MUTU 3
Mfundo Yaikulu mu Uthenga wa Aneneri 12 Inali Yokhudza Tsiku la Yehova
1, 2. (a) Kodi mfundo yaikulu mu uthenga wa aneneri onse 12 inali yokhudza chiyani? (b) Kodi ena mwa aneneri 12 anafotokoza bwanji mwachindunji zokhudza tsiku la Yehova?
“TSIKU lalikulu la Yehova lili pafupi. Lili pafupi ndipo likubwera mofulumira kwambiri.” (Zefaniya 1:14) Aneneri a Mulungu, mobwerezabwereza ankachenjeza anthu kuti tsiku la Yehova layandikira. Ndipo nthawi zambiri ankanena za mmene kubwera kwa tsikuli kungakhudzire moyo wa anthu watsiku ndi tsiku, makhalidwe awo ndi zochita zawo. Nthawi zonse uthenga wa aneneriwa unali wolimbikitsa anthu kuti achite zinthu mwachangu. Kodi mukanachita chiyani zikanakhala kuti aneneriwo akukuuzani uthenga umenewu mwachindunji?
2 Mukamawerenga mabuku a aneneri 12, mudzaona kuti onse ananena zokhudza tsiku la Yehova ngakhale kuti ena sanalitchule mwachindunji.a Komabe tisanayambe kuphunzira uthenga wofunika kwambiri umene aneneriwa ankapereka, womwe uli m’mitu yotsatira ya buku lino, tiyeni tikambirane za mfundo yomwe aneneriwa ankanena mobwerezabwereza. Mfundo imeneyi ndi yokhudza tsiku la Yehova. Aneneri 6 mwa aneneri 12 amenewa anagwiritsa ntchito mawu akuti “tsiku la Yehova” kapena mawu ena ofanana ndi amenewa. Mwachitsanzo, Yoweli anafotokoza momveka bwino kuti tsiku limeneli lidzakhala “tsiku lalikulu ndi lochititsa mantha la Yehova.” (Yoweli 1:15; 2:1, 2, 30-32) Nayenso Amosi anauza Aisiraeli kuti akonzekere kukumana ndi Mulungu wawo, chifukwa chakuti tsiku la Yehova lidzakhala tsiku lamdima. (Amosi 4:12; 5:18) Patapita nthawi, Zefaniya ananena mawu amene ali m’ndime yoyamba ija. Komanso Yerusalemu atatsala pang’ono kuwonongedwa, Obadiya anachenjeza anthu kuti: “Tsiku la Yehova limene adzawononge mitundu yonse ya anthu lili pafupi.”—Obadiya 15.
3. N’chifukwa chiyani tinganene kuti aneneri amene anagwira ntchito yawo Ayuda atabwerera kwawo, ankalengeza za tsiku la Yehova?
3 Mukapitiriza kuphunzira mabuku a aneneriwa, muonanso kuti aneneri awiri omwe anatumizidwa kukalengeza uthenga kwa Ayuda atabwerera kuchokera ku ukapolo, anatchulanso zokhudza tsiku la Yehova. Zekariya ananena za tsiku limene mitundu yonse youkira Yerusalemu idzawonongedwe. Iye anafotokoza momveka bwino zimene zidzachitike pa ‘tsiku limene lidzatchedwa tsiku la Yehova.’ (Zekariya 12:9; 14:7, 12-15) Komanso Malaki anachenjeza anthu zokhudza kubwera kwa “tsiku la Yehova lalikulu ndi lochititsa mantha.”—Malaki 4:1-5.
