1 Samueli
15 Ndiyeno Samueli anauza Sauli kuti: “Yehova anandituma kudzakudzoza kuti ukhale mfumu ya anthu ake Aisiraeli.+ Ndiye tamvera zimene Yehova wanena.+ 2 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Ndibwezera Aamaleki chifukwa cha zimene anachitira Aisiraeli polimbana nawo pamene Aisiraeliwo ankachokera ku Iguputo.+ 3 Tsopano pita ukaphe Aamaleki+ ndiponso kuwononga+ zinthu zonse zimene ali nazo. Usakasiye aliyense.* Ukaphe+ mwamuna ndi mkazi, mwana wamngʼono ndi wakhanda, ngʼombe ndi nkhosa komanso ngamila ndi bulu.’”+ 4 Sauli anaitanitsa anthu ku Telayimu nʼkuwawerenga. Panali asilikali oyenda pansi 200,000 ndiponso amuna a ku Yuda 10,000.+
5 Kenako Sauli anafika mumzinda wa Amaleki nʼkubisala mʼchigwa. 6 Ndiyeno, Sauli anauza Akeni+ kuti: “Chokani pakati pa Aamaleki kuti ndisakuphereni limodzi,+ chifukwa munasonyeza chikondi chokhulupirika kwa Aisiraeli onse+ pamene ankachokera ku Iguputo.” Choncho Akeni anachokadi pakati pa Aamaleki. 7 Kenako Sauli anapha Aamaleki+ kuyambira ku Havila+ mpaka ku Shura,+ pafupi ndi Iguputo. 8 Iye anagwira Agagi+ mfumu ya Amaleki ndipo sanamuphe, koma anthu ena onse anawapha ndi lupanga.+ 9 Sauli ndi anthu ake anasiya* Agagi, nkhosa ndi ngʼombe zabwino kwambiri, ziweto zonenepa, nkhosa zamphongo ndi zina zonse zimene zinali zabwino.+ Iwo sanafune kupha zimenezi, koma zinthu zonse zimene zinali zachabechabe ndi zosafunika anaziwononga.
10 Ndiyeno Yehova anauza Samueli kuti: 11 “Ndikumva chisoni kuti ndinaika Sauli kukhala mfumu. Iye wasiya kunditsatira, ndipo sanamvere mawu anga.”+ Samueli anakhumudwa kwambiri ndi nkhaniyi moti analirira Yehova usiku wonse.+ 12 Samueli atadzuka mʼmamawa kuti akaonane ndi Sauli, anamva kuti: “Sauli anapita ku Karimeli+ ndipo wamangako chipilala kuti anthu azimukumbukira,+ kenako wapita ku Giligala.” 13 Patapita nthawi Samueli anamʼpeza Sauli, ndipo Sauli anauza Samueli kuti: “Yehova akudalitseni. Ndachita zimene Yehova ananena.” 14 Koma Samueli anati: “Nanga bwanji ndikumva kulira kwa nkhosa ndi ngʼombe?”+ 15 Sauli anayankha kuti: “Zachokera kwa Aamaleki. Anthuwa sanaphe* nkhosa ndi ngʼombe zabwino kwambirizi kuti ziperekedwe nsembe kwa Yehova Mulungu wanu. Koma zina zonse zotsala taziwononga.” 16 Samueli anauza Sauli kuti: “Khala chete! Dikira ndikuuze zimene Yehova wandiuza usiku wapitawu.”+ Sauli anayankha kuti: “Lankhulani!”
17 Ndiyeno Samueli anati: “Kodi sunkadziona ngati wachabechabe+ utasankhidwa kukhala mtsogoleri wa mafuko a Isiraeli komanso pamene Yehova anakudzoza kuti ukhale mfumu ya Isiraeli?+ 18 Kenako Yehova anakutuma kuti, ‘Pita ukaphe anthu ochimwa, Aamaleki.+ Ukamenyane nawo mpaka ukawaphe onse.’+ 19 Ndiye nʼchifukwa chiyani sunamvere mawu a Yehova, koma unathamangira kutenga zinthu zawo mwadyera+ nʼkuyamba kuchita zinthu zoipa pamaso pa Yehova?”
