MUTU 2
Aneneri Amene Uthenga Wawo Ungatithandize
1. Kodi n’chifukwa chiyani muyenera kuphunzira za aneneri 12 amene analemba mabuku omalizira a Malemba Achiheberi?
KODI mungakonde kudziwa bwino aneneri 12 a Mulungu? Aneneri 12 amenewa anakhalapo kale kwambiri Yesu asanabwere padzikoli, choncho simungaonane nawo maso ndi maso. Ngakhale zili choncho, mungathe kuwadziwa bwino ndipo mungaphunzire mmene iwo ankachitira zinthu posonyeza kuti akukumbukira “tsiku lalikulu la Yehova.” Ndipo zimene muphunzire n’zofunika kwambiri pa moyo wa Mkhristu aliyense amene akuyesetsa kukumbukira tsiku lalikulu la Yehova.—Zefaniya 1:14; 2 Petulo 3:12.
2, 3. Kodi zimene zimatichitikira masiku ano zikufanana bwanji ndi zimene zinkachitikira aneneri 12?
2 M’Malemba muli anthu ambiri amene ankadziwika kuti aneneri, ndipo mabuku ambiri a m’Baibulo amadziwika ndi mayina a aneneri amenewa. Mofanana ndi aneneri ena onse, aneneri 12 amene tikambirane m’bukuli, ndi zitsanzo zabwino kwambiri pa nkhani ya kukhulupirika ndi kulimba mtima. Ena mwa iwo ankasangalala kwambiri chifukwa anali ndi mwayi woona anthu akusintha mitima ndi maganizo awo n’kuyambanso kumvera Mulungu, atamva uthenga umene aneneriwo ankalengeza. Koma ena mwa aneneriwa ankakhumudwa kwambiri chifukwa ankaona anthu osamvera akuphwanya mfundo za Yehova n’kumachita zinthu zosemphana ndi chifuniro chake. Ena ankakhumudwanso chifukwa ankaona anthu amene ankati ndi olambira Yehova akuchita zinthu mosalabadira machenjezo amene iwo ankapereka komanso akuchita zinthu zina motayirira.
3 Mofanana ndi ifeyo, aneneri 12 amenewa anakhala ndi moyo pa nthawi imene anthu ambiri anasiya kulambira Mulungu woona, komanso panali mavuto ambiri a zandale ndipo anthu ankachita makhalidwe oipa. Popeza aneneriwa anali anthu “monga ife tomwe,” ayenera kuti nthawi zina ankachita mantha komanso ankakumana ndi mavuto osiyanasiyana. (Yakobo 5:17) Komabe, iwo anapereka chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife, ndipo tiyenera kuganizira mozama mauthenga amene iwo analemba. Mauthenga amenewa analembedwa “m’malemba aulosi” n’cholinga choti atithandize “ifeyo amene mapeto a nthawi zino atifikira.”—Aroma 15:4; 16:26; 1 Akorinto 10:11.
12 MMENE ZINTHU ZINALILI PA NTHAWI YA ANENERI
4. Kodi mabuku a aneneri 12 anasanjidwa mogwirizana ndi nthawi imene aneneriwo anakhala ndi moyo? Nanga ndi aneneri ati amene anali oyambirira kugwiritsidwa ntchito ndi Yehova kuti achenjeze komanso kulimbikitsa anthu ake?
4 Mwina mungaganize kuti m’Baibulo, mabuku a aneneriwa, omwe akuyambira pa Hoseya mpaka pa Malaki, anasanjidwa mogwirizana ndi nthawi imene aneneriwo anakhala ndi moyo. Koma zinthu sizili choncho. Mwachitsanzo, Yona, Yoweli, Amosi, Hoseya ndi Mika, onse anakhala ndi moyo m’zaka za m’ma 800 ndi 700 B.C.E.a Pa nthawi imeneyi, mafumu ambiri a ufumu wakum’mwera wa Yuda ndiponso a ufumu wakumpoto wa Isiraeli, anali osakhulupirika. Nawonso anthu awo anali osakhulupirika ndipo zimenezi zinakwiyitsa Mulungu. Inali nthawi imeneyi pamene Asuri, ndipo kenako Ababulo, anayamba kulamulira dziko lonse lapansi. Pa nthawiyi, Aisiraeli sankadziwa kuti Yehova adzagwiritsa ntchito maufumu amphamvu kwambiri padziko lonse amenewa popereka chilango kwa iwowo. Komabe, inuyo mukudziwa bwino kuti mobwerezabwereza, Mulungu ankatumiza aneneri ake okhulupirika kuti akachenjeze Aisiraeli ndi Ayuda.