4. Kodi ena mwa aneneri 12 amenewa, ananena chiyani zokhudza tsiku la Yehova?
4 Ngakhale kuti aneneri 6 enawo sanagwiritse ntchito mwachindunji mawu akuti “tsiku la Yehova,” uthenga wawo umanenabe za tsikuli. Mwachitsanzo, Hoseya ananena zoti Yehova adzaimba mlandu Aisiraeli, kenako Ayuda. (Hoseya 8:13, 14; 9:9; 12:2) Nthawi zambiri mauthenga amenewa ankanena za zimene Yehova anachita pa nthawi imeneyo. Mwachitsanzo, Yona analengeza zoti Mulungu adzapereka chiweruzo kwa anthu a ku Nineve. Nayenso Mika anafotokoza zimene zidzachitike Mulungu akadzapereka chiweruzo kwa anthu osamvera. (Yona 3:4; Mika 1:2-5) Ndipo Nahumu ananena motsimikiza kuti Yehova adzapereka chilango kwa adani ake. (Nahumu 1:2, 3) Habakuku anadandauliranso Mulungu chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo zomwe zinkachitika, komanso anafotokoza zinthu zina zokhudza “tsiku la nsautso.” (Habakuku 1:1-4, 7; 3:16) Ndiponso mauthenga ena amene ali m’mabuku amenewa amanena za zinthu zimene zikukhudza Akhristu oona. Mwachitsanzo, Hagai, yemwe ali m’gulu la aneneri amene anatumikira Mulungu Ayuda atabwerera kwawo kuchokera ku ukapolo, analosera za kugwedezedwa kwa mitundu ya anthu. (Hagai 2:6, 7) Ndipotu mtumwi Paulo anagwira mawu lemba la Hagai 2:6 polimbikitsa Akhristu kuti apitirize kukhala ndi makhalidwe abwino, n’cholinga choti asadzawonongedwe pamene Mulungu azidzachotsa kumwamba kophiphiritsira, komwe ndi koipa.—Aheberi 12:25-29; Chivumbulutso 21:1.
KODI TSIKU LA YEHOVA N’CHIYANI?
5, 6. Malinga ndi zimene aneneri anafotokoza, kodi tsiku la Yehova lidzakhala lotani?
5 Zingakhale zomveka ngati mutadzifunsa kuti, ‘Kodi tsiku la Yehova lidzakhala lotani? Kodi kuganizira tsiku limeneli kuyenera kukhudza bwanji moyo wanga panopa komanso m’tsogolo?’ Zimene aneneri ananena zinasonyeza kuti tsiku la Yehova ndi nthawi imene iye adzapereke chilango kwa adani ake ndiponso kuti ndi tsiku lankhondo. N’kutheka kuti pa tsiku lochititsa mantha limeneli, kumwamba kudzachitika zinthu zodabwitsa komanso zoopsa. Baibulo limati: “Dzuwa ndi mwezi zidzachita mdima, ndipo nyenyezi zidzasiya kuwala.” (Yoweli 2:2, 11, 30, 31; 3:15; Amosi 5:18; 8:9) Nanga padziko lapansili padzachitika chiyani? Mika ananena kuti: “Mapiri asungunuka kumapazi [a Yehova] ndipo zigwa zigawanika. Zonsezi zisungunuka ngati phula losungunuka ndi moto ndipo ziyenda ngati madzi othiridwa pamalo otsetsereka.” (Mika 1:4) Ngakhale kuti mwina mawu amenewa ndi ophiphiritsa, koma tikutha kuona kuti zimene Mulungu adzachite pa tsikulo zidzakhala zoopsa kwa anthu amene akukhala padziko lapansi. Komabe sikuti tsikuli lidzakhala loopsa kwa anthu onse. Aneneri omwewo ananenanso kuti anthu amene ‘akuyesetsa kuchita zabwino’ adzalandira madalitso ambirimbiri ndipo adzapitiriza kukhala ndi moyo.—Amosi 5:14; Yoweli 3:17, 18; Mika 4:3, 4.
6 Ena mwa aneneri 12 amenewa anafotokoza momveka bwino kwambiri zimene zidzachitike pa tsiku la Yehova. Mwachitsanzo, Habakuku anasonyeza mmene Yehova adzaphwanyire “mapiri amuyaya” komanso “zitunda zimene zidzakhalapo mpaka kalekale.” Mapiri ndi zitunda zimenezi ndi zizindikiro zoyenerera zoimira mabungwe a anthu amene akuoneka ngati adzakhalapo mpaka kalekale. (Habakuku 3:6-12) Zoonadi, tsiku la Yehova “ndi tsiku lamkwiyo, tsiku lansautso ndi zowawa, tsiku la mphepo yamkuntho ndi losakaza, tsiku lamdima wochititsa mantha, tsiku lamitambo yakuda ndi lamdima wandiweyani.”—Zefaniya 1:14-17.