20 Sauli anayankha Samueli kuti: “Komatu ndamvera mawu a Yehova. Ndagwira ntchito imene Yehova anandituma ndipo ndabweretsa Agagi mfumu ya Amaleki, koma Aamalekiwo ndawapha.+ 21 Anthuwa atenga nkhosa ndi ngʼombe zabwino kwambiri pa zinthu zimene zinayenera kuwonongedwa kuti akazipereke nsembe kwa Yehova Mulungu wanu ku Giligala.”+
22 Samueli anati: “Kodi Yehova amasangalala ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zina+ kuposa kumvera mawu a Yehova? Dikira ndikuuze! Kumvera kumaposa nsembe,+ ndipo kumvetsera mosamala kumaposa mafuta+ a nkhosa zamphongo. 23 Chifukwa kupanduka+ nʼchimodzimodzi ndi tchimo la kuwombeza,+ ndipo kuchita zinthu modzikuza nʼchimodzimodzi ndi kugwiritsa ntchito mphamvu zamatsenga ndiponso kulambira mafano.* Popeza wakana mawu a Yehova,+ iyenso wakukana kuti ukhale mfumu.”+
24 Sauli anayankha Samueli kuti: “Ndachimwa. Sindinamvere lamulo la Yehova komanso mawu anu chifukwa choopa anthu ndipo ndinamvera zimene ananena. 25 Chonde ndikhululukireni tchimo langa, ndipo tibwerere limodzi kuti ndikalambire Yehova.”+ 26 Koma Samueli anamuyankha kuti: “Sindibwerera nawe chifukwa wakana mawu a Yehova, ndipo Yehova wakukana kuti upitirize kukhala mfumu ya Isiraeli.”+ 27 Pamene Samueli ankatembenuka kuti azipita, Sauli anagwira mʼmunsi mwa mkanjo wodula manja wa Samueli ndipo mkanjowo unangʼambika. 28 Zitatero, Samueli anamuuza kuti: “Yehova wangʼamba ufumu wa Isiraeli nʼkuuchotsa kwa iwe lero, ndipo adzaupereka kwa munthu wina woyenera kuposa iweyo.+ 29 Kuwonjezera apo, Wolemekezeka wa Isiraeli+ sadzalephera kukwaniritsa mawu ake,+ ndipo sadzasintha maganizo* chifukwa iye si munthu kuti asinthe maganizo.”*+
30 Atatero Sauli anati: “Ndachimwa. Komabe, chonde ndilemekezeni pamaso pa akulu a anthu anga ndi Aisiraeli. Tiyeni tibwerere limodzi ndikalambire Yehova Mulungu wanu.”+ 31 Choncho Samueli anabwerera limodzi ndi Sauli ndipo Sauli analambira Yehova. 32 Kenako Samueli anati: “Mʼbweretseni kuno Agagi mfumu ya Amaleki.” Atatero, Agagi anapita kwa Samueli mokayikira.* Mumtima mwake ankaganiza kuti: ‘Panopa pondipha ndiye padutsa.’ 33 Koma Samueli anati: “Akazi anaferedwa ana awo chifukwa cha lupanga lako, choncho mayi akonso aferedwa kuposa akazi onse.” Kenako Samueli anadula Agagi mapisimapisi pamaso pa Yehova ku Giligala.+
34 Ndiyeno Samueli anapita ku Rama, koma Sauli anapita kunyumba kwake ku Gibeya. 35 Samueli analirira Sauli ndipo sanaonanenso naye mpaka tsiku limene Samueliyo anamwalira.+ Yehova anamva chisoni kuti anaika Sauli kukhala mfumu ya Isiraeli.+