5. Kodi ndi aneneri ati amene Yehova anawatumiza kuti akapereke uthenga wake wachiweruzo, dziko la Yuda ndi mzinda wake wa Yerusalemu zitatsala pang’ono kuwonongedwa?
5 Nthawi yoti Yehova apereke chiweruzo padziko la Yuda ndi mzinda wake wa Yerusalemu itatsala pang’ono kukwana, iye anatumiza gulu lina la aneneri omwe ankagwira ntchito yawo mwakhama. Kodi ndi aneneri ati omwe anali m’gulu limeneli? M’gululi munali Zefaniya, Nahumu, Habakuku ndi Obadiya. Aneneri onsewa anagwira ntchito yawo m’zaka za m’ma 600 B.C.E. M’chaka cha 607 B.C.E., Ababulo anawononga mzinda wa Yerusalemu ndiponso anatenga Ayuda n’kupita nawo ku ukapolo. Izi zinali zomvetsa chisoni kwambiri pa zinthu zonse zimene zinachitika m’zaka zimenezi. Apanso zinthu zinachitika mogwirizana ndi maulosi ochenjeza amene Mulungu anapereka kudzera mwa ena mwa aneneri anayi amenewa. Iwo anayesetsa kuchenjeza anthu kuti asiye kuchita zinthu zoipa, monga kuledzera ndi kuchita chiwawa, koma anthuwo sanasinthe.—Habakuku 1:2, 5-7; 2:15-17; Zefaniya 1:12, 13.
6. Kodi Yehova anathandiza bwanji anthu amene anabwerera kwawo kuchokera ku ukapolo?
6 Anthu a Mulungu atabwerera kwawo kuchokera ku ukapolo, anafunika utsogoleri wabwino, kulimbikitsidwa ndiponso kupatsidwa malangizo abwino amene akanawathandiza kuti apitirizebe kulambira koona. Choncho, Mulungu anatumizanso aneneri ena omwe anali Hagai, Zekariya ndi Malaki kuti athandize anthu akewo. Aneneriwa anagwira ntchito yawo m’zaka za m’ma 500 ndi 400 B.C.E. Pamene mukuphunzira zambiri zokhudza aneneri 12 amenewa, monga ntchito yawo komanso mmene ankasonyezera mwakhama kuti Yehova yekha ndiye woyenera kulamulira, mupeza mfundo zofunika kwambiri zimene mungagwiritse ntchito pochita utumiki wanu m’nthawi yovuta ino. Tsopano tiyeni tikambirane za aneneri onsewa mogwirizana ndi nthawi imene anachita utumiki wawo.
ANAYESETSA KUTHANDIZA MITUNDU YA ANTHU OSAMVERA
7, 8. Kodi zimene zinachitikira Yona zingatilimbikitse bwanji kuthana ndi mtima wodzikayikira?