7. Kodi pali ulosi wotani wokhudza anthu amene amatsutsana ndi Mulungu, ndipo udzakwaniritsidwa bwanji?
7 Taganizirani mavuto oopsa kwambiri amene anthu otsutsana ndi Mulungu adzakumane nawo. Baibulo limati: “Munthu aliyense mnofu wake udzawola ali chiimire, maso ake adzawola ali m’malo mwake ndiponso lilime lake lidzawola m’kamwa mwake.” (Zekariya 14:12) Kaya uthenga waulosi umenewu ndi wophiphiritsa kapena ayi, ukusonyezeratu kuti anthu ambiri adzakumana ndi tsoka loopsa kwambiri. Ngakhale zitakhala kuti uthenga waulosiwu ndi wophiphiritsa, malilime a adani a Mulungu adzawola m’njira yakuti sadzathanso kulankhula mawu onyoza. Ndipo maso awo adzawola m’njira yakuti zimene ankaona, kapena kuti kuganizira kuti achite mogwirizana polimbana ndi anthu a Mulungu, zidzalephereka.
N’CHIFUKWA CHIYANI MULUNGU, YEMWE NDI WACHIKONDI, ADZAWONONGE OIPA?
8, 9. (a) Kodi muyenera kukumbukira chiyani, kuti mumvetse chifukwa chake Yehova amawononga oipa? (b) Kodi zimene Yehova adzachite powononga oipa zikugwirizana bwanji ndi kukhulupirika kwanu pa moyo wanu watsiku ndi tsiku?
8 Mwina munamvapo anthu ena akufunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani Mulungu, yemwe ndi wachikondi, adzawononge adani ake mwanjira imeneyi? Kodi Mulungu akuyeneradi kuwononga anthu padzikoli? Kodi si paja Yesu analimbikitsa anthu kuti azikonda ngakhale adani awo n’cholinga choti asonyeze kuti iwo ndi ana a Atate wakumwamba?’ (Mateyu 5:44, 45) Kuti mupeze mayankho a mafunso amenewa, choyamba ganizirani kaye za mmene mavutowa anayambira kalelo. Kumbukirani kuti poyamba, Mulungu analenga Adamu ndi mkazi wake Hava m’chifaniziro chake, ndipo iwo anali anthu angwiro, koma anachimwa kenako n’kufa. Adamu ndi Hava anapatsira ana awo uchimo ndi imfa, ndipo zikukhudzanso ifeyo masiku ano. Iwo anasankha kukhala kumbali ya Satana Mdyerekezi pa nkhani yokhudza amene ali woyenerera kulamulira anthu onse. (Genesis 1:26; 3:1-19) Kwa zaka zambirimbiri, Satana wakhala akuyesetsa kuti atsimikizire kuti zimene iyeyo ananena ndi zoona. Iye ananena kuti ngati anthu atakopedwa kuti asiye kutumikira Yehova, akhozadi kusiya kumutumikira. Koma mukudziwa kuti Satana walephera kutsimikizira mfundo yakeyi. Mwachitsanzo, Yesu Khristu komanso atumiki ena ambirimbiri a Yehova Mulungu amamutumikira ndi mtima wosagawanika, ndipo asonyeza kuti amamutumikira chifukwa chomukonda. (Aheberi 12:1-3) Sitikukayikira kuti nanunso mukudziwa mayina a anthu ambiri omwe akutumikira Mulungu mokhulupirika.
