Yehova pankhani yokhudza mtundu wa Aamaleki. Aamaleki anatsutsa atumiki a Mulungu, ndipo Yehova anapereka chiweruzo choti Aamaleki aphedwe ndi zoweta zawo zonse. Koma Mfumu Sauli sinaphe mfumu ya Aamaleki ndi zoweta zina zabwino.—1 Samueli 15:1-11.
4 Yehova anatuma mneneri Samueli kuti akadzudzule Sauli. Kodi Sauli anachitanji? Analimbikira kunena kuti anagonjetsadi Aamaleki koma kungoti anasankha kusunga mfumu yawo yamoyo. Komatu zimenezo zinasemphana ndi lamulo la Yehova. (1 Samueli 15:20) Sauli anayesa kuloza chala anthu pomati iye anasunga nyamazo chifukwa cha anthuwo. Anati: “Ndinaopa anthuwo, ndi kumvera mawu awo.” (1 Samueli 15:24) Zikuoneka kuti kunyada kunam’kulira, mpaka anauza Samueli kuti am’lemekeze pamaso pa anthu. (1 Samueli 15:30) M’kupita kwa nthaŵi, Yehova anakana zoti Sauli akhalebe mfumu.—1 Samueli 16:1.
5 Mfumu Uziya ya Yuda ‘inalakwira Yehova Mulungu wake; popeza inaloŵa m’Kachisi wa Yehova kufukiza.’ (2 Mbiri 26:16) Koma malinga ndi lamulo, ndi ansembe okha amene anayenera kufukiza nsembe. Pamene mkulu wa ansembe anayesa kuletsa Uziya, mfumuyo inakwiya. Ndiye chinachitika n’chiyani? Baibulo limati: “Khate linabuka pamphumi pake . . . pakuti Yehova adam’kantha. Ndipo mfumu Uziya anali wakhate mpaka tsiku la imfa yake.”—2 Mbiri 26:19-21.
6 Kodi n’chifukwa chiyani onse aŵiri Sauli ndi Uziya zinawavuta kulandira uphungu? Vuto lalikulu linali kunyada. Aliyense anali kuganiza modzikweza kwambiri. Anthu ambiri amaloŵa m’mavuto chifukwa cha khalidwe limeneli. Amachita ngati kuti akavomereza uphungu ndiye kuti ndi opereŵera penapake kapena kuti adziwonongera mbiri yawo. Koma munthu wonyada ndi wopereŵerabe. Kunyada kumasokoneza maganizo ake kotero kuti amayamba kukana thandizo limene Yehova akupereka mwa Mawu ake ndi gulu lake. N’chifukwa chake Yehova akutichenjeza kuti: “Kunyada kutsogolera kuwonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kupunthwa.”—Miyambo 16:18; Aroma 12:3.
Kulandira Uphungu
7 Malemba alinso ndi zitsanzo zina za anthu amene analandira uphungu, ndipo tingaphunzirepo kanthu. Taganizani za Mose, amene apongozi ake anamupatsa uphungu wokhudza mmene akanachitira ndi ntchito yake yaikulu. Mose anawamvera iwo nagwiritsa ntchito uphunguwo nthaŵi yomweyo. (Eksodo 18:13-24) N’chifukwa chiyani Mose analandira uphungu ngakhale kuti anali ndi ulamuliro waukulu? Chifukwa n’chakuti anali wodzichepetsa. ‘Mose anali wofatsa woposa anthu onse a padziko lapansi.’ (Numeri 12:3) Kodi kufatsa n’kofunika bwanji? Zefaniya 2:3 amasonyeza kuti kumapatsa moyo.
8 Mfumu Davide anachita chigololo ndi Bateseba ndipo anayesa kubisa tchimo lakelo mwa kuphetsa Uriya mwamuna wa Batesebayo. Yehova anatumiza mneneri Natani kukadzudzula Davide. Iye anali wolapa ndipo anavomera pomwepo kuti: ‘Ndachimwira Yehova.’ (2 Samueli 12:13) Ngakhale kuti Mulungu anavomereza kulapako, Davide anavutikabe chifukwa cha machimo akewo. Yehova anamuuza kuti lupanga “silidzachoka pa nyumba [yake],” akazi ake adzapatsidwa kwa “mnansi [wake],” ndi kuti mwana wake wobadwa m’chigololoyo “adzafa ndithu.”—2 Samueli 12:10, 11, 14.
9 Mfumu Davide anadziŵa kuti kumvera uphungu wabwino kuli ndi phindu lake. Nthaŵi ina, anayamika Mulungu chifukwa cha munthu amene anamupatsa uphungu. (1 Samueli 25:32-35) Kodi ife ndi mmene tilili? Ngati tili otero, sitidzanena ndi kuchita zinthu zambiri zimene tingadzachite nazo chisoni. Nanga bwanji tikachita zinazake ndipo n’kupatsidwa uphungu kapena kulangidwa kumene? Tisaiwale kuti ndiwo umboni wakuti Yehova akutikonda, ndipo akufuna kuti tikakhale ndi moyo wabwino kosatha.—Miyambo 3:11, 12; 4:13.
Makhalidwe Apamwamba Ofunika Kukhala Nawo
10 Kuti tikhale mabwenzi abwino a Yehova ndi abale athu achikristu, tifunika kukhala ndi makhalidwe enaake. Yesu anatchula khalidwe lina pamene anaika kamwana pakati pa ophunzira ake nati: “Ngati simutembenuka, nimukhala monga tianato, simudzaloŵa konse mu Ufumu wa Kumwamba. Chifukwa chake yense amene adzichepetsa yekha monga kamwana aka, yemweyo ali wopambana mu Ufumu wa Kumwamba.” (Mateyu 18:3, 4) Ophunzira a Yesu anafunika kukhala odzichepetsa, pajatu anali atakanganapo zoti wamkulu ndani.—Luka 22:24-27.
11 Mtumwi Petro analemba kuti: “Nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.” (1 Petro 5:5) Timadziŵa kuti tifunika kudzichepetsa pamaso pa Mulungu, koma lembali likusonyeza kuti tifunikanso kudzichepetsa kwa okhulupirira anzathu. Tikatero, sitidzaipidwa ena akatipatsako nzeru pankhani inayake. M’malo mwake tidzaphunzira kwa iwo.—Miyambo 12:15.
12 Khalidwe lina logwirizana kwambiri ndi kudzichepetsa ndilo kuganizira ubwino wa ena. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Munthu asafune zake za iye yekha, koma za mnzake. . . . Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu. Khalani osakhumudwitsa, kapena Ayuda, kapena Ahelene, kapena Mpingo wa Mulungu.” (1 Akorinto 10:24-33) Paulo sananene kuti tisiye zonse zimene timakonda, koma akutilimbikitsa kusachita chilichonse chimene chingalimbitse wina mtima kuchita zimene chikumbumtima chake chikumuuza kuti n’zolakwika.
13 Kodi mumaika ubwino wa ena patsogolo m’malo mwa zokonda zanu? Tonsefe tifunika kuphunzira kuchita zimenezo. Tingachite zimenezi m’njira zambiri. Mwachitsanzo, titenge nkhani ya kavalidwe ndi kudzikongoletsa. Zinthu zimenezi zimayendera makonda a munthu malinga ndi malangizo a m’Malemba onena za kuvala mwaulemu, mwaudongo, ndi mwaukhondo. Ndiye tinene kuti mwadziŵa kuti chifukwa cha chikhalidwe cha anthu kwanuko, kavalidwe ndi kudzikongoletsa kwanu zikulepheretsa ena kumva uthenga wa Ufumu, kodi mungasinthe? Kunena zoona, kuthandiza wina kupeza moyo wosatha ndi kofunika kwambiri kuposa kusangalatsa mtima wanu.
14 Yesu anapereka chitsanzo pankhani yodzichepetsa ndi kuganizira ena, mpaka anasambitsa mapazi a ophunzira ake. (Yohane 13:12-15) Za iye, Mawu a Mulungu amati: “Mukhale nawo mtima m’kati mwanu umene unalinso mwa Kristu Yesu, ameneyo, pokhala nawo maonekedwe a Mulungu, sanachiyesa cholanda kukhala wofana ndi Mulungu, koma anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe a kapolo, nakhala m’mafanizidwe a anthu; ndipo popezedwa m’maonekedwe ngati munthu, anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa.”—Afilipi 2:5-8; Aroma 15:2, 3.
Musakane Mwambo wa Yehova
15 Popeza ndife ochimwa, tifunika kusintha maganizo ndi khalidwe lathu kuti tionetse umunthu wonga wa Mulungu wathu. Tifunika kuvala ‘munthu watsopano.’ (Akolose 3:5-14) Uphungu ndi mwambo zimatithandiza kuzindikira mbali zimene tifunika kusintha ndiponso kudziŵa mmene tingasinthire. Gwero lalikulu la malangizo amene timafunikira ndi Baibulo basi. (2 Timoteo 3:16, 17) Mabuku ofotokozera Baibulo ndi misonkhano zimene gulu la Yehova limakonza zimatithandiza kuchita zimene Mawu a Mulungu amanena. Ngakhale ngati uphunguwo tinaumvapo kale, kodi timazindikira kuti n’ngofunikabe n’kuyesa kuwongolera?
16 Chifukwa chakuti Yehova amatikonda, amatithandiza pa mavuto athu. Anthu mamiliyoni ambiri athandizidwa ndi maphunziro a Baibulo apanyumba. Makolo amapereka uphungu ndi mwambo kwa ana awo pofuna kuwathandiza kupeŵa khalidwe limene lingawadzetsere mavuto. (Miyambo 6:20-23) Mumpingo, ena nthaŵi zambiri amapempha uphungu ndi nzeru kwa atumiki odziŵa zambiri kuti apititse patsogolo ntchito yawo ya m’munda. Nthaŵi zina akulu amapemphana uphungu kapena amapempha kwa ena ozoloŵera utumiki. Amene ali ndi ziyeneretso zauzimu amagwiritsa ntchito Baibulo kuthandiza amene akufuna thandizo, ndipo amatero ndi mzimu wachifatso. Popereka uphungu, kumbukirani ‘kudzipenyerera nokha, mungayesedwe nanunso.’ (Agalatiya 6:1, 2) Inde, tonsefe tifunika uphungu ndi mwambo kuti tilambire Mulungu woona yekha mogwirizana.
Bwerezani Zimene Mwakambirana
• Kodi Yehova mwachikondi amatithandiza bwanji kuona mbali zimene ife patokha tifunikira kusintha?
• N’chifukwa chiyani ambiri zimawavuta kulandira uphungu, nanga kuipa kwake n’kotani?
• Kodi ndi makhalidwe apamwamba ati amene adzatithandiza kulandira uphungu, nanga Yesu anapereka chitsanzo chotani pamenepa?
[Mafunso]
1. (a) N’chifukwa chiyani ife tonse timafunika uphungu ndi mwambo? (b) Kodi ndi funso liti limene tifunika kuliganizira?
2. Kodi tifunika kuchita chiyani ena akatipatsa uphungu?
3, 4. (a) Kodi Baibulo lili ndi chiyani chimene chingatithandize kuona uphungu ndi mwambo moyenera? (b) Kodi Mfumu Sauli anatani atapatsidwa uphungu, ndipo chinachitika n’chiyani?
5. Kodi chinachitikira Mfumu Uziya n’chiyani atakana uphungu?
6. (a) N’chifukwa chiyani onse aŵiri Sauli ndi Uziya anakana uphungu? (b) N’chifukwa chiyani kukana uphungu ndi vuto lalikulu masiku ano?
7. Kodi zimene Mose anachita atapatsidwa uphungu zingatiphunzitse zinthu zolimbikitsa zotani?
8. (a) Kodi Davide anachita machimo otani? (b) Kodi Davide anatani pamene Natani anamudzudzula? (c) Kodi machimo a Davide anabweretsa mavuto otani?
9. Kodi tisamaiwale chiyani tikapatsidwa uphungu kapena kulangidwa?
10. Kodi Yesu anati ndi khalidwe liti limene limafunika kwa aja amene adzaloŵa mu Ufumu?
11. (a) Kodi tifunika kukhala odzichepetsa kwa ndani, nanga n’chifukwa chiyani? (b) Ngati ndife odzichepetsa, kodi tidzachitanji ena akatipatsa uphungu?
12. (a) Kodi ndi khalidwe lofunika liti lomwe likugwirizana kwambiri ndi kudzichepetsa? (b) N’chifukwa chiyani tifunika kuganizira mmene khalidwe lathu limakhudzira ena?
13. Kodi ndi chitsanzo chiti chimene chingasonyeze ngati tili ndi chizoloŵezi chotsatira uphungu wa m’Malemba?
14. Kodi n’chifukwa chiyani tifunika kukhala odzichepetsa ndi oganizira ena?
15. (a) Kodi tifunika kusintha chiyani kuti tikhale ndi umunthu umene Mulungu amasangalala nawo? (b) Kodi Yehova watipatsa uphungu ndi mwambo kudzera kuti?
16. Kodi Yehova amapereka thandizo lotani kwa ife patokha?
[Chithunzi patsamba 142]
Uziya anakana uphungu ndipo anakanthidwa ndi khate
[Chithunzi patsamba 142]
Mose anapindula mwa kulandira uphungu kwa Yetero