7 Kodi munayamba mwadzikayikirapo, mwina n’kumaona kuti chikhulupiriro chanu chayamba kuchepa? Ngati zili choncho, kuganizira zimene zinachitikira Yona kungakuthandizeni kwambiri. Yona anakhala ndi moyo m’zaka za m’ma 800 B.C.E. Muyenera kuti mukudziwa zoti Mulungu anauza Yona kuti apite kumzinda wa Nineve, womwe unali likulu la ufumu wa Asuri, umene unkakula kwambiri pa nthawiyo. Yona anauzidwa zoti akadzudzule anthu a ku Nineve kuti asiye zoipa zimene ankachita. Koma m’malo mopita kumzinda wa Nineve, womwe unali pamtunda wa makilomita pafupifupi 900 kumpoto chakum’mawa kwa Yerusalemu, Yona anakwera chombo, mwina chopita kudoko lina la ku Spain. Apa Yona ankapita kudera lina losiyaniratu ndi kumene anatumidwa, limene linali pamtunda wa makilomita oposa 3,500 kuchokera ku Nineve. Kodi mukuganiza kuti Yona anachita zimenezi chifukwa chiyani? Kodi iye ankachita mantha, kapena chikhulupiriro chake chinangochepa chabe pa nthawiyi? Kapenanso kodi iye sankafuna zoti anthu a ku Nineve amve uthenga wake n’kulapa, poopera kuti anthuwo angathe kudzaukira Aisiraeli? Baibulo silitiuza chifukwa chenicheni. Koma zimene Yona anachitazi zikutithandiza kuona chifukwa chake tikufunikira kumatetezera mtima wathu.
8 Muyeneranso kuti mukudziwa zimene Yona anachita Mulungu atamupatsa chilango. Pamene Yona anali m’mimba mwa “chinsomba chachikulu” chomwe chinamumeza, anavomereza mfundo yakuti: “Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.” (Yona 1:17; 2:1, 2, 9) Ndiyeno Yona atapulumutsidwa ndi Mulungu mozizwitsa, anapita ku Nineve kukalengeza uthenga umene Mulungu anamuuza. Koma kenako iye anakhumudwa kwambiri ataona kuti Yehova sanawononge anthu a mumzindawo chifukwa choti analapa atamvera uthenga umene iyeyo ankalengeza. Apanso, Yehova anathandiza mneneri wakeyo kuti asinthe mtima wake wodzikonda. Ngakhale kuti anthu ena angamaone kwambiri zolakwa za Yona, Mulungu ankamuona kuti iye anali mtumiki wake wokhulupirika ndi womvera.—Luka 11:29.
9. Kodi uthenga waulosi wa Yoweli ungakuthandizeni bwanji?
9 Kodi munayamba mwakhumudwapo chifukwa choti anthu amakunyozani kuti uthenga wa m’Baibulo umene mukulengeza umangoopseza anthu? Anthu a m’nthawi ya mneneri Yoweli, yemwe dzina lake limatanthauza kuti “Yehova Ndiye Mulungu,” ankaonanso chimodzimodzi uthenga umene iye ankalengeza. Zikuoneka kuti iye analemba uthenga wake wa maulosi ali ku Yuda cha m’ma 820 B.C.E., m’nthawi ya Mfumu Uziya. Zikuonekanso kuti Yoweli anayamba utumiki wake chakumapeto kwa utumiki wa Yona. Yoweli analosera zoti kudzabwera mliri wa dzombe lowononga kwambiri lomwe lidzawononge dziko lonse la Yuda, ndipo ananenanso kuti mliriwo uzidzachitika mobwerezabwereza. Zoonadi, tsiku lalikulu ndi lochititsa mantha la Mulungu linali litatsala pang’ono kufika. Komabe, mukapitiriza kuphunzira uthenga wa Yoweli muona kuti sikuti iye ankangolengeza uthenga wachiwonongeko wokhawokha. Iye ankalengezanso uthenga wolimbikitsa, monga wakuti anthu okhulupirika ‘adzapulumuka.’ (Yoweli 2:32) Anthu amene alapa amasangalala chifukwa amadziwa kuti Yehova anawakhululukira ndiponso aziwadalitsa. Zimenezi n’zolimbikitsa kwambiri kwa ife chifukwa ifenso timalengeza uthenga wofanana ndi umenewu. Yoweli analosera kuti mzimu woyera, womwe ndi mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito, udzatsanuliridwa “pa chamoyo chilichonse.” Kodi mukutha kuona mmene ulosi umenewu ukukukhudzirani? Ndipotu Yoweli ananena motsindika mfundo yokhayo imene ingathandize anthu kupulumuka. Iye anati: “Aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.”—Yoweli 2:28, 32.