9 Koma nanunso mukukhudzidwa ndi nkhani imeneyi, yomwe idzathetsedwe pamene Yehova azidzawononga oipa onse. Mwachitsanzo, mukamawerenga mabuku 12 amenewa, muona kuti ena mwa aneneriwa anafotokoza kuti anthu ena ankakhala moyo wongofuna kusangalala n’kumanyalanyaza kulambira Yehova. Aneneriwa analimbikitsa anthu a Mulungu kuti ‘aganizire mofatsa zimene ankachitazi’ ndiponso kuti asinthe moyo wawo. (Hagai 1:2-5; 2:15, 18; Amosi 3:14, 15; 5:4-6) Apatu aneneriwa ankathandiza anthu kuti adziwe mmene angakhalire ndi moyo wabwino. Anthu amene anamvera uthenga wa aneneriwa anasonyeza kuti Yehova ndiye wolamulira wawo wamkulu, ndiponso kuti Satana ndi wabodza. Yehova adzasonyeza kuti ndi wokhulupirika kwa anthu amenewa pamene iye azidzawononga adani ake.—2 Samueli 22:26.
10. Malinga ndi zimene Mika ananena, kodi pali chifukwa china chiti chomwe chikusonyeza kuti m’poyenera kuti Yehova awononge oipa?
10 Pali chifukwa chinanso chimene chidzachititse Mulungu kuti awononge oipa. Tabwererani kaye m’mbuyo m’zaka za m’ma 700 B.C.E., pamene Mika anali mneneri ku Yuda. Polankhula ngati kuti iyeyo anali mtundu wa anthu, anayerekezera mmene zinthu zinalili pa nthawiyo ku Yuda ndi munda wa mpesa, kapenanso munda umene akololamo kale mphesa kapena nkhuyu zake, ndipo simunatsale chilichonse. Zinali zovuta kwambiri kuti m’dzikolo mupezeke anthu olungama. Aisiraeli ankasaka abale awo, n’kumawadikirira panjira kuti akhetse magazi. Atsogoleri awo ndiponso oweruza awo ankalandira ziphuphu poweruza milandu. (Mika 7:1-4) Inuyo mukanakhala ndi moyo pa nthawi imeneyo, kodi mukanamva bwanji? N’zodziwikiratu kuti mukanamvera chisoni anthu osalakwa omwe ankavutika. Nanga Yehova amamva bwanji? Nayenso amakhudzidwa kwambiri akamaona anthu akuponderezedwa. Masiku ano, Yehova amaona zonse zimene anthu akuchita. Kodi mukuganiza kuti iye amaona zotani? Iye amaona anthu akupondereza ndi kuzunza anzawo mwankhanza kwambiri. Koma anthu amene ali okhulupirika ndi ochepa kwambiri poyerekezera ndi chiwerengero cha anthu padziko lonse. Komabe sitikuyenera kuda nkhawa. Yehova adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika chifukwa choti amakonda anthu amene akuvutikawo.—Ezekieli 9:4-7.
11. (a) Kodi n’chiyani chidzachitikire anthu oopa Mulungu pa tsiku la Yehova? (b) Kodi uthenga wochenjeza wa Yona unawakhudza bwanji anthu a ku Nineve?
11 Apa zikuonekeratu kuti adani a Mulungu adzawonongedwa pa tsiku la Yehova, koma amene amamuopa ndi kumutumikira adzapulumutsidwa.b Mneneri Mika analosera kuti mitundu ya anthu idzakhamukira kuphiri la nyumba ya Yehova, ndipo zimenezi zidzachititsa kuti padziko lonse pakhale mtendere ndi mgwirizano. (Mika 4:1-4) Kodi zimene aneneri ankalengeza kalelo zokhudza tsiku la Yehova zinathandiza anthu ena kusintha moyo wawo? Inde, anthu ena anasinthadi. Mwachitsanzo, kumbukirani kuti Yona atalengeza uthenga wachiweruzo ku Nineve, anthu a mumzindawo, omwe anali oipa ndiponso okonda chiwawa, “anayamba kukhulupirira Mulungu” ndipo ‘analapa ndi kusiya njira zawo zoipa.’ Chifukwa cha zimenezo, Yehova anasintha maganizo ndipo pa nthawiyo sanawononge anthuwo. (Yona 3:5, 10) Mosakayikira, uthenga wakuti Yehova anali atatsala pang’ono kupereka chiweruzo ku Nineve unathandiza kwambiri anthu a mumzindawo kuti asinthe moyo wawo.
