Hoseya
12 “Efuraimu akudya mphepo.
Akuthamangitsa mphepo yakumʼmawa tsiku lonse.
Iye akuchulukitsa mabodza ndi chiwawa.
Wachita pangano ndi Asuri+ ndipo wapititsa mafuta ku Iguputo.+
2 Pali mlandu umene Yehova akufuna kuimba Yuda.+
Adzalanga Yakobo mogwirizana ndi njira zake.
Ndipo adzamubwezera mogwirizana ndi zochita zake.+
3 Pamene Yakobo anali mʼmimba anagwira chidendene cha mʼbale wake.+
Iye analimbana ndi Mulungu ndi mphamvu zake zonse.+
4 Anapitiriza kulimbana ndi mngelo ndipo anapambana.
Analira komanso anachonderera kuti amudalitse.”+
Mulungu anamupeza ku Beteli ndipo kumeneko Mulungu analankhula nafe.*+
5 Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba,+
Amakumbukiridwa ndi dzina lakuti Yehova.+
6 “Choncho bwerera kwa Mulungu wako.+
Uzisonyeza chikondi chokhulupirika ndi chilungamo,+
Ndipo nthawi zonse uziyembekezera Mulungu wako.
Pa ntchito zanga zonse, palibe amene angapeze cholakwa kapena tchimo.’
9 Koma ine ndine Yehova Mulungu wako kuchokera pamene unali ku Iguputo.+
Ndidzakuchititsa kukhalanso mʼmatenti,
Ngati pa masiku achikondwerero.
10 Ndinalankhula ndi aneneri,+
Ndipo ndinawaonetsa masomphenya ambiri.
Ndinalankhula mafanizo kudzera mwa aneneri.
11 Ku Giliyadi anthu akuchita zachinyengo*+ ndiponso akulankhula mabodza.
Ku Giligala, akupereka nsembe ngʼombe zamphongo.+
Ndipo maguwa awo ansembe ali ngati milu yamiyala mʼmunda.+
12 Yakobo anathawira mʼdera la Aramu.*+
Ndipo Isiraeli+ ankagwira ntchito kumeneko kuti apeze mkazi,+
Ankalondera nkhosa kuti apeze mkazi.+