10. Kodi Yehova anagwiritsa ntchito bwanji munthu wamba amene nthawi zina ankagwira ntchito zina zakumunda?
10 Mungamvetse bwino mmene Amosi ankamvera mumtima mwake, ngati nthawi zina mumachita mantha kulengeza uthenga wamphamvu umene mwauzidwa kuti mulengeze, makamakanso kwa anthu opanda chidwi. Poyamba, Amosi anali asanachitepo utumiki uliwonse monga mneneri komanso sanali mwana wa mneneri, koma anali woweta nkhosa ndipo pa nyengo ina chaka chilichonse ankagwiranso ntchito zina zakumunda. Iye anapatsidwa utumiki wa uneneri chakumapeto kwa zaka za m’ma 800 B.C.E., pa nthawi imene Mfumu Uziya ankalamulira ku Yuda. Ngakhale kuti sankachokera m’banja lotchuka, Amosi (yemwe dzina lake limatanthauza “Kukhala Katundu” kapena “Kunyamula Katundu”) analengeza uthenga wofunika kwambiri kwa Ayuda, Aisiraeli ndiponso mitundu ina yapafupi. Kodi sizolimbikitsa kudziwa kuti Yehova angathandize munthu wamba kuti agwire ntchito yapadera ngati imeney?
11. Kodi Hoseya anali wokonzeka kuchita chiyani pokwaniritsa chifuniro cha Mulungu?
11 Kodi munayamba mwadzifunsa kuti, ‘Kodi ndine wokonzeka kudzimana chiyani kuti ndichite chifuniro cha Yehova?’ Ganizirani za Hoseya, amene anakhala ndi moyo chapanthawi ya Yesaya ndi Mika, ndipo anagwira ntchito ya uneneri kwa zaka pafupifupi 60. Yehova anauza Hoseya kuti akwatire Gomeri, ‘mkazi wadama.’ (Hoseya 1:2) Patapita nthawi, Gomeri anabereka ana atatu, ndipo zikuoneka kuti ndi mwana mmodzi yekha amene anali wa Hoseya. N’chifukwa chiyani Yehova anauza Hoseya kuti apitirizebe kukhala ndi mkazi wake wachigololoyo, ngakhale kuti kuchita zimenezi kunali kovuta kwambiri? Apa Yehova ankapereka phunziro labwino pa nkhani ya kukhulupirika ndi kukhululukira ena. Pa nthawiyo, anthu a mu ufumu wakumpoto anali atasiya kulambira Mulungu, mofanana ndi mmene mkazi wachigololo amasiyira mwamuna wake. Komabe, n’zolimbikitsa kwambiri kuganizira kuti Yehova anasonyeza chikondi anthu akewo ndipo anayesetsa kuwathandiza kuti alape.
12. Kodi tingapindule bwanji tikaganizira chitsanzo cha Mika ndiponso zimene anthu anachita atamva uthenga wake?
12 Kodi simukuvomereza kuti m’nthawi yovuta ino n’zovuta kukhala wolimba mtima komanso kudalira Yehova ndi mtima wonse? Koma mukamadalira Yehova komanso kukhala wolimba mtima, mudzakhala ngati mneneri Mika. Mneneriyu anakhala ndi moyo pa nthawi yofanana ndi Hoseya komanso Yesaya. Iye ankalengeza uthenga wodzudzula Ayuda ndi Aisiraeli m’zaka za m’ma 700 B.C.E. Iye anagwira ntchitoyi pa nthawi ya ulamuliro wa Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, omwe anali mafumu a Yuda. Zinthu zinaipiratu mu ufumu wakumpoto wa Isiraeli chifukwa chakuti anthu ankachita makhalidwe oipa kwambiri komanso ankalambira mafano. Ufumu umenewu unawonongedwa pamene Asuri anagonjetsa mzinda wa Samariya mu 740 B.C.E. Nawonso anthu a ku Yuda ankasinthasintha, chifukwa nthawi zina ankakhala okhulupirika kwa Yehova koma nthawi zina ankakhala osakhulupirika. Ngakhale kuti zinthu zinaipa choncho, Mika analimbikitsidwa ataona kuti anthu a ku Yuda asintha n’kuyamba kuchita zabwino pomvera uthenga wochokera kwa Mulungu umene iye ankalengeza. Zimenezi zinachititsa anthuwo kuti akhale kanthawi ndithu asanawonongedwe. Masiku anonso timalimbikitsidwa tikaona anthu ena akumvetsera uthenga umene timalalikira, womwe ungawathandize kudzapulumuka.
ANALOSERA ZA TSOKA LIMENE LINALI PAFUPI
13, 14. (a) Kodi chitsanzo cha Zefaniya chingakuthandizeni bwanji pa kulambira kwanu? (b) Kodi ntchito imene Zefaniya ankagwira inathandiza bwanji kusintha zinthu pa nkhani yolambira?
13 Maulamuliro a Iguputo ndiponso Asuri, omwe anali amphamvu kwambiri padziko lonse, anayamba kuchepa mphamvu, ndipo Ababulo anayamba kukhala ndi mphamvu zambiri. Pasanapite nthawi yaitali, ulamuliro wa Babulo unachita zinthu zimene zinakhudza kwambiri mtundu wa Ayuda. Komabe, panali aneneri a Mulungu amene ankachenjeza ndi kulimbikitsa anthu olambira Yehova. Tiyeni tikambirane za ena mwa aneneri amenewo, ndipo tikamachita zimenezi tizikumbukira kuti Akhristu masiku ano amalalikiranso uthenga wochenjeza anthu.
14 Ngati inuyo munasiya miyambo inayake ya makolo n’cholinga choti muthe kuchita chifuniro cha Yehova, ndiye kuti mungamvetse bwino mmene zinthu zinalili pa moyo wa Zefaniya. Zikuoneka kuti iye anali mdzukulu wa mdzukulu wa Mfumu Hezekiya, ndipo anali wachibale wa Mfumu Yosiya. Choncho Zefaniya anali wochokera ku banja lachifumu la Yuda. Ngakhale zinali choncho, Zefaniya anamvera Mulungu ndipo analengeza uthenga wodzudzula utsogoleri woipa wa ku Yuda. Dzina lakuti Zefaniya limatanthauza kuti “Yehova Wabisa,” ndipotu zimene iye ankachita polengeza uthenga wake zikugwirizana ndi tanthauzo la dzina lakeli. Izi zili choncho chifukwa iye ankatsindika mfundo yakuti, ndi chifundo cha Mulungu chokha chimene chingathandize munthu kuti ‘adzabisike pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.’ (Zefaniya 2:3) N’zosangalatsa kuti ntchito yolengeza uthenga wa Mulungu, imene Zefaniya ankaigwira molimba mtima inabala zipatso. Mwachitsanzo, Mfumu Yosiya, yemwe pa nthawiyo anali mnyamata, anatsogolera pa ntchito yobwezeretsanso kulambira koona. Iye anachita zimenezi pochotsa mafano ndi kukonzanso kachisi. (2 Mafumu, chaputala 22-23) Zefaniya pamodzi ndi aneneri anzake (Nahumu ndi Yeremiya) ayenera kuti ankathandiza kwambiri mfumuyo kapenanso ankaipatsa malangizo. Koma n’zomvetsa chisoni kuti ambiri mwa Ayuda anangolapa mwachiphamaso chabe. Izi zinadziwika chifukwa Yosiya atamwalira kunkhondo, Ayudawo anayambiranso kulambira mafano. Pasanapite zaka zambiri, iwo anatengedwa n’kupita ku ukapolo ku Babulo.
15. (a) N’chifukwa chiyani uthenga wachiweruzo umene Nahumu ankalengeza unali woyenera kwa anthu a ku Nineve? (b) Kodi mukuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira mzinda wa Nineve?
15 Mwina mumadziona kuti ndinu munthu wachabechabe ndipo anthu sakuwerengerani n’komwe. Komabe tisaiwale kuti Akhristu ali ndi mwayi waukulu kwambiri wokhala “antchito anzake a Mulungu,” ngakhale kuti ambiri mwa iwo amaoneka kuti ndi anthu wamba. (1 Akorinto 3:9) Mofanana ndi zimenezi, sitidziwa zambiri za mneneri Nahumu, kupatulapo zoti iye anali wochokera m’mudzi winawake waung’ono wotchedwa Elikosi, womwe mwina unali ku Yuda. Komatu uthenga wake unali wamphamvu ndiponso wofunika kwambiri. N’chifukwa chiyani tikutero? Nahumu analosera uthenga wodzudzula mzinda wa Nineve, womwe unali likulu la ufumu wa Asuri. M’mbuyomo, anthu a mumzindawu anamvera uthenga wa Yona, koma patapita nthawi anayambiranso kuchita zoipa. Zithunzi zojambulidwa pamiyala mochita kugoba zomwe zapezeka pamene panali mzinda wakale wa Nineve, zikusonyeza kuti zimene Nahumu ananena kuti Nineve unali “mzinda wokhetsa magazi,” n’zoona. (Nahumu 3:1) Zithunzizo zikusonyeza nkhanza zimene anthu a mumzindawo ankachitira akapolo omwe ankawagwira pa nkhondo. Nahumu analosera mwamphamvu ndiponso mosapita m’mbali kuti mzinda wa Nineve udzawonongedwa kotheratu. Uthengawo unakwaniritsidwadi, ngati mmenenso zidzachitikire ndi uthenga womwe tikulengeza masiku ano.
16, 17. Kodi tingaphunzire chiyani kwa Habakuku ngati zinthu zina zimene tikuyembekezera zokhudza mapeto sizinakwaniritsidwebe?
16 Kale, anthu ena amene ankawerenga Baibulo ankaganiza kuti tsiku la Yehova lifika pa nthawi imene iwowo anali kuyembekezera, koma sizinachitike. Masiku anonso, anthu ena angakhumudwe akamaona ngati Mulungu akuchedwa kupereka chiweruzo. Kodi inunso munayamba mwaganizirapo zimenezi? Ngati zili choncho, dziwani kuti nayenso Habakuku anadandaulira Mulungu kuti: “Inu Yehova, kodi ndidzalirira thandizo koma inu osandimva kufikira liti? . . . N’chifukwa chiyani kufunkha ndi chiwawa zikuchitika pamaso panga?”—Habakuku 1:2, 3.
17 Habakuku anatumikira monga mneneri pa nthawi imene mu ufumu wa Yuda munali mavuto ambiri kuposa nthawi ina iliyonse m’mbuyomo. Pa nthawiyi, Yosiya, yemwe anali mfumu yabwino, anali atamwalira ndipo mzinda wa Yerusalemu unali utatsala pang’ono kuwonongedwa mu 607 B.C.E. Anthu ambiri ku Yuda ankachita zinthu zopanda chilungamo komanso chiwawa chinali paliponse. Habakuku anachenjeza Ayuda kuti asachite mgwirizano ndi Aiguputo chifukwa zimenezo sizikanawathandiza kuti asawonongedwe ndi Ababulo omwe ankakonda kupha anthu. Iye analemba uthenga womveka bwino ndiponso wamphamvu, ndipo analimbikitsa Ayuda kuti: “Wolungama adzakhalabe ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.” (Habakuku 2:4) Mtumwi Paulo anagwira mawu lemba limeneli katatu konse m’mabuku a Malemba Achigiriki ndipo zimenezi zikusonyeza kuti mawu amenewa ndi ofunika kwambiri kwa ife. (Aroma 1:17; Agalatiya 3:11; Aheberi 10:38) Kuwonjezera pamenepa, kudzera mwa Habakuku, Yehova akutiuza mawu olimbikitsa akuti: “Masomphenyawa akuyembekezera nthawi yake yoikidwiratu ndipo . . . sadzachedwa.”—Habakuku 2:3.
18. N’chifukwa chiyani Yehova anauza Obadiya kuti alosere kuti Aedomu adzawonongedwa?
18 Mneneri Obadiya amasiyana ndi aneneri ena onse chifukwa iye analemba buku lalifupi kwambiri pa mabuku onse a Malemba Achiheberi, ndipo buku lakeli lili ndi mavesi 21 okha basi. Zomwe tikudziwa zokhudza iyeyu n’zakuti analosera kuti Aedomu adzawonongedwa. Aedomu anali mbadwa za mchimwene wa Yakobo, choncho iwo anali ‘abale’ a Aisiraeli. (Deuteronomo 23:7) Koma Aedomu anachitira nkhanza kwambiri anthu a Mulungu, ngati kuti sanali abale awo. Mu 607 B.C.E., chapanthawi imene Obadiya analemba buku lake, Aedomu anatseka njira kuti Ayuda asathawe pa nthawi imene Ababulo ankawononga mzinda wawo. Komanso Aedomu ankagwira Ayuda omwe ankathawa n’kumawapereka m’manja mwa Ababulowo. Chifukwa cha zimenezi, Yehova analosera kuti Aedomu adzawonongedwa kotheratu, ndipo ulosi umenewu unakwaniritsidwadi. Mofanana ndi Nahumu, sitikudziwa zambiri za Obadiya. Komabe n’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Mulungu angagwiritse ntchito anthu wamba kuti alengeze uthenga wake.—1 Akorinto 1:26-29.
UTHENGA WAWO UNALI WOLIMBIKITSA, WOTONTHOZA KOMANSO WOCHENJEZA
19. Kodi Hagai analimbikitsa bwanji anthu a Mulungu?
19 Mneneri Hagai anali woyamba pa aneneri atatu amene anatumikira Mulungu, Ayuda okhulupirika atabwerera kwawo kuchokera ku ukapolo ku Babulo mu 537 B.C.E. Iye ayenera kuti anali m’gulu la Ayuda oyambirira kubwerera ku Yerusalemu. Hagai anayesetsa kulimbikitsa Ayuda kuti alimbane ndi mayesero osiyanasiyana ochokera kwa anthu a mitundu ina komanso kuti asayambe kukonda chuma. Iye anachita zimenezi mothandizana ndi Bwanamkubwa Zerubabele, Mkulu wa Ansembe Yoswa ndiponso mneneri Zekariya. Iwo anafunika kugwira ntchito imene anabwererera, yomwe inali kumanganso kachisi wa Yehova. Mauthenga anayi osapita m’mbali amene Hagai anapereka mu 520 B.C.E., anatsindika kwambiri za dzina la Yehova ndiponso anasonyeza kuti iye yekha ndiye woyenera kulamulira. Mukamawerenga buku la Hagai, mupeza kuti mawu akuti “Yehova wa makamu” alimo nthawi zokwana 15. Mauthenga amphamvu a Hagai analimbikitsa anthu kuti ayambenso kugwira ntchito yomanganso kachisi. Zimenezi ziyenera kutilimbikitsa kwambiri ifeyo masiku ano podziwa kuti Yehova ali ndi mphamvu zopanda malire. Iye ndi Wolamulira Wamkulu ndipo amalamulira zolengedwa zauzimu zambirimbiri.—Yesaya 1:24; Yeremiya 32:17, 18.
20. Kodi Zekariya analimbana ndi khalidwe lotani limene anthu ambiri pa nthawiyo anali nalo?
20 Nthawi zina mwina mungakhumudwe chifukwa choti atumiki ena a Mulungu ayamba kufooka mwauzimu. Ngati zili choncho, mungamvetse bwino mmene zimenezi zinam’khudzira mneneri Zekariya. Zekariya anali ndi ntchito yaikulu yoti athandize olambira anzake kuti azigwira mwakhama ntchito yomanga kachisi mpaka kumaliza. Iye anachita zimenezi mofanana ndi Hagai, amene analinso mneneri pa nthawi yofanana ndi iyeyo. Zekariya anagwira ntchito mwakhama polimbikitsa anthu kuti apitirizebe kugwira ntchito yofunika kwambiriyo. Ngakhale kuti anthu ambiri pa nthawiyo ankachita zinthu mosadziletsa pongofuna kudzisangalatsa, iye anayesetsa kuwalimbikitsa kuti akhalebe ndi chikhulupiriro cholimba chomwe anayenera kuchisonyeza pogwira ntchito. Zekariya anayesetsa kwambiri kulimbikitsa anthuwo, moti anagwiradi ntchitoyo mpaka kuimaliza. Komanso iye analemba maulosi ambiri onena za Khristu. Ifenso tingalimbikitsidwe ndi uthenga wakuti “Yehova wa makamu” sadzaiwala anthu amene akuyesetsa kuchita chifuniro chake.—Zekariya 1:3.
ANKAYEMBEKEZERA MESIYA
21. (a) N’chifukwa chiyani uthenga wa Malaki unali wofunikira kwambiri? (b) Kodi ndi mfundo yolimbikitsa iti imene Malaki analemba pomaliza buku lake, lomwenso ndi lomaliza m’Malemba Achiheberi?
21 Mneneri womaliza pa aneneri 12 amenewa ndi Malaki, amene anachita zinthu zogwirizana ndi dzina lake, lomwe limatanthauza kuti, “Mtumiki Wanga.” Tikudziwa zochepa chabe zokhudza Malaki, yemwe anali mneneri m’zaka za m’ma 450 B.C.E. Koma tikaona maulosi ake, tingadziwe kuti iye anali munthu wolimba mtima amene anadzudzula anthu a Mulungu chifukwa cha machimo awo komanso chinyengo chimene ankachita. Zimene Malaki anafotokoza zokhudza mmene zinthu zinalili pa nthawiyo, zikufanana ndi zimene Nehemiya anafotokoza ndipo mwina anthu awiriwa anakhala ndi moyo pa nthawi yofanana. Koma kodi n’chifukwa chiyani uthenga umene Malaki ankalengeza unali wofunikira kwambiri? N’chifukwa choti pa nthawiyi anthu ambiri anali atafooka mwauzimu ngakhale kuti zaka zambiri m’mbuyomo iwo ankatumikira Mulungu mwakhama chifukwa cholimbikitsidwa ndi Zekariya komanso Hagai. Moyo wauzimu wa Ayuda unafika poipa kwambiri. Malaki anadzudzula molimba mtima ansembe omwe anali odzikweza komanso achinyengo. Iye anadzudzulanso anthu chifukwa choti ankalambira Yehova monyinyirika ndiponso ankapereka nsembe zosayenera. Komabe monga mmene Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti m’tsogolomu zinthu zidzakhala bwino kwambiri, Malaki analosera za kubwera kwa Yohane M’batizi, yemwe anali kalambulabwalo wa Mesiya, ndipo kenako analosera za kubwera kwa Khristu weniweniyo. Buku la Malaki ndi lomaliza pa Malemba Achiheberi ndipo uthenga womaliza m’bukuli ndi wolimbikitsa kwambiri kwa anthu onse oopa Mulungu. Malaki analemba kuti: “Dzuwa la chilungamo lidzakuwalirani.”—Malaki 4:2, 5, 6.
22. Kodi mukuphunzira chiyani mukaganizira mtima umene aneneri 12 amenewa anali nawo, komanso uthenga umene iwo analemba?
22 Mungathe kuona kuti aneneri amenewa, omwe analemba mabuku 12 omaliza a Malemba Achiheberi, anali ndi chikhulupiriro komanso ankatumikira Mulungu mwakhama. (Aheberi 11:32; 12:1) Mauthenga ndiponso zitsanzo zawo zingatiphunzitse mfundo zofunika kwambiri pamene tikuyembekezera mwachidwi “tsiku la Yehova.” (2 Petulo 3:10) Tsopano tiyeni tione mmene mauthenga aulosi amenewa angatithandizire kuti tidzapeze moyo wosatha m’tsogolomu.
a Yerekezerani zimenezi ndi tchati chomwe chili patsamba 20 ndi 21. Mwachitsanzo, muona kuti mneneri Mika ndi Hoseya anatumikira pa nthawi yofanana ndi imene Yesaya anali mneneri wa Mulungu ku Yerusalemu.