MUTU 6
Kuchita Zinthu ‘Mwachilungamo’ N’kofunika Kwambiri Kuti Timudziwe Mulungu
1. N’chifukwa chiyani inuyo mwachibadwa mumafuna zinthu zachilungamo?
KUYAMBIRA kale kwambiri, nthawi zonse padzikoli pakhala pakupezeka anthu odziwika bwino pa nkhani yolimbikitsa chilungamo. Koma taganizirani mfundo iyi: Anthu amakonda chilungamo chifukwa analengedwa m’chifaniziro cha Mulungu. Mwachibadwa, inuyo mumafuna kuchita zinthu mwachilungamo ndiponso mumafuna kuti ena azikuchitirani zinthu mwachilungamo chifukwa munalengedwa m’chifaniziro cha Yehova, yemwe ndi Mulungu amene ‘amasangalala’ ndi chilungamo.—Yeremiya 9:24; Genesis 1:27; Yesaya 40:14.
2, 3. N’chifukwa chiyani tiyenera kuphunzira mabuku 12 a aneneri ngati tikufuna kudziwa mfundo za chilungamo cha Yehova?
2 Mukamawerenga mabuku osiyanasiyana a m’Baibulo, mungadziwe mfundo zokhudza chilungamo cha Mulungu. Koma mungadziwe mfundo zambiri zokhudza chilungamo ngati mutaphunzira mabuku a aneneri 12. Nkhani yokhudza chilungamo yatchulidwa mobwerezabwereza m’mabuku amenewa moti bungwe linalake lofalitsa Mabaibulo, linatulutsa buku lamutu wakuti Chilungamo Chichitike! (Justice Now!) Bukuli limafotokoza nkhani za m’mabuku a Hoseya, Amosi ndi Mika. Mwachitsanzo, taonani zimene Amosi analemba polimbikitsa anthu kuchita chilungamo. Iye anati: “Chilungamo chiyende ngati madzi ndiponso ngati mtsinje wosaphwa nthawi zonse.” Komanso taonani mfundo imene Mika anaiika koyambirira pa zinthu zimene inuyo muyenera kuchita. Iye anati: “Kodi Yehova akufuna chiyani kwa iwe? Iye akufuna kuti uzichita chilungamo, ukhale wokoma mtima ndiponso uziyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.”—Amosi 5:24; Mika 6:8.
3 Choncho, kuti timudziwe bwino Yehova komanso kuti tithe kumutsanzira, tikufunikira kumvetsa bwino mfundo zake zachilungamo. Chilungamo ndi khalidwe limodzi mwa makhalidwe akuluakulu a Yehova, choncho sitinganene kuti timamudziwa ngati sitimamvetsa bwino za chilungamo chakechi. Zoonadi, tikufunika kumvetsa bwino chilungamo cha Mulungu chifukwa ngakhalenso atumiki ake akale ankadziwa kuti “Yehova amakonda chilungamo.”—Salimo 33:5; 37:28.
4. Fotokozani chifukwa chake mabuku a aneneri 12 angakuthandizeni kuti muzikhulupirira kwambiri zoti Mulungu ndi wachilungamo.
4 Nthawi ina yake Yehova asanapereke chiweruzo pa Yerusalemu, mneneri Habakuku anafunsa kuti: “Inu Yehova, kodi ndidzalirira thandizo . . . kufikira liti? . . . Lamulo latha mphamvu ndipo anthu sakuchitanso chilungamo. Chilungamo chapotozedwa chifukwa anthu oipa akupondereza anthu olungama.” (Habakuku 1:2, 4) Habakuku, yemwe anali wokhulupirika, anamudziwa bwino Yehova kudzera m’Malemba amene analipo pa nthawiyo komanso zimene zinamuchitikira pa moyo wake. Motero, iye ankakhulupirira kuti Mulungu amalimbikitsa chilungamo. Komabe, mneneriyu ankafuna kudziwa chifukwa chake Yehova amalolera kuti zoipa zizichitika. Mulungu anatsimikizira Habakuku kuti adzachita zinthu mwachilungamo kwa anthu onse okhulupirika. (Habakuku 2:4) Ngati Habakuku ndiponso anthu ena ankakhulupirira mfundo imeneyi, inunso muli ndi zifukwa zomveka zokhulupirira kuti Mulungu adzachita zimenezi. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti tsopano tili ndi Baibulo lonse lathunthu ndipo mungathe kuwerenga nkhani zambiri zokhudza mmene Yehova wakhala akusonyezera makhalidwe ake, monga chilungamo. Choncho inuyo muli ndi mwayi waukulu woti mungamudziwe bwino Yehova n’kuyamba kukhulupirira zoti iye amachita zinthu mwachilungamo nthawi zonse.
5. Kodi uthenga womwe Yehova anauza anthu kudzera mwa aneneri 12 ukutilimbikitsa kuchita chiyani?
5 Pamene Yehova ankauza atumiki ake kuti akapereke uthenga kwa Aisiraeli, anawauza kuti akatsindike mfundo yakuti ayenera kumachita zinthu mwachilungamo. (Yesaya 1:17; 10:1, 2; Yeremiya 7:5-7; Ezekieli 45:9) Yehova anauzanso aneneri 12 kuti azitsindika mfundoyi mu uthenga wawo. (Amosi 5:7, 12; Mika 3:9; Zekariya 8:16, 17) Munthu aliyense amene angawerenge mabuku awo, angaone kuti aneneriwa ankalimbikitsa anthu kuchita zinthu mwachilungamo pa moyo wawo watsiku ndi tsiku. Masiku ano, tingagwiritse ntchito mfundo za m’mabuku 12 a aneneriwa m’njira zambiri. Koma tiyeni tikambirane mbali ziwiri zimene aneneriwo anatsindika zokhudza zinthu zomwe anthu ankayenera kuchita mwachilungamo, ndipo kenako tiona zimene ifeyo tingachite potsatira malangizo amenewo.
TIZISONYEZA CHILUNGAMO PA NKHANI ZAMALONDA NDIPONSO ZOKHUDZA NDALAMA
6, 7. N’chifukwa chiyani tonsefe tiyenera kuona kuti chilungamo n’chofunika kwambiri pa nkhani za malonda ndi zokhudza ndalama?
6 Yesu anati: “Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha.” (Luka 4:4; Deuteronomo 8:3) Apa Yesu sanatsutse zoti timafunikira chakudya. Ndipotu anthu ambiri amagwira ntchito, kapena munthu wina m’banja mwawo amagwira ntchito n’cholinga choti azipeza chakudya. Nawonso atumiki a Mulungu akale ankachita chimodzimodzi. Mwachitsanzo, ena ankagwira ntchito zosachita kulembedwa, monga ulimi, ukalipentala, kuwomba nsalu ndi kusoka zovala, ndiponso kuumba ziwiya zakukhitchini. Anthu ena ankalemba anzawo ntchito kapena ganyu, monga yokolola mbewu, yopera ufa, yopanga mafuta a maolivi, kapena yopanga vinyo. Komanso panali ena omwe ankachita malonda ogula ndi kugulitsa zinthu zosiyanasiyana. Anthu enanso ankagwira ntchito zina, monga kukonza madenga a nyumba kapena kuimba zipangizo zosiyanasiyana zoimbira nyimbo.—Ekisodo 35:35; Deuteronomo 24:14, 15; 2 Mafumu 3:15; 22:6; Mateyu 20:1-8; Luka 15:25.
7 Kodi mukutha kuona kuti zimenezi zikufanana ndi zimene mumachita pa moyo wanu, mwinanso zimene anzanu kapena achibale anu amachita? N’zoona kuti mmene timagwirira ntchito masiku ano, n’zosiyana ndi mmene anthu kalelo ankachitira. Koma kodi simukuvomereza zoti Mulungu amaonabe kuti anthu ayenera kuchita chilungamo pa nkhani ngati zimenezi? Mauthenga amene Yehova anapereka kudzera mwa aneneri 12, anasonyeza kuti iye amafuna kuti anthu ake azichita zinthu mwachilungamo pa nkhani zokhudza ntchito, malonda ndiponso ndalama. Tikamakambirana zitsanzo za nkhani zimenezi, muziganizira mmene nkhaniyo ikukukhudzirani ndiponso mmene mungagwiritsire ntchito malangizo ake kuti muzichita zinthu mwachilungamo.—Salimo 25:4, 5.
8, 9. (a) Malinga ndi lemba la Malaki 3:5, n’chifukwa chiyani kuchita zachinyengo kuli koopsa kwambiri? (b) Kodi Malemba amalimbikitsa olemba anthu ntchito komanso olembedwa ntchito kuti aziyembekezera zotani pa ntchito?
8 Kudzera mwa mneneri Malaki, Mulungu analengeza kuti: “Anthu inu ndidzakuyandikirani kuti ndikuweruzeni. Sindidzazengereza kupereka umboni wotsutsa amatsenga, achigololo, olumbira monama komanso ochita chinyengo pa malipiro a munthu waganyu. . . . Anthu amenewa sakundiopa.” (Malaki 3:5) Apa Yehova anadzudzula anthu omwe ankachitira chinyengo anthu amene anawalemba ntchito kapena ganyu. Kodi kuchita chinyengo koteroko kunali koopsa bwanji? Yehova anasonyeza kuti kuchitira chinyengo wantchito n’kofanana ndi machimo ena akuluakulu, monga kukhulupirira mizimu, chigololo ndiponso bodza. Ndipo Akhristu amadziwa kuti Mulungu adzaweruza “adama, ochita zamizimu, opembedza mafano, ndi onse abodza.”—Chivumbulutso 21:8.
9 Zimene zinkachitika pa nkhani yokhudza ntchito pa nthawiyo, sinali nkhani yongokhudza kuphwanya mfundo za makhalidwe abwino basi, koma zinkakhudzanso chilungamo cha Yehova. Mulungu ananena kuti chifukwa anthu ‘ankachita chinyengo pa malipiro a munthu waganyu, adzawayandikira kuti awaweruze.’ Koma Mulungu sananene kuti munthu amene ali ndi antchito ayenera kumangochita chilichonse chimene wantchito kapena antchitowo angapemphe. Fanizo la Yesu la anthu aganyu amene anakagwira ntchito m’munda wampesa, likusonyeza kuti wolemba anthu ntchito ali ndi mphamvu zoika malipiro amene azipatsa antchito akewo komanso kuwauza zoyenera kuchita pogwira ntchitoyo. (Mateyu 20:1-7, 13-15) Tikuona kuti m’fanizo la Yesuli, wantchito aliyense anapatsidwa dinari imodzi, kaya anagwira ntchitoyo tsiku lonse kapena ayi. Dinari imodzi inali malipiro amene anagwirizana kuti aliyense azipatsidwa “pa tsiku.” Tikuonanso kuti wolemba anthu ntchitoyu sanachitire antchitowo zinthu zopanda chilungamo kuti apeze phindu mwachinyengo.—Yeremiya 22:13.
10. N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala ndi mmene timachitira zinthu ndi anthu amene tinawalemba ntchito kapena ganyu?
10 Ngati muli ndi bizinezi ndipo muli ndi antchito, kapena mumalemba anthu ganyu, kodi mumawapatsa malipiro awo pa nthawi yake? Kodi malipiro amene mumawapatsa komanso zinthu zimene mumawauza kuti achite, zikugwirizana ndi mfundo zachilungamo za pa Malaki 3:5? Ndi bwino kuganizira zimenezi chifukwa nkhani yochitira antchito zinthu zopanda chilungamo yafotokozedwanso m’Malemba Achigiriki. Ponena za anthu amene amachitira antchito awo zinthu zopanda chilungamo, mtumwi Yakobo ananena kuti, ‘Yehova akuwatsutsa.’ (Yakobo 5:1, 4, 6) Motero, sitikulakwitsa ngati titanena kuti anthu amene amachita zinthu mopanda chilungamo pa nkhani yokhudza “malipiro a munthu waganyu” sanafike pomudziwa bwino Yehova, chifukwa sakutsanzira chilungamo chake.
11, 12. (a) Kodi ndi zinthu ziti zopanda chilungamo zimene zatchulidwa pa lemba la Hoseya 5:10? (b) Kodi inuyo mungagwiritse ntchito bwanji mfundo yopezeka pa Hoseya 5:10?
11 Tsopano taonani chifukwa chake Yehova analankhula motsutsana ndi anthu ena otchuka m’nthawi ya Hoseya. Kudzera mwa Hoseya, Yehova anati: “Akalonga a Yuda akhala ngati anthu osuntha malire. Ndidzawakhuthulira mkwiyo wanga ngati madzi.” (Hoseya 5:10) N’chifukwa chiyani Hoseya anadzudzula anthuwo? Kalelo, mlimi aliyense ku Yuda ankadalira kwambiri malo ndiponso munda wake, ndipo m’malire mwake ankaikamo miyala kapena zikhomo. Choncho ‘kusuntha malire’ kunali kubera mlimiyo malo ake chifukwa kunkachepetsa munda wake womwe ankaudalira kwambiri pa moyo wake. Hoseya anayerekezera akalonga a ku Yuda, omwe ankafunika kulimbikitsa chilungamo, ndi anthu amene ankasuntha malire pobera anthu ena.—Deuteronomo 19:14; 27:17; Yobu 24:2; Miyambo 22:28.
12 Masiku ano, anthu ena amene amachita malonda ogula ndi kugulitsa nyumba kapena malo, angaganize ‘zosuntha malire’ a malowo kuti abere anthu ogula. Komabe mfundoyi ikugwira ntchito kwa aliyense, monga ochita malonda, olemba anzawo ntchito, olembedwa ntchito, kapenanso munthu amene angapereke ndalama kwa ena kuti amuthandize pa zinthu zina. Monga mukudziwira, ena amazengereza kusainirana pa nkhani zamalonda n’cholinga choti m’tsogolo, asadzavutike kuchita zinthu zochepa poyerekezera ndi zimene anagwirizana, kapena kuwonjezera zinthu zina pa zimene anagwirizana kale. Ena amalemba ndi kusainirana ndithu akamachita malonda kapena akamalemba ena ntchito. Komabe, nthawi zambiri m’malo ena amalemba dala zinthu zosamveka kapena zosaoneka bwino, n’cholinga choti winayo asamvetse bwino zimene akugwirizanazo pofuna kuti m’tsogolo adzam’chitire zinthu mwachinyengo. Kodi mukuganiza kuti munthu wochita zinthu zimenezi, kaya ndi wogulitsa malonda kapena wogula, bwana kapena wantchito, akumudziwadi bwino Mulungu yemwe ndi wachilungamo? Kudzera m’Mawu ake, Baibulo, Yehova anati: ‘Usasunthire kumbuyo malire a munda wa ana amasiye. Pakuti Wowawombola ndi wamphamvu, ndipo adzawateteza pa mlandu wawo ndi iwe.’—Miyambo 23:10, 11; Habakuku 2:9.
13. Malinga ndi lemba la Mika 6:10-12, kodi pakati pa anthu a Mulungu pankachitika zinthu ziti zopanda chilungamo?
13 Lemba la Mika 6:10-12 likutchulanso mfundo zina pa nkhani ya chilungamo. Lembali limati: “Kodi m’nyumba ya munthu woipa mukupezekabe chuma chopezedwa mopanda chilungamo, ndiponso muyezo woperewera wa efa umene ndi wosaloleka? Kodi ndingakhale woyera ndili ndi sikelo yachinyengo, ndiponso thumba lachinyengo lamiyala yoyezera zinthu? . . . Anthu okhalamo akulankhula zonama ndipo lilime la m’kamwa mwawo ndi lachinyengo.” Ngakhale kuti masiku ano timayeza zinthu pogwiritsa ntchito malita ndi makilogalamu, osati muyezo wa efa, mfundo ya Mika ndi yoonekeratu. Anthu amalonda a m’nthawi imeneyo anali akathyali. Iwo ankachitira anthu zinthu zopanda chilungamo chifukwa sankagwiritsa ntchito masikelo ndi miyala yoyezera yovomerezeka. Mulungu ananena kuti anthu amenewo, omwe ‘lilime la m’kamwa mwawo linali lachinyengo’ omwenso ankachita zachinyengo pa nkhani za malonda, anali ‘anthu oipa.’—Deuteronomo 25:13-16; Miyambo 20:10; Amosi 8:5.
14. Kodi zimene Mika anachenjeza zingatithandize kupewa zinthu ziti zopanda chilungamo zomwe zikuchitika masiku ano?
14 Kodi zimene Mika ananena zokhudza masikelo komanso miyala yoyezera yachinyengo, zikukhudzanso mmene mumayendetsera bizinezi yanu kapena zimene mumachita kuntchito kwanu? Nkhani imeneyi ndi yofunika kuiganizira mofatsa chifukwa chakuti anthu ogula malonda kapena anthu ena amachitiridwa zachinyengo m’njira zambiri. Mwachitsanzo, anthu kapena makampani ena omanga nyumba amagwiritsa ntchito simenti yochepa pomanga nyumba. Kapena mmisiri angagwiritse ntchito zipangizo zina zotsika mtengo komanso zosalimba m’malo amene akuona kuti ndi osaonekera. Anthu ena amalonda amagulitsa zinthu zakale, koma n’kumanena kuti n’zatsopano. Mwina munamvapo za zinthu zina zachinyengo zimene amalonda amachita pofuna kupindula kwambiri pa malonda awo. Kodi inuyo muyenera kuchita nawo zimenezi? Buku lina laposachedwapa lonena za kufunika kokhala wokhulupirika nthawi zonse, linanena kuti a Mboni za Yehova “amakhulupirira kuti Mlengi wawo akuwaona, ndipo ambiri angalolere kufa m’malo mwa kuba.” Bukuli linanenanso kuti: “Makampani amene amagwiritsa ntchito ndalama zambiri amafuna kwambiri anthu amenewa kuti awalembe ntchito.” N’chifukwa chiyani zili choncho? N’chifukwa chakuti Akhristu oona amadziwa kuti Yehova ‘amafuna kuti azichita chilungamo’ pa nkhani zamalonda kapena zokhudza ndalama.—Mika 6:8.
‘AKALONGA ADZALAMULIRA MWACHILUNGAMO’
15, 16. Kodi atsogoleri a m’nthawi ya Mika ankawachitira chiyani anthu a Mulungu?
15 Mungaone m’mabuku 12 a aneneri kuti pa nthawi zina anthu sankachita zinthu mwachilungamo ngakhale pang’ono. Anthu omwe anali ndi maudindo komanso omwe ankafunikira kusonyeza chitsanzo chabwino pochitira anthu zachilungamo, sankachita zimenezo. (Ekisodo 18:21; 23:6-8; Deuteronomo 1:17; 16:18) Choncho Mika anawapempha kuti: “Tamverani inu atsogoleri a mbadwa za Yakobo ndi inu olamulira a nyumba ya Isiraeli. Kodi si inu oyenera kudziwa chilungamo? Inu mumadana ndi zinthu zabwino ndi kukonda zinthu zoipa. Mumasenda khungu la anthu ndi kuchotsa mnofu pamafupa awo.”—Mika 3:1-3; Yesaya 1:17.
16 Mawu amenewa ayenera kuti anadabwitsa kwambiri anthu omwe anali ozolowera moyo wakumudzi. Iwo ankadziwa kuti nthawi zina m’busa amameta ubweya wa nkhosa zomwe akuzisamalira ndi kuziteteza. (Genesis 38:12, 13; 1 Samueli 25:4) Koma “olamulira a nyumba ya Isiraeli,” omwe ankafunikira “kudziwa chilungamo,” sankasamalira bwino anthu a Mulungu ndipo ankakhala ngati akusenda khungu ndi kuchotsa mnofu wa nkhosa komanso kuswa mafupa ake. (Salimo 95:7) Pogwiritsanso ntchito chitsanzo china cha moyo wakumudzi, Mika ananena kuti akalonga omwe ‘ankalandira ziphuphu poweruza,’ anali ngati chitsamba chaminga kapena mpanda wa mitengo yaminga. (Mika 7:3, 4) Taganizirani kuti mukudutsa pakati pa zitsamba zaminga kapena pampanda wa mitengo yaminga. N’zachidziwikire kuti mingayo ingakukaleni komanso ingakole zovala zanu n’kung’ambika. Zimenezi zikutipatsa chithunzi cha zimene olamulira ankachita potsogolera anthu a Mulungu. M’malo mochita zinthu mwachilungamo ndi abale awo, iwo anali achinyengo komanso okonda ziphuphu.—Mika 3:9, 11.
17. Malinga ndi lemba la Zefaniya 3:3, kodi atsogoleri a anthu a Mulungu anali ndi khalidwe lotani?
17 Nayenso Zefaniya anatchula mfundo yofanana ndi imeneyi, pamene anati: “Akalonga ake anali mikango imene inali kubangula. Oweruza ake anali mimbulu yoyenda usiku imene sinatafune mafupa mpaka m’mawa.” (Zefaniya 3:3) Kodi mukutha kuona m’maganizo mwanu atsogoleri a anthu a Mulungu, omwe anali ngati mikango yolusa, akuchita zinthu zopanda chilungamo? Kapena kodi mukutha kuona oweruza omwe anali ngati mimbulu yosusuka, akumeza chilichonse moti pofika m’mawa pakungotsala mafupa okhaokha? Malinga ndi mmene zinthu zinalili pa nthawiyo, zinali zosatheka kuti pakhale chilungamo chifukwa atsogoleri omwe anali ngati mimbulu yosusuka, ankakhadzula anthu m’malo mowasamalira.
18. Kodi oweruza ku Isiraeli ankafunikira kuwachitira chiyani anthu a Mulungu?
18 N’zoonekeratu kuti atsogoleri amenewo, amene anali mumtundu wosankhidwa ndi Mulungu, sankamudziwa Mulunguyo. Akanakhala kuti ankamudziwa, akanamvera mawu amene Zekariya analemba, akuti: “Anthu inu muzichita zinthu izi: Muzilankhulana zoona zokhazokha. Poweruza milandu m’zipata za mizinda yanu, muziweruza mogwirizana ndi choonadi komanso molimbikitsa mtendere.” (Zekariya 8:16) Ku Isiraeli, akulu a mumzinda ankakumana pachipata cha mzinda pamene ankaweruza milandu. Iwo ankafunika kuweruza osati mongotengeka maganizo atangomvetsera mbali imodzi yokha ya mlanduwo, koma mogwirizana ndi mfundo za Mulungu. (Deuteronomo 22:15) Komanso Yehova anali atawachenjeza kuti asamaweruze mokondera munthu aliyense, kaya ndi wolemera, wotchuka kapena munthu wamba. (Levitiko 19:15; Deuteronomo 1:16, 17) Oweruzawo anayenera ‘kuweruza mogwirizana ndi mtendere’ kuti athandize anthu omwe anasemphana maganizo n’cholinga choti ayambenso kukhala mwamtendere.
19, 20. (a) N’chifukwa chiyani akulu achikhristu angaphunzire zambiri m’mabuku a aneneri 12? (b) Kodi akulu angasonyeze bwanji kuti amadziwa Yehova ndiponso chilungamo chake?
19 Pamene mtumwi Paulo ankalembera kalata Akhristu ena, anatchula mfundo ina yopezeka pa Zekariya 8:16. (Aefeso 4:15, 25) Choncho zimenezi zikutithandiza kukhulupirira kuti machenjezo ndiponso malangizo onena za chilungamo amene ali m’mabuku a aneneri 12, angagwirenso ntchito mumpingo masiku ano. Akulu, kapena kuti oyang’anira, ayenera kupereka chitsanzo chabwino pa nkhani yodziwa Yehova ndiponso kutsatira mfundo zake zachilungamo. Lemba la Yesaya 32:1 limanena kuti iwo ndi “akalonga” amene ayenera kuchita zinthu “mwachilungamo.” Kodi ndi mfundo ziti zothandiza akulu zimene tingapeze m’machenjezo ndi malangizo opezeka m’mabuku 12 a aneneri?
20 Akulu achikhristu ayenera kuganizira mfundo za choonadi cha m’Malemba kuti adziwe mmene Yehova amaganizira pa nkhani zosiyanasiyana. Akafuna kusankha zochita, iwo ayenera kuganizira mfundo zimenezo m’malo mongodalira maganizo awo kapena m’malo mochita zimene akuona kuti n’zolondola. Baibulo limasonyeza kuti nthawi zina iwo angafunike kuweruza milandu yovuta, yomwe ingafunike nthawi yambiri yokonzekera. Pa milandu ngati imeneyi, mkulu aliyense angafunike nthawi yambiri yofufuza mfundo za m’Baibulo komanso malangizo othandiza opezeka m’mabuku ofalitsidwa ndi gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. (Ekisodo 18:26; Mateyu 24:45) Akulu akamayesetsa kuchita zinthu zimenezi mwakhama, zidzakhala zosavuta kuti azichita zinthu zogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna, monga kudana ndi zoipa komanso kukonda zabwino. Zimenezi zidzawathandiza kuti ‘azichita zinthu zachilungamo pachipata cha mzinda,’ kutanthauza kuti ‘azichita chilungamo chenicheni poweruza milandu.’—Amosi 5:15; Zekariya 7:9.
21. N’chifukwa chiyani akulu ayenera kupewa kukondera, komabe nthawi zina angayesedwe bwanji kuti achite zinthu mokondera?
21 Nthawi zina anthu amene ali ndi udindo woweruza angachite zinthu mokondera akamaweruza milandu ngakhale kuti akudziwa mfundo za m’Baibulo. Malaki anadandaula kwambiri chifukwa ansembe, amene ankayenera kuphunzitsa ena kuti adziwe Mulungu, anali “kukondera pa nkhani zokhudza chilamulo.” (Malaki 2:7-9) Kodi iwo ankachita bwanji zimenezi? Mika ananena kuti atsogoleri ena ‘sankaweruza asanalandire chiphuphu ndipo ansembe ankangophunzitsa kuti apeze malipiro.’ (Mika 3:11) Kodi n’chiyani chingachititse mkulu kuti aziganizanso choncho masiku ano? Pali zinthu zambiri. Mwachitsanzo, mkulu angachite zimenezi ngati akuweruza mlandu wa munthu amene m’mbuyomu, wakhala akum’patsa zinthu zambiri kapena kumuchitira zinthu zina zabwino. Mwinanso mkuluyo angaone kuti akhoza kudzathandizidwa ndi munthuyo m’tsogolo. Nthawi zinanso mkulu angafunike kuweruza mlandu womwe ukukhudzanso wachibale wake. Kodi iye adzaweruza moganizira kwambiri za chibalecho kapena mfundo za m’Baibulo? Mkulu angayesedwe kuti achite zinthu mokondera ngati akuweruza milandu kapena pamene akufunika kuona ngati m’bale wina akukwaniritsa mfundo za m’Malemba zimene zingamuchititse kuti apatsidwe udindo wina mumpingo.—1 Samueli 2:22-25, 33; Machitidwe 8:18-20; 1 Petulo 5:2.
22. (a) Kodi akulu ali ndi udindo wotani pa nkhani yosonyeza chilungamo? (b) Kodi akulu ayenera kusonyeza makhalidwe ena ati opezeka m’Mawu a Mulungu, akamachita zinthu ndi munthu wolakwa?
22 Munthu wina akachita tchimo lalikulu, abusa auzimu mumpingo amayesetsa kutetezera mpingowo kuti usaipitsidwe. (Machitidwe 20:28-30; Tito 3:10, 11) Koma ngati wochimwayo walapa moona mtima, akulu amayesetsa “kumuthandiza munthu woteroyo ndi mzimu wofatsa.” (Agalatiya 6:1) M’malo mochita zinthu mouma mtima, iwo amatsatira malangizo akuti: “Muzichita chilungamo chenicheni poweruza milandu. Muzisonyezana kukoma mtima kosatha ndi chifundo.” (Zekariya 7:9) Malamulo amene Yehova anapereka pa nkhani yoweruza milandu ku Isiraeli, amapereka umboni wotsimikizira kuti iye ndi wachilungamo komanso wachifundo. Pa milandu yambiri yomwe oweruza a m’nthawiyo ankaweruza, iwo anali ndi ufulu ndithu woweruza malinga ndi mmene nkhaniyo inalili. Choncho iwo akanatha kusonyeza chifundo kwa munthu wochimwa, malinga ndi mmene mlandu wake unalili komanso mtima umene iye anasonyeza. Masiku anonso, oyang’anira achikhristu ayenera kuyesetsa kuweruza mwa “chilungamo chenicheni” ndiponso kusonyeza “kukoma mtima kosatha ndi chifundo.” Akamachita zimenezi, iwo angasonyeze kuti akumudziwadi Yehova.
23, 24. (a) Kodi akulu angatani kuti ‘aziweruza molimbikitsa mtendere’? (b) Kodi mabuku a aneneri 12 akuthandizani kumvetsa chiyani pa nkhani ya chilungamo?
23 Kumbukirani lemba la Zekariya 8:16, lomwe limati: “Poweruza milandu m’zipata za mizinda yanu, muziweruza mogwirizana ndi choonadi komanso molimbikitsa mtendere.” N’chifukwa chiyani Yehova anauza Zekariya kulemba mfundo imeneyi? Iye ankafuna kuti anthu ‘aziweruza molimbikitsa mtendere.’ Ngakhale m’nthawi ya atumwi, nthawi zina Akhristu ena ankasemphana maganizo, kapena kukangana kumene. Monga mmene Paulo anathandizira Eodiya ndi Suntuke, masiku ano akulu angafunikenso kuthandiza Akhristu omwe asemphana maganizo. (Afilipi 4:2, 3) Akulu ayenera kuyesetsa mwakhama kuti ‘aziweruza molimbikitsa mtendere,’ kapena kuti kuthandiza Akhristu omwe anasemphana maganizo kuti ayambenso kugwirizana. Uphungu wa m’Malemba umene iwo amapereka ndiponso mtima umene amasonyeza akamapereka uphunguwo, ziyenera kulimbikitsa mtendere mumpingo komanso mtendere ndi Mulungu. Akulu akamachita zimenezi, adzasonyeza kuti amadziwadi Yehova ndiponso chilungamo chake.
24 M’nkhaniyi takambirana mfundo ziwiri, zomwe ndi kuchita chilungamo pa nkhani za malonda ndi zokhudza ndalama komanso kuchita chilungamo poweruza milandu. Mfundo zimenezi zikusonyeza kuti tonsefe tiyenera kutsatira malangizo opezeka m’mabuku a aneneri 12, onena za kufunika kochita zinthu mwachilungamo. Choncho, timasangalala ndi madalitso ochuluka ngati ifeyo ndiponso anthu omwe timachita nawo zinthu zosiyanasiyana, timayesetsa kuchita zinthu ‘mwachilungamo.’