KODI TSIKU LA YEHOVA LIMAKUKHUDZANI BWANJI?
12, 13. (a) Kodi aneneri 12 analosera zokhudza mitundu iti? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti uthenga waulosi wa aneneri 12 uyenera kukwaniritsidwanso m’tsogolo?
12 Komabe anthu ena anganene kuti: ‘Aneneri amenewo anakhalapo zaka zambiri zapitazo, ndiye kodi uthenga wawo wonena za tsiku la Yehova ukundikhudza bwanji?’ N’zoona kuti aneneri amenewo anakhalapodi zaka zambirimbiri zapitazo, Yesu asanabadwe. Komabe, tiyenera kuganizira kufunika kwa uthenga wawo wonena za tsiku la Yehova m’nthawi yathu ino. Kodi uthengawu ungatithandize bwanji? Pali mfundo yofunika kwambiri yomwe ingatithandize kuona mmene tingapindulire ndi uthenga wa aneneriwo. Ifeyo tiyenera kuzindikira kuti aneneriwa anapereka uthenga waulosi wonena za tsiku la Yehova pochenjeza Aisiraeli, Ayuda, mitundu imene inawazungulira ndiponso maulamuliro ena amene anali amphamvu kwambiri padziko lonse pa nthawiyo.c Mfundo yofunika kwambiri imene tiyenera kuikumbukira ndi yakuti maulosi amenewa anakwaniritsidwa. Mwachitsanzo, Asuri analandadi mzinda wa Samariya n’kuuwononga, dziko la Yuda linawonongedwa mu 607 B.C.E., ndipo patangopita zaka zochepa, mitundu ina yankhanza yozungulira madera amenewa nayonso inawonongedwa. Patapita nthawi, maulamuliro amphamvu padziko lonse, omwe anali Asuri, ndipo kenako Babulo, anatha. Zonsezi zinachitika pokwaniritsa maulosi.
13 Tsopano ganizirani zimene zinachitika pa Pentekosite mu 33 C.E., patapita nthawi yaitali ambiri mwa maulosiwa atakwaniritsidwa koyamba. Pa tsikulo, mtumwi Petulo ananena kuti mzimu woyera wa Mulungu unatsanulidwa pa okhulupirira pokwaniritsa ulosi wa Yoweli. Kenako Petulo ananena mawu ochokera m’buku la Yoweli, kuti: “Dzuwa lidzasanduka mdima, ndipo mwezi udzasanduka magazi. Zimenezi zidzachitika tsiku lalikulu ndi laulemerero la Yehova lisanafike.” (Machitidwe 2:20) Izi zikusonyeza kuti maulosi onena za tsiku la Yehova adzakwaniritsidwanso m’njira zina. Koma ulosi wa Yoweli unakwaniritsidwa kachiwiri mu 70 C.E. pamene asilikali achiroma anawononga Yerusalemu, ndipo nthawi imeneyi inalidi ya mdima ndi magazi.
14, 15. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti maulosi onena za tsiku la Yehova akutikhudza masiku ano? (b) Kodi tingayembekezere kuti tsiku la Yehova lidzayamba liti?
14 Komabe, ulosi wa Yoweli komanso maulosi ena okhudza tsiku la Yehova adzakwaniritsidwa komaliza m’tsogolo, ndipo zimenezi zikutikhudza ifeyo m’nthawi ino. N’chifukwa chiyani tikutero? Petulo analangiza Akhristu kuti ‘azikumbukira nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova.’ Ndiyeno mtumwiyu ananenanso kuti: “Pali kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekezera mogwirizana ndi lonjezo lake, ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.” (2 Petulo 3:12, 13) Mzinda wa Yerusalemu utangowonongedwa mu 70 C.E., sipanakhazikitsidwe kumwamba kwatsopano (boma latsopano la Mulungu) komanso dziko latsopano (anthu olungama olamuliridwa ndi boma limeneli). Choncho mawu aulosi onena za tsiku la Yehova ayenera kuti adzakwaniritsidwanso m’njira ina. Zoonadi, maulosi amenewa akutikhudzanso ifeyo, amene tikukhala ‘m’nthawi yapadera’ yovuta kwambiri.—2 Timoteyo 3:1.
15 Mawu osiyanasiyana ofotokoza za tsiku la Yehova amene akupezeka m’mabuku 12 a m’Baibulo amenewa amatichititsa kuganiza za mawu a Yesu Khristu akuti: “Kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pa chiyambi cha dziko mpaka tsopano, ndipo sichidzachitikanso.” Iye ananena kuti chisautso chachikulu “chikadzangotha, dzuwa lidzachita mdima ndipo mwezi sudzapereka kuwala kwake. Nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndipo mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka.” (Mateyu 24:21, 29) Zimenezi zikutithandiza kuzindikira nthawi imene tsiku la Yehova likuyenera kuyamba. Tsikuli lili pafupi kwambiri. Malemba amasonyeza kuti “Babulo Wamkulu,” yemwe ndi zipembedzo zonyenga zonse pamodzi, adzawonongedwa pa chisautso chachikulu. Ndiyeno chisautso chachikulu chimenechi chikadzafika pachimake, tsiku la Yehova lidzasesa adani onse a Mulungu padziko lapansili.—Chivumbulutso 17:5, 12-18; 19:11-21.
16. Kodi maulosi okhudza tsiku la Yehova adzakwaniritsidwa m’njira yaikulu iti?
16 Anthu a Mboni za Yehova akuzindikira kuti zinthu zosiyanasiyana zomwe zikuchitika masiku ano zikukwaniritsa maulosi onena za tsiku la Yehova. Kawirikawiri zimene zikuchitika m’zipembedzo zonyenga zimafanana m’njira zambiri ndi zimene anthu akale a mitundu yosiyanasiyana ankachita. Ena mwa iwo anali anthu ampatuko a ku Yerusalemu, Asamariya osakhulupirika, Aedomu ankhanza, Asuri achiwawa komanso Ababulo. Komatu zipembedzo zonse zonyenga zidzawonongedwa chisautso chachikulu chikadzangoyamba kumene, chakumayambiriro kwa tsiku la Yehova. Kenako amalonda limodzi ndi andale omwe akuchita chigololo ndi zipembedzo zonyengazi, nawonso adzawonongedwa mkati mwa “tsiku lalikulu ndi lochititsa mantha la Yehova” limeneli.—Yoweli 2:31.
KHALANI OKONZEKA
17, 18. (a) N’chifukwa chiyani Amosi ananena kuti, “Tsoka kwa anthu amene akulakalaka tsiku la Yehova”? (b) Kodi n’chiyani chidzachitikire anthu amene sanakonzekere tsiku la Yehova?
17 Popeza kuti mauthenga achiweruzo akukhudza kwambiri zipembedzo zonyenga, Akhristu ena angaganize kuti iwo sadzakhudzidwa, maulosi amenewa akamadzakwaniritsidwa. Komabe, zimene Amosi anauza Aisiraeli n’zothandiza kwambiri kwa aliyense. Iye anati: “Tsoka kwa anthu amene akulakalaka tsiku la Yehova!” Aisiraeli ena a m’nthawi ya Amosi ankaganiza kuti tsiku la Yehova lidzawabweretsera madalitso okhaokha, ndipo ankakhulupirira kuti Mulungu adzabweretsa tsikuli kuti ateteze anthu ake basi. Ndipotu iwo ankachita kulakalaka kuti tsikuli libwere mofulumira. Ngakhale kuti iwo ankaganiza choncho, Amosi ananena kuti kwa anthu onse odzikonda, tsikuli lidzakhala “lamdima osati kuwala.” Zoonadi, Aisiraeli amenewo anayenera kulandira mkwiyo wa Yehova, mosiyana ndi zimene iwo ankayembekezera.—Amosi 5:18.
18 Kenako Amosi anafotokoza zimene zidzachitike kwa anthu amene ankalakalaka tsiku la Yehova. Iye anayerekezera zimene zidzachitikire anthu amenewa ndi zomwe zingachitike kwa munthu yemwe akuthawa mkango koma n’kukumana ndi chimbalangondo. Pothawa chimbalangondocho, munthuyo akulowa m’nyumba n’kutseka chitseko. Ali wefuwefu, iye akutsamira khoma koma kenako njoka ikumuluma. Zidzakhalanso chimodzimodzi ndi anthu omwe sanakonzekere tsiku la Yehova.—Amosi 5:19.
19. Kodi tiyenera kukonzekera motani tsiku la Yehova?
19 Kodi mukutha kuona kuti nkhaniyi ndi yothandiza kwambiri kwa inu? Kumbukirani kuti uthenga wa Amosi umenewu unkapita kwa anthu amene anali odzipereka kwa Mulungu ndipo anali naye pa ubwenzi wapadera. Komabe, panali zinthu zina zimene anthuwo anafunika kusintha, monga zochita zawo komanso khalidwe lawo. Choncho, ifenso masiku ano m’pofunika kuti tiziunika bwinobwino moyo wathu kuti tione mbali zimene tikufunikira kusintha n’cholinga choti tisonyeze kuti tikukonzekera tsiku lofunika kwambiri limeneli. Koma kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife okonzekadi? N’zodziwikiratu kuti tiyenera kukonzekera mosiyana ndi mmene amachitira munthu yemwe akukonzekera kuthawa m’dera lina, mwina chifukwa cha tsoka lachilengedwe. Munthu wotero amasunga chakudya, madzi abwino, ndalama kapenanso amaphunzira kumanga msasa kapena tenti, yomwe angamakhalemo akathawa kwawo. Zefaniya ananena kuti: “Siliva kapena golide wawo sadzawapulumutsa pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.” Choncho kukhala okonzeka sikukutanthauza kusunga zinthu zenizeni. (Zefaniya 1:18; Miyambo 11:4; Ezekieli 7:19) M’malomwake, tiyenera kukhala tcheru mwauzimu ndipo moyo wathu watsiku ndi tsiku uzisonyeza kuti ndife okonzekadi. Zimene timachita tsiku ndi tsiku zizisonyeza kuti tili ndi mtima wabwino. Mika ananena kuti: “Ine ndidzadikirira Yehova. Ndidzayembekezera moleza mtima Mulungu wa chipulumutso changa.”—Mika 7:7.
20. Kodi n’chiyani chimene sichingasinthe mmene timaonera nkhani ya kukhala okonzeka?
20 Ngati inunso mukuyembekezera tsiku la Yehova moleza mtima, zochita zanu za tsiku ndi tsiku zidzasonyeza kuti ndinu wokonzeka. Simudzadera nkhawa za nthawi yeniyeni imene tsiku la Yehova lidzafike, kapena kuda nkhawa kuti mwakhala mukudikirira kwa nthawi yaitali. Maulosi onse onena za tsiku limeneli adzakwaniritsidwa pa nthawi imene Yehova akuona kuti ndi yoyenerera, ndipo tsiku limeneli silidzachedwa. Yehova anauza mneneri Habakuku kuti: “Masomphenyawa akuyembekezera nthawi yake yoikidwiratu ndipo akuthamangira kumapeto kwake. Zimene zili m’masomphenyazi si zonama. Ngakhale masomphenyawa atazengereza [malinga n’kuona kwa anthu], uziwayembekezerabe chifukwa adzakwaniritsidwa ndithu. Iwo sadzachedwa [malinga n’kuona kwa Yehova].”—Habakuku 2:3.
21. Kodi zimene tiphunzire m’buku lino zikuthandizani bwanji?
21 M’buku lino, muphunzira mmene mungasonyezere kuti mukuyembekezera moleza mtima Mulungu wa chipulumutso chanu. Kodi buku lino likuthandizani bwanji? M’buku lino, tikambirana kwambiri za mabuku ena a m’Baibulo, omwe mwina simunawazolowere kwambiri. Mabuku amenewa ndi ang’onoang’ono, omwe akuyambira pa Hoseya mpaka Malaki, ndipo analembedwa ndi aneneri 12. Motero, muphunzira mfundo zambiri zochititsa chidwi. Mwachitsanzo, m’Gawo 2, muphunzira zimene mungachite kuti ‘muyesetse kuyandikira kwa Yehova’ n’cholinga choti mupitirize kukhala ndi moyo. (Amosi 5:4, 6) Kudzera m’mabuku 12 amenewa, mungadziwe zimene mungachite kuti mum’dziwe bwino Yehova komanso kufunika komutumikira. Mungadziwenso zimene mungachite kuti muwonjezere utumiki wanu. Mothandizidwa ndi mabuku a aneneri amenewa, sitikukayikira kuti mumvetsa bwino kwambiri makhalidwe amene Yehova ali nawo. M’Gawo 3, mumvetsa bwino zimene Yehova amayembekezera kuti inuyo muzichita pamene mukuchita zinthu ndi anthu a pa banja panu ndiponso anthu ena. Zimenezi zingakuthandizeni kuti mukonzekere tsiku lake lalikulu. Pomaliza, m’Gawo 4, muphunzira malangizo amene aneneriwa anapereka, okhudza mtima umene muyenera kukhala nawo pamene tsiku la Yehova latsala pang’ono kwambiri kufika. Muphunziranso mmene malangizo a aneneriwo angakhudzire utumiki wanu wachikhristu. Mosakayikira, musangalala kwambiri pamene mukuphunzira mauthenga amene aneneriwa analemba, omwe akukhudza kwambiri tsogolo lanu.
22. Kodi muyenera kuchita chiyani potsatira malangizo omwe ali m’mabuku 12 a aneneri?
22 Kodi mukukumbukira mawu a Zefaniya osonyeza kuti tsiku la Yehova lili pafupi kwambiri, omwe ali m’ndime yoyambirira ya nkhani ino? (Zefaniya 1:14) Uthenga wake unakhudza kwambiri moyo wa Mfumu Yosiya, yemwe pa nthawiyo anali mnyamata. Ali ndi zaka 16 zokha, Yosiya anayamba kufunafuna Yehova. Atafika zaka 20, anayamba ntchito yapadera yothetsa kulambira mafano. Iye anayamba ntchitoyi mogwirizana ndi uthenga umene Zefaniya anauza anthu a ku Yuda ndiponso ku Yerusalemu. (2 Mbiri 34:1-8; Zefaniya 1:3-6) Kodi uthenga wochenjeza wonena za tsiku la Yehova umakukhudzani kwambiri pa moyo wanu watsiku ndi tsiku ngati mmene unakhudzira moyo wa Yosiya? M’nkhani yotsatirayi tiona mmene uthenga wa aneneri 12 amenewa ungathandizire munthu aliyense payekha.
a Mneneri Yesaya komanso Ezekieli anachenjeza za tsiku la Yehova. Yesaya anakhala ndi moyo pa nthawi imodzi ndi aneneri ngati Hoseya ndi Mika ndipo Ezekieli anakhala ndi moyo pa nthawi imodzi ndi aneneri ngati Habakuku ndi Obadiya.—Yesaya 13:6, 9; Ezekieli 7:19; 13:5; werengani ndime 4 mpaka 6, m’Mutu 2 wa buku lino.
b Kuti mupeze umboni wina wotsimikizira kuti anthu oopa Mulungu zinthu zidzawayendera bwino pa tsiku la Yehova, werengani Hoseya 6:1; Yoweli 2:32; Obadiya 17; Nahumu 1:15; Habakuku 3:18, 19; Zefaniya 2:2, 3; Hagai 2:7; Zekariya 12:8, 9; ndiponso Malaki 4:2.
c Ena mwa aneneri 12 amenewa analosera za kuwonongedwa kwa mitundu ingapo, osati mtundu umodzi